Yesaya
40 “Limbikitsani anthu anga. Ndithu alimbikitseni,” akutero Mulungu wanu.+
2 “Mulankhuleni Yerusalemu momufika pamtima.*
Muuzeni kuti ntchito imene ankagwira mokakamizidwa yatha,
Komanso kuti malipiro a zolakwa zake aperekedwa.+
Kuchokera mʼdzanja la Yehova, iye walandira malipiro okwanira* a machimo ake onse.”+
3 Winawake akufuula mʼchipululu kuti:
“Konzani njira ya Yehova!+
Mulungu wathu mukonzereni msewu wowongoka+ wodutsa mʼchipululu.+
4 Chigwa chilichonse chikwezedwe mʼmwamba,
Ndipo phiri lililonse ndi chitunda chilichonse zitsitsidwe.
Malo okumbikakumbika asalazidwe,
Ndipo malo azitunda akhale chigwa.+
5 Ulemerero wa Yehova udzaonekera,+
Ndipo anthu onse adzauonera limodzi,+
Chifukwa pakamwa pa Yehova panena.”
6 Tamvera! Winawake akunena kuti: “Lengeza mofuula!”
Wina akufunsa kuti: “Ndilengeze mofuula za chiyani?”
“Anthu onse ali ngati udzu wobiriwira.
Chikondi chawo chonse chokhulupirika chili ngati duwa lakutchire.+
Ndithu anthu ali ngati udzu wobiriwira.
Fuula mwamphamvu,
Iwe mkazi amene ukubweretsa uthenga wabwino wonena za Yerusalemu.
Fuula, usachite mantha.
Lengeza kumizinda ya ku Yuda kuti: “Mulungu wanu ali nanu.”+
10 Taonani! Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, adzabwera nʼkuonetsa mphamvu zake,
Mphoto yake ili ndi iyeyo,
Ndipo malipiro amene amapereka ali pamaso pake.+
11 Iye adzasamalira* gulu la nkhosa zake ngati mʼbusa.+
Ndi dzanja lake, adzasonkhanitsa pamodzi ana a nkhosa,
Ndipo adzawanyamulira pachifuwa pake.
Nkhosa zimene zikuyamwitsa adzazitsogolera mwachikondi.+
12 Ndi ndani anayezapo madzi onse amʼnyanja pachikhatho cha dzanja lake?+
Ndi ndani anayezapo kumwamba ndi dzanja lake?
Ndi ndani anasonkhanitsapo fumbi lonse lapadziko lapansi mʼmbale yoyezera+
Kapena kuyeza mapiri pachoyezera
Komanso zitunda pasikelo?
13 Ndi ndani amene anayezapo* mzimu wa Yehova,
Ndipo ndi ndani amene angamulangize ngati mlangizi wake?+
14 Kodi anafunsirapo nzeru kwa ndani kuti amuthandize kumvetsa zinthu?
Ndi ndani amene amamuphunzitsa njira yachilungamo,
Kapena kumuphunzitsa kuti adziwe zinthu,
Kapenanso kumusonyeza njira yokhalira womvetsadi zinthu?+
15 Taonani! Mitundu ya anthu ili ngati dontho la madzi lochokera mumtsuko,
Ndipo iye amawaona ngati fumbi limene lili pasikelo.+
Iyetu amanyamula zilumba ngati akunyamula fumbi.
16 Ngakhale mitengo yonse ya ku Lebanoni singakwane kusonkhezera moto kuti usazime,*
Ndipo nyama zake zamʼtchire nʼzosakwanira kukhala nsembe yopsereza.
17 Kwa iye, mitundu yonse ya anthu ili ngati chinthu chomwe sichinakhaleko.+
Samaiona ngati kanthu, amangoiona ngati chinthu chimene kulibeko.+
18 Kodi Mulungu mungamuyerekezere ndi ndani?+
Kodi munganene kuti amafanana ndi chiyani?+
19 Mmisiri amapanga fano lachitsulo,*
Mmisiri wina wa zitsulo amachikuta ndi golide,+
Ndipo amachipangira matcheni asiliva.
Amafunafuna mmisiri waluso
Kuti amupangire chifaniziro chosema chimene sichingagwe.+
21 Kodi simukudziwa?
Kodi simunamve?
Kodi simunauzidwe kuchokera pachiyambi?
Kodi simunamvetse umboni umene wakhalapo kuchokera pamene maziko a dziko lapansi anakhazikitsidwa?+
22 Pali winawake amene amakhala pamwamba pa dziko lapansi lomwe ndi lozungulira,+
Ndipo amene amakhala mʼdzikolo ali ngati ziwala.
Iye anatambasula kumwamba ngati nsalu yopyapyala,
Ndipo anakufutukula ngati tenti yoti azikhalamo.+
23 Iye amachotsa paudindo anthu olamulira
Ndipo amachititsa oweruza* apadziko lapansi kuoneka ngati sanakhalepo nʼkomwe.
24 Iwo ali ngati mbewu zimene zangodzalidwa kumene,
Ali ngati mbewu zimene zangofesedwa kumene,
Thunthu lawo langoyamba kumene kuzika mizu munthaka.
Mphepo yawawomba nʼkuuma
Ndipo auluzika ndi mphepo ngati mapesi.+
25 “Kodi mungandiyerekezere ndi ndani amene ndingafanane naye?” akutero Woyerayo.
26 “Kwezani maso anu kumwamba ndipo muone.
Kodi ndi ndani amene analenga zinthu zimenezi?+
Ndi amene akutsogolera gulu lonse la nyenyezi ndipo zonse amaziwerenga.
Iliyonse amaiitana poitchula dzina lake.+
Chifukwa cha kuchuluka kwa mphamvu zake zoopsa ndiponso chifukwa chakuti ali ndi mphamvu zambiri zochitira zinthu,+
Palibe iliyonse imene imasowa.
27 Nʼchifukwa chiyani iwe Yakobo, komanso nʼchifukwa chiyani iwe Isiraeli ukunena kuti,
‘Yehova sakuona zimene zikuchitika pa moyo wanga,
Ndipo Mulungu akunyalanyaza zinthu zopanda chilungamo zimene zikundichitikiraʼ?+
28 Kodi iwe sukudziwa? Kodi sunamve?
Yehova, Mlengi wa malekezero a dziko lapansi ndi Mulungu mpaka kalekale.+
Iye satopa kapena kufooka.+
Palibe amene angamvetse* nzeru zake.+
29 Iye amapereka mphamvu kwa munthu wotopa
Ndipo munthu amene alibe mphamvu amamupatsa mphamvu zambiri.+
30 Anyamata adzatopa nʼkufooka,
Ndipo amuna achinyamata adzapunthwa nʼkugwa,
31 Koma anthu amene amayembekezera Yehova adzapezanso mphamvu.
Iwo adzaulukira mʼmwamba ngati kuti ali ndi mapiko a chiwombankhanga.+
Adzathamanga koma osafooka.
Adzayenda koma osatopa.”+