Kalata Yachiwiri Yopita kwa Akorinto
7 Okondedwa, popeza talonjezedwa zinthu zimenezi,+ tiyeni tidziyeretse ndipo tichotse chinthu chilichonse choipitsa thupi ndi mzimu,+ kuti tikhale oyera pamene tikuopa Mulungu.
2 Titsegulireni mitima yanu.*+ Ifetu sitinalakwire aliyense, sitinaipitse aliyense ndipo sitinadyere aliyense masuku pamutu.+ 3 Ponena zimenezi sikuti ndikukuimbani mlandu. Paja ndanena kale kuti inuyo muli mʼmitima yathu, kuti tife limodzi kapena tikhale ndi moyo limodzi. 4 Ndimalankhula nanu momasuka kwambiri komanso ndimakunyadirani kwabasi. Ndalimbikitsidwa kwambiri ndipo ndikusangalala kwambiri pa mavuto onse amene tikukumana nawo.+
5 Titafika ku Makedoniya+ sitinapume koma tinapitiriza kukumana ndi mavuto osiyanasiyana. Anthu ena ankatitsutsa ndipo tinkadera nkhawa mipingo. 6 Komabe Mulungu, amene amalimbikitsa anthu amene ali ndi nkhawa,+ anatilimbikitsa ndi kubwera kwa Tito. 7 Koma osati chifukwa tinali ndi Tito basi koma chifukwanso cha mmene inuyo munamulimbikitsira. Iye anatibweretseranso uthenga wakuti mukufunitsitsa kundiona, mukumva chisoni kwambiri ndiponso mukundidera nkhawa. Nditamva zimenezi ndinasangalalanso kwambiri.
8 Choncho ngakhale kuti ndinakuchititsani kumva chisoni ndi kalata yanga,+ sindikudandaula. (Ndikuona kuti kalatayo inakuchititsani kumva chisoni, koma kwa nthawi yochepa.) Ndiye ngakhale kuti poyambapo ndinadandaula, 9 panopa ndikusangalala. Sikuti ndikusangalala chifukwa munamva chisoni, koma chifukwa chakuti chisonicho chinakuchititsani kulapa. Popeza munamva chisoni mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu, zimene tinalemba sizinakuvulazeni. 10 Kumva chisoni mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu kumachititsa munthu kulapa nʼkupulumuka ndipo munthu sangadandaule nazo.+ Koma kumva chisoni ngati anthu amʼdziko kumabweretsa imfa. 11 Ndipo taonani mmene chisoni chogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu chimenechi chakuthandizirani. Chakuthandizani kukhala akhama kwambiri, chakuchititsani kudziyeretsa, kuipidwa ndi choipa, kukhala ndi mantha, kufunitsitsa kulapa, kukhala odzipereka ndiponso kukonza zolakwika.+ Mwasonyeza kuti ndinu oyera* mʼmbali zonse pa nkhani imeneyi. 12 Ngakhale kuti ndinakulemberani, sindinachite zimenezo chifukwa cha wolakwayo+ kapena wolakwiridwayo ayi, koma kuti zidziwike pamaso pa Mulungu kuti mukufunitsitsa kumvera mawu athu. 13 Nʼchifukwa chake talimbikitsidwa.
Komabe kuwonjezera pa kulimbikitsidwa, tinasangalalanso kwambiri titaona kuti Tito akusangalala, chifukwa nonsenu munamulimbikitsa. 14 Ndinalankhula mokunyadirani kwa iyeyo ndipo simunandichititse manyazi. Koma zimene tinalankhula monyadira kwa Tito nʼzoona, ngati mmene zilili zinthu zonse zimene tinakuuzani. 15 Ndiponso iyeyo amakukondani kwambiri nonsenu akakumbukira kumvera kwanu,+ komanso mmene munamulandirira mwaulemu kwambiri. 16 Ndikusangalala kwambiri chifukwa choti mumandilimbikitsa* pa zinthu zonse zimene mumachita.