Yesaya
65 “Ine ndalola kuti anthu amene sanafunse za ine andifunefune.
Ndalola kuti anthu amene sanandifunefune andipeze.+
Mtundu umene sunaitane pa dzina langa ndauuza kuti, ‘Ndili pano, ndili pano!’+
2 Ndatambasula manja anga tsiku lonse kwa anthu amakani,+
Kwa anthu amene akuyenda mʼnjira yoipa,+
Potsatira maganizo awo,+
3 Anthu amene amandikhumudwitsa nthawi zonse mopanda manyazi,+
Amene amapereka nsembe mʼminda+ komanso kufukiza nsembe zautsi panjerwa.
4 Iwo amakhala pansi kumanda,+
Ndipo usiku wonse amakhala mʼmalo obisika,*
Nʼkumadya nyama ya nkhumba,+
Ndipo mʼmiphika yawo muli msuzi wa zinthu zodetsedwa.+
Iwo ali ngati utsi mʼmphuno mwanga, ngati moto umene ukuyaka tsiku lonse.
6 Taonani! Zalembedwa pamaso panga.
Ine sindikhala chete,
Koma ndiwabwezera,+
Ndiwabwezera nʼkuwapatsa chilango chifukwa cha zonse zimene achita,*
7 Chifukwa cha zolakwa zawo komanso zolakwa za makolo awo,”+ akutero Yehova.
“Chifukwa choti afukiza nsembe zautsi pamapiri
Ndipo andinyoza pazitunda,+
Ine ndiwayezera malipiro awo onse choyamba.”*
8 Yehova wanena kuti:
“Munthu angathe kugwiritsa ntchito phava la mphesa popanga vinyo watsopano
Ndipo wina amanena kuti, ‘Musaliwononge, chifukwa muli zinthu zabwino* mmenemu.’
Inenso ndidzachita zofanana ndi zimenezi chifukwa cha atumiki anga,
Sindidzawawononga onse.+
9 Mwa Yakobo ndidzatulutsamo mwana*
Ndipo mwa Yuda ndidzatulutsamo amene adzalandire mapiri anga ngati cholowa chake.+
Anthu anga osankhidwa adzatenga dziko lamapiriro kuti likhale lawo,
Ndipo atumiki anga adzakhala mmenemo.+
10 Sharoni+ adzakhala malo odyetserako nkhosa
Ndipo chigwa cha Akori+ chidzakhala malo opumulirapo ngʼombe,
Anthu anga amene akundifunafuna ndidzawachitira zimenezi.
11 Koma inu muli mʼgulu la anthu amene asiya Yehova,+
Anthu amene aiwala phiri langa loyera,+
Amene amayalira tebulo mulungu wa Mwayi,
Komanso amene amadzaza makapu ndi vinyo wosakaniza nʼkupereka kwa mulungu wa Zokonzedweratu.
12 Choncho ine ndikonzeratu zoti inu mudzaphedwe ndi lupanga,+
Ndipo nonsenu mudzawerama kuti muphedwe,+
Chifukwa ine ndinakuitanani koma simunayankhe,
Ndinalankhula koma simunamvetsere.+
Munapitiriza kuchita zinthu zoipa pamaso panga
Ndipo munasankha zinthu zimene sizinandisangalatse.”+
13 Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti:
“Atumiki anga adzadya, koma inu mudzakhala ndi njala.+
Atumiki anga adzamwa,+ koma inu mudzakhala ndi ludzu.
Atumiki anga adzasangalala,+ koma inu mudzachita manyazi.+
14 Atumiki anga adzafuula mosangalala chifukwa chokhala ndi chimwemwe mumtima,
Koma inu mudzalira chifukwa chopwetekedwa mtima
Ndipo mudzalira mofuula chifukwa chosweka mtima.
15 Inu mudzasiya dzina limene anthu anga osankhidwa azidzagwiritsa ntchito potemberera
Ndipo Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, adzapha aliyense wa inu,
Koma atumiki ake adzawapatsa dzina lina,+
16 Moti aliyense wofuna kudalitsidwa padziko lapansi
Adzadalitsidwa ndi Mulungu amene amanena zoona,*
Ndipo aliyense wochita lumbiro padziko lapansi
Chifukwa mavuto akale adzaiwalika
Adzabisidwa kuti ndisawaonenso.+
17 Taonani! Ndikulenga kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano.+
Ndipo zinthu zakale sizidzakumbukiridwanso,
Kapena kuvutitsa maganizo.+
18 Choncho kondwerani ndipo muzisangalala mpaka kalekale ndi zimene ndikulenga.
Chifukwa ndikulenga Yerusalemu kuti akhale chinthu chosangalatsa
Ndiponso anthu ake kuti akhale chinthu chokondweretsa.+
19 Ndidzasangalala ndi Yerusalemu ndipo ndidzakondwera ndi anthu anga.+
Mwa iye simudzamvekanso phokoso losonyeza kuti munthu akulira kapena kulira chifukwa cha mavuto.”+
20 “Kumeneko sikudzakhalanso mwana wakhanda amene adzangokhala ndi moyo masiku ochepa okha,
Kapena munthu wachikulire amene sadzakwanitsa zaka zimene munthu amafunika kukhala ndi moyo.
Chifukwa aliyense amene adzamwalire ali ndi zaka 100 adzaonedwa ngati kamnyamata,
Ndipo wochimwa adzatembereredwa, ngakhale atakhala ndi zaka 100.*
22 Sadzamanga nyumba kuti wina azikhalamo,
Kapena kudzala kuti ena adye.
Chifukwa masiku a anthu anga adzakhala ngati masiku a mtengo,+
Ndipo anthu anga osankhidwa adzasangalala mokwanira ndi ntchito ya manja awo.
23 Sadzagwira ntchito mwakhama pachabe,+
Kapena kubereka ana kuti akumane ndi mavuto,
Chifukwa iwo ndiponso ana awo+
24 Iwo asanandiitane, ine ndidzayankha.
Asanamalize kulankhula, ine ndidzamva.
25 Mmbulu ndi mwana wa nkhosa zidzadyera pamodzi,
Mkango udzadya udzu ngati ngʼombe yamphongo,+
Ndipo chakudya cha njoka chidzakhala fumbi.
Zimenezi sizidzapweteka aliyense kapena kuwononga chilichonse mʼphiri langa lonse loyera,”+ akutero Yehova.