Yoweli
Lengezani mʼphiri langa loyera kuti kukubwera nkhondo.
Anthu onse okhala mʼdzikoli anjenjemere,
Chifukwa tsiku la Yehova likubwera+ ndipo lili pafupi.
2 Limeneli ndi tsiku lamdima ndi lachisoni,+
Tsiku lamitambo ndi lamdima wandiweyani.+
Tsikuli lili ngati mmene kuwala kwa mʼbandakucha kumaonekera pamwamba pa mapiri.
Pali mtundu wa anthu ambiri ndiponso amphamvu.+
Kuyambira kalekale, palibenso mtundu wina womwe ungafanane nawo,
Ndipo sikudzakhalanso mtundu wina wofanana nawo,
Kumibadwomibadwo.
Dziko lomwe lili patsogolo pawo lili ngati munda wa Edeni,+
Koma kumbuyo kwawo kuli chipululu,
Ndipo palibe chilichonse chingapulumuke.
5 Amadumphadumpha ndipo amachita mkokomo ngati magaleta oyenda pamwamba pa mapiri,+
Ndiponso ngati moto walawilawi umene ukutentha mapesi.
Ali ngati anthu amphamvu omwe ayalana pokonzekera kumenya nkhondo.+
6 Anthu adzakhala ndi nkhawa chifukwa cha mtunduwo.
Nkhope zawo zonse zidzakhala zamantha.
7 Amathamanga ngati asilikali.
Amakwera khoma ngati asilikali.
Aliyense amayenda mʼnjira yake,
Ndipo saphonya njira zawo.
8 Iwo sakankhanakankhana.
Aliyense amayenda mʼnjira yake.
Wina akalasidwa nʼkugwa,
Enawo sabwerera mʼmbuyo.
9 Iwo amathamangira mʼmizinda ndipo amathamanga pakhoma la mpanda.
Amakwera nyumba ndipo amalowera pawindo ngati mbala.
10 Dzombelo likamayenda, dziko limanjenjemera ndipo kumwamba kumagwedezeka.
Dzuwa ndi mwezi zada,+
Ndipo nyenyezi zasiya kuwala.
11 Yehova adzawalankhula asilikali ake mokweza+ chifukwa anthu amumsasa wake ndi ambiri.+
Amene akukwaniritsa mawu ake ndi wamphamvu.
Tsiku la Yehova ndi lalikulu komanso lochititsa mantha.+
Ndani angalimbe pa tsiku limeneli?”+
12 Yehova wanenanso kuti, “Tsopano bwererani kwa ine ndi mtima wonse.+
Salani kudya,+ lirani momvetsa chisoni ndiponso mokweza.
13 Ngʼambani mitima yanu,+ osati zovala zanu,+
Ndipo bwererani kwa Yehova Mulungu wanu,
Chifukwa iye ndi wachifundo, wokoma mtima, wosakwiya msanga+ ndiponso wachikondi chokhulupirika chochuluka.+
Iye adzasintha maganizo okubweretserani tsoka.
14 Ndani akudziwa kuti mwina adzasintha maganizo,+
Ndipo adzakusiyirani madalitso,
Nsembe yambewu ndi nsembe yachakumwa kuti mupereke kwa Yehova Mulungu wanu?
15 Lizani lipenga mu Ziyoni.
Lengezani za nthawi yosala kudya. Itanitsani msonkhano wapadera.+
16 Sonkhanitsani anthu ndipo muyeretse mpingo.+
Sonkhanitsani amuna achikulire,* ana komanso makanda.+
Mkwati atuluke mʼchipinda chake ndipo nayenso mkwatibwi atuluke mʼchipinda chake.
‘Inu Yehova, mverani chisoni anthu anu,
Ndipo musachititse manyazi cholowa chanu,
Kuti anthu a mitundu ina awalamulire.
Anthu a mitundu ina asanene kuti: “Kodi Mulungu wawo ali kuti?”’+
19 Yehova adzayankha anthu ake kuti:
‘Ndikukutumizirani mbewu, vinyo watsopano ndi mafuta.
Anthu inu mudzakhuta.+
Sindidzachititsanso kuti muzinyozedwa pakati pa anthu a mitundu ina.+
20 Mdani wakumpoto ndidzamuthamangitsira kutali ndi inu.
Ndidzamuthamangitsira kudziko louma komanso lopanda anthu,
Nkhope yake itayangʼana kunyanja yakumʼmawa,*
Nkhongo yake italoza kunyanja yakumadzulo.*
Fungo lake lonunkha lidzamveka,
Ndipo fungo lake loipalo lidzafalikira mʼdziko lonselo,+
Chifukwa Mulungu adzachita zinthu zazikulu.’
21 Usachite mantha iwe dziko.
Sangalala chifukwa Yehova adzachita zinthu zazikulu.
22 Inu zilombo zakutchire musachite mantha,
Chifukwa malo odyetserako ziweto kutchire adzamera msipu wobiriwira.+
Mitengo nayonso idzabereka zipatso.+
Mtengo wa mkuyu ndi mtengo wa mpesa udzabereka zipatso zambiri.+
23 Inu ana aamuna a Ziyoni sangalalani chifukwa cha Yehova Mulungu wanu.+
Iye adzakupatsani mvula yoyambirira pa mlingo woyenera,
Ndipo adzakugwetserani mvula yamvumbi,
Mvula yoyambirira ndi mvula yomaliza, ngati mmene zinalili poyamba.+
25 Ndidzakubwezerani mbewu za zaka zonse
Zimene dzombe, ana a dzombe opanda mapiko komanso dzombe losakaza zinadya.
Limeneli ndi gulu langa lankhondo limene ndinakutumizirani.+
Ndipo mudzatamanda dzina la Yehova Mulungu wanu,+
Amene wakuchitirani zodabwitsa.
Anthu anga sadzachitanso manyazi mpaka kalekale.+
27 Mudzadziwa kuti ine ndili pakati pa Isiraeli,+
Komanso kuti ine ndine Yehova Mulungu wanu+ ndipo palibenso wina.
Anthu anga sadzachitanso manyazi mpaka kalekale.
28 Zimenezi zikadzachitika ndidzapereka* mzimu wanga+ kwa chamoyo chilichonse,
Ndipo ana anu aamuna ndi ana anu aakazi adzalosera.
Amuna achikulire adzalota maloto,
Ndipo anyamata adzaona masomphenya.+
29 Ngakhale akapolo anga aamuna ndi aakazi,
Ndidzawapatsa mzimu wanga mʼmasiku amenewo.
30 Ndidzachita zodabwitsa kumwamba ndi padziko lapansi.
Padzakhala magazi, moto ndi utsi wambiri wokwera mʼmwamba.+