Angelo—Kodi Amayambukira Moyo Wanu?
KODI ANGELO alikodi? Kapena kodi iwo ali kokha zotulukapo za kulingalira? Ngati iwo aliko, kodi angayambukire moyo wanu?
Pali kokha magwero amodzi odalirika kaamba ka mayankho ku mafunso oterewa. Amenewo ali zolembedwa zowuziridwa zimene Mulungu wapereka ku mtundu wa anthu—mawu ake, Baibulo Loyera. Ponena za ilo mtumwi Paulo analemba kuti: “Lemba liri lonse adaliuzira Mulungu ndipo lipindulitsa . . . [pa kulungamitsa zinthu NW].”—2 Timoteo 3:16.
Chotero, tingakhale ndi chidaliro kuti Baibulo lidzatipatsa ife mayankho olondola ponena za kukhalako kwa angelo ndi kuti kaya amatiyambukira ife. Ndithudi Mlengi wa chilengedwe angatiuze ife ngati angelo anali pakati pa chilengedwe chake.
Kodi Angelo Ali Enieni?
Baibulo limasonyeza mowonekera bwino kuti: “Amene [Mulungu] ayesa angelo ake mizimu.” (Ahebri 1:7) Chotero Mlengi ali ndi zolengedwa zauzimu m’mabwalo akumwamba. Izi ziri zosawoneka kwa ife, ndipo ziri za mphamvu.—Masalmo 104:4; 2 Petro 2:11.
Kodi Mulungu anali ndi cholinga kaamba ka angelo kukhala kokha osakhala anthu, enieni ongoyerekeza? Ngati zimenezo zinali tero, nchifukwa ninji Baibulo limasonyeza angelo monga okhala ndi malingaliro? Mwachitsanzo, limatiuza ife kuti pamene maziko a dziko lapansi anakhazikitsidwa, angelo “anaimba limodzi mokondwera, ndi ana onse a Mulungu [angelo] anafuula ndi chimwemwe.”—Yobu 38:4-7.
Chikuwonekera kuti, monga zolengedwa za Mulungu za luntha za padziko lapansi, zolengedwa za luntha zauzimu, angelo, ali ndi umunthu wawo. Ngakhale kuti Baibulo limatchula kokha maina a angelo aŵiri (Mikayeli ndi Gabriyeli), chenicheni chakuti angelo ali ndi maina chimawonjezera ku umunthu wawo. (Luka 1:11, 19, 26; Yuda 9) Baibulo mwamphamvu limatsutsa kulambira angelo, ndipo chimenecho chimaphatikizapo kupemphera kwa iwo. M’malo mwakuti tipemphere kwa angelo, mtumwi Paulo akutilangiza kuti: “Komatu m’zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu.”—Afilipi 4:6; Chivumbulutso 19:10; 22:8, 9.
Koma kodi angelo anapangidwiratu kukhala opanda mphamvu ya kusankha kwaumwini pakati pa chabwino ndi choipa monga maroboti opanda malingaliro? Ayi, angelo ali zinthu zokhala ndi ufulu wa kudzisankhira, monga mmene anthu aliri. Mwachitsanzo, pamene angelo ena anapandukira malamulo a Mulungu m’tsiku la Nowa, Mulungu anawakana iwo, ndipo iwo anachotsedwa m’mabwalo a kumwamba a Mulungu. Mkhalidwe wa kusamvera kwawo unali chisonyezo chenicheni cha umunthu wa ungelo.—Genesis 6:1, 2; 2 Petro 2:4; Mateyu 25:41.
Chotero, Baibulo limatipatsa ife chidziŵitso chothandiza ponena za chiyambi, khalidwe, ndi chibadwa cha angelo. Kupyola pa chimene Mawu a Mulungu amanena ponena za iwo kungapangitse munthu kufufuza kopanda chifuno pa mafunso amene Baibulo silimayankha. Icho chingakhoze ngakhale kutsogolera ku kupereka chisamaliro chosayenera kapena kulambira angelo. (Akolose 2:18) Baibulo limatikumbutsa ife “kutsimikizira zinthu zonse” ndipo osati ‘kupyola chimene chalengezedwa kale kukhala mbiri yabwino.’—Afilipi 1:10; Agalatiya 1:8.
Angelo m’Chifuno cha Mulungu
Ngakhale kuti ambiri angavomereze pa chiyambi ndi chizindikiritso cha angelo, ochepera ali odziŵa kwenikweni chifukwa cha kukhalapo kwawo ndi mmene angelo amayambukirira miyoyo yathu lerolino.
Mu Baibulo, mawu aŵiri ogwiritsiridwa ntchito kaamba ka “angelo” ali mal·’akhʹ (Chihebri) ndi agʹge·los (Chigriki). Onse aŵiriwa amatanthauza “mthenga.” Iwo amatiuza ife chinachake ponena za imodzi ya ntchito ya angelo. Angelo amatumikira monga athenga, kapena operekera, pakati pa Mulungu ndi munthu.
Mwachitsanzo, mngelo anatumizidwa kukapereka uthenga kwa Abrahamu wonena za mwana wake wamwamuna Isaki ndi dalitso lomwe likadza kupyolera mwa iye, dalitso lomwe tingakhoze kulandira. (Genesis 22:11-17) Mngelo anatumizidwa kukalankhula ndi Mose. (Machitidwe 7:37, 38) Mulungu anatumizanso mngelo ndi malangizo kwa mneneri Eliya. (2 Mafumu 1:3) Ndipo mngelo anawonekera kwa Yosefe, atate wopeza wa Yesu, ndi malangizo apadera onena za mwanayo.—Mateyu 2:13.
Angelo atumizidwanso kuchinjiriza anthu a Mulungu: “Mngelo wa Yehova azinga kuwachinjiriza iwo akuwopa iye, nawalanditsa iwo.” (Masalmo 34:7) Mwachitsanzo, mngelo anatulutsa mtumwi Petro kuchoka m’ndende. (Machitidwe 12:6-11) Angelo aŵiri anathandiza Loti ndi ana ake akazi kupulumuka chiwonongeko cha Sodomu ndi Gomora mwakuwaperekeza iwo kutuluka m’malo amenewo. Mkazi wa Loti, ngakhale kuli tero, sanachite m’chigwirizano ndi angelowo, chotero iye anapita ku chiwonongeko ndi mizindayo.—Genesis 19:1-26.
Baibulo limatchula zochitika zina zambiri za kuthandiza kwa angelo, kuchirikiza chimene Ahebri 1:7 ndi 14 amanena: “Ndipo za angelo anenadi: ‘Amene ayesa angelo ake mizimu, ndi omtumikira iye akhale laŵi lamoto.’ Kodi siiri yonse mizimu yotumikira, yotumidwa kuti itumikire iwo amene adzalowa chipulumutso?”
Mngelo anabweretsa chitonthozo chokulira kwa Yesu. Usiku imfa yake isanadze, Yesu anadziŵa chomwe chinamulalira patsogolo—kuti iye adzaperekedwa, kumenyedwa, ndi kuphedwa mwauchifwamba. Iye anafunikira mphamvu kuti apirire chiyeso chimenechi cha umphumphu wake. Nthaŵi imeneyo yovuta, mngelo anawonekera kwa iye ‘kukamulimbikitsa.’ Ndi dalitso lotani nanga limene chitonthozo chaungelo chimenecho chinakhalira kwa Yesu! Monga chotulukapo, ngakhale kuti iye anakumana ndi chisautso choterocho chakuti “thukuta lake linakhala ngati madontho akulu a mwazi alinkugwa pansi,” iye anali wokhoza kupirira mokhulupirika kufikira imfa.—Luka 22:43, 44.
Mulungu anagwiritsiranso ntchito angelo kuwononga adani a anthu ake. Pamene ulamuliro wa dziko la Asuri unawopsyeza alambiri akale a Mulungu, zotsatirazi zinachitika: “Ndipo kunali, usiku womwewo mthenga wa Yehova anatuluka, nakantha m’misasa ya Asuri zikwi zana limodzi mphambu makumi asanu ndi atatu kudza zisanu, ndipo pouka anthu mamawa, tawonani, onsewo ndi mitembo.” (2 Mafumu 19:35) Inu mungawone mphamvu yowopsya ya angelo—chinangotenga kokha mngelo m’modzi kupha otsutsa Mulungu 185,000 ndi anthu ake!
Herode wonyoza nayenso anayang’anizana ndi mphamvu za angelo. Pamene Herode anayamba kudzimva iye mwini monga Mulungu, “pomwepo mngelo wa Ambuye anamkantha, chifukwa sanampatsa Mulungu ulemerero; ndipo anadyedwa ndi mphutsi, natsirizika.”—Machitidwe 12:21-23.
Tikudziŵitsidwa kuti mwamsanga, pamene Mulungu abweretsa dongosolo lonse loipa iri la zinthu kumapeto ake, angelo adzagwiritsidwanso ntchito monga owononga. “Mwana wa munthu adzatuma angelo ake, ndipo iwo adzasonkhanitsa pamodzi, ndi kuchotsa mu Ufumu wake zokhumudwitsa zonse, ndi anthu akuchita kusayeruzika, ndipo adzawataya iwo mu ng’anjo yamoto.”—Mateyu 13:41, 42.
Chotero, angelo ali kutalitali ndi zimene anthu ambiri angalingalire. Mkonzi wa chipembedzo wa ku German Dr. Manfred Barthel ananena kuti: “Ngati tifuna kulingalira angelo a Ambuye monga mmene akonzi a Chipangano Chatsopano anawonera iwo, choyamba tidzafunikira kuiwalako zidutswa za akerubi . . . zomwe zimakometsera makardi athu otumizira moni.”—Chimene Baibulo Kwenikweni Limanena.
Kodi Angelo Amakuyambukirani Motani?
Komabe, funso likalipobe: Kodi nchiyani chimene angelo akuchita lerolino? Kodi iwo akutiyambukira ife tsopano lino? Inde, iwo ndithudi ali!
Kumbukirani kuti mu ulosi wake wonena za “mapeto a dongosolo la zinthu” Yesu ananeneratu kuti: “Pamene Mwana wa munthu adzadza mu ulemerero wake, [akumalingalira mphamvu za Ufumu], ndi angelo onse pamodzi naye, pomwepo iye adzakhala pa chimpando cha kuwala kwake ndipo adzasonkhanidwa pamaso pake anthu a mitundu yonse; ndipo iye adzalekanitsa iwo wina ndi mnzake.”—Mateyu 24:3; 25:31, 32.
Kodi kulekanitsa kumeneku kwa anthu kudzakwaniritsidwa motani? Yesu ananeneratu kuti: “Uthenga uwu wabwino wa Ufumu udzalalikidwa pa dziko lonse lapansi, ukhale umboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.” (Mateyu 24:14) Inde, Mulungu amagwiritsira ntchito anthu ake pa dziko lapansi kuchita ntchito yolalikira imeneyi ya dziko lonse.
Ufumu wa Mulungu uli boma limene lidzabweretsa yankho lokha ku mavuto a mtundu wa anthu. Lerolino, uthenga wonena za iwo ukulengezedwa kuzungulira dziko lonse ndi Mboni za Yehova zoposa pa mamiliyoni atatu, amene ali ndi angelo owachirikiza. “Padzatero pa chimaliziro cha nthaŵi ya pansi pano: angelo adzatuluka, nadzawasankhula oipa pakati pa abwino.”—Mateyu 13:49.
Ntchito iyi yolalikira yotsogozedwa ndi angelo ikulandira kuyankha kosakanizana lerolino kuchokera wa anthu. Ena amati ali otanganitsidwa kwenikweni kumvetsera kapena kungokana kuchita tero. Ena amakhala osinkhasinkha kapena osagamulapo. Komabe, ambiri owona mtima, odera nkhaŵa ponena za mtsogolo mwawo, ayankha mofunitsitsa. Motani?
M’maiko 208, Mboni za Yehova zikutsogoza maphunziro a Baibulo apanyumba ndi mamiliyoni angapo a anthu omwe ali “odera nkhaŵa ponena za kusowa kwawo kwauzimu” ndi amene ali ‘anjala kaamba ka chilungamo.’ (Mateyu 5:3, 6) Zokumana nazo zambiri zimasonyeza kuti angelo kaŵirikaŵiri amatsogoza atumiki a Mulungu kukumana ndi anthu owona mtima oterowo ndi uthenga wa chipulumutso. Chivumbulutso 14:6 chimalongosola mophiphiritsira “mngelo wowuluka m’mwamba” wokhala ndi “uthenga wabwino wosatha, aulalikire kwa iwo akukhala padziko.” Chimenecho ndithudi chikuchitika tsopano lino! Kodi chimenechi chidzayambukira motani mtsogolo mwanu?
Angelo Mtsogolo Mwanu
Baibulo limazindikiritsa mowonekera bwino nthaŵi zathu monga “masiku otsiriza” a dongosolo liripoli. (2 Timoteo 3:1-5) Baibulo limatidziŵitsanso ife kuti angelo tsopano “akuimirira pa ngondya zinayi za dziko, akugwira mphepo zinayi za dziko.” (Chivumbulutso 7:1) Kodi chophiphiritsirachi chimatanthauzanji?
Kukhala kwawo pa “ngondya” za dziko lapansi, angelo ali m’malo a kuleka “mphepo” yowononga kuchokera ku mbali zonse. Palibe malo a dziko lapansi amene adzapulumutsidwa, chimene chidzatanthauza “kuipsya,” kapena chiwonongeko, kaamba ka dongosolo loipa iri ndi achirikizi ake onse. Angelo a Mulungu chotero akutchulidwa kukhala ali okonzekera kupita ku ntchito pamene chizindikiro chaperekedwa!—Chivumbulutso 7:3; 19:11-21.
“Kuipsa” kowonongako, ngakhale kuli tero, kudzakhala kokha pa awo amene sakuyankha ku uthenga wochirikizidwa ndi angelo womwe ukulalikidwa tsopano kuzungulira dziko lonse lapansi. Ilo silidzaipsa awo omwe akufunafuna Mulungu ndi kumvetsera ku uthenga wa Ufumu. Iwo adzapulumutsidwa, popeza kuti mawu a Mulungu amanena kuti: “Funani Yehova, ofatsa inu nonse a m’dziko, . . . Funani chilungamo, funani chifatso, kapena mudzabisika tsiku la mkwiyo wa Yehova.”—Zefaniya 2:3.
Nchiyani kenaka chimene chidzakhala chotulukapo cha “ofatsa” oterowo? Masalmo 37:11 amanena kuti: “Ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.” Kwa utali wotani? “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.” (Masalmo 37:29) Chimenecho chimatanthauza kuti moyo wosatha udzakhala wothekera padziko lapansi limene lidzasinthidwira m’paradaiso, monga mmene Yesu Kristu anasonyezera.—Luka 23:43.
Chotero, pamenepo, funso limene mufunikira kufunsa liri lakuti: ‘Kodi mtsogolo mwanga mudzakhala motani?’ Yankho limadalira pa mmene mumayankhira ku chitsogozo chaungelo. Kodi mudzamvetsera ndi kuyankha pamene mwafikiridwa ndi uthenga umene iwo akuchirikiza? Ngati mudzatero, mudzakhala pakati pa awo omwe angapitirizebe kuyang’ana mtsogolo ndi chidaliro, okhala ndi lonjezo la Mulungu lotsimikizirika: “Dziko lapansi lipita ndi chilakolako chake; koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthaŵi yonse.”—1 Yohane 2:17.
[Chithunzi patsamba 7]
Angelo tsopano ‘akugwira mphepo zinayi.’ Nchifukwa ninji?