Chivumbulutso Chimene Yohane Analandira
22 Ndipo anandionetsa mtsinje wa madzi a moyo,+ oyera ngati mwala wonyezimira wa kulusitalo, ukuyenda kuchokera kumpando wachifumu wa Mulungu ndi wa Mwanawankhosa.+ 2 Mtsinjewo unadutsa pakati pa msewu waukulu wamumzindawo. Kumbali zonse ziwiri za mtsinjewo kunali mitengo ya moyo imene inkabereka zipatso zokolola maulendo 12, ndipo inkabereka zipatso mwezi uliwonse. Masamba a mitengoyo anali ochiritsira mitundu ya anthu.+
3 Mulungu sadzatembereranso mzindawo. Koma mpando wachifumu wa Mulungu ndi wa Mwanawankhosa+ udzakhala mumzindamo ndipo akapolo a Mulungu adzachita utumiki wopatulika kwa iye. 4 Iwo adzaona nkhope yake+ ndipo dzina lake lidzakhala pazipumi zawo.+ 5 Komanso, usiku sudzakhalakonso+ ndipo sadzafunikiranso kuwala kwa nyale kapena kwa dzuwa, chifukwa Yehova* Mulungu adzawaunikira.+ Ndipo iwo adzalamulira monga mafumu mpaka kalekale.+
6 Iye anandiuza kuti: “Mawu awa ndi odalirika ndiponso oona.+ Yehova,* Mulungu amene anauzira aneneri+ kuti apereke mauthenga, watumiza mngelo wake kuti adzaonetse akapolo ake zinthu zimene zikuyenera kuchitika posachedwa. 7 Taonani! Ndikubwera mofulumira.+ Wosangalala ndi aliyense amene akutsatira mawu a ulosi amumpukutuwu.”+
8 Ine Yohane, ndi amene ndinamva komanso kuona zinthu zimenezi. Nditamva komanso kuona zinthu zimenezi, ndinagwada nʼkuwerama pamapazi a mngelo amene ankandionetsa zinthu zimenezi kuti ndimulambire. 9 Koma iye anandiuza kuti: “Samala! Usachite zimenezo! Inetu ndangokhala kapolo mnzako, kapolo wa aneneri amene ndi abale ako komanso wa anthu amene akutsatira mawu amumpukutu umenewu. Lambira Mulungu.”+
10 Anandiuzanso kuti: “Usasunge mwachinsinsi mawu a ulosi amumpukutuwu, chifukwa nthawi yoikidwiratu yayandikira. 11 Amene akuchita zosalungama, apitirize kuchita zosalungamazo ndipo amene akuchita zonyansa apitirizebe kuchita zonyansazo. Koma wolungama apitirize kuchita zachilungamo ndipo woyera apitirize kukhala woyera.
12 ‘Taonani! Ndikubwera mofulumira ndipo ndili ndi mphoto yoti ndipereke kwa aliyense mogwirizana ndi ntchito yake.+ 13 Ine ndine Alefa ndi Omega,*+ woyamba ndi wotsiriza, chiyambi ndi mapeto. 14 Osangalala ndi amene achapa mikanjo yawo+ kuti akhale ndi ufulu wodya zipatso zamʼmitengo ya moyo,+ ndiponso kuti aloledwe kulowa mumzindawo kudzera pamageti ake.+ 15 Kunja kuli anthu amene ali ngati agalu* komanso amene amachita zamizimu, achiwerewere,* opha anthu, olambira mafano ndi aliyense amene amakonda kunama komanso kuchita zachinyengo.’+
16 ‘Ine Yesu, ndinatumiza mngelo wanga kuti adzachitire umboni zinthu zimenezi kwa iwe kuti zithandize mipingo. Ine ndine muzu komanso mbadwa ya Davide.+ Ndinenso nthanda yowala kwambiri.’”+
17 Mzimu ndi mkwatibwi+ akupitiriza kunena kuti, “Bwera!” ndipo aliyense amene wamva anene kuti, “Bwera!” Komanso aliyense amene akumva ludzu abwere.+ Aliyense amene akufuna, amwe madzi opatsa moyo kwaulere.+
18 “Ine ndikuchitira umboni kwa aliyense amene wamva mawu a ulosi wamumpukutuwu kuti: Wina akawonjezera pa zimenezi,+ Mulungu adzamuwonjezera miliri imene yalembedwa mumpukutuwu.+ 19 Ndipo wina akachotsa kalikonse pa mawu amumpukutu wa ulosi umenewu, Mulungu adzachotsa gawo lake pa zimene zalembedwa mumpukutuwu. Kutanthauza kuti sadzamulola kudya zipatso zamʼmitengo ya moyo+ komanso sadzamulola kulowa mumzinda woyerawo.+
20 Amene akuchitira umboni zinthu zimenezi akuti, ‘Inde, ndikubwera mofulumira.’”+
“Ame! Bwerani, Ambuye Yesu.”
21 Kukoma mtima kwakukulu kwa Ambuye Yesu kukhale ndi oyerawo.