Zimene Muyenera Kudziŵa Ponena za Nsanje
KODI nsanje nchiyani? Ndi mkhalidwe wamphamvu wa mtima umene ungachititse munthu kuda nkhaŵa, kumva chisoni, kapena kukwiya. Tingachite nsanje pamene tiona kuti wina akuchita bwino kwambiri pantchito kuposa ife. Kapena tingachite nsanje pamene mnzathu athokozedwa kwambiri kuposa ife. Koma kodi kuchita nsanje nkoipa nthaŵi zonse?
Anthu ogwidwa ndi nsanje amakonda kunyumwira anthu ena amene iwo aganiza kuti ndi adani awo. Mfumu Sauli wa Israyeli wakale anachita zimenezi. Poyamba anakonda Davide, mnyamata wake wonyamula zida, moti anafika ndi pakumkweza kukhala mtsogoleri wa gulu la nkhondo. (1 Samueli 16:21; 18:5) Ndiyeno tsiku lina Mfumu Sauli anamva akazi akutamanda Davide ndi mawu akuti: “Sauli anapha zikwi zake, koma Davide zikwi zake zankhani.” (1 Samueli 18:7) Sauli sanayenera kulola zimenezi kuyambukira ubwenzi wake wabwino ndi Davide. Komabe, anakwiya. “Kuyambira tsiku lomwelo ndi mtsogolo mwake, Sauli anakhala maso pa Davide.”—1 Samueli 18:9.
Munthu wansanje sangafunire mnzake choipa. Mwina angangoipidwa ndi chipambano cha mnzakeyo nakhumba kukhala ndi mikhalidwe imodzimodziyo. Komano, njiru ndiyo nsanje ya mtundu woipa kwambiri. Munthu wanjiru mwachinsinsi angamamane zabwino uja amene amachita naye nsanje kapena angakhumbe kuti tsoka limgwere. Nthaŵi zina, munthu wanjiru amalephera kubisa malingaliro ake. Angasonkhezereke kuvulaza mnzake poyera, monga momwedi Mfumu Sauli anayesera kupha Davide. Kangapo konse, Sauli anaponya mkondo poyesa “kupyoza Davide kumphatikiza kukhoma.”—1 Samueli 18:11; 19:10.
‘Komatu ine ndilibe nsanje,’ mungatero. Zoona, nsanje singalamulire moyo wanu. Komabe, pamlingo wina wake tonsefe nsanje imatikhudza—nsanje yathu ndi ija ya anzathu. Ngakhale kuti timafulumira kuona nsanje mwa anzathu, tingachedwe kuiona mwa ife eni.
‘Kukhumbitsa Kuchita Njiru’
Mbiri ya chibadwa cha anthu chauchimo imene Mawu a Mulungu, Baibulo, amavumbula imasonyeza machimo a njiru kaŵirikaŵiri. Kodi mukukumbukira nkhani ya Kaini ndi Abele? Ana aŵiriwa a Adamu ndi Hava anapereka nsembe kwa Mulungu. Abele anatero chifukwa chakuti anali munthu wachikhulupiriro. (Ahebri 11:4) Anali ndi chikhulupiriro cha kukhoza kwa Mulungu kukwaniritsira chifuno Chake chachikulu ponena za dziko lapansi. (Genesis 1:28; 3:15; Ahebri 11:1) Abele anakhulupiriranso kuti Mulungu adzafupa anthu okhulupirika ndi moyo m’Paradaiso alinkudza pa dziko lapansi. (Ahebri 11:6) Nchifukwa chake Mulungu anakonda nsembe ya Abele. Ngati Kaini akanakondadi mphwake, akanakondwera pamene Mulungu anadalitsa Abele. M’malo mwake, Kaini “anakwiya kwambiri.”—Genesis 4:5.
Mulungu analimbikitsa Kaini kuchita zabwino kuti nayenso alandire dalitso. Ndiyeno Mulungu anamchenjeza: “Ukaleka kuchita zabwino, uchimo ubwatama pakhomo: kwa iwe kudzakhala kulakalaka kwake, ndipo [iwenso sudzaulamulira kodi, NW]”? (Genesis 4:7) Mwachisoni, Kaini sanalamulire mkwiyo wake wansanje. Unamsonkhezera kupha mphwake wolungama. (1 Yohane 3:12) Chiyambire nthaŵiyo, kulimbana ndi nkhondo zatenga miyoyo miyandamiyanda. “Zimene zingakhale zochititsa zina zazikulu za nkhondo ndizo kukhumba dziko lokulirapo, kukhumba chuma chochuluka, kukhumba mphamvu zambiri, kapena kukhumba chitetezo,” ikutero The World Book Encyclopedia.
Akristu oona samatenga mbali m’nkhondo za dzikoli. (Yohane 17:16) Komabe, nzachisoni kuti Akristu ena amaloŵa m’kulimbana kwa pakamwa nthaŵi zina. Ngati ena mumpingo akhalira mbali wina, kulimbanako kungasanduke nkhondo za pakamwa. “Zichokera kuti nkhondo, zichokera kuti zolimbana mwa inu?” Yakobo mlembi wa Baibulo anafunsa motero okhulupirira anzake. (Yakobo 4:1) Anayankha funsolo mwa kusonyeza umbombo wawo wa kukonda chuma nawonjezera kuti, “Muchita kaduka,” kapena “nsanje.” (Yakobo 4:2, NW, mawu amtsinde) Inde, kukonda chuma kungachititse munthu kukhala ndi kaduka ndi nsanje kwa aja amene amaoneka kuti ali ndi moyo wabwino. Nchifukwa chake, Yakobo anachenjeza za ‘kukhumbitsa kwa munthu kuchita nsanje [“njiru,” NW].’—Yakobo 4:5.
Kodi kupenda zochititsa nsanje kuli ndi phindu lotani? Eya, kungatithandize kukhala oona mtima ndi kukhala ndi ubwenzi wabwino ndi ena. Kungatithandizenso kukhala achifundo, ololera, ndi okhululuka kwambiri. Koposa zonse, kumasonyeza kuti munthu afunika kwambiri makonzedwe a Mulungu achikondi achipulumutso ndi omlanditsa ku zikhoterero zaumunthu zauchimo.—Aroma 7:24, 25.
Dziko Lopanda Nsanje Yoipa
Kwa anthu, dziko lopanda nsanje yoipa limamveka kukhala losatheka. Mlembi Rom Landau anavomereza kuti: “Nzeru ya mibadwo yambiri imene anthu akundika, ndi zonse zimene afilosofi . . . ndi akatswiri a zamaganizo anena pankhaniyo, sizimapereka chitsogozo kwa munthu wozunzika ndi nsanje. . . . Kodi pali dokotala aliyense amene anachiritsapo nsanje ya munthu?”
Koma Mawu a Mulungu amapereka chiyembekezo cha kupeza moyo wangwiro waumunthu m’dziko latsopano limene palibe aliyense adzavutikanso ndi nsanje yoipa kapena njiru. Ndiponso, mtendere wa dziko latsopanolo sudzasokonezedwa ndi anthu amikhalidwe yoipa yotero.—Agalatiya 5:19-21; 2 Petro 3:13.
Komabe, si nsanje iliyonse imene ili yosayenera. Ndi iko komwe, Baibulo limati Yehova “ali Mulungu wansanje.” (Eksodo 34:14) Kodi zimenezo zimatanthauzanji? Ndipo kodi Baibulo limati bwanji ponena za nsanje yoyenera? Panthaŵi imodzimodziyo, kodi munthu angalamulire motani nsanje yosayenera? Onani nkhani zotsatira.