Kalata Yachiwiri ya Petulo
3 Okondedwa, iyi tsopano ndi kalata yachiwiri imene ndikukulemberani, ndipo mofanana ndi yoyamba ija, ndikukulimbikitsani kuti muzigwiritsa ntchito bwino mphamvu zanu zoganiza pokukumbutsani zimene mukudziwa kale.+ 2 Ndikuchita zimenezi kuti mukumbukire mawu amene aneneri oyera ananena kalero komanso lamulo limene Ambuye ndi Mpulumutsi wathu anapereka kudzera mwa atumwi.* 3 Choyamba dziwani kuti mʼmasiku otsiriza kudzakhala anthu amene azidzalankhula zinthu zonyoza. Potsatira zinthu zimene amalakalaka,+ 4 azidzati: “Kodi kukhalapo* kwake kolonjezedwa kuja kuli kuti?+ Taonani, palibe chimene chasintha kungochokera tsiku limene makolo athu anamwalira. Zinthu zonse zikupitiriza kuchitika ndendende ngati mmene zakhala zikuchitikira kuyambira pachiyambi cha chilengedwe.”+
5 Anthu amenewa amanyalanyaza mwadala mfundo yakuti, kalero panali kumwamba ndi dziko lapansi lomwe linatuluka mʼmadzi ndi kuima pamwamba pa madziwo chifukwa cha mawu a Mulungu.+ 6 Ndipo kudzera mʼzinthu zimenezi, dziko la pa nthawiyo linawonongedwa pamene linamira mʼmadzi a chigumula.+ 7 Koma ndi mawu a Mulungu omwewo, kumwamba ndi dziko lapansi zimene zilipo panopa, azisungira moto ndipo akuzisungabe mpaka pa tsiku limene adzaweruze komanso kuwononga anthu osaopa Mulungu.+
8 Komabe okondedwa, musalephere kuzindikira mfundo yakuti, kwa Yehova* tsiku limodzi lili ngati zaka 1,000, ndipo zaka 1,000 zili ngati tsiku limodzi.+ 9 Yehova* sakuchedwa kukwaniritsa zimene analonjeza+ ngati mmene anthu ena amaonera kuti akuchedwa. Koma akukulezerani mtima chifukwa sakufuna kuti munthu aliyense adzawonongedwe, koma akufuna kuti anthu onse alape.+ 10 Komabe, tsiku la Yehova*+ lidzafika ngati wakuba,+ pamene kumwamba kudzachoka+ ndi mkokomo waukulu. Ndipo zinthu zimene zimapanga kumwamba ndi dziko lapansi zidzatentha kwambiri nʼkusungunuka, moti dziko lapansi ndi ntchito zake zidzaonekera poyera.+
11 Popeza zinthu zonsezi zidzasungunuka chonchi, ganizirani za mtundu wa anthu amene muyenera kukhala. Muyenera kukhala anthu akhalidwe loyera ndipo muzichita ntchito zosonyeza kuti ndinu odzipereka kwa Mulungu. 12 Muzichita zimenezi pamene mukuyembekezera komanso kukumbukira nthawi zonse* kubwera kwa tsiku la Yehova.*+ Pa tsikuli kumwamba kudzapsa ndi moto nʼkuwonongekeratu+ ndipo zinthu zimene zimapanga kumwamba ndi dziko lapansi zidzatentha kwambiri nʼkusungunuka. 13 Koma pali kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano zimene ife tikuyembekezera mogwirizana ndi lonjezo lake,+ ndipo mmenemo mudzakhala chilungamo.+
14 Choncho okondedwa, popeza mukuyembekezera zinthu zimenezi, yesetsani kuchita zonse zimene mungathe kuti Mulungu adzakupezeni muli oyera, opanda cholakwa ndiponso muli mumtendere.+ 15 Kuwonjezera pamenepo, muziona kuti kuleza mtima kwa Ambuye wathu ndi chipulumutso, monganso mmene mʼbale wathu wokondedwa Paulo anakulemberani mogwirizana ndi nzeru zimene anapatsidwa.+ 16 Iye anafotokoza zimenezi ngati mmene amachitira mʼmakalata ake onse. Komabe mʼmakalata akewo muli zinthu zina zovuta kuzimvetsa, zimene anthu osaphunzitsika komanso achikhulupiriro chosalimba akuzipotoza. Amachita zimenezi ngati mmene amachitiranso ndi Malemba ena onse, zomwe zidzachititse kuti adzawonongedwe.
17 Choncho inu okondedwa, popeza mwadziwiratu zimenezi, chenjerani kuti anthu ophwanya malamulowo asakusocheretseni ndi zochita zawo zoipa nʼkuchititsa kuti mugwe chifukwa cholephera kukhala olimba.+ 18 Musatero ayi, koma muzichita zinthu zimene zingakuthandizeni kuti mupitirize kulandira kukoma mtima kwakukulu kwa Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu, ndiponso kuti mumudziwe bwino kwambiri. Kwa iye kukhale ulemerero, kuyambira panopa mpaka muyaya. Ame.