Anachita Chifuniro cha Yehova
Yesu Anacheza ndi Ana
UTUMIKI wa Yesu wazaka zitatu ndi theka unali pafupi kutha. Posakhalitsa anali kukaloŵa m’Yerusalemu ndi kufa imfa yopweteka. Anali kudziŵa zimene zidzachitika, popeza anali atauza ophunzira ake kuti: “Mwana wa munthu aperekedwa m’manja a anthu, ndipo adzamupha Iye.”—Marko 9:31.
Ndithudi, Yesu anafuna kugwiritsa ntchito bwino tsiku, ola ndi nthaŵi iliyonse imene inatsala. Ophunzira ake anafunikirabe chisamaliro. Yesu anaona kuti ophunzirawo anafunikanso uphungu wamphamvu ponena za kufunika kwa kudzichepetsa ndi kuipa kwa kukhumudwitsa ena nthaŵi zonse. (Marko 9:35-37,42-48)Anafunikiranso malangizo ponena za ukwati, chisudzulo ndi umbeta. (Mateyu 19:3-12) Podziŵa kuti anali pafupi kufa, mosakayikira Yesu analankhula kwa ophunzira ake mwachidule komanso mwachangu. Nthaŵi inali yamtengo wapatali—chimene chinapangitsa zochita za Yesu panthaŵiyo kukhala zachilendo kwabasi.
Yesu Alandira Ana
Nkhani ya m’Baibulo imati: “Ndipo analinkudza nato kwa Iye tiana kuti akatikhudze.” Ophunzira ake poona zimenezi, anawadzudzula nthaŵi yomweyo. Mwinamwake anaganiza kuti Yesu anali wolemekezeka kwambiri ngakhalenso wotangwanika kosati nkusamala za ana. Talingalirani mmene ophunzirawo anadabwira pamene Yesu anakwiya nawo! “Lolani tiana tidze kwa Ine,” anatero kwa iwo. “Musatiletse: pakuti Ufumu wa Mulungu uli wa totere.” Yesu anapitiriza kuti: “Ndithu ndinena ndi inu, munthu aliyense wosalandira Ufumu wa Mulungu ngati kamwana, sadzaloŵamo konse.”—Marko 10:13-15.
Yesu anaona mikhalidwe yabwino mwa ana. Iwo amafunsafunsa ndipo amakhulupirira munthu wamkulu. Amalandira mawu a makolo awo ngakhalenso kuwachirikiza pakati pa ana anzawo. Mkhalidwe wawo womvera ndi kuphunzitsika ngwoyenera kutsanziridwa ndi onse ofuna kuloŵa mu Ufumu wa Mulungu. Monga mmene Yesu ananenera, “Ufumu wa Mulungu uli wa totere.”—Yerekezerani ndi Mateyu 18:1-5.
Koma Yesu sanali kugwiritsa ntchito anawo mwafanizo chabe. Nkhaniyo imasonyeza bwino kuti Yesu anakondadi kukhala nawo pafupi. Marko akufotokoza kuti Yesu “anatiyangata, natidalitsa, ndi kuika manja ake pa ito.” (Marko 10:16) Nkhani ya Marko ndi yokhayo imene imatchula mfundo yosangalatsa yakuti Yesu “anatiyangata.”a Motero Yesu anachita zoposa zimene makolowo anayembekezera, kuti ‘adzangowakhudza’ anawo.
Kodi Yesu anali kutanthauzanji ‘poika manja ake’ pa anawo? Sanali kuchita mwambo wachipembedzo, monga paubatizo. Ngakhale kuti panthaŵi zina, kuika manja kunatanthauza kupatsa munthu udindo, panthaŵi zina kunangotanthauza kupereka madalitso. (Genesis 48:14; Machitidwe 6:6) Choncho Yesu ayenera kuti anali kudalitsa anawo.
Mulimonsemo, Marko anagwiritsa ntchito liwu lamphamvu la “madalitso” (ka·teu·lo·geʹo), kutanthauza mphamvu yaikulu. Zimenezi zikusonyeza kuti Yesu anadalitsa ana mofunitsitsa, mwachikondi ndiponso mosangalala. Mwachionekere, Yesu sanaone ana monga mtolo wotopetsa ndi wotayitsa nthaŵi.
Phunziro kwa Ife
Njira imene Yesu anachitira ndi ana komanso akulu sinali yowaopseza kapena kuwachepetsa. “Sanali kuchedwa kumwetulira ndiponso anali kuseka,” limatero buku lina la umboni. Nkosadabwitsa kuti anthu amisinkhu yonse ankamasuka kukhala naye. Polingalira za chitsanzo cha Yesu, tingadzifunse kuti, ‘Kodi anthu ena amandiona kukhala wosavuta kulankhula nane’? ‘Kodi ndimaoneka kukhala wotangwanika kwambiri moti sindisamala zochita za ena’? Kukulitsa chidwi chochokera pansi pa mtima mwa anzathu kudzatisonkhezera kudzipereka monga mmene Yesu anachitira. Anthu enanso adzaona chidwi chathu chenicheni ndipo iwo adzayandikira kwa ife.—Miyambo 11:25.
Monga mmene nkhani ya Marko ikusonyezera, Yesu anasangalala kukhala pamodzi ndi ana. Mwachionekere, anapeza nthaŵi ya kuwaonerera pamene anali kuseŵera, popeza anatchula maseŵero awo mu limodzi la mafanizo ake. (Mateyu 11:16-19) Mwinamwake ana ena amene Yesu anawadalitsa anali aang’ono msinkhu kwambiri osatha kumzindikira iye ndi zimene anaphunzitsa. Koma zimenezi sizinampangitse Yesu kuona kuti anali kutaya nthaŵi. Anacheza ndi ana chifukwa anawakonda. Ana ambiri amene Yesu anakumana nawo mu utumiki wake ayenera kuti anasonkhezeredwa kusonyezanso chikondi mwa kukhala ophunzira ake pambuyo pake.
Ngati Yesu anacheza ndi ana m’milungu yomaliza yovuta kwambiri m’moyo wake, ndithudi tiyenera kupatula nthaŵi yocheza nawo pamoyo wathu wotangwanikawu. Tiyenera kukumbukira makamaka aja amene ali ndi zosoŵa zapadera, monga ana amasiye. Ndithudi, ana onse amakula bwino pamene aonetsedwa chisamaliro, ndipo Yehova akufuna kuti tiwaonetse chikondi ndi kuwathandiza mmene tingathere.—Salmo 10:14.
[Mawu a M’munsi]
a Baibulo lina limati Yesu “anawafungata.” Linanso limati “anawanyamula.”