Miyambo
11 Yehova amanyasidwa ndi masikelo achinyengo,
3 Kukhulupirika kwa anthu owongoka mtima nʼkumene kumawatsogolera,+
Koma wochita zinthu mwachinyengo adzawonongedwa chifukwa cha mabodza ake.+
4 Chuma chidzakhala chopanda* phindu pa tsiku la mkwiyo woopsa,+
Koma chilungamo nʼchimene chidzapulumutse munthu ku imfa.+
5 Chilungamo cha munthu wopanda cholakwa chimawongola njira yake,
Koma woipa adzagwa chifukwa cha kuipa kwake komwe.+
6 Chilungamo cha anthu owongoka mtima chidzawapulumutsa,+
Koma anthu ochita zinthu mwachinyengo adzagwidwa ndi zolakalaka zawo.+
7 Munthu woipa akafa, chiyembekezo chake chimathera pomwepo,
Ndipo zonse zimene amayembekezera kuchita ndi mphamvu zake zimalephereka.+
9 Wampatuko* amawononga mnzake ndi pakamwa pake,
Koma anthu olungama amapulumutsidwa chifukwa chodziwa zinthu.+
10 Mzinda umasangalala chifukwa cha makhalidwe abwino a anthu olungama,
Ndipo anthu oipa akawonongedwa anthu amafuula mosangalala.+
11 Mzinda umakhala wapamwamba chifukwa cha madalitso a anthu olungama,+
Koma umagwetsedwa chifukwa cha pakamwa pa anthu oipa.+
12 Aliyense wopanda nzeru amasonyeza kuti akuipidwa ndi* mnzake,
Koma munthu amene alidi wozindikira amakhala chete.+
14 Pakakhala popanda malangizo anzeru, anthu amagwa.
15 Munthu amene amalonjeza kuti adzapereka ngongole ya munthu wachilendo mwiniwakeyo akadzalephera kubweza, zinthu sizidzamuyendera bwino.+
Koma amene amapewa* kugwirana dzanja pochita mgwirizano adzakhala wotetezeka.
20 Anthu amtima wopotoka, Yehova amanyasidwa nawo,+
Koma amene amachita zinthu mosalakwitsa kanthu amamusangalatsa.+
21 Musakaikire mfundo yakuti:* Munthu woipa sadzalephera kulangidwa,+
Koma ana a anthu olungama adzapulumuka.
22 Mofanana ndi ndolo yagolide imene ili pamphuno ya nkhumba,
Ndi mmenenso amakhalira mkazi wokongola amene amakana nzeru.
23 Zimene munthu wolungama amalakalaka zimakhala ndi zotsatira zabwino.+
Koma zimene oipa amayembekezera zimabweretsa mkwiyo woopsa.
24 Munthu amapereka mowolowa manja* ndipo pamapeto pake amakhala ndi zinthu zochuluka.+
Munthu wina amaumira zimene amafunika kupatsa anthu ena, koma amasauka.+
26 Wokana kugulitsa mbewu zake, anthu adzamʼtemberera.
Koma wolola kuzigulitsa adzamudalitsa.
27 Munthu amene amafunitsitsa kuchita zabwino, adzakomeredwa mtima.+
Koma wofunitsitsa kuchita zoipa, zoipazo zidzamʼbwerera.+
28 Munthu amene amadalira chuma chake adzakumana ndi mavuto,+
Koma anthu olungama adzasangalala ngati mtengo wa masamba obiriwira.+
29 Aliyense wobweretsa mavuto* kwa anthu amʼbanja lake cholowa chake chidzakhala mphepo,+
Ndipo munthu wopusa adzakhala wantchito wa munthu wanzeru.