Lingaliro la Baibulo
Kugwirizana pa Zachipembedzo m’Banja—Chifukwa Chake Kuli Kofunika
BANJA lakhala pansi kuti lidye chakudya chamadzulo. Pamene tate akupemphera, mayi akupemphera chamumtima kwa mulungu wina. M’banja lina mayi amapita kutchalitchi, koma mwamuna wake amapita kusunagoge. Alipo mabanja ena amene ali ndi kholo limodzi limene limaphunzitsa ana za Bambo Krisimasi, pamene kholo lina limawauza za Hanukkah.
Malinga ndi kafukufuku wa posachedwapa, zinthu ngati zimenezi zafala kwambiri chifukwa anthu ambiri akukwatirana ndi anthu osakhala achipembedzo chawo. Kafukufuku wina anasonyeza kuti masiku ano ku United States, 21 peresenti ya Akatolika amakwatirana ndi osiyana nawo chikhulupiriro; ndiponso 30 peresenti ya Amormoni; 40 peresenti ya Asilamu; komanso kupitirira 50 peresenti ya Ayuda. Pakuti kwa zaka zambiri anthu akhala akudana kwambiri chifukwa chosiyana zipembedzo, anthu ena akuona kuti kukwatirana ndi anthu a zipembedzo zina n’kugonjetsa kudana pakati pa zipembedzo. Wolemba nyuzi wina analemba kuti: “Maukwati osiyanasiyana a anthu osagwirizana pa chinachake ayenera kuvomerezedwa ndi aliyense.” Kodi limeneli ndi lingaliro la Baibulo?
Tiyenera kuzindikira kuti Baibulo silivomereza kusankhana mtundu kulikonse. Mawu a Mulungu amalimbikitsa kusasankhana mitundu. Mtumwi Petro analongosola momvekera bwino za nkhani imeneyi ponena kuti: “Zoona ndizindikira kuti Mulungu alibe tsankhu; koma m’mitundu yonse, wakumuwopa iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.” (Machitidwe 10:34, 35) Kuphatikiza apo, Baibulo limaphunzitsa kuti atumiki oona a Yehova ayenera kukwatira “mwa Ambuye” mokha. (1 Akorinto 7:39) N’chifukwa chiyani ayenera kutero?
Cholinga cha Ukwati
Mulungu anafuna kuti ukwati ukhale ubwenzi wathithithi kwambiri. (Genesis 2:24) Pamene Mulungu ankakhazikitsa ukwati, sankaganiza za unansi chabe. Pamene Yehova anapatsa mkazi ndi mwamuna oyambawo ntchito yolera ana ndi kusamalira mudzi wawo wa padziko lapansi, iye anasonyeza kuti iwo anayenera kugwira ntchito pamodzi mogwirizana kuti akwaniritse chifuno chake. (Genesis 1:28) Adakatsatira njira imeneyi potumikira Mulungu , mwamuna ndi mkazi adakasangalala, osati chabe ndi unansi, koma ubwenzi wathithithi komanso wokhalitsa.—Yerekezani ndi Malaki 2:14.
Yesu ankanena ubwenzi umenewo pamene ananena mawu otchuka aja akuti: “Salinso awiri koma thupi limodzi. Chifukwa chake ichi chimene Mulungu anachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.” (Mateyu 19:6) Yesu anagwiritsa ntchito mawu ophiphiritsa kuti asonyeze kufanana kwa ukwati ndi goli limene limamangirira pamodzi nyama zonyamula katundu kuti zizikoka kapena kusuntha katundu limodzi. Taganizani mmene zingavutire ngati nyama ziŵiri zimene zili pagoli zikukokera golilo mbali zosiyana! Mofananamo, amene amakwatira kunja kwa chikhulupiriro choona angavutike kuti akhale mogwirizana ndi malamulo a Baibulo uku mkazi kapena mwamuna wawo akuwatsutsa. Baibulo limalondola pamene limati: “Musakhale omangidwa m’goli ndi osakhulupira.”—2 Akorinto 6:14.
Ukwati Wabwino
Kugwirizana pakulambira koona kungalimbitse banja kwambiri. Wolemba wina anatsirira ndemanga yakuti “Kulambira pamodzi ndiko chizindikiro china chachikulu cha mabanja athanzi, ndi achimwemwe.” Mlaliki 4:9, 10 amati: “Aŵiri aposa mmodzi; pakuti ali ndi mphotho yabwino m’ntchito zawo. Pakuti akagwa, wina adzautsa mnzake.”
Popanga kulambira kukhala chinthu chofunika kwambiri m’moyo wawo, anthu achikristu okwatirana amakhala ogwirizana osati mwakuthupi chabe komanso mwauzimu. Pamene akupemphera pamodzi, kuphunzira Mawu a Mulungu pamodzi, kusonkhana ndi Akristu anzawo, ndi kuuza ena chikhulupiriro chawo, amaumba ubwenzi wauzimu umene umawayanjanitsa kwambiri muukwatimo. Mkazi wina wachikristu anatsirira ndemanga iyi: “Kulambira koona ndi mbali ya moyo wa munthu. Sindingasankhe dala kukwatiwa ndi munthu amene malinga ndi chikhulupiriro chake samandiona monga mmene ndimadzionera.”—Yerekezani ndi Marko 3:35.
Amene amakwatiwa “mwa ambuye” amadziŵa kuti amuna awo adzatsanzira chitsanzo cha Yesu cha makhalidwe. Amuna achikristu ayenera kuchitira akazi awo monga mmene Yesu anachitira mwachikondi ndi mpingo. Akazi achikristu ayenera kuchitira amuna awo ulemu. (1 Akorinto 11:3; Aefeso 5:25, 29, 33) Akristu amachita zimenezi osati chifukwa cha chikhumbo chofuna kusangalatsana, koma chofuna kusangalatsa Mulungu, amene amaona zimene anthu okwatirana onse amachitirana.—Malaki 2:13, 14; 1 Petro 3:1-7.
Kukhulupirira zinthu zofanana kumachititsanso Akristu okwatirana kuthetsa kusagwirizana kwinakwake mwamtendere. Baibulo limalangiza Mkristu aliyense kusamala kuti “asapenyerere zake za iye yekha, koma yense apenyererenso za mnzake.” (Afilipi 2:4) Ngakhale kuti munthu aliyense amafuna kuti zinthu zikhale mmene amakondera, okwatirana amene ali ogwirizana m’chikhulupiriro amafuna kutsogozedwa ndi Mulungu pothetsa kusagwirizana kwawo kulikonse. (2 Timoteo 3:16, 17) Potero amatsatira malangizo a Baibulo kwa Akristu kuti ayenera kukhala “amaganizo amodzi.”—1 Akorinto 1:10, NW; 2 Akorinto 13:11; Afilipi 4:2.
Kukondana Komanso Kukonda Zinthu Zofanana
N’zoona kuti banja si kungokhala ndi chikhulupiriro chofanana kokha ayi. Kukondana ndi kofunikanso. (Nyimbo ya Solomo 3:5; 4:7, 9; 5:10) Koma kuti banja lipitirirebe, kukonda zinthu zofanana n’kofunika kwambiri. Malingana ndi buku lotchedwa Are you the One For Me? (Kodi Ndiwe Wondiyenera?) “anthu okwatirana amene amakondanso zinthu zofanana amakhala ndi mwayi waukulupo wotha kupanga ubwenzi wosangalala, wogwirizana, ndiponso wokhalitsa.”
Tsoka ilo, anthu amene akondana mwina sangakambirane zinthu zikuluzikulu zimene amasiyana mpaka atakwatirana. Mongoyerekeza, taganizirani mutagula nyumba imene chifukwa chachikulu chimene mwaikondera ndicho maonekedwe ake. Komano, mukuzindikira kuti maziko ake ndi achabechabe mutaloŵamo kale. Chifukwa chakuti maziko ake ndi osalimba zina zonse zimene zinali kupangitsa nyumbayo kuoneka ngati yokongola zimakhala zopanda pake. Mofananamo, munthu angathe kukondana ndi munthu wosiyana naye chikhulupiriro amene akuoneka kuti angagwirizane naye maganizo—koma atakwatirana angapeze kuti ubwenzi wawo ndi wosalimba ngakhale pang’ono.
Taganizirani mavuto ena amene angabwere panthaŵi ina m’maukwati a anthu osiyana zipembedzo: Kodi banjalo lizikalambira kuti? Kodi nanga pa nkhani ya zauzimu ana aziphunzitsidwa ku chipembedzo chiti? Kodi ndalama zoperekedwa pochirikiza chipembedzo ziziperekedwa ku chipembedzo chiti? Kodi mkazi kapena mwamuna azilimbikira kuchita nawo miyambo inayake yachipembedzo imene mnzakeyo amaiona ngati yachikunja? (Yesaya 52:11) Banja lililonse limafunika kuti aliyense wa okwatiranawo ayenera kusintha ndithu zina ndi zina; komabe, kusatsatira malamulo a Baibulo—ngakhale pachifukwa chofuna kupulumutsa banja—n’kosaloleka kwa Mulungu.—Yerekezani ndi Deuteronomo 7:3, 4; Nehemiya 13:26, 27.
Kuti apitirire kukhala mwamtendere m’banjamo, okwatirana ena amene mabanja awo ali ogawanika mwachipembedzo amachita zinthu zokhudza chipembedzo chawo paokhapaokha. Komabe, n’zomvetsa chisoni, kuti kupembedza mosiyana kumachititsa kuti m’banjamo mukhale mpata wauzimu. Mayi wina wachikristu amene anakwatiwa ndi munthu amene sanali wa chikhulupiriro chake anati: “Ngakhale kuti tinali titakwatirana kwa zaka 40, mwamuna wanga sankandidziwa bwinobwino ayi.” Koma banja limene mwamuna pamodzinso ndi mkazi, amalambira “mumzimu ndi m’choonadi,” limaona Mulungu kukhala wofunika kwambiri. Baibulo limanena zimenezi m’mwambi wakuti, “chingwe cha nkhosi zitatu sichiduka msanga.”— Yohane 4:23, 24; Mlaliki 4:12.
Nanga Ana Bwanji?
Ena amene amaganiza zodzakhala ndi banja la zikhulupiriro zosiyana amalingalira kuti adzawasonyeza ana awowo zipembedzo zonse ziŵiri ndi kuwalola kuti asankhepo okha. N’zoona kuti makolo onse aŵiri ali ndi kuyenera kwa lamulo komanso monga mwa makhalidwe koti angathe kuwaphunzitsa ana awo zauzimu, koma potsiriza anawo amasankha okha choti achite.a
Baibulo limalangiza ana kuti ayenera kumvera makolo onse “mwa Ambuye.” (Aefeso 6:1) Miyambo 6:20 amanena zomwezi motere: “Mwananga, sunga malangizo a atate wako, usasiye malamulo a mako.” M’malo mosonyezedwa ziphunzitso zosiyana, ana oleredwa ndi makolo onse aŵiri okhala ndi chikhulupiriro chofanana amakhala ogwirizana mu njira imene Baibulo limaitcha kuti “Ambuye mmodzi, chikhulupiriro chimodzi, ubatizo umodzi.”—Aefeso 4:5; Deuteronomo 11:19.
“Mwa Ambuye” Mwenimwenidi
Ngati kukonda zinthu zofanana kuli njira yokhalira ndi banja lopambana, kodi kungakhale kwa nzeru kukwatira kapena kukwatiwa ndi aliyense kungoti poti amati ndi Mkristu? Baibulo limayankha motere: “Iye wakunena kuti akhala mwa Iye [Yesu], ayeneranso mwini wake kuyenda monga anayenda Iyeyo.” (1 Yohane 2:6) Choncho, Mkristu amene akufuna kukwatira kapena kukwatiwa ayeneranso kufuna mnzake wachikristu amene amafunitsitsadi kutsatira Yesu. Woyembekeza kukwatiwa naye ameneyu ayenera kukhala kuti anapatulira moyo wake kwa Mulungu ndipo anabatizidwa. Ndiye kutinso amatsanzira mkhalidwe wachikondi wa Yesu ndi kulalikira kwake kwa changu Ufumu wa Mulungu. Monga momwe anali kuchitira Yesu, ndiye kuti nayenso chinthu chofunika kwambiri m’moyo mwake ndicho kuchita chifuniro cha Mulungu.— Mateyu 6:33; 16:24; Luka 8:1; Yohane 18:37.
Amene akufuna kukwatira koma n’kumadikirabe mopirira kuti apeze mnzawo wowayenera m’banja la olambira Mulungu, akusonyeza chizoloŵezi cha kuika chifuno cha Mulungu patsogolo m’moyo wawo. Potsirizira pake chizoloŵezi chimenechi chimadzachititsa kuti banja lidzakhale lachimwemwe, ndiponso lokhutiritsa.—Mlaliki 7:8; Yesaya 48:17,18.
[Mawu a M’munsi]
a Onani nkhani yakuti “Lingaliro la Baibulo: Kodi Ana Ayenera Kudzisankhira Chipembedzo Chawo?” mu Galamukani! wa March 8, 1997 masamba 26-7. Onaninso, masamba 24-5 a bolosha la Mboni za Yehova ndi Maphunziro, lofalitsidwa ndi Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania, 1995.
[Bokosi patsamba 20]
Chithanzo kwa Mabanja Osiyana Zipembedzo
Pazifukwa zosiyanasiyana mabanja ambiri tsopano lino ndi osiyana zipembedzo. Ena anachita kusankha kupeza mnzawo amene ali wa chipembedzo china. Koma mabanja ambiri anali ndi chikhulupiriro chofanana poyamba, koma kenaka anagawanika zipembedzo nthaŵi imene mmodzi wa iwo anayamba mtundu wina wa kupembedza. Palinso zinthu zina zimene zimapangitsa kusiyana zipembedzo m’banja. Komabe, kaya zifukwazo zikhale zotani, okwatiranawo sayenera kuswa kapena kuchepetsa malumbiro a ukwati kokha chifukwa chakuti asiyana maganizo pa kusankha kwawo chipembedzo. Baibulo limalemekeza kuyera komanso kukhazikika kwa ukwati, ngakhale ngati okwatiranawo sali ogwirizana pakulambira. (1 Petro 3:1, 2) Mtumwi Paulo analemba kuti: “Ngati mbale wina ali naye mkazi wosakhulupira, ndipo iye avomera mtima kukhala naye pamodzi, asalekane naye.” (1 Akorinto 7:12) Ngati atagwiritsidwa ntchito, malamulo amene ali m’Baibulo angathe kuthandiza banja lililonse kukhala ndi mtendere muubwenzi wachikondi komanso wolemekezeka.— Aefeso 5:28-33; Akolose 3:12-14; Tito 2:4, 5; 1 Petro 3:7-9.