Deuteronomo
11 “Muzikonda Yehova Mulungu wanu+ ndipo nthawi zonse muzichita zofuna zake, kutsatira malangizo ake, zigamulo zake komanso malamulo ake. 2 Inuyo mukudziwa kuti lero ndikulankhula ndi inu, osati ndi ana anu amene sakudziwa komanso sanaone chilango cha Yehova Mulungu wanu,+ ukulu wake,+ dzanja lake lamphamvu+ komanso mkono wake wotambasula. 3 Iwo sanaone zizindikiro ndi zinthu zimene anachita mʼdziko la Iguputo kwa Farao mfumu ya Iguputo komanso mʼdziko lake lonse.+ 4 Sanaonenso zimene Mulungu anachitira gulu la asilikali a ku Aiguputo, mahatchi a Farao ndi magaleta ake ankhondo, amene anamira mʼmadzi a mʼNyanja Yofiira pamene ankakuthamangitsani, ndipo Yehova anawawononga nʼkutheratu.+ 5 Iwo sanaone zimene Mulungu wakuchitirani mʼchipululu mpaka kudzafika malo ano, 6 kapena zimene anachitira Datani ndi Abiramu, ana a Eliyabu, mwana wa Rubeni, pamene dziko linatsegula pakamwa pake nʼkuwameza pamodzi ndi mabanja awo, matenti awo ndi chamoyo chilichonse chimene anali nacho. Dziko linawameza Aisiraeli onse akuona.+ 7 Inu munaona ndi maso anu zinthu zonse zazikulu zimene Yehova anachita.
8 Muzisunga malamulo onse amene ndikukupatsani lero, kuti mukhale amphamvu nʼkulowa mʼdziko limene mukuwolokerako kuti mukalitenge kukhala lanu, 9 kutinso mukhale ndi moyo nthawi yaitali+ mʼdziko limene Yehova analumbira kwa makolo anu kuti adzawapatsa iwowo ndi mbadwa* zawo,+ dziko loyenda mkaka ndi uchi.+
10 Dziko limene mukupita kukalitenga kuti likhale lanu, si lofanana ndi dziko la Iguputo limene munatulukamo. Kumeneko munkafesa mbewu zanu nʼkumazithirira ndi mapazi* anu ngati kuti mukuthirira dimba la ndiwo zamasamba. 11 Koma dziko limene mwatsala pangʼono kuwolokerako nʼkukalitenga kuti likhale lanu ndi dziko lamapiri ndi zigwa.+ Limamwa madzi a mvula amene amagwa kuchokera kumwamba.+ 12 Limeneli ndi dziko limene Yehova Mulungu wanu akulisamalira. Nthawi zonse maso a Yehova Mulungu wanu amakhala padziko limeneli, kuyambira kumayambiriro kwa chaka mpaka kumapeto.
13 Ndiyeno mukadzamvera mokhulupirika malamulo anga amene ndikukupatsani lero, komanso kukonda Yehova Mulungu wanu nʼkumamutumikira ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse,+ 14 ndidzakupatsaninso mvula pa nthawi yake mʼdziko lanu, mvula yoyambirira ndi mvula yomaliza, ndipo mudzakolola mbewu zanu nʼkukhala ndi vinyo watsopano komanso mafuta.+ 15 Ndidzameretsa msipu mʼdziko lanu kuti ziweto zanu zidye, ndipo inu mudzadya nʼkukhuta.+ 16 Samalani kuti mitima yanu isakopeke nʼkupatuka ndi kuyamba kulambira milungu ina nʼkumaiweramira.+ 17 Mukatero mkwiyo wa Yehova udzakuyakirani ndipo iye adzatseka kumwamba moti mvula sidzagwa+ komanso nthaka sidzapereka zokolola zake. Zikadzatero mudzatha mofulumira mʼdziko labwino limene Yehova akukupatsani.+
18 Mawu angawa muwasunge mʼmitima yanu ndipo muziwatsatira pa moyo wanu. Muwamange padzanja lanu kuti muziwakumbukira ndipo akhale ngati chomanga pachipumi panu.*+ 19 Muziphunzitsa ana anu mawu amenewa, ndipo muzilankhula nawo mawuwa mukakhala pansi mʼnyumba mwanu, mukamayenda pamsewu, mukamagona komanso mukadzuka.+ 20 Muziwalemba pamafelemu a nyumba zanu ndi pamageti a mizinda yanu, 21 kuti inuyo ndi ana anu mukhale ndi moyo wautali+ mʼdziko limene Yehova analumbira kwa makolo anu kuti adzawapatsa,+ kwa nthawi yonse imene thambo lidzakhale pamwamba pa dziko lapansi.
22 Mukasunga mosamala malamulo onsewa amene ndikukupatsani nʼkumawatsatira, kukonda Yehova Mulungu wanu,+ kuyenda mʼnjira zake zonse ndi kumʼmamatira,+ 23 Yehova adzathamangitsa mitundu yonseyi pamaso panu,+ ndipo mitundu yamphamvu ndi yaikulu kuposa inu mudzailanda dziko.+ 24 Malo alionse amene mapazi anu adzaponde adzakhala anu.+ Malire a dziko lanu adzayambira kuchipululu kukafika ku Lebanoni, kuyambira ku mtsinje wa Firate, kukafika kunyanja yakumadzulo.*+ 25 Palibe munthu amene adzalimbane nanu.+ Yehova Mulungu wanu adzachititsa dziko lonse limene mudzayendemo kugwidwa ndi mantha aakulu ndipo adzakuopani,+ mogwirizana ndi zimene anakulonjezani.
26 Onani, lero ndikuika dalitso ndi temberero pamaso panu:+ 27 mudzalandira dalitsoli mukadzamvera malamulo a Yehova Mulungu wanu, amene ndikukupatsani lero,+ 28 ndipo mudzalandira temberero limeneli ngati simudzamvera malamulo a Yehova Mulungu wanu,+ nʼkupatuka panjira imene ndikukulamulani lero kuti muziyendamo nʼkuyamba kutsatira milungu imene simukuidziwa.
29 Yehova Mulungu wanu akadzakulowetsani mʼdziko limene mukupita kukalitenga kuti likhale lanu, mukatchule dalitsoli paphiri la Gerizimu ndipo temberero mukalitchulire* paphiri la Ebala.+ 30 Pajatu mapiri amenewa ali kutsidya lina la mtsinje wa Yorodano chakumadzulo,* mʼdziko la Akanani amene akukhala ku Araba, moyangʼanizana ndi Giligala, pafupi ndi mitengo ikuluikulu ya ku More.+ 31 Inu muwoloka Yorodano nʼkukalowa mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani kuti likhale lanu.+ Mukakalitenga nʼkuyamba kukhalamo, 32 muzikaonetsetsa kuti mukusunga malamulo ndi zigamulo zonse zimene ndikuika pamaso panu lero.”+