Mafunso Ogwiritsa Ntchito Pophunzira Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
Nkhani 1
Mulungu Ayamba Kupanga Zinthu
Kodi zinthu zonse zabwino zinachokera kuti, ndipo kodi mungapereke chitsanzo cha zinthu zimenezi?
Kodi chinthu choyamba chimene Mulungu analenga n’chiyani?
N’chifukwa chiyani mngelo woyamba anali wapadera kwambiri?
Fotokozani mmene dziko lapansi linalili poyambirira. (Onani chithunzi.)
Kodi Mulungu anayamba n’kuchita chiyani pokonza dziko lapansi kuti padzakhale zinyama ndi anthu?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Yeremiya 10:12.
Kodi ndi makhalidwe ati a Mulungu amene amaoneka m’chilengedwe chake? (Yes. 40:26; Aroma 11:33)
Ŵerengani Akolose 1:15-17.
Kodi Yesu anachita chiyani pa ntchito yolenga zinthu, ndipo zimenezi ziyenera kukhudza bwanji mmene timamuonera? (Akol. 1:15-17)
Ŵerengani Genesis 1:1-10.
Kodi dziko lapansi linachokera kuti? (Gen. 1:1)
Kodi n’chiyani chinachitika pa tsiku loyamba lolenga zinthu? (Gen. 1:3-5)
Fotokozani zimene zinachitika m’tsiku lachiŵiri lolenga zinthu. (Gen. 1:7, 8)
Nkhani 2
Munda Wokongola
Kodi Mulungu anakonza bwanji dziko lapansi kuti likhale malo athu okhalamo?
Tchulani mitundu yosiyanasiyana ya zinyama zimene Mulungu anapanga. (Onani chithunzi.)
N’chifukwa chiyani munda wa Edene unali wapadera?
Kodi Mulungu anafuna kuti dziko lonse lapansi likhale chiyani?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Genesis 1:11-25.
Kodi Mulungu analenga chiyani pa tsiku lachitatu lolenga zinthu? (Gen. 1:12)
Kodi n’chiyani chinachitika pa tsiku lachinayi lolenga zinthu? (Gen. 1:16)
Kodi Mulungu anapanga zinyama zamitundu yotani pa tsiku lachisanu ndi lachisanu ndi chimodzi? (Gen. 1:20, 21, 25)
Ŵerengani Genesis 2:8, 9.
Kodi Mulungu anaika mitengo iŵiri yapadera yotani m’mundamo, ndipo kodi inaimira chiyani?
Nkhani 3
Mwamuna ndi Mkazi Oyamba
Kodi chithunzi chimene chili mu Nkhani 3 chikusiyana bwanji ndi chimene chili mu Nkhani 2?
Kodi ndani anapanga mwamuna woyamba, ndipo kodi dzina la mwamunayo linali ndani?
Kodi Mulungu anapatsa Adamu ntchito yotani?
N’chifukwa chiyani Mulungu anagonetsa Adamu tulo tatikulu?
Kodi Adamu ndi Hava akanakhala ndi moyo kwa nthaŵi yaitali bwanji, ndipo kodi Yehova anafuna kuti agwire ntchito yotani?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Salmo 83:18.
Kodi Mulungu dzina lake ndani, ndipo ali ndi ulamuliro wapadera wotani padziko lapansi? (Yer. 16:21; Dan. 4:17)
Ŵerengani Genesis 1:26-31.
Ŵerengani Genesis 2:7-25.
Kodi Adamu anafunikira kuchita chiyani kuti akwanitse ntchito imene anapatsidwa yotcha maina zinyama? (Gen. 2:19)
Kodi lemba la Genesis 2:24 limatithandiza bwanji kuona mmene Yehova amaonera ukwati, kupatukana, ndi kusudzulana? (Mat. 19:4-6, 9)
Nkhani 4
Chifukwa Chake Anataya Malo Ao
M’chithunzichi, kodi n’chiyani chikuchitikira Adamu ndi Hava?
N’chifukwa chiyani Yehova anawalanga?
Kodi njoka inamuuza chiyani Hava?
Kodi ndani anachititsa njokayo kulankhula ndi Hava?
N’chifukwa chiyani Adamu ndi Hava anataya malo awo okhala a Paradaiso?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Genesis 2:16, 17 ndi 3:1-13, 24.
Kodi funso limene njoka inafunsa Hava linapereka bwanji chithunzi cholakwika cha Yehova? (Gen. 3:1-5; 1 Yoh. 5:3)
Kodi Hava ndi chitsanzo chotichenjeza m’njira yotani? (Afil. 4:8; Yak. 1:14, 15; 1 Yoh. 2:16)
Kodi Adamu ndi Hava analephera bwanji kuvomereza kulakwa kwawo? (Gen. 3:12, 13)
Kodi akerubi amene anaikidwa kum’maŵa kwa munda wa Edene anasonyeza bwanji kuti anali ku mbali ya ulamuliro wa Yehova? (Gen. 3:24)
Ŵerengani Chivumbulutso 12:9.
Kodi zinthu zamuyendera bwanji Satana pa ntchito yake yosocheretsa anthu kuti asamvere ulamuliro wa Mulungu? (1 Yoh. 5:19)
Nkhani 5
Moyo Wobvuta Uyamba
Kodi moyo wa Adamu ndi Hava unali wotani kunja kwa munda wa Edene?
N’chiyani chinayamba kuchitikira Adamu ndi Hava, ndipo n’chifukwa chiyani?
N’chifukwa chiyani ana a Adamu ndi Hava anali oti adzakalamba ndi kufa?
Ngati Adamu ndi Hava akanamvera Yehova, kodi iwowo ndi ana awo akanakhala ndi moyo wotani?
Kodi kusamvera kunamubweretsera bwanji ululu Hava?
Kodi maina a ana aamuna aŵiri oyambirira a Adamu ndi Hava anali ndani?
Kodi ana enawo m’chithunzichi ndi ndani?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Genesis 3:16-23 ndi 4:1, 2.
Kodi moyo wa Adamu unakhudzidwa bwanji ndi kutembereredwa kwa nthaka? (Gen. 3:17-19; Aroma 8:20, 22)
Kodi dzina loti Hava, lotanthauza kuti “Wamoyo,” linali loyenerera chifukwa chiyani? (Gen. 3:20)
Kodi Yehova anasonyeza bwanji kuti anali kuganizira Adamu ndi Hava ngakhale atachimwa? (Gen. 3:7, 21)
Ŵerengani Chivumbulutso 21:3, 4.
Kodi ndi zinthu ‘zoyamba’ ziti zimene mukufunitsitsa kudzaona zitachotsedwa?
Nkhani 6
Mwana Wabwino, ndi Woipa
Kodi Kaini ndi Abele ayamba kugwira ntchito zotani?
Kodi Kaini ndi Abele abweretsa mphatso zotani kwa Yehova?
N’chifukwa chiyani Yehova akukondwera ndi mphatso ya Abele, ndipo n’chifukwa chiyani sakukondwera ndi mphatso ya Kaini?
Kodi Kaini ndi munthu wotani, ndipo Yehova akuyesera bwanji kumuthandiza kuti asinthe?
Kodi Kaini akuchita chiyani ali aŵiriŵiri ndi mbale wake kumunda?
Fotokozani zimene zinachitika kwa Kaini atapha mbale wake.
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Genesis 4:2-26.
Kodi Yehova anafotokoza motani ngozi imene Kaini analimo? (Gen. 4:7)
Kodi Kaini anasonyeza bwanji mtima umene anali nawo? (Gen. 4:9)
Kodi Yehova amaona bwanji kukhetsa mwazi wa munthu wosalakwa? (Gen. 4:10; Yes. 26:21)
Ŵerengani 1 Yohane 3:11, 12.
N’chifukwa chiyani Kaini anakwiya kwambiri, ndipo kodi zimenezi ndi chenjezo kwa ife masiku ano motani? (Gen. 4:4, 5; Miy. 14:30; 28:22)
Kodi Baibulo limasonyeza motani kuti ngakhale makolo ndi achibale athu onse atakhala otsutsa Yehova, tingakhalebe okhulupirika kwa iye? (Sal. 27:10; Mat. 10:21, 22)
Ŵerengani Yohane 11:25.
Kodi Yehova amatilimbikitsa bwanji za anthu onse amene amafa chifukwa chochita chilungamo? (Yoh. 5:24)
Nkhani 7
Munthu Wolimba Mtima
Kodi Enoke anali wosiyana motani ndi anthu ena?
N’chifukwa chiyani anthu a m’nthaŵi ya Enoke anachita zoipa zambiri?
Kodi anthu ankachita zinthu zoipa zotani? (Onani chithunzi.)
N’chifukwa chiyani Enoke anafunika kulimba mtima?
Kodi m’masiku amenewo anthu ankakhala ndi moyo zaka zingati, koma kodi Enoke anakhala ndi moyo zaka zingati?
Kodi chinachitika n’chiyani Enoke atafa?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Genesis 5:21-24, 27.
Ŵerengani Genesis 6:5.
Kodi zinthu zinaipa motani padziko lapansi Enoke atafa, ndipo kodi zimenezi tingaziyerekezere bwanji ndi zimene zikuchitika masiku ano? (2 Tim. 3:13)
Ŵerengani Ahebri 11:5.
Kodi ndi khalidwe liti la Enoke limene ‘linakondweretsa Mulungu,’ ndipo zotsatirapo zake zinali zotani? (Gen. 5:22)
Ŵerengani Yuda 14, 15.
Kodi Akristu masiku ano angatsanzire bwanji kulimba mtima kwa Enoke pochenjeza anthu za nkhondo ya Armagedo imene ikubwera? (2 Tim. 4:2; Aheb. 13:6)
Nkhani 8
Zimphona pa Dziko
Kodi chinachitika n’chiyani pamene angelo ena a Mulungu anamvera Satana?
N’chifukwa chiyani angelo ena anasiya ntchito yawo kumwamba n’kubwera padziko lapansi?
N’chifukwa chiyani angelowo analakwa pobwera padziko lapansi n’kudzipangira matupi aumunthu?
Kodi ana a angelowo anali osiyana ndi anthu ena motani?
Monga momwe mukuonera pa chithunzipa, kodi ana a angelowo anachita chiyani pamene anasanduka zimphona?
Enoke atafa, kodi ndi munthu wabwino uti amene anakhala padziko lapansi, ndipo n’chifukwa chiyani Mulungu anamukonda?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Genesis 6:1-8.
Kodi lemba la Genesis 6:6 limasonyeza chiyani za mmene khalidwe lathu lingakhudzire mmene Yehova amamvera? (Sal. 78:40, 41; Miy. 27:11)
Ŵerengani Yuda 6.
Kodi angelo amene ‘sanasunge chikhalidwe chawo choyamba’ m’masiku a Nowa ali ngati chikumbutso kwa ife masiku ano motani? (1 Akor. 3:5-9; 2 Pet. 2:4, 9, 10)
Nkhani 9
Nowa Akhoma Chingalawa
Kodi m’banja la Nowa munali anthu angati, ndipo mayina a ana ake aamuna atatu anali ndani?
Kodi ndi kanthu kachilendo kotani kamene Mulungu anapempha Nowa kuchita, ndipo anamupempha kuchita zimenezi chifukwa chiyani?
Kodi anthu okhala pafupi ndi Nowa anachita chiyani pamene anawauza za chingalawa?
Kodi Mulungu anauza Nowa kuti achite chiyani ndi zinyama?
Mulungu atatseka khomo la chingalawa, kodi Nowa ndi banja lake anafunika kuchita chiyani?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Genesis 6:9-22.
Kodi n’chiyani chinachititsa Nowa kukhala munthu wabwino kopambana wolambira Mulungu woona? (Gen. 6:9, 22)
Kodi Yehova amachiona bwanji chiwawa, ndipo kodi zimenezi ziyenera kukhudza bwanji mmene timasankhira zosangalatsa? (Gen. 6:11, 12; Sal. 11:5)
Kodi tingatsanzire bwanji Nowa pamene talandira malangizo kudzera ku gulu la Yehova? (Gen. 6:22; 1 Yoh. 5:3)
Ŵerengani Genesis 7:1-9.
Kodi mfundo yakuti Yehova anaona munthu wopanda ungwiroyo Nowa monga munthu wolungama imatilimbikitsa bwanji masiku ano? (Gen. 7:1; Miy. 10:16; Yes. 26:7)
Nkhani 10
Chigumula Chachikulu
N’chifukwa chiyani sizikanatheka kuti munthu wina aliyense aloŵe m’chingalawa pamene mvula inayamba kugwa?
Kodi Yehova anachititsa mvula kugwa kwa mausana ndi mausiku angati, ndipo madziwo anakwera mpaka kufika pati?
Kodi n’chiyani chinachitikira chingalawa pamene madzi anayamba kumiza dziko lapansi?
Kodi zimphona zinapulumuka pa Chigumula, nanga n’chiyani chinachitikira atate awo a zimphonazo?
Kodi n’chiyani chinachitikira chingalawa patatha miyezi isanu?
N’chifukwa chiyani Nowa anatulutsa khungubwi m’chingalawamo?
Kodi Nowa anadziŵa bwanji kuti madzi aphwa padziko?
Kodi Mulungu ananena chiyani kwa Nowa, iye ndi banja lake atakhala m’chingalawa kwa nthaŵi yopitirira chaka chimodzi?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Genesis 7:10-24.
Ŵerengani Genesis 8:1-17.
Kodi lemba la Genesis 8:17 limasonyeza bwanji kuti cholinga cha Yehova choyambirira cha dziko lapansi sichinasinthe? (Gen. 1:22)
Ŵerengani 1 Petro 3:19, 20.
Kodi angelo opanduka atabwerera kumwamba anaweruzidwa motani? (Yuda 6)
Kodi nkhani ya Nowa ndi banja lake imalimbitsa bwanji chikhulupiriro chathu choti Yehova angathe kupulumutsa anthu ake? (2 Pet. 2:9)
Nkhani 11
Utawaleza Woyamba
Monga momwe asonyezera pachithunzipa, kodi chinthu choyamba chimene Nowa anachita atatuluka m’chingalawa chinali chiyani?
Kodi Mulungu anapatsa Nowa ndi banja lake lamulo lotani Chigumula chitatha?
Kodi Mulungu analonjeza chiyani?
Tikaona utawaleza, kodi uyenera kutikumbutsa chiyani?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Genesis 8:18-22.
Kodi ifeyo masiku ano tingapereke bwanji ‘chonunkhira chokondweretsa’ kwa Yehova? (Gen. 8:21; Aheb. 13:15, 16)
Kodi Yehova ananena chiyani chokhudza mtima wa munthu, ndipo tiyenera kuchenjera ndi chiyani? (Gen. 8:21; Mat. 15:18, 19)
Ŵerengani Genesis 9:9-17.
Kodi Mulungu anapanga pangano lotani ndi zolengedwa zonse zapadziko lapansi? (Gen. 9:10, 11)
Kodi pangano la utawaleza lidzakhalapo mpaka liti? (Gen. 9:16)
Nkhani 12
Anthu Amanga Chinsanja
Kodi Nimrode anali ndani, ndipo kodi Mulungu ankamuona bwanji munthu ameneyu?
M’chithunzichi, n’chifukwa chiyani anthu anali kuumba njerwa?
N’chifukwa chiyani Yehova sanakondwere ndi ntchito yomangayo?
Kodi Mulungu analetsa bwanji ntchito yomanga chinsanjayo?
Kodi mzindawo unatchedwa chiyani, ndipo kodi dzina limenelo linatanthauza chiyani?
Kodi n’chiyani chinachitikira anthuwo Mulungu atasokoneza zinenero zawo?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Genesis 10:1, 8-10.
Kodi Nimrode anasonyeza makhalidwe otani, ndipo kodi zimenezi zikutipatsa chenjezo lotani? (Miy. 3:31)
Ŵerengani Genesis 11:1-9.
Kodi cholinga chomangira chinsanja chinali chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani zinali zachidziŵikire kuti ntchito yomangayo sipita patali? (Gen. 11:4; Miy. 16:18; Yoh. 5:44)
Nkhani 13
Abrahamu—Bwenzi la Mulungu
Kodi mu mzinda wa Uri munkakhala anthu otani?
Kodi munthu amene ali m’chithunziyu ndi ndani, anabadwa liti, ndipo ankakhala kuti?
Kodi Mulungu anauza Abrahamu kuchita chiyani?
N’chifukwa chiyani Abrahamu anatchedwa bwenzi la Mulungu?
Kodi ndani anapita nawo ndi Abrahamu pamene anachoka ku Uri?
Kodi Mulungu anauza Abrahamu chiyani atafika ku dziko la Kanani?
Kodi Mulungu analonjeza Abrahamu chiyani pamene anali ndi zaka 99?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Genesis 11:27-32.
Kodi pakati pa Abrahamu ndi Loti panali ubale wotani? (Gen. 11:27)
Ngakhale kuti Tera ndi amene anadziŵika kuti anasamutsira banja lake ku Kanani, tikudziŵa bwanji kuti kwenikweni anali Abrahamu amene anayambitsa zimenezi, ndipo n’chifukwa chiyani anatero? (Gen. 11:31; Mac. 7:2-4)
Ŵerengani Genesis 12:1-7.
Kodi Yehova ananena mfundo zina zotani zowonjezera pa pangano la Abrahamu pamene Abrahamu anafika ku dziko la Kanani? (Gen. 12:7)
Ŵerengani Genesis 17:1-8, 15-17.
Kodi dzina la Abramu linasinthidwa motani ali ndi zaka 99, ndipo n’chifukwa chiyani linasinthidwa? (Gen. 17:5)
Kodi Yehova analonjeza Sara madalitso otani a m’tsogolo? (Gen. 17:15, 16)
Ŵerengani Genesis 18:9-19.
Kodi pa Genesis 18:19 akutiuza kuti atate ali ndi udindo wotani? (Deut. 6:6, 7; Aef. 6:4)
Kodi n’chiyani chimene chinachitikira Sara chimene chikusonyeza kuti Yehova sitingam’bisire chilichonse? (Gen. 18:12, 15; Sal. 44:21)
Nkhani 14
Mulungu Ayesa Abrahamu
Kodi Mulungu analonjeza Abrahamu chiyani, ndipo kodi Mulungu anasunga bwanji lonjezo lake?
Monga momwe chithunzichi chikusonyezera, kodi Mulungu anayesa bwanji chikhulupiriro cha Abrahamu?
Kodi Abrahamu anachita chiyani, ngakhale kuti sanamvetsetse cholinga cha zimene Mulungu anamulamula kuchita?
Kodi n’chiyani chinachitika pamene Abrahamu anatenga mpeni kuti aphe mwana wake?
Kodi chikhulupiriro cha Abrahamu mwa Mulungu chinali cholimba motani?
Kodi Mulungu anapereka chiyani kwa Abrahamu kuti aphere nsembe, ndipo anachita zimenezi motani?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Genesis 21:1-7.
N’chifukwa chiyani Abrahamu anadula mwana wake pa tsiku lake lachisanu ndi chitatu? (Gen. 17:10-12; 21:4)
Ŵerengani Genesis 22:1-18.
Kodi Isake anasonyeza bwanji kugonjera kwa atate ake, Abrahamu, ndipo zimenezi zinaimira bwanji chochitika cham’tsogolo chofunika kwambiri kuposa chimenechi? (Gen. 22:7-9; 1 Akor. 5:7; Afil. 2:8, 9)
Nkhani 15
Mkazi wa Loti Anacheuka
N’chifukwa chiyani Abrahamu ndi Loti analekana?
N’chifukwa chiyani Loti anasankha kukakhala ku Sodomu?
Kodi anthu a ku Sodomu anali otani?
Kodi angelo aŵiri anachenjeza Loti za chiyani?
N’chifukwa chiyani mkazi wa Loti anasanduka chulu cha mchere?
Kodi tingaphunzire chiyani kuchokera pa zimene zinachitikira mkazi wa Loti?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Genesis 13:5-13.
Pa nkhani yothetsa mavuto pakati pa anthu, kodi tingaphunzire chiyani kwa Abrahamu? (Gen. 13:8, 9; Aroma 12:10; Afil. 2:3, 4)
Ŵerengani Genesis 18:20-33.
Kodi zimene Yehova anachita ndi Abrahamu zimatitsimikizira motani kuti Yehova ndi Yesu adzaweruza molungama? (Gen. 18:25, 26; Mat. 25:31-33)
Ŵerengani Genesis 19:1-29.
Kodi nkhani ya m’Baibulo imeneyi imasonyeza bwanji mmene Mulungu amaonera kugonana kwa amuna okhaokha kapena akazi okhaokha? (Gen. 19:5, 13; Lev. 20:13)
Kodi pali kusiyana kotani pa zimene Abrahamu ndi Loti anachita atamva malangizo a Mulungu, ndipo kodi tingaphunzire chiyani pamenepa? (Gen. 19:15, 16, 19, 20; 22:3)
Ŵerengani Luka 17:28-32.
Kodi mkazi wa Loti anali ndi mtima wotani pa nkhani ya chuma, ndipo kodi zimenezi zikutichenjeza bwanji ifeyo? (Luka 12:15; 17:31, 32; Mat. 6:19-21, 25)
Ŵerengani 2 Petro 2:6-8.
Potsanzira Loti, kodi tiyenera kuliona bwanji dziko losaopa Mulungu limene latizungulirali? (Ezek. 9:4; 1 Yoh. 2:15-17)
Nkhani 16
Isake Apeza Mkazi Wabwino
Kodi mwamuna ndi mkazi amene ali m’chithunzichi ndi ndani?
Kodi Abrahamu anachita chiyani kuti apezere mwana wake mkazi, ndipo n’chifukwa chiyani anachita zimenezi?
Kodi pemphero la mtumiki wa Abrahamu linayankhidwa motani?
Kodi Rebeka anayankha chiyani atamufunsa ngati akufuna kukwatiwa ndi Isake?
Kodi n’chiyani chinachititsa Isake kuyambiranso kukondwa?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Genesis 24:1-67.
Kodi Rebeka anasonyeza makhalidwe abwino otani pamene anakumana ndi mtumiki wa Abrahamu pachitsime? (Gen. 24:17-20; Miy. 31:17, 31)
Kodi zimene Abrahamu anakonzera Isake zikupereka chitsanzo chabwino chotani kwa Akristu masiku ano? (Gen. 24:37, 38; 1 Akor. 7:39; 2 Akor. 6:14)
N’chifukwa chiyani tiyenera kupeza nthaŵi yosinkhasinkha, monga momwe Isake anachitira? (Gen. 24:63; Sal. 77:12; Afil. 4:8)
Nkhani 17
Amapasa Amene Anali Osiyana
Kodi Esau ndi Yakobo anali ndani, ndipo kodi anali osiyana motani?
Kodi Esau ndi Yakobo anali ndi zaka zingati pamene agogo awo Abrahamu anamwalira?
Kodi Esau anachita chiyani chimene chinamvetsa chisoni kwambiri amayi ake ndi atate ake?
N’chifukwa chiyani Esau anakwiyira kwambiri mbale wake, Yakobo?
Kodi Isake anapereka malangizo otani kwa mwana wake Yakobo?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Genesis 25:5-11, 20-34.
Kodi Yehova ananeneratu chiyani chokhudza ana aŵiri aamuna a Rebeka? (Gen. 25:23)
Kodi panali kusiyana kotani pa mmene Yakobo ndi Esau ankaonera ukulu? (Gen. 25:31-34)
Ŵerengani Genesis 26:34, 35; 27:1-46; ndi 28:1-5.
Kodi kusayamikira zinthu zauzimu kwa Esau kunaonekera motani? (Gen. 26:34, 35; 27:46)
Kuti Yakobo alandire madalitso a Mulungu, kodi Isake anamuuza kuti achite chiyani? (Gen. 28:1-4)
Ŵerengani Ahebri 12:16, 17.
Kodi chitsanzo cha Esau chikusonyeza chiyani za zimene zimachitikira anthu amene saona zinthu zauzimu kukhala zofunika?
Nkhani 18
Yakobo Amka ku Harana
Kodi mkazi wachitsikana amene ali m’chithunzichi ndi ndani, ndipo kodi Yakobo anamuchitira chiyani?
Kodi Yakobo anali wokonzeka kuchita chiyani kuti akwatire Rakele?
Kodi Labani anachita chiyani nthaŵi yoti Yakobo akwatire Rakele itakwana?
Kodi Yakobo anavomera kuchita chiyani kuti akwatire Rakele?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Genesis 29:1-30.
Ngakhale pamene Labani anamuchitira zachinyengo, kodi Yakobo anasonyeza bwanji kuti anali munthu wodzisungira ulemu, ndipo kodi tingaphunzire chiyani pa zimenezi? (Gen. 25:27; 29:26-28; Mat. 5:37)
Kodi chitsanzo cha Yakobo chimasonyeza bwanji kusiyana kwa chikondi chenicheni ndi chikondi chonyenga? (Gen. 29:18, 20, 30; Nyimbo 8:6)
Kodi ndi akazi anayi ati amene anadzakhala mbali ya banja la Yakobo kenaka n’kumuberekera ana aamuna? (Gen. 29:23, 24, 28, 29)
Nkhani 19
Yakobo Ali ndi Banja Lalikulu
Kodi ana aamuna sikisi amene mkazi woyamba wa Yakobo, Leya, anamuberekera mayina awo anali ndani?
Kodi Zilipa, mdzakazi wa Leya, anaberekera Yakobo ana aamuna aŵiri ati?
Kodi ana aamuna aŵiri amene mdzakazi wa Rakele, Biliha, anaberekera Yakobo mayina awo anali ndani?
Kodi Rakele anabereka ana aamuna aŵiri ati, ndipo n’chiyani chinachitika pamene anali kubereka mwana wamwamuna wachiŵiriyo?
Malinga ndi chithunzichi, kodi Yakobo anakhala ndi ana aamuna angati, ndipo n’chiyani chinachokera mwa iwo?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Genesis 29:32-35; 30:1-26; ndi 35:16-19.
Malinga ndi mmene zinachitikira ndi ana aamuna a Yakobo khumi ndi aŵiri, kodi anyamata achihebri kale ankawatcha maina motani?
Ŵerengani Genesis 37:35.
Ngakhale kuti ndi Dina yekha amene watchulidwa m’Baibulo, kodi tikudziŵa bwanji kuti Yakobo anali ndi ana ena aakazi? (Gen. 37:34, 35)
Nkhani 20
Dina Alowa M’bvuto
N’chifukwa chiyani Abrahamu ndi Isake sanafune kuti ana awo akwatire anthu a m’dziko la Kanani?
Kodi Yakobo anasangalala kuti mwana wake wamkazi azicheza ndi atsikana achikanani?
Kodi mwamuna amene akuyang’ana Dina m’chithunzichi ndi ndani, ndipo kodi anachita chinthu choipa chotani?
Kodi azichimwene a Dina, Simeoni ndi Levi, anachita chiyani atamva zimene zinachitikazo?
Kodi Yakobo anagwirizana ndi zimene Simeoni ndi Levi anachita?
Kodi mavuto onse a m’banjali anayamba bwanji?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Genesis 34:1-31.
Kodi nthaŵi imene Dina anakacheza ndi atsikana a m’dziko la Kanani inali yokhayo basi? Fotokozani. (Gen. 34:1)
N’chifukwa chiyani tinganene kuti Dina mbali ina anachita kuziputa dala kuti agonedwe ndi mwamuna? (Agal. 6:7)
Kodi achinyamata masiku ano angasonyeze bwanji kuti aphunzirapo kanthu pa chitsanzo chochenjeza cha Dina? (Miy. 13:20; 1 Akor. 15:33; 1 Yoh. 5:19)
Nkhani 21
Abale a Yosefe Amuda
N’chifukwa chiyani abale ake a Yosefe ankamuchitira nsanje, ndipo kodi anachita chiyani?
Kodi abale ake a Yosefe akufuna kumuchita chiyani, koma kodi Rubeni akuti chiyani?
Kodi chikuchitika n’chiyani pamene Aismayeli amalonda abwera?
Kodi abale ake a Yosefe akuchita chiyani kuti atate awo aganize kuti Yosefe wafa?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Genesis 37:1-35.
Kodi n’chiyani chinachititsa abale ake a Yosefe kum’chitira zoipa? (Gen. 37:11, 18; Miy. 27:4; Yak. 3:14-16)
Kodi n’chiyani chimene Yakobo anachita chimene chili chachibadwa kuchita munthu akakhala pachisoni? (Gen. 37:35)
Nkhani 22
Yosefe Aikidwa M’ndende
Kodi Yosefe ali ndi zaka zingati pamene akupita naye ku Igupto ndipo n’chiyani chikuchitika pamene akufika kumeneko?
Kodi chachitika n’chiyani kuti Yosefe aikidwe m’ndende?
Kodi Yosefe akupatsidwa udindo wanji m’ndendemo?
Ali m’ndende, kodi Yosefe akuchitira chiyani woperekera zakumwa ndi wophika wa Farao?
Kodi chikuchitika n’chiyani woperekera zakumwayo atatuluka m’ndende?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Genesis 39:1-23.
Popeza kunalibe lamulo la Mulungu lolembedwa loletsa chigololo mu nthaŵi ya Yosefe, n’chiyani chinamuchititsa kuthaŵa mkazi wa Potifara? (Gen. 2:24; 20:3; 39:9)
Ŵerengani Genesis 40:1-23.
Fotokozani mwachidule maloto amene woperekera zakumwa analota ndi tanthauzo lake limene Yehova anapatsa Yosefe? (Gen. 40:9-13)
Kodi wophika analota chiyani, ndipo kodi zinatanthauza chiyani? (Gen. 40:16-19)
Kodi gulu la kapolo wokhulupirika ndi wanzeru masiku ano latsatira bwanji mtima wa Yosefe? (Gen. 40:8; Sal. 36:9; Yoh. 17:17; Mac. 17:2, 3)
Kodi lemba la Genesis 40:20 limatithandiza bwanji kudziŵa mmene Akristu ayenera kuonera mapwando okondwerera tsiku lobadwa? (Mlal. 7:1; Marko 6:21-28)
Nkhani 23
Maloto a Farao
Kodi n’chiyani chinachitikira Farao usiku wina?
N’chifukwa chiyani woperekera zakumwa uja tsopano anakumbukira Yosefe?
Monga momwe asonyezera m’chithunzichi, kodi Farao analota maloto aŵiri otani?
Kodi Yosefe ananena kuti malotowo anatanthauzanji?
Kodi zinachitika bwanji kuti Yosefe akhale munthu wofunika kwambiri ndiponso wachiŵiri kwa Farao mu Igupto?
N’chifukwa chiyani abale a Yosefe anabwera ku Igupto, ndipo n’chifukwa chiyani sanathe kumuzindikira?
Kodi Yosefe anakumbukira maloto ati, ndipo anamuthandiza kumvetsetsa chiyani?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Genesis 41:1-57.
Kodi Yosefe anapereka bwanji ulemu kwa Yehova, ndipo Akristu masiku ano angatsatire chitsanzo chake motani? (Gen. 41:16, 25, 28; Mat. 5:16; 1 Pet. 2:12)
Kodi zaka za chakudya chochuluka ku Igupto zotsatiridwa ndi zaka za njala zimasonyeza bwino motani kusiyana kumene kulipo pakati pa moyo wauzimu wa anthu a Yehova masiku ano ndi wa anthu a m’Matchalitchi Achikristu? (Gen. 41:29, 30; Amosi 8:11, 12)
Ŵerengani Genesis 42:1-8 ndi 50:20.
Kodi n’kulakwa kuti munthu wolambira Yehova aweramire munthu polemekeza udindo wake ngati umenewo uli mwambo wa kumene akukhala? (Gen. 42:6)
Nkhani 24
Yosefe Ayesa Abale Ake
N’chifukwa chiyani Yosefe akunena kuti abale ake ndi azondi?
N’chifukwa chiyani Yakobo akulola kuti mwana wake wamwamuna wamng’ono kwambiri, Benjamini, apite ku Igupto?
Kodi chikho cha siliva cha Yosefe chikupezeka bwanji m’thumba la Benjamini?
Kodi Yuda akudzipereka kuchita chiyani kuti Benjamini amasulidwe?
Kodi abale ake a Yosefe asintha motani?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Genesis 42:9-38.
Kodi zimene Yosefe ananena pa Genesis 42:18 ndi chikumbutso chabwino motani kwa anthu amene ali ndi udindo m’gulu la Yehova masiku ano? (Neh. 5:15; 2 Akor. 7:1, 2)
Ŵerengani Genesis 43:1-34.
Ngakhale kuti Rubeni anali woyamba kubadwa, kodi pali umboni wotani wakuti Yuda anakhala wolankhulira abale ake? (Gen. 43:3, 8, 9; 44:14, 18; 1 Mbiri 5:2)
Kodi zikuoneka kuti Yosefe anayesa abale ake motani, ndipo anawayesa chifukwa chiyani? (Gen. 43:33, 34)
Ŵerengani Genesis 44:1-34.
Kodi Yosefe anadzionetsa ngati munthu wotani monga njira imodzi yopusitsira abale ake kuti asamuzindikire? (Gen. 44:5, 15; Lev. 19:26)
Kodi abale ake a Yosefe anasonyeza bwanji kuti mtima wansanje umene anali nawo kale pa mbale wawo unatha tsopano? (Gen. 44:13, 33, 34)
Nkhani 25
Banja Lisamukira ku Igupto
Kodi n’chiyani chikuchitika pamene Yosefe akudziulula kwa abale ake?
Kodi mokoma mtima Yosefe akufotokozera abale akewo chiyani?
Kodi Farao akunena chiyani atamva za abale a Yosefe?
Kodi m’banja mwa Yakobo muli anthu angati pamene akusamukira ku Igupto?
Kodi banja la Yakobo linadzatchedwa chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Genesis 45:1-28.
Kodi nkhani ya m’Baibulo ya Yosefe imasonyeza bwanji kuti Yehova angasinthe zinthu zimene ena amafuna kuti ziipire atumiki ake kukhala zinthu zowakomera? (Gen. 45:5-8; Yes. 8:10; Afil. 1:12-14)
Ŵerengani Genesis 46:1-27.
Kodi Yehova analimbikitsa bwanji Yakobo pamene anali kupita ku Igupto? (Gen. 46:1-4)
Nkhani 26
Yobu Akhulupirira Mulungu
Kodi Yobu anali ndani?
Kodi Satana anayesera kuchita chiyani, koma kodi anapambana?
N’chiyani chimene Yehova analoleza Satana kuchita, ndipo n’chifukwa chiyani anamuloleza kuchita zimenezo?
N’chifukwa chiyani mkazi wa Yobu anamuuza kuti ‘tukwana Mulungu ufe’? (Onani chithunzi.)
Monga mukuonera pa chithunzi chachiŵiricho, kodi Yehova anadalitsa bwanji Yobu, ndipo anamudalitsa chifukwa chiyani?
Ngati ifeyo, mofanana ndi Yobu, tikhala okhulupirika kwa Yehova, kodi tidzalandira madalitso otani?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Yobu 1:1-22.
Kodi Akristu masiku ano angatsanzire bwanji Yobu? (Yobu 1:1; Afil. 2:15; 2 Pet. 3:14)
Ŵerengani Yobu 2:1-13.
Kodi Yobu ndi mkazi wake anachita bwanji zinthu m’njira ziŵiri zosiyana pamene anali kuzunzidwa ndi Satana? (Yobu 2:9, 10; Miy. 19:3; Mika 7:7; Mal. 3:14)
Ŵerengani Yobu 42:10-17.
Kodi pali kufanana kotani pa mphoto imene Yobu analandira ndi imene Yesu analandira chifukwa chokhala okhulupirika? (Yobu 42:12; Afil. 2:9-11)
Kodi timalimbikitsidwa bwanji ndi madalitso amene Yobu analandira chifukwa chokhala wokhulupirika kwa Mulungu? (Yobu 42:10, 12; Aheb. 6:10; Yak. 1:2-4, 12; 5:11)
Nkhani 27
Mfumu Yoipa Ilamula Igupto
Pachithunzipa, kodi mwamuna amene ali ndi chikotiyo ndi ndani, ndipo kodi akumenya ndani?
Yosefe atamwalira, kodi chinachitika n’chiyani kwa Aisrayeli?
N’chifukwa chiyani Aigupto anayamba kuopa Aisrayeli?
Kodi Farao analamula akazi amene ankathandiza azimayi achiisrayeli pobereka kuti azichita chiyani?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Eksodo 1:6-22.
Kodi Yehova anayamba kukwaniritsa lonjezo lake kwa Abrahamu m’njira yotani? (Eks. 1:7; Gen. 12:2; Mac. 7:17)
Kodi akazi achihebri othandiza azimayi pobereka anasonyeza bwanji kuti analemekeza kupatulika kwa moyo? (Eks. 1:17; Gen. 9:6)
Kodi akazi othandiza azimayi poberekawo anadalitsidwa bwanji chifukwa cha kukhulupirika kwawo kwa Yehova? (Eks. 1:20, 21; Miy. 19:17)
Kodi Satana anayesera bwanji kulepheretsa cholinga cha Yehova chokhudza Mbewu yolonjezedwa ya Abrahamu? (Eks. 1:22; Mat. 2:16)
Nkhani 28
M’mene Mose Anapulumutsidwira
Kodi mwana wakhanda ali pachithunziyu ndi ndani, ndipo wagwira chala cha ndani?
Kodi mayi ake a Mose anachita chiyani kuti amupulumutse kuti asaphedwe?
Kodi mtsikana wamng’ono ali pachithunziyu ndi ndani, ndipo anachita chiyani?
Pamene mwana wamkazi wa Farao anapeza khandalo, kodi Miriamu anaperekapo maganizo otani?
Kodi mwana wamkazi wa mfumuyo ananena chiyani kwa mayi a Mose?
Funso lowonjezera:
Ŵerengani Eksodo 2:1-10.
Kodi mayi a Mose anali ndi mwayi wotani wophunzitsa Mose ali wakhanda, ndipo kodi zimenezi ndi chitsanzo chotani kwa makolo masiku ano? (Eks. 2:9, 10; Deut. 6:6-9; Miy. 22:6; Aef. 6:4; 2 Tim. 3:15)
Nkhani 29
Chifukwa Chake Mose Akuthawa
Kodi Mose anakulira kuti, koma kodi anadziŵa chiyani za makolo ake?
Kodi Mose ali ndi zaka 40 anachita chiyani?
Kodi Mose ananena chiyani kwa mwamuna wachiisrayeli amene ankamenya mnzake, ndipo kodi mwamunayo anayankha kuti chiyani?
N’chifukwa chiyani Mose anathawa ku Igupto?
Kodi Mose anathaŵira kuti, ndipo kodi kumeneko anakumana ndi ndani?
Kodi Mose anachita chiyani kwa zaka 40 atathaŵa ku Igupto?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Eksodo 2:11-25.
Ngakhale kuti anaphunzitsidwa nzeru za ku Igupto kwa zaka zambiri, kodi Mose anasonyeza bwanji kuti anali wokhulupirika kwa Yehova ndi anthu ake? (Eks. 2:11, 12; Aheb. 11:24)
Ŵerengani Machitidwe 7:22-29.
Kodi tingaphunzire chiyani pa nkhani ya Mose pamene anayesera payekha kupulumutsa Aisrayeli ku ukapolo ku Igupto? (Mac. 7:23-25; 1 Pet. 5:6, 10)
Nkhani 30
Chitsamba Choyaka Moto
Kodi phiri limene lili pa chithunzipa dzina lake n’chiyani?
Kodi mawu ochokera pa chitsamba choyaka moto anati chiyani, ndipo anali mawu a ndani?
Kodi Mose anayankha bwanji Mulungu atamuuza kuti adzatsogolera anthu a Mulungu kuchoka ku Igupto?
Kodi Mulungu anauza Mose kuti akanene chiyani anthu akakamufunsa amene anamutuma?
Kodi Mose akanatha bwanji kupereka umboni woti Mulungu anamutuma?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Eksodo 3:1-22.
Kodi zimene zinachitikira Mose zimatilimbikitsa bwanji kuti, ngakhale ngati tikuona kuti sitingakwanitse utumiki winawake, Yehova adzatithandiza? (Eks. 3:11, 13; 2 Akor. 3:5, 6)
Ŵerengani Eksodo 4:1-20.
Kodi Mose anasintha bwanji mtima wake pa zaka 40 zimene anakhala ku Midyani, ndipo kodi ndi phunziro lotani limene anthu amene akukalamira maudindo mu mpingo angaphunzirepo pamenepa? (Eks. 2:11, 12; 4:10, 13; Mika 6:8; 1 Tim. 3:1, 6, 10)
Ngakhale tilangidwe ndi Yehova kudzera m’gulu lake, kodi chitsanzo cha Mose chingatilimbikitse bwanji? (Eks. 4:12-14; Sal. 103:14; Aheb. 12:4-11)
Nkhani 31
Mose ndi Aroni Aona Farao
Kodi zozizwitsa zimene Mose ndi Aroni anachita zinawakhudza motani Aisrayeli?
Kodi Mose ndi Aroni anauza Farao chiyani, ndipo kodi Farao anayankha kuti chiyani?
Monga momwe asonyezera pachithunzipa, kodi Aroni ataponya ndodo yake pansi chinachitika n’chiyani?
Kodi Yehova anaphunzitsa bwanji Farao phunziro, ndipo kodi Farao anachitapo chiyani?
Kodi chinachitika n’chiyani mliri wachikhumi utatha?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Eksodo 4:27-31 ndi 5:1-23.
Kodi Farao anatanthauza chiyani pamene ananena kuti: “Sindim’dziŵa Yehova.” (Eks. 5:2; 1 Sam. 2:12; Aroma 1:21)
Ŵerengani Eksodo 6:1-13, 26-30.
Kodi zikutipangitsa ifeyo kumva bwanji podziŵa kuti Yehova anamugwiritsirabe ntchito Mose, ngakhale kuti Moseyo ankadziona kuti sanali woyenera kugwira ntchito imene anapatsidwa? (Eks. 6:12, 30; Luka 21:13-15)
Ŵerengani Eksodo 7:1-13.
Pamene Mose ndi Aroni molimba mtima anauza Farao ziweruzo za Yehova, kodi anasiyira atumiki a Mulungu masiku ano chitsanzo chotani? (Eks. 7:2, 3, 6; Mac. 4:29-31)
Kodi Yehova anasonyeza bwanji kuti anali wopambana kuposa milungu ya ku Igupto? (Eks. 7:12; 1 Mbiri 29:12)
Nkhani 32
Miriri 10
Pogwiritsa ntchito zithunzi zimene zasonyezedwa pano, fotokozani miliri itatu yoyambirira imene Yehova anabweretsa pa Igupto.
Kodi miliri itatu yoyambirira inali yosiyana bwanji ndi miliri ina yonse yotsatira?
Kodi mliri wachinayi, wachisanu, ndi wachisanu ndi chimodzi inali yotani?
Fotokozani mliri wachisanu ndi chiŵiri, wachisanu ndi chitatu ndi wachisanu ndi chinayi.
Kodi Yehova anauza Aisrayeli kuchita chiyani mliri wachikhumi usanachitike?
Kodi mliri wachikhumi unali wotani, ndipo n’chiyani chinachitika mliriwo utatha?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Eksodo 7:19–8:23.
Ngakhale kuti ansembe amatsenga a ku Igupto anatha kuchita zinthu zofanana ndi miliri iŵiri yoyambirira ya Yehova, kodi iwo anakakamizika kuvomereza chiyani mliri wachitatu utatha? (Eks. 8:18, 19; Mat. 12:24-28)
Kodi mliri wachinayi unasonyeza bwanji mphamvu imene Yehova ali nayo yotha kuteteza anthu ake, ndipo kudziŵa zimenezi kumachititsa anthu a Mulungu kumva bwanji pamene akuyandikira “chisautso chachikulu” chimene chinanenedweratu? (Eks. 8:22, 23; Chiv. 7:13, 14; 2 Mbiri 16:9)
Ŵerengani Eksodo 8:24; 9:3, 6, 10, 11, 14, 16, 23-25; ndi 10:13-15, 21-23.
Kodi ndi magulu aŵiri ati amene zochita zawo zinavumbulidwa poyera ndi Miliri Khumi, ndipo kodi zimenezi zikukhudza bwanji mmene timaonera magulu ameneŵa masiku ano? (Eks. 8:10, 18, 19; 9:14)
Kodi lemba la Eksodo 9:16 limatithandiza bwanji kumvetsa chifukwa chake Yehova walola kuti Satana akhalepobe mpaka pano? (Aroma 9:21, 22)
Ŵerengani Eksodo 12:21-32.
Kodi Paskha anachititsa motani kuti anthu ambiri apulumuke, ndipo kodi Paskha ankaimira chiyani? (Eks. 12:21-23; Yoh. 1:29; Aroma 5:18, 19, 21; 1 Akor. 5:7)
Nkhani 33
Kuoloka Nyanja Yofiira
Kodi ndi amuna angati achiisrayeli, limodzi ndi akazi ndi ana amene anatuluka mu Igupto, ndipo kodi ndani anatsagana nawo?
Kodi Farao anamva bwanji atalola Aisrayeli kupita, ndipo anachita chiyani?
Kodi Yehova anachita chiyani polepheretsa Aigupto kuti asaukire anthu ake?
Kodi chinachitika n’chiyani Mose atatambasulira ndodo yake pa Nyanja Yofiira, ndipo Aisrayeli anachita chiyani?
Kodi chinachitika n’chiyani pamene Aigupto anathamangira m’nyanjamo pothamangitsa Aisrayeli?
Kodi Aisrayeli anasonyeza bwanji kuti anali okondwa ndiponso oyamikira kwa Yehova chifukwa chowapulumutsa?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Eksodo 12:33-36.
Kodi Yehova anachita chiyani poonetsetsa kuti anthu ake alipidwe chifukwa cha zaka zambiri zimene anakhala akapolo a Aigupto? (Eks. 3:21, 22; 12:35, 36)
Ŵerengani Eksodo 14:1-31.
Kodi mawu a Mose olembedwa pa Eksodo 14:13, 14 amakhudza bwanji atumiki a Yehova masiku ano pamene akuyembekezera nkhondo ya Armagedo imene ikubwera kutsogoloku? (2 Mbiri 20:17; Sal. 91:8)
Ŵerengani Eksodo 15:1-8, 20, 21.
N’chifukwa chiyani atumiki a Yehova ayenera kumuimbira nyimbo zomutamanda? (Eks. 15:1, 2; Sal. 105:2, 3; Chiv. 15:3, 4)
Kodi ndi chitsanzo chotani chotamanda Yehova chimene Miriamu ndi akazi ena pa Nyanja Yofiira anasiyira akazi achikristu masiku ano? (Eks. 15:20, 21; Sal. 68:11)
Nkhani 34
Mtundu Watsopano wa Chakudya
M’chithunzichi, kodi anthuwo akutola chiyani pansipo, ndipo kodi dzina lake n’chiyani?
Kodi Mose akupatsa anthuwo malangizo otani otolera mana?
Kodi Yehova akuuza anthuwo kuchita chiyani pa tsiku lachisanu ndi chimodzi, ndipo n’chifukwa chiyani akuwauza zimenezo?
Kodi Yehova akuchita chozizwitsa chotani pamene manayo akusungidwa kufika tsiku lachisanu ndi chiŵiri?
Kodi Yehova akudyetsa anthuwo mana kwa nthaŵi yaitali bwanji
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Eksodo 16:1-36 ndi Numeri 11:7-9.
Kodi lemba la Eksodo 16:8 limasonyeza bwanji kufunika kolemekeza anthu oikidwa ndi Mulungu mu mpingo wachikristu? (Aheb. 13:17)
M’chipululu, kodi Aisrayeli anakumbutsidwa bwanji tsiku lililonse kuti moyo wawo unadalira pa Yehova? (Eks. 16:14-16, 35; Deut. 8:2, 3)
Kodi Yesu anapereka tanthauzo lophiphiritsira lotani la mana, ndipo kodi timapindula bwanji ndi “mkate wochokera m’mwamba” umenewu? (Yoh. 6:31-35, 40)
Ŵerengani Yoswa 5:10-12.
Kodi Aisrayeli anadya mana zaka zingati? Kodi zimenezi zinawayesa bwanji, ndipo kodi tingaphunzire chiyani pa nkhani imeneyi? (Eks. 16:35; Num. 11:4-6; 1 Akor. 10:10, 11)
Nkhani 35
Yehova Apereka Malamulo Ake
Pafupifupi miyezi iŵiri chichokereni ku Igupto, kodi Aisrayeli akumanga kuti mahema awo?
Kodi Yehova akunena kuti akufuna kuti anthuwo achite chiyani, ndipo anthuwo akuyankha chiyani?
N’chifukwa chiyani Yehova akupatsa Mose miyala iŵiri yaphanthiphanthi?
Kupatulapo Malamulo Khumi, kodi ndi malamulo ena ati amene Yehova anapatsa Aisrayeli?
Kodi ndi malamulo aŵiri ati amene Yesu Kristu ananena kuti ndi aakulu kupambana ena onse?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Eksodo 19:1-25; 20:1-21; 24:12-18; ndi 31:18.
Kodi mawu amene analembedwa pa Eksodo 19:8 amatithandiza bwanji kudziŵa zimene zimafunika pa kudzipatulira kwachikristu? (Mat. 16:24; 1 Pet. 4:1-3)
Ŵerengani Deuteronomo 6:4-6; Levitiko 19:18; ndi Mateyu 22:36-40.
Kodi Akristu amasonyeza bwanji kuti amakonda Mulungu ndi anansi awo? (Marko 6:34; Mac. 4:20; Aroma 15:2)
Nkhani 36
Mwana wa Ng’ombe wa Golidi
M’chithunzichi, kodi anthuwo akuchita chiyani, ndipo akuchita zimenezo chifukwa chiyani?
N’chifukwa chiyani Yehova wakwiya, ndipo kodi Mose akuchita chiyani ataona zimene anthuwo akuchita?
Kodi Mose akuuza ena mwa amunawo kuchita chiyani?
Kodi nkhani imeneyi iyenera kutiphunzitsa chiyani?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Eksodo 32:1-35.
Kodi nkhani imeneyi ikusonyeza bwanji mmene Yehova amaonera kuphatikiza chipembedzo chonyenga ndi kulambira koona? (Eks. 32:4-6, 10; 1 Akor. 10:7, 11)
Kodi Akristu ayenera kusamala motani akamasankha zosangalatsa, monga kuimba ndi kuvina? (Eks. 32:18, 19; Aef. 5:15, 16; 1 Yoh. 2:15-17)
Kodi fuko la Levi linapereka bwanji chitsanzo chabwino cha kutsatira chilungamo? (Eks. 32:25-28; Sal. 18:25)
Nkhani 37
Chihema Cholambirira
Kodi nyumba imene ili pachinthunzipa n’chiyani, ndipo kodi ntchito yake n’chiyani?
N’chifukwa chiyani Yehova anauza Mose kuti apange chihemacho m’njira yoti chingathe kumasulidwa mosavuta?
Kodi bokosi limene lili m’kachipinda kakumapeto kwa chihemacho n’chiyani, ndipo m’bokosilo muli chiyani?
Kodi Yehova akusankha ndani kuti akhale mkulu wa ansembe, ndipo kodi mkulu wa ansembe amachita chiyani?
Tchulani zinthu zitatu zimene zili m’chipinda chokulirapo cha chihemacho.
Kodi m’bwalo la chihema chokomanako muli zinthu ziŵiri ziti, ndipo kodi zimagwira ntchito yanji?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Eksodo 25:8-40; 26:1-37; 27:1-8; ndi 28:1.
Kodi akerubi amene anali pa “likasa la mboni” ankaimira chiyani? (Eks. 25:20, 22; Num. 7:89; 2 Maf. 19:15)
Ŵerengani Eksodo 30:1-10, 17-21; 34:1, 2; ndi Ahebri 9:1-5.
Kodi n’chifukwa chiyani Yehova anagogomezera kuti ansembe amene anali kutumikira m’chihema chokomanako afunika kukhala oyera, ndipo kodi zimenezi ziyenera kutikhudza bwanji ifeyo masiku ano? (Eks. 30:18-21; 40:30, 31; Aheb. 10:22)
Kodi mtumwi Paulo anasonyeza bwanji kuti chihema chokomanako ndi pangano la Chilamulo zinali zitasiya kugwira ntchito panthaŵi imene analemba kalata yake yopita kwa Akristu achihebri? (Aheb. 9:1, 9; 10:1)
Nkhani 38
Azondi 12
Kodi zipatso za nkhuyu zimene zili m’chithunzichi zikuoneka zotani, ndipo kodi zinachokera kuti?
N’chifukwa chiyani Mose akutuma azondi 12 ku dziko la Kanani?
Kodi azondi 10 akunena chiyani atabwerera kwa Mose?
Kodi azondi aŵiri akusonyeza bwanji kuti anadalira Yehova, ndipo kodi maina awo ndi ndani?
N’chifukwa chiyani Yehova wakwiya, ndipo kodi akuuza Mose chiyani?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Numeri 13:1-33.
Kodi ndani anasankhidwa kuti akazonde dzikolo, ndipo kodi anali ndi mwayi wapadera wotani? (Num. 13:2, 3, 18-20)
N’chifukwa chiyani Yoswa ndi Kalebi anali ndi maganizo osiyana ndi a azondi enawo, ndipo kodi zimenezi zikutiphunzitsa chiyani? (Num. 13:28-30; Mat. 17:20; 2 Akor. 5:7)
Ŵerengani Numeri 14:1-38.
Kodi tiyenera kumvera chenjezo lotani lokhudza kung’ung’udza motsutsana ndi anthu amene akuimira Yehova padziko lapansi pano? (Num. 14:2, 3, 27; Mat. 25:40, 45; 1 Akor. 10:10)
Kodi lemba la Numeri 14:24 limasonyeza bwanji kuti Yehova amachita chidwi ndi mtumiki wake aliyense payekha? (1 Maf. 19:18; Miy. 15:3)
Nkhani 39
Ndodo ya Aroni Ichita Maluwa
Kodi ndani akuukira ulamuliro wa Mose ndi Aroni, ndipo kodi akunena chiyani kwa Mose?
Kodi Mose akuuza Kora ndi omutsatira ake 250 kuchita chiyani?
Kodi Mose akunena chiyani kwa anthuwo, ndipo kodi chikuchitika n’chiyani atangotha kulankhula?
Kodi chikuchitika n’chiyani kwa Kora ndi otsatira ake 250?
Kodi Eliezara, mwana wa Aroni, akuchita chiyani ndi mbale zamoto za anthu akufawo, ndipo n’chifukwa chiyani akuchita zimenezi?
N’chifukwa chiyani Yehova akuchititsa ndodo ya Aroni kuchita maluwa? (Onani chithunzi.)
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Numeri 16:1-49.
Kodi Kora ndi otsatira ake anachita chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani kuchita zimenezo kunali kupandukira Yehova? (Num. 16:9, 10, 18; Lev. 10:1, 2; Miy. 11:2)
Kodi Kora ndi “akalonga a khamulo” okwana 250 anali ndi maganizo olakwika otani? (Num. 16:1-3; Miy. 15:33; Yes. 49:7)
Ŵerengani Numeri 17:1-11 ndi 26:10.
Kodi kuchita maluwa kwa ndodo ya Aroni kunasonyeza chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani Yehova ananena kuti isungidwe m’likasa? (Num. 17:5, 8, 10)
Kodi tingaphunzire phunziro lofunika kwambiri lotani kuchokera ku chizindikiro cha ndodo ya Aroni? (Num. 17:10; Mac. 20:28; Afil. 2:14; Aheb. 13:17)
Nkhani 40
Mose Amenya Thanthwe
Kodi Yehova akuwasamala bwanji Aisrayeli panthaŵi imene ali m’chipululu?
Kodi Aisrayeli akudandaula chiyani atamanga misasa pa Kadesi?
Kodi Yehova akuwapatsa bwanji madzi anthuwo ndi nyama zawo?
M’chithunzichi, kodi munthu amene akudzilozayo ndi ndani, ndipo n’chifukwa chiyani akuchita zimenezo?
N’chifukwa chiyani Yehova wakwiyira Mose ndi Aroni, ndipo akuwalanga bwanji?
N’chiyani chikuchitika pa phiri la Hori, ndipo ndani akukhala mkulu wansembe wa Israyeli?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Numeri 20:1-13, 22-29 ndi Deuteronomo 29:5.
Kodi tikuphunzirapo chiyani pa mmene Yehova anasamalira Aisrayeli m’chipululu? (Deut. 29:5; Mat. 6:31; Aheb. 13:5; Yak. 1:17)
Kodi Yehova anamva bwanji pamene Mose ndi Aroni analephera kumulemekeza pamaso pa Aisrayeli? (Num. 20:12; 1 Akor. 10:12; Chiv. 4:11)
Kodi tingaphunzire chiyani pa zimene Mose anachita atalangidwa ndi Yehova? (Num. 12:3; 20:12, 27, 28; Deut. 32:4; Aheb. 12:7-11)
Nkhani 41
Njoka Yamkuwa
M’chithunzichi, kodi n’chiyani chimene achikulungiza pamtengocho, ndipo n’chifukwa chiyani Yehova anauza Mose kuti achiike pamenepo?
Kodi anthuwo akusonyeza bwanji kuti sakuthokoza chifukwa cha zinthu zonse zimene Mulungu wawachitira?
Kodi anthuwo akupempha Mose kuchita chiyani Yehova atawatumizira njoka za ululu powalanga?
N’chifukwa chiyani Yehova akuuza Mose kuti apange njoka yamkuwa?
Kodi tingaphunzirepo chiyani pa nkhani imeneyi?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Numeri 21:4-9.
Kodi kudandaula kwa Aisrayeli ndi zimene Yehova anawapatsa kuli ndi phunziro lanji kwa ife? (Num. 21:5, 6; Aroma 2:4)
M’zaka zapatsogolo, kodi Aisrayeli anagwiritsa ntchito bwanji njoka yamkuwa ija, ndipo kodi Mfumu Hezekiya inachitapo chiyani? (Num. 21:9; 2 Maf. 18:1-4)
Ŵerengani Yohane 3:14, 15.
Kodi kupachika njoka yamkuwa pa mtengo wophiphiritsira kunaimira bwanji kupachikidwa kwa Yesu Kristu? (Agal. 3:13; 1 Pet. 2:24)
Nkhani 42
Bulu Alankhula
Kodi Balaki ndi ndani, ndipo n’chifukwa chiyani akuitanitsa Balamu?
N’chifukwa chiyani bulu wa Balamu akugona pa msewu?
Kodi Balamu akumva buluyo akunena kuti chiyani?
Kodi m’ngelo akunena chiyani kwa Balamu?
Kodi chikuchitika n’chiyani pamene Balamu akuyesera kutemberera Aisrayeli?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Numeri 21:21-35.
N’chifukwa chiyani Aisrayeli anagonjetsa Mfumu Sihoni ya Aamori ndi Mfumu Ogi ya ku Basana? (Num. 21:21, 23, 33, 34)
Ŵerengani Numeri 22:1-40.
Kodi cholinga cha Balamu poyesera kutemberera Aisrayeli chinali chotani, ndipo kodi tingaphunzirepo chiyani pa zimenezi? (Num. 22:16, 17; Miy. 6:16, 18; 2 Pet. 2:15; Yuda 11)
Ŵerengani Numeri 23:1-30.
Ngakhale kuti Balamu ankalankhula ngati kuti amalambira Yehova, kodi zochita zake zinasonyeza bwanji kuti sanali wolambira Yehova? (Num. 23:3, 11-14; 1 Sam. 15:22)
Ŵerengani Numeri 24:1-25.
Kodi nkhani ya m’Baibulo imeneyi imalimbitsa bwanji chikhulupiriro chathu choti zolinga za Yehova zidzakwaniritsidwa? (Num. 24:10; Yes. 54:17)
Nkhani 43
Yoswa Akhala M’tsogoleri
M’chithunzichi, kodi anthu aŵiri amene ali ndi Mosewo ndi ndani?
Kodi Yehova akuuza Yoswa chiyani?
N’chifukwa chiyani Mose akukwera pamwamba pa Phiri la Nebo, ndipo kodi Yehova akumuuza chiyani?
Kodi Mose akufa ali ndi zaka zingati?
N’chifukwa chiyani anthuwo ali ndi chisoni, koma kodi ali ndi chifukwa chotani chokhalira okondwa?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Numeri 27:12-23.
Kodi Yoswa anapatsidwa udindo waukulu wotani ndi Yehova, ndipo kodi masiku ano timaona bwanji kuti Yehova amasamala anthu Ake? (Num. 27:15-19; Mac. 20:28; Aheb. 13:7)
Ŵerengani Deuteronomo 3:23-29.
N’chifukwa chiyani Yehova sanalole kuti Mose ndi Aroni akafike nawo ku dziko lolonjezedwa, ndipo kodi tingaphunzirepo chiyani pa zimenezi? (Deut. 3:25-27; Num. 20:12, 13)
Ŵerengani Deuteronomo 31:1-8, 14-23.
Kodi mawu amene Mose anauza Aisrayeli potsanzikana nawo amasonyeza bwanji kuti analandira modzichepetsa chilango chochokera kwa Yehova? (Deut. 31:6-8, 23)
Ŵerengani Deuteronomo 32:45-52.
Kodi Mawu a Mulungu ayenera kukhudza motani miyoyo yathu? (Deut. 32:47; Lev. 18:5; Aheb. 4:12)
Ŵerengani Deuteronomo 34:1-12.
Ngakhale kuti Mose sanamuonedi Yehova maso ndi maso, kodi lemba la Deuteronomo 34:10 limasonyeza chiyani za ubwenzi wake ndi Yehova? (Eks. 33:11, 20; Num. 12:8)
Nkhani 44
Rahabi Abisa Azondi
Kodi Rahabi amakhala kuti?
Kodi amuna aŵiri amene ali m’chithunzichi ndi ndani, ndipo n’chifukwa chiyani ali ku Yeriko?
Kodi mfumu ya ku Yeriko ikulamula Rahabi kuchita chiyani, ndipo iye akuyankha chiyani?
Kodi Rahabi akuthandiza bwanji amuna aŵiriwo, ndipo akuwapempha chiyani?
Kodi azondi aŵiriwo akulonjeza Rahabi chiyani?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Yoswa 2:1-24.
Kodi lonjezo la Yehova lolembedwa pa Eksodo 23:28 linakwaniritsidwa bwanji pamene Aisrayeli anakaukira Yeriko? (Yos. 2:9-11)
Ŵerengani Ahebri 11:31.
Kodi chitsanzo cha Rahabi chimasonyeza bwanji kufunika kokhala ndi chikhulupiriro? (Aroma 1:17; Aheb. 10:39; Yak. 2:25)
Nkhani 45
Kuoloka Mtsinje wa Yordano
Kodi Yehova akuchita chozizwitsa chotani kuti Aisrayeli awoloke mtsinje wa Yordano?
Kodi Aisrayeli ayenera kuchita chiyani chofunika chikhulupiriro kuti athe kuwoloka mtsinje wa Yordano?
N’chifukwa chiyani Yehova akuuza Yoswa kusonkhanitsa miyala 12 ikuluikulu kuchokera m’mphepete mwa mtsinjewo?
Kodi chikuchitika n’chiyani ansembe atangotuluka mu Yordano?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Yoswa 3:1-17.
Monga momwe nkhani imeneyi ikusonyezera, kodi tiyenera kuchita chiyani kuti Yehova atithandize ndi kutidalitsa? (Yos. 3:13, 15; Miy. 3:5; Yak. 2:22, 26)
Kodi mtsinje wa Yordano unkaoneka bwanji pamene Aisrayeli anawoloka kupita ku Dziko Lolonjezedwa, ndipo zimenezi zinalemekeza bwanji dzina la Yehova? (Yos. 3:15; 4:18; Sal. 66:5-7)
Ŵerengani Yoswa 4:1-18.
Kodi miyala 12 imene anaitenga mu mtsinje wa Yordano n’kuiika ku Giligala inali ndi ntchito yanji? (Yos. 4:4-7)
Nkhani 46
Malinga a Yeriko
Kodi Yehova akuuza ankhondo ndi ansembe kuti achite chiyani kwa masiku asanu ndi limodzi?
Kodi amunawo ayenera kuchita chiyani pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri?
Monga mukuonera pachinthunzipa, kodi n’chiyani chikuchitikira malinga a Yeriko?
N’chifukwa chiyani chingwe chofiira chikulendewera pa zeneraro?
Kodi Yoswa akuuza amuna ankhondowo kuchita chiyani kwa anthuwo ndi mzindawo, koma kodi ayenera kuchita chiyani ndi siliva, golidi, mkuwa, ndi chitsulo?
Kodi azondi aŵiriwo akuuzidwa kuchita chiyani?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Yoswa 6:1-25.
Kodi kuguba kwa Aisrayeli kuzungulira Yeriko patsiku lachisanu ndi chiŵiri n’kofanana bwanji ndi ntchito yolalikira ya Mboni za Yehova m’masiku otsiriza ano? (Yos. 6:15, 16; Yes. 60:22; Mat. 24:14; 1 Akor. 9:16)
Kodi ulosi umene unalembedwa pa Yoswa 6:26 unakwaniritsidwa bwanji patatha zaka 500, ndipo kodi zimenezi zikutiphunzitsa chiyani za mawu a Yehova? (1 Maf. 16:34; Yes. 55:11)
Nkhani 47
Mbala mu Israyeli
M’chithunzichi, kodi munthu amene akukwirira katundu wotengedwa ku Yerikoyu ndi ndani, ndipo amene akumuthandizawo ndi ndani?
Kodi n’chifukwa chiyani zimene wachita Akani ndi anthu a m’banja lake zili zoipa kwambiri?
Kodi Yehova akunena chiyani Yoswa atamufunsa chifukwa chake Aisrayeli agonja pankhondo ku mzinda wa Ai?
Kodi n’chiyani chikuchitikira Akani ndi anthu a m’banja lake atawabweretsa kwa Yoswa?
Kodi kuweruzidwa kwa Akani kukutiphunzitsa phunziro lofunika kwambiri lotani?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Yoswa 7:1-26.
Kodi mapemphero a Yoswa anasonyeza chiyani za ubwenzi wake ndi Mlengi wake? (Yos. 7:7-9; Sal. 119:145; 1 Yoh. 5:14)
Kodi chitsanzo cha Akani chimasonyeza chiyani, ndipo limenelo ndi chenjezo kwa ife motani? (Yos. 7:11, 14, 15; Miy. 15:3; 1 Tim. 5:24; Aheb. 4:13)
Ŵerengani Yoswa 8:1-29.
Kodi aliyense wa ife ali ndi udindo wotani ku mpingo wachikristu masiku ano? (Yos. 7:13; Lev. 5:1; Miy. 28:13)
Nkhani 48
Agibeoni Anzeru
Kodi anthu a mu mzinda wa Gibeoni ndi osiyana motani ndi Akanani a m’mizinda yoyandikana nawo?
Monga momwe asonyezera pachithunzipa, kodi Agibeoni anachita chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani anachita zimenezo?
Kodi Yoswa ndi atsogoleri a Aisrayeli akuwalonjeza chiyani Agibeoniwo, koma n’chiyani chimene akuzindikira patatha masiku atatu?
Kodi chikuchitika n’chiyani mafumu a mizinda ina atamva zoti Agibeoni apangana mtendere ndi Israyeli?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Yoswa 9:1-27.
Popeza Yehova anali atalamula mtundu wa Israyeli “kupasula nzika zonse za m’dziko” kodi ndi makhalidwe ake ati amene anaoneka pamene sanawononge Agibeoni? (Yos. 9:22, 24; Mat. 9:13; Mac. 10:34, 35; 2 Pet. 3:9)
Mwa kusunga pangano limene anapangana ndi Agibeoni, kodi Yoswa anapereka motani chitsanzo chabwino kwa Akristu masiku ano? (Yos. 9:18, 19; Mat. 5:37; Aef. 4:25)
Ŵerengani Yoswa 10:1-5.
Kodi a khamu lalikulu masiku ano amatsanzira bwanji Agibeoni, ndipo amasanduka mdani wa ndani? (Yos. 10:4; Zek. 8:23; Mat. 25:35-40; Chiv. 12:17)
Nkhani 49
Dzuwa Liima
M’chithunzichi, kodi Yoswa akunena kuti chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani akutero?
Kodi Yehova akuthandiza bwanji Yoswa ndi amuna ake ankhondo?
Kodi Yoswa akugonjetsa mafumu angati, ndipo zikumutengera nthaŵi yaitali bwanji?
N’chifukwa chiyani Yoswa akugaŵa dziko la Kanani?
Kodi Yoswa akufa ali ndi zaka zingati, ndipo n’chiyani chikuchitikira anthuwo pambuyo pake?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Yoswa 10:6-15.
Kudziŵa kuti Yehova anachititsa dzuwa ndi mwezi kuima chifukwa cha Aisrayeli kumatipatsa chikhulupiriro chotani masiku ano? (Yos. 10:8, 10, 12, 13; Sal. 18:3; Miy. 18:10)
Ŵerengani Yoswa 12:7-24.
Kodi ndi ndani kwenikweni amene anagonjetsa mafumu 31 ku Kanani, ndipo n’chifukwa chiyani zimenezi zili zofunika kwa ife masiku ano? (Yos. 12:7; 24:11-13; Deut. 31:8; Luka 21:9, 25-28)
Ŵerengani Yoswa 14:1-5.
Kodi dziko linagaŵidwa bwanji pakati pa mafuko a Israyeli, ndipo zimenezi zikusonyeza chiyani za m’mene anthu adzalandirire malo m’Paradaiso? (Yos. 14:2; Yes. 65:21; Ezek. 47:21-23; 1 Akor. 14:33)
Ŵerengani Oweruza 2:8-13.
Mofanana ndi Yoswa mu Israyeli, ndi ndani masiku ano amene amakhala ngati woletsa mpatuko? (Ower. 2:8, 10, 11; Mat. 24:45-47; 2 Ates. 2:3-6; Tito 1:7-9; Chiv. 1:1; 2:1, 2)
Nkhani 50
Akazi Awiri Olimba Mtima
Kodi oweruza ndi ndani, ndipo mayina a ena a iwo ndi ati?
Kodi Debora ali ndi maudindo apadera otani, ndipo zimenezi zikuphatikizapo chiyani?
Pamene Israyeli akuopsezedwa ndi Mfumu Yabini ndi mkulu wa gulu lake lankhondo, Sisera, kodi ndi uthenga wotani wochokera kwa Yehova umene Debora akuuza Woweruza Baraki, ndipo akuti ndi ndani amene adzatamandidwa?
Kodi Yaeli akusonyeza bwanji kuti iye ndi mkazi wolimba mtima?
Kodi chikuchitika n’chiyani Mfumu Yabini itamwalira?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Oweruza 2:14-22.
Kodi Aisrayeli anadzibweretsera bwanji mkwiyo wa Yehova, ndipo kodi tingaphunzirepo chiyani pamenepa? (Ower. 2:20; Miy. 3:1, 2; Ezek. 18:21-23)
Ŵerengani Oweruza 4:1-24.
Kodi ndi maphunziro otani okhudza chikhulupiriro ndi kulimba mtima amene akazi achikristu angaphunzire kwa Debora ndi Yaeli masiku ano? (Ower. 4:4, 8, 9, 14, 21, 22; Miy. 31:30; 1 Akor. 16:13)
Ŵerengani Oweruza 5:1-31.
Kodi nyimbo yosangalalira kupambana ya Baraki ndi Debora tingaigwiritse ntchito bwanji ngati pemphero lokhudza nkhondo imene ikubwera ya Harmagedo? (Ower. 5:3, 31; 1 Mbiri 16:8-10; Chiv. 7:9, 10; 16:16; 19:19-21)
Nkhani 51
Rute ndi Naomi
Kodi Naomi anapezeka bwanji ku dziko la Moabu?
Kodi Rute ndi Oripa ndi ndani?
Kodi Rute ndi Oripa aliyense akuyankha bwanji Naomi atawauza kuti abwerere kwawo?
Kodi Boazi ndi ndani, ndipo kodi akuthandiza bwanji Rute ndi Naomi?
Kodi mwana wa Boazi ndi Rute dzina lake ndi ndani, ndipo n’chifukwa chiyani tiyenera kumukumbukira?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Rute 1:1-17.
Kodi ndi mawu abwino kwambiri otani osonyeza chikondi chokhulupirika amene Rute akunena? (Rute 1:16, 17)
Kodi maganizo a Rute amasonyeza bwino motani mtima umene a “nkhosa zina” ali nawo pa odzozedwa amene ali padziko lapansi masiku ano? (Yoh. 10:16; Zek. 8:23)
Ŵerengani Rute 2:1-23.
Kodi Rute akupereka chitsanzo chabwino kwambiri chotani kwa atsikana masiku ano? (Rute 2:17, 18; Miy. 23:22; 31:15)
Ŵerengani Rute 3:5-13.
Kodi Boazi anakuona bwanji kufunitsitsa kwa Rute kukwatiwa naye m’malo mofuna kukwatiwa ndi mwamuna wina wachinyamata?
Kodi mtima umene Rute anali nawo ukutiphunzitsa chiyani za chikondi chokhulupirika? (Rute 3:10; 1 Akor. 13:4, 5)
Ŵerengani Rute 4:7-17.
Kodi amuna achikristu masiku ano angakhale bwanji ngati Boazi? (Rute 4:9, 10; 1 Tim. 3:1, 12, 13; 5:8)
Nkhani 52
Gideoni ndi Amuna Ake 300
N’chifukwa chiyani Aisrayeli ali m’vuto lalikulu, ndipo ali m’vuto lotani?
N’chifukwa chiyani Yehova akuuza Gideoni kuti ali ndi amuna ankhondo ochulukitsitsa?
Kodi ndi amuna angati amene akutsala Gideoni atauza amuna amantha kuti abwerere kwawo?
Kuchokera pa chithunzichi, fotokozani mmene Yehova akuchepetsera amuna ankhondo a Gideoni kufika pa amuna 300 okha basi.
Kodi Gideoni akukonzekeretsa bwanji amuna ake 300, ndipo kodi Aisrayeli akupambana bwanji nkhondoyo?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Oweruza 6:36-40.
Kodi Gideoni anachita chiyani kuti atsimikizire zimene Yehova anali kufuna?
Kodi ifeyo masiku ano timadziŵa bwanji zimene Yehova akufuna? (Miy. 2:3-6; Mat. 7:7-11; 2 Tim. 3:16, 17)
Ŵerengani Oweruza 7:1-25.
Kodi tingaphunzire phunziro lotani kwa amuna 300 amene anakhala tcheru mosiyana ndi amene anali osasamala? (Ower. 7:3, 6; Aroma 13:11, 12; Aef. 5:15-17)
Mofanana ndi mmene amuna 300 aja anaphunzirira mwa kutsanzira Gideoni, kodi ifeyo timaphunzira bwanji mwa kutsanzira Gideoni Wamkulu, Yesu Kristu? (Ower. 7:17; Mat. 11:29, 30; 28:19, 20; 1 Pet. 2:21)
Kodi lemba la Oweruza 7:21 limatithandiza bwanji kukhala okhutira kutumikira m’njira iliyonse m’gulu la Yehova? (1 Akor. 4:2; 12:14-18; Yak. 4:10)
Ŵerengani Oweruza 8:1-3.
Tikafuna kuthetsa kusiyana maganizo kumene kwabuka ndi mbale kapena mlongo, kodi tingaphunzire chiyani pa mmene Gideoni anathetsera mkangano umene unabuka ndi Aefraimu? (Miy. 15:1; Mat. 5:23, 24; Luka 9:48)
Nkhani 53
Lonjezo la Yefita
Kodi Yefita ndi ndani, ndipo anakhala ndi moyo pa nthaŵi iti?
Kodi Yefita akulonjeza Yehova chiyani?
N’chifukwa chiyani Yefita akumva chisoni atabwerera kunyumba pambuyo popambana nkhondo yomenyana ndi Aamoni?
Kodi mwana wa Yefita akunena chiyani atamva zimene bambo ake analonjeza?
N’chifukwa chiyani anthu akumukonda mwana wa Yefita?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Oweruza 10:6-18.
Kodi mbiri ya kusakhulupirika kwa Aisrayeli kwa Yehova iyenera kukhala chenjezo lotani kwa ife? (Ower. 10:6, 15, 16; Aroma 15:4; Chiv. 2:10)
Ŵerengani Oweruza 11:1-11, 29-40.
Kodi tikudziŵa bwanji kuti pamene Yefita anapereka mwana wake wamkazi kukhala “nsembe yopsereza” sizinatanthauze kuti anamupha n’kumupereka nsembe? (Ower. 11:30; Lev. 16:24; Deut. 18:10, 12)
Kodi Yefita anapereka mwana wake wamkazi monga nsembe m’njira yotani?
Kodi tingaphunzire chiyani pa nkhani ya mmene Yefita anaonera lonjezo lake kwa Yehova? (Ower. 11:35, 39; Mlal. 5:4, 5; Mat. 16:24)
Kodi mwana wamkazi wa Yefita ndi chitsanzo chabwino motani kwa Akristu achinyamata kuti aone utumiki wa nthaŵi zonse monga ntchito ya moyo wawo wonse? (Ower. 11:36; Mat. 6:33; Afil. 3:8)
Nkhani 54
Munthu Wamphamvu Kopambana
Kodi munthu wamphamvu kopambana onse dzina lake ndi ndani, ndipo ndani anamupatsa mphamvu zimenezo?
Panthaŵi ina, kodi Samsoni akuchita chiyani kwa mkango waukulu, monga momwe mukuonera pachithunzipa?
Kodi pachithunzipa Samsoni akuuza Delila chinsinsi chotani, ndipo zimenezi zinachititsa bwanji kuti Afilisti am’gwire?
Kodi Samsoni akuchititsa bwanji kuti adani ake achifilisti 3,000 afe patsiku limene iye anafa?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Oweruza 13:1-14.
Kodi Manowa ndi mkazi wake ndi chitsanzo chabwino chotani kwa makolo polera ana awo? (Ower. 13:8; Sal. 127:3; Aef. 6:4)
Ŵerengani Oweruza 14:5-9 ndi 15:9-16.
Kodi nkhani za mmene Samsoni anaphera mkango, kudula zingwe zatsopano zimene anamumangira, ndi kugwiritsa ntchito chibwano cha bulu kupha amuna 1,000 zimasonyeza chiyani za mmene mzimu woyera wa Yehova umagwirira ntchito?
Kodi mzimu woyera umatithandiza bwanji masiku ano? (Ower. 14:6; 15:14; Zek. 4:6; Mac. 4:31)
Ŵerengani Oweruza 16:18-31.
Kodi Samsoni anakhudzidwa bwanji ndi mayanjano oipa, ndipo tingaphunzirepo chiyani pamenepa? (Ower. 16:18, 19; 1 Akor. 15:33)
Nkhani 55
Kamnyamata Katumikira Mulungu
Kodi kamnyamata kamene kali pachithunzipa dzina lake ndani, ndipo anthu enawo ndi ndani?
Kodi Hana anapemphera motani tsiku lina atapita ku chihema cha Yehova, ndipo kodi Yehova anamuyankha motani?
Kodi Samueli ali ndi zaka zingati pamene akutengedwa kukatumikira pa chihema cha Yehova, ndipo kodi mayi ake akumuchitira chiyani chaka chilichonse?
Kodi ana a Eli mayina awo ndi ndani, ndipo kodi ndi anthu otani?
Kodi Yehova akuitana Samueli motani, ndipo akumupatsa uthenga wotani?
Kodi Samueli akukhala ndani atakula, ndipo chikuchitika n’chiyani atakalamba?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani 1 Samueli 1:1-28.
Kodi ndi chitsanzo chabwino chotani chimene Elikana akupereka kwa mitu ya mabanja pankhani yotsogolera mabanja awo pa kulambira koona? (1 Sam. 1:3, 21; Mat. 6:33; Afil. 1:10)
Kodi tingaphunzire phunziro lotani kwa Hana pa zimene anachita atakumana ndi vuto lothetsa nzeru? (1 Sam. 1:10, 11; Sal. 55:22; Aroma 12:12)
Ŵerengani 1 Samueli 2:11-36.
Kodi Eli analemekeza ana ake kwambiri kuposa Yehova motani, ndipo kodi zimenezi zingakhale chenjezo lotani kwa ifeyo? (1 Sam. 2:22-24, 27, 29; Deut. 21:18-21; Mat. 10:36, 37)
Ŵerengani 1 Samueli 4:16-18.
Kodi ndi uthenga wa mbali zinayi wotani watsoka umene ukubwera kuchokera kunkhondo, ndipo kodi ukumukhudza motani Eli?
Ŵerengani 1 Samueli 8:4-9.
Kodi Aisrayeli analakwira kwambiri Yehova motani, ndipo kodi ifeyo tingachirikize mokhulupirika Ufumu wake motani masiku ano? (1 Sam. 8:5, 7; Yoh. 17:16; Yak. 4:4)
Nkhani 56
Sauli—Mfumu Yoyamba
Pachithunzipa, kodi Samueli akuchita chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani akuchita zimenezi?
N’chifukwa chiyani Yehova amakonda Sauli, ndipo kodi iye ndi munthu wotani?
Kodi mwana wa Sauli dzina lake ndani, ndipo kodi mwanayo akuchita chiyani?
N’chifukwa chiyani Sauli akupereka nsembe m’malo modikira Samueli kuti adzachite zimenezi?
Kodi tingaphunzire maphunziro otani pa nkhani ya Sauli?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani 1 Samueli 9:15-21 ndi 10:17-27.
Kodi khalidwe la Sauli lodzichepetsa linamuthandiza bwanji kupeŵa kuchita zinthu mosaganiza bwino anthu ena atalankhula za iye mopanda ulemu? (1 Sam. 9:21; 10:21, 22, 27; Miy. 17:27)
Ŵerengani 1 Samueli 13:5-14.
Kodi Sauli anachita tchimo lanji ku Giligala? (1 Sam. 10:8; 13:8, 9, 13)
Ŵerengani 1 Samueli 15:1-35.
Kodi ndi tchimo lalikulu lotani limene Sauli anachita lokhudza Agagi, mfumu ya Aamaleki? (1 Sam. 15:2, 3, 8, 9, 22)
Kodi Sauli anayesera bwanji kusonyeza kuti sanalakwe ndi kukankhira tchimo lakelo kwa ena? (1 Sam. 15:24)
Kodi masiku ano tikapatsidwa uphungu tiyenera kukumbukira chenjezo liti? (1 Sam. 15:19-21; Sal. 141:5; Miy. 9:8, 9; 11:2)
Nkhani 57
Mulungu Asankha Davide
Kodi mnyamata amene ali pachithunziyu dzina lake ndani, ndipo tikudziŵa bwanji kuti ndi wolimba mtima?
Kodi Davide amakhala kuti, ndipo atate ake ndi agogo ake mayina awo ndani?
N’chifukwa chiyani Yehova akuuza Samueli kupita kunyumba ya Jese ku Betelehemu?
Kodi chikuchitika n’chiyani Jese atabweretsa ana ake aamuna asanu ndi aŵiri kwa Samueli?
Atalowetsa Davide m’nyumbamo, kodi Yehova akuuza Samueli chiyani?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani 1 Samueli 17:34, 35.
Kodi zochitika zimenezi zikugogomezera bwanji kulimba mtima kwa Davide ndi kudalira kwake Yehova? (1 Sam. 17:37)
Ŵerengani 1 Samueli 16:1-14.
Kodi mawu a Yehova pa 1 Samueli 16:7 amatithandiza bwanji kukhala opanda tsankho ndiponso kusakondera anthu ena chifukwa cha maonekedwe awo? (Mac. 10:34, 35; 1 Tim. 2:4)
Kodi chitsanzo cha Sauli chimasonyeza bwanji kuti Yehova akamuchotsera munthu mzimu wake woyera, malo opanda kanthu otsalawo angadzazidwe ndi mzimu woipa, kapena chilakolako chofuna kuchita zoipa? (1 Sam. 16:14; Mat. 12:43-45; Agal. 5:16)
Nkhani 58
Davide ndi Goliati
Kodi Goliati akuputa gulu lankhondo la Aisrayeli kuti lichite chiyani?
Kodi Goliati ndi wamkulu bwanji, ndipo kodi Mfumu Sauli ikulonjeza kuti idzapereka mphoto yotani kwa munthu amene aphe Goliati?
Kodi Davide akuuza Sauli chiyani atamuuza kuti sangathe kumenyana ndi Goliati chifukwa chakuti Davideyo ndi mnyamata wamng’ono?
Kodi mmene Davide akuyankhira Goliati zikusonyeza bwanji kuti akudalira Yehova?
Monga momwe mukuonera pachithunzipa, kodi Davide anagwiritsira ntchito chiyani kupha Goliati, ndipo chikuchitika n’chiyani kwa Afilistiwo pambuyo pa zimenezi?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani 1 Samueli 17:1-54.
Kodi chinsinsi cha kupanda mantha kwa Davide chinali chiyani, ndipo kodi tingatsanzire bwanji kulimba mtima kwake? (1 Sam. 17:37, 45; Aef. 6:10, 11)
N’chifukwa chiyani Akristu ayenera kupeŵa mzimu wampikisano ngati wa Goliati pochita maseŵera kapena zosangalatsa zina? (1 Sam. 17:8; Agal. 5:26; 1 Tim. 4:8)
Kodi mawu a Davide amasonyeza bwanji kuti ankakhulupirira kuti Mulungu amuthandiza? (1 Sam. 17:45-47; 2 Mbiri 20:15)
M’malo mongofotokoza nkhondo ya pakati pa magulu ankhondo aŵiri otsutsana, kodi nkhani imeneyi imasonyeza bwanji kuti nkhondoyo kwenikweni inali pakati pa milungu yonyenga ndi Mulungu woona, Yehova? (1 Sam. 17:43, 46, 47)
Kodi otsalira a odzozedwa amatsanzira bwanji chitsanzo cha Davide chodalira Yehova? (1 Sam. 17:37; Yer. 1:17-19; Chiv. 12:17)
Nkhani 59
Chifukwa Chake Davide Akuthawa
N’chifukwa chiyani Sauli akuchitira nsanje Davide, koma kodi mwana wa Sauli, Jonatani, ndi wosiyana bwanji ndi Sauli?
Kodi chikuchitika n’chiyani tsiku lina pamene Davide akuyimbira Sauli zeze?
Kodi Sauli akunena kuti Davide ayenera kuchita chiyani asanam’patse mwana wake wamkazi Mikala kuti akhale mkazi wake, ndipo n’chifukwa chiyani Sauli akunena zimenezi?
Pamene Davide akuyimbira Sauli zeze, kodi n’chiyani chikuchitika kachitatu, monga momwe chithunzichi chikusonyezera?
Kodi Mikala akuthandiza bwanji kupulumutsa Davide, ndipo kwa zaka zisanu ndi ziŵiri Davide ayenera kuchita chiyani?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani 1 Samueli 18:1-30.
Kodi chikondi cholimba chimene Jonatani anali nacho pa Davide chinaimira bwanji chikondi chimene chilipo pakati pa a “nkhosa zina” ndi a “kagulu kankhosa”? (1 Sam. 18:1; Yoh. 10:16; Luka 12:32; Zek. 8:23)
Poganizira kuti Jonatani ndi amene anayenera kudzakhala wolowa m’malo mwa Sauli, kodi lemba la 1 Samueli 18:4 likusonyeza bwanji kuti Jonatani anagonjera kwambiri munthu amene anasankhidwa kukhala mfumu?
Ŵerengani 1 Samueli 19:1-17.
Kodi Jonatani anaika bwanji moyo wake pachiswe pamene ananena mawu amene analembedwa pa 1 Samueli 19:4, 5? (1 Sam. 19:1, 6)
Nkhani 60
Abigayeli ndi Davide
Kodi mkazi amene akubwera kudzakumana ndi Davide m’chithunzichi dzina lake ndi ndani, ndipo kodi ndi munthu wotani?
Kodi Nabala ndi ndani?
N’chifukwa chiyani Davide akutuma amuna ake ena kukapempha chithandizo kwa Nabala?
Kodi Nabala ananena chiyani kwa amuna a Davide, ndipo Davide akuchita chiyani atamva zimenezo?
Kodi Abigayeli anasonyeza bwanji kuti ndi mkazi wanzeru?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani 1 Samueli 22:1-4.
Kodi anthu a m’banja la Davide anapereka chitsanzo chabwino chotani cha mmene tiyenera kuthandizirana pa ubale wathu wachikristu? (Miy. 17:17; 1 Ates. 5:14)
Ŵerengani 1 Samueli 25:1-43.
N’chifukwa chiyani Nabala akufotokozedwa ndi mawu oipa kwambiri? (1 Sam. 25:2-5, 10, 14, 21, 25)
Kodi akazi achikristu okwatiwa angaphunzire chiyani masiku ano ku chitsanzo cha Abigayeli? (1 Sam. 25:32, 33; Miy. 31:26; Aef. 5:24)
Kodi Abigayeli analepheretsa Davide kuchita zinthu ziŵiri ziti zolakwa? (1 Sam. 25:31, 33; Aroma 12:19; Aef. 4:26)
Kodi zimene Davide anachita atamva mawu a Abigayeli zimathandiza bwanji amuna masiku ano kuona akazi monga momwe Yehova amawaonera? (Mac. 21:8, 9; Aroma 2:11; 1 Pet. 3:7)
Nkhani 61
Davide Akulongedwa Ufumu
Kodi Davide ndi Abisai anachita chiyani pamene Sauli anali kugona mu msasa wake?
Kodi Davide akufunsa Sauli mafunso otani?
Atasiyana ndi Sauli, kodi Davide akupita kuti?
Kodi n’chiyani chikumvetsa chisoni kwambiri Davide, moti mpaka analemba nyimbo yokoma?
Kodi Davide ali ndi zaka zingati pamene akulongedwa ufumu ku Hebroni, ndipo ana ake ena mayina awo ndi ndani?
Kodi kenaka Davide akulamuliranso kuti monga mfumu?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani 1 Samueli 26:1-25.
Mawu a Davide omwe analembedwa pa 1 Samueli 26:11 akusonyeza kuti anali ndi maganizo otani okhudza kakonzedwe ka zinthu ka Mulungu? (Sal. 37:7; Aroma 13:2)
Ngati tayesetsa kusonyeza kukoma mtima kwachikondi kwa munthu wina, koma munthu amene tamusonyeza zimenezoyo sakuyamikira zimene tachitazo, kodi mawu a Davide opezeka pa 1 Samueli 26:23 angatithandize bwanji kukhalabe ndi maganizo oyenera? (1 Maf. 8:32; Sal. 18:20)
Ŵerengani 2 Samueli 1:26.
Kodi Akristu masiku ano angakhale bwanji ndi “chikondano chenicheni” ngati chimene Davide ndi Jonatani anali nacho? (1 Pet. 4:8; Akol. 3:14; 1 Yoh. 4:12)
Ŵerengani 2 Samueli 5:1-10.
Kodi Davide anakhala mfumu kwa zaka zingati, ndipo zaka zimenezi zinagaŵidwa bwanji? (2 Sam. 5:4, 5)
Kodi Davide anatchuka chifukwa chiyani, ndipo kodi zimenezi zimatikumbutsa chiyani ifeyo masiku ano? (2 Sam. 5:10; 1 Sam. 16:13; 1 Akor. 1:31; Afil. 4:13)
Nkhani 62
Bvuto M’banja la Davide
Kodi pamapeto pake n’chiyani chikuchitikira dziko la Kanani ndi chithandizo cha Yehova?
Kodi n’chiyani chikuchitika madzulo enaake Davide ali pa tsindwi la mphala yake?
N’chifukwa chiyani Yehova wakwiyira kwambiri Davide?
M’chithunzichi, kodi Yehova akutumiza ndani kukauza Davide za machimo ake, ndipo kodi munthu ameneyo akunena kuti n’chiyani chidzachitikira Davide?
Kodi Davide akukhala ndi vuto lotani?
Pambuyo pa Davide, ndani akukhala mfumu ya Israyeli?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani 2 Samueli 11:1-27.
Kodi kuchita khama pa utumiki wa Yehova kumatiteteza bwanji?
Kodi n’chiyani chinakopa Davide kuti achimwe, ndipo zimenezi zikupereka chenjezo lotani kwa atumiki a Yehova masiku ano? (2 Sam. 11:2; Mat. 5:27-29; 1 Akor. 10:12; Yak. 1:14, 15)
Ŵerengani 2 Samueli 12:1-18.
Kodi ndi phunziro lotani limene akulu ndi makolo angaphunzire pa nkhani ya mmene Natani analankhulira ndi Davide pomupatsa uphungu? (2 Sam. 12:1-4; Miy. 12:18; Mat. 13:34)
N’chifukwa chiyani Yehova anachitira chifundo Davide? (2 Sam. 12:13; Sal. 32:5; 2 Akor. 7:9, 10)
Nkhani 63
Mfumu Yanzeru Solomo
Kodi Yehova akumufunsa chiyani Solomo, ndipo akuyankha bwanji?
Chifukwa chakuti wakondwera ndi zimene Solomo wapempha, kodi Yehova akulonjeza kuti amupatsa chiyani?
Kodi ndi nkhani yothetsa nzeru yotani imene akazi aŵiri akubweretsa kwa Solomo?
Monga momwe mukuonera pachithunzipa, kodi Solomo anathetsa bwanji nkhaniyo?
Kodi ufumu wa Solomo ndi wotani, ndipo n’chifukwa chiyani uli wotero?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani 1 Mafumu 3:3-28.
Kodi amuna amene amapatsidwa maudindo m’gulu la Mulungu masiku ano angaphunzire chiyani ku mawu ochokera pansi pamtima a Solomo amene ali pa 1 Mafumu 3:7? (Sal. 119:105; Miy. 3:5, 6)
Kodi zimene anapempha Solomo ndi chitsanzo chabwino chotani cha zimene tiyenera kupempherera? (1 Maf. 3:9, 11; Miy. 30:8, 9; 1 Yoh. 5:14)
Kodi zimene Solomo anachita pothetsa mkangano wa akazi aŵiri aja zimatipatsa chikhulupiriro chotani chokhudza ulamuliro wam’tsogolo wa Solomo Wamkulu, Yesu Kristu? (1 Maf. 3:28; Yes. 9:6, 7; 11:2-4)
Ŵerengani 1 Mafumu 4:29-34
Kodi Yehova anayankha bwanji pempho la Solomo loti akhale ndi mtima womvera? (1 Maf. 4:29)
Poona zimene anthu anayesetsa kuchita kuti akamve nzeru za Solomo, kodi kuphunzira Mawu a Mulungu tiyenera kukuona bwanji? (1 Maf. 4:29, 34; Yoh. 17:3; 2 Tim. 3:16)
Nkhani 64
Solomo Amanga Kachisi
Kodi zikutenga nthaŵi yaitali motani kuti Solomo amalize kumanga kachisi wa Yehova, ndipo n’chifukwa chiyani kachisiyo akudya ndalama zochuluka kwambiri?
Kodi m’kachisimo muli zipinda zazikulu zingati, ndipo m’chipinda cham’katikati akuikamo chiyani?
Kodi Solomo akunena chiyani m’pemphero lake pamene kachisiyo watha kumangidwa?
Kodi Yehova akusonyeza bwanji kuti wakondwera ndi pemphero la Solomo?
Kodi akazi a Solomo akumupangitsa kuchita chiyani, ndipo n’chiyani chikuchitikira Solomo?
N’chifukwa chiyani Yehova wakwiyira Solomo, ndipo kodi Yehova akunena chiyani kwa iye?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani 1 Mbiri 28:9, 10.
Mogwirizana ndi mawu a Davide olembedwa pa 1 Mbiri 28:9, 10, kodi tiyenera kuyesetsa kuchita chiyani tsiku lililonse pamoyo wathu? (Sal. 19:14; Afil. 4:8, 9)
Ŵerengani 2 Mbiri 6:12-21, 32-42.
Kodi Solomo anasonyeza bwanji kuti palibe nyumba yomangidwa ndi anthu imene Mulungu Wam’mwambamwamba angakhalemo? (2 Mbiri 6:18; Mac. 17:24, 25)
Kodi mawu a Solomo opezeka pa 2 Mbiri 6:32, 33 amasonyeza chiyani za Yehova? (Mac. 10:34, 35; Agal. 2:6)
Ŵerengani 2 Mbiri 7:1-5.
Mofanana ndi mmene ana a Israyeli anakhudzidwira mumtima n’kunena mawu olemekeza Yehova ataona ulemerero wake, kodi nafenso masiku ano tiyenera kukhudzidwa motani tikaganizira mmene Yehova wadalitsira anthu ake? (2 Mbiri 7:3; Sal. 22:22; 34:1; 96:2)
Ŵerengani 1 Mafumu 11:9-13.
Kodi moyo wa Solomo umasonyeza bwanji kufunika kokhala wokhulupirika mpaka mapeto? (1 Maf. 11:4, 9; Mat. 10:22; Chiv. 2:10)
Nkhani 65
Ufumu Ukugawanika
Kodi amuna aŵiri amene ali m’chithunziŵa mayina awo ndi ndani, ndipo kodi amunawo ndi ndani?
Kodi Ahiya akuchita chiyani ndi mwinjiro umene wavala, ndipo kodi zimenezo zikutanthauza chiyani?
Kodi Solomo akuyesera kumutani Yerobiamu?
N’chifukwa chiyani anthu akupanga Yerobiamu kukhala mfumu pa mafuko 10?
N’chifukwa chiyani Yerobiamu akupanga ana ang’ombe aŵiri agolidi, ndipo n’chiyani chikuchitikira dzikolo posakhalitsa?
Kodi n’chiyani chikuchitikira ufumu wa mafuko aŵiri ndi kachisi wa Yehova ku Yerusalemu?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani 1 Mafumu 11:26-43.
Kodi Yerobiamu anali munthu wotani, ndipo kodi Yehova anamulonjeza chiyani ngati akanasunga malamulo a Mulungu? (1 Maf. 11:28, 38)
Ŵerengani 1 Mafumu 12:1-33.
Kodi makolo ndi akulu angaphunzire chiyani ku chitsanzo choipa cha Rehobiamu chokhudza kugwiritsa ntchito molakwika udindo umene tili nawo? (1 Maf. 12:13; Mlal. 7:7; 1 Pet. 5:2, 3)
Kodi achinyamata masiku ano ayenera kufunsa ndani akamafuna kuchita zinthu zikuluzikulu m’moyo? (1 Maf. 12:6, 7; Miy. 1:8, 9; 2 Tim. 3:16, 17; Aheb. 13:7)
Kodi n’chiyani chinachititsa Yerobiamu kukhazikitsa malo aŵiri olambirira ana ang’ombe, ndipo kodi zimenezi zinasonyeza bwanji kupandiratu chikhulupiriro mwa Yehova? (1 Maf. 11:37; 12:26-28)
Kodi ndani anatsogolera anthu a ufumu wa mafuko 10 popandukira kulambira koona? (1 Maf. 12:32, 33)
Nkhani 66
Yezebeli—Mkazi Woipa wa Mfumu
Kodi Yezebeli ndi ndani?
N’chifukwa chiyani Mfumu Ahabu anakwiya tsiku lina?
Kodi Yezebeli akuchita chiyani kuti atenge munda wamphesa wa Naboti n’kuupereka kwa mwamuna wake, Ahabu?
Kodi Yehova akutumiza ndani kukalanga Yezebeli?
Monga momwe mukuonera pachithunzipa, kodi chikuchitika n’chiyani Yehu atafika kunyumba yachifumu ya Yezebeli?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani 1 Mafumu 16:29-33 ndi 18:3, 4.
Kodi zinthu zinaipa motani ku Israyeli mu nthaŵi ya Mfumu Ahabu? (1 Maf. 14:9)
Ŵerengani 1 Mafumu 21:1-16.
Kuchokera ku chitsanzo cha Ahabu, kodi tingaphunzirenji za zimene tingachite tikakhumudwitsidwa? (1 Maf. 21:4; Aroma 5:3-5)
Ŵerengani 2 Mafumu 9:30-37.
Kodi tingaphunzirenji kuchokera ku changu cha Yehu pochita chifuniro cha Yehova? (2 Maf. 9:4-10; 2 Akor. 9:1, 2; 2 Tim. 4:2)
Nkhani 67
Yehosafati Adalira Yehova
Kodi Yehosafati ndi ndani, ndipo akukhala ndi moyo pa nthaŵi iti?
N’chifukwa chiyani Aisrayeli akuchita mantha, ndipo ambiri a iwo akuchita chiyani?
Kodi Yehova akuyankha motani pemphero la Yehosafati?
Kodi Yehova akuchititsa chiyani kuchitika nkhondo isanayambe?
Kodi tingaphunzire phunziro lotani kwa Yehosafati?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani 2 Mbiri 20:1-30.
Kodi Yehosafati anasonyeza bwanji zimene atumiki okhulupirika a Mulungu ayenera kuchita akakumana ndi zinthu zochititsa mantha? (2 Mbiri 20:12; Sal. 25:15; 62:1)
Popeza Yehova nthaŵi zonse wakhala ndi njira yomwe amagwiritsa ntchito polankhula ndi anthu ake, kodi masiku ano amagwiritsa ntchito njira yanji? (2 Mbiri 20:14, 15; Mat. 24:45-47; Yoh. 15:15)
Mulungu akadzayambitsa “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu, Wamphamvuyonse,” kodi tidzakhala bwanji ngati mmene analili Yehosafati? (2 Mbiri 20:15, 17; 32:8; Chiv. 16:14, 16)
Potsanzira Alevi, kodi apainiya ndi amishonale masiku ano amathandizira bwanji pa ntchito yapadziko lonse yolalikira? (2 Mbiri 20:19; Aroma 10:13-15; 2 Tim. 4:2)
Nkhani 68
Anyamata Awiri Oukitsidwa
Kodi anthu atatu amene ali m’chithunziŵa ndi ndani, ndipo n’chiyani chikuchitikira kamnyamatako?
Kodi Eliya akupempherera chiyani chokhudza kamnyamatako, ndipo n’chiyani chikuchitika kenako?
Kodi dzina la wothandiza wa Eliya ndi ndani?
N’chifukwa chiyani Elisa akuitanidwa kunyumba kwa mkazi wa ku Sunemu?
Kodi Elisa akuchita chiyani, ndipo n’chiyani chikuchitikira mwana wakufayo?
Kodi Yehova ali ndi mphamvu zotani, monga momwe zinaonekera mwa Eliya ndi Elisa?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani 1 Mafumu 17:8-24.
Kodi kumvera ndi kukhulupirika kwa Eliya kunayesedwa bwanji? (1 Maf. 17:9; 19:1-4, 10)
N’chifukwa chiyani chikhulupiriro cha mkazi wamasiye wa ku Zerefati chinali chochititsa chidwi kwambiri? (1 Maf. 17:12-16; Luka 4:25, 26)
Kodi zimene zinachitikira mkazi wamasiye wa ku Zerefati zikusonyeza bwanji kuti mawu a Yesu amene analembedwa pa Mateyu 10:41, 42 ndi oona? (1 Maf. 17:10-12, 17, 23, 24)
Ŵerengani 2 Mafumu 4:8-37.
Kodi mkazi wa ku Sunemu akutiphunzitsa chiyani za kuchereza alendo? (2 Maf. 4:8; Luka 6:38; Aroma 12:13; 1 Yoh. 3:17)
Kodi tingachite zinthu zachifundo m’njira zotani kwa atumiki a Mulungu masiku ano? (Mac. 20:35; 28:1, 2; Agal. 6:9, 10; Aheb. 6:10)
Nkhani 69
Mtsikana Athandiza Ngwazi
M’chithunzichi, kodi buthuli likuuza mayiyo chiyani?
Kodi mayi ali pachithunziyu ndi ndani, ndipo kodi buthuli likuchita chiyani kunyumba ya mayiyo?
Kodi Elisa akuuza mtumiki wake kukauza Namani chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani Namani akukwiya?
Kodi chikuchitika n’chiyani Namani atamvera atumiki ake?
N’chifukwa chiyani Elisa akukana mphatso ya Namani, koma kodi Gehazi akuchita chiyani?
Kodi n’chiyani chikuchitikira Gehazi, ndipo tingaphunzirepo chiyani pamenepa?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani 2 Mafumu 5:1-27.
Kodi chitsanzo cha buthu la ku Israyeli lija chingalimbikitse bwanji achinyamata masiku ano? (2 Maf. 5:3; Sal. 8:2; 148:12, 13)
N’chifukwa chiyani ndi bwino kukumbukira chitsanzo cha Namani tikalandira uphungu wochokera m’Malemba? (2 Maf. 5:15; Aheb. 12:5, 6; Yak. 4:6)
Kodi tingaphunzire maphunziro otani mwa kusiyanitsa chitsanzo cha Elisa ndi cha Gehazi? (2 Maf. 5:9, 10, 14-16, 20; Mat. 10:8; Mac. 5:1-5; 2 Akor. 2:17)
Nkhani 70
Yona ndi Chinsomba
Kodi Yona ndi ndani, ndipo Yehova akumuuza kuti achite chiyani?
Chifukwa chakuti sakufuna kupita kumene Yehova wamuuza, kodi Yona akuchita chiyani?
Kodi Yona akuuza amalinyero kuchita chiyani kuti aletse mafunde?
Monga mukuonera pachithunzipa, kodi n’chiyani chikuchitika pamene Yona akumira?
Kodi Yona akukhala m’mimba mwa chinsomba kwa nthaŵi yaitali bwanji, ndipo ali m’menemo akuchita chiyani?
Kodi Yona akupita kuti atatuluka m’mimba mwa chinsombacho, ndipo kodi zimenezi zikutiphunzitsa chiyani?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Yona 1:1-17.
Kodi zikuoneka kuti Yona anamva bwanji za ntchito imene anamupatsa yoti akalalikire kwa anthu a ku Nineve? (Yona 1:2, 3; Miy. 3:7; Mlal. 8:12)
Ŵerengani Yona 2:1, 2, 10.
Kodi zimene zinamuchitikira Yona zimatilimbikitsa bwanji kuti Yehova adzayankha mapemphero athu? (Sal. 22:24; 34:6; 1 Yoh. 5:14)
Ŵerengani Yona 3:1-10.
Kodi tikulimbikitsidwa bwanji ndi mfundo yakuti Yehova anapitirizabe kumugwiritsa ntchito Yona ngakhale kuti poyamba analephera kukwanitsa ntchito imene anamupatsa? (Sal. 103:14; 1 Pet. 5:10)
Kodi zimene zinachitikira Yona ndi anthu a ku Nineve zikutiphunzitsa chiyani za kuweruziratu anthu a m’gawo lathu? (Yona 3:6-9; Mlal. 11:6; Mac. 13:48)
Nkhani 71
Mulungu Alonjeza Paradaiso
Kodi Yesaya anali ndani, kodi anakhalapo liti, ndipo kodi Yehova anamusonyeza chiyani?
Kodi liwu lakuti “paradaiso” limatanthauza chiyani, ndipo kodi limakukumbutsani za chiyani?
Kodi Yehova anauza Yesaya kulemba chiyani za Paradaiso watsopano?
N’chifukwa chiyani Adamu ndi Hava anataya malo okongola amene ankakhalamo?
Kodi Yehova akulonjeza chiyani kwa anthu amene amamukonda?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Yesaya 11:6-9.
Kodi Mawu a Mulungu amapereka chithunzi chotani cha mtendere umene udzakhalepo pakati pa zinyama ndi anthu m’dziko latsopano? (Sal. 148:10, 13; Yes. 65:25; Ezek. 34:25)
Kodi mawu a Yesaya akukwaniritsidwa motani mwauzimu pakati pa anthu a Yehova masiku ano? (Aroma 12:2; Aef. 4:23, 24)
Kodi ndani ayenera kuyamikiridwa chifukwa cha kusintha kwa khalidwe la anthu panopa ndiponso m’dziko latsopano? (Yes. 48:17, 18; Agal. 5:22, 23; Afil. 4:7)
Ŵerengani Chivumbulutso 21:3, 4.
Kodi Malemba amasonyeza bwanji kuti kukhala kwa Mulungu ndi anthu kumatanthauza kuti ali nawo mophiphiritsira, osati ali nawodi limodzi padziko lapansi pano? (Lev. 26:11, 12; 2 Mbiri 6:18; Yes. 66:1; Chiv. 21:2, 3, 22-24)
Kodi ndi misozi ndi kupweteka kwa mtundu wanji kumene kudzachotsedwe? (Luka 8:49-52; Aroma 8:21, 22; Chiv. 21:4)
Nkhani 72
Mulungu Athandiza Mfumu Hezekiya
Kodi mwamuna ali m’chithunziyu ndi ndani, ndipo n’chifukwa chiyani ali m’mavuto ambiri?
Kodi makalata amene Hezekiya waika pamaso pa Mulungu ndi otani, ndipo Hezekiya akupempherera chiyani?
Kodi Hezekiya ndi mfumu yotani, ndipo Yehova akumutumizira uthenga wotani kudzera mwa mneneri Yesaya?
Kodi mngelo wa Yehova anachita chiyani kwa Asuri, monga momwe chikusonyezera chithunzichi?
Ngakhale kuti ufumu wa mafuko aŵiri uli ndi mtendere kwa kanthaŵi, n’chiyani chikuchitika Hezekiya atamwalira?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani 2 Mafumu 18:1-36.
Kodi kazembe wa Asuri anafuna bwanji kufooketsa chikhulupiriro cha Aisrayeli? (2 Maf. 18:19, 21; Eks. 5:2; Sal. 64:3)
Pochita zinthu ndi otsutsa, kodi Mboni za Yehova zimatsanzira bwanji chitsanzo cha Hezekiya? (2 Maf. 18:36; Sal. 39:1; Miy. 26:4; 2 Tim. 2:24)
Ŵerengani 2 Mafumu 19:1-37.
Kodi anthu a Yehova masiku ano amatsanzira bwanji Hezekiya mu nthaŵi zovuta? (2 Maf. 19:1, 2; Miy. 3:5, 6; Aheb. 10:24, 25; Yak. 5:14, 15)
Kodi Mfumu Sanakeribu anagonja patatu motani, ndipo kodi amaphiphiritsira ndani mwaulosi? (2 Maf. 19:32, 35, 37; Chiv. 20:2, 3)
Ŵerengani 2 Mafumu 21:1-6, 16.
N’chifukwa chiyani tinganene kuti Manase anali mmodzi mwa mafumu oipitsitsa amene analamulirapo ku Yerusalemu? (2 Mbiri 33:4-6, 9)
Nkhani 73
Mfumu Yabwino Yomaliza
Kodi Yosiya ali ndi zaka zingati pamene akukhala mfumu, ndipo akuyamba kuchita chiyani atakhala mfumu kwa zaka zisanu ndi ziŵiri?
Kodi mukuona Yosiya akuchita chiyani pachithunzi choyambachi?
Kodi mkulu wa ansembe akupeza chiyani pamene amunawo akukonza kachisi?
N’chifukwa chiyani Yosiya akung’amba zovala zake?
Kodi mneneri wachikazi Hulida akuuza Yosiya uthenga wanji wochokera kwa Yehova?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani 2 Mbiri 34:1-28.
Kodi Yosiya akupereka chitsanzo chotani kwa anthu amene mwina anavutika ali ana? (2 Mbiri 33:21-25; 34:1, 2; Sal. 27:10)
Kodi ndi zinthu zofunika zotani zimene Yosiya anachita pofuna kupititsa patsogolo kulambira koona m’chaka chake cha 8, cha 12, ndi cha 18 monga mfumu? (2 Mbiri 34:3, 8)
Kodi tingaphunzire chiyani chokhudza kusamalira malo athu olambirira ku zitsanzo zimene anatisiyira Mfumu Yosiya ndi Mkulu wa Ansembe Hilikiya? (2 Mbiri 34:9-13; Miy. 11:14; 1 Akor. 10:31)
Nkhani 74
Munthu Wosaopa
Kodi mnyamata ali m’chithunziyu ndi ndani?
Kodi Yeremiya akuganiza chiyani pankhani yoti akhale mneneri, koma kodi Yehova akumuuza chiyani?
Kodi Yeremiya akuuzabe anthu uthenga wotani?
Kodi ansembe akuyesera bwanji kuletsa Yeremiya, koma kodi iye akusonyeza bwanji kuti sakuopa?
Kodi n’chiyani chikuchitika pamene Aisrayeli sakusintha njira zawo zoipa?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Yeremiya 1:1-8.
Monga momwe chitsanzo cha Yeremiya chikusonyezera, kodi n’chiyani chimamuchititsa munthu kukhala woyenera kutumikira Yehova? (2 Akor. 3:5, 6)
Kodi chitsanzo cha Yeremiya chimalimbikitsa motani Akristu achinyamata masiku ano? (Mlal. 12:1; 1 Tim. 4:12)
Ŵerengani Yeremiya 10:1-5.
Kodi Yeremiya anagwiritsa ntchito chitsanzo chogwira mtima kwambiri chotani kuti asonyeze kupanda pake kokhulupirira mafano? (Yer. 10:5; Yes. 46:7; Hab. 2:19)
Ŵerengani Yeremiya 26:1-16.
Popereka uthenga wochenjeza anthu masiku ano, kodi otsalira odzozedwa amvera bwanji lamulo la Yehova kwa Yeremiya loti ‘asasiyepo mawu amodzi’? (Yer. 26:2; Deut. 4:2; Mac. 20:27)
Kodi Yeremiya anapereka chitsanzo chabwino chotani kwa Mboni za Yehova masiku ano zikamalengeza chenjezo la Yehova ku mitundu ya anthu? (Yer. 26:8, 12, 14, 15; 2 Tim. 4:1-5)
Ŵerengani 2 Mafumu 24:1-17.
Kodi n’zotsatirapo zoipa zotani zimene zinachitika chifukwa chakuti Ayuda sanakhulupirike kwa Yehova? (2 Maf. 24:2-4, 14)
Nkhani 75
Anyamata Anai M’Babulo
Kodi anyamata anayi amene ali pachithunzipa ndi ndani, ndipo n’chifukwa chiyani ali m’Babulo?
Kodi n’chiyani chimene Nebukadinezara akulinganiza kuchitira anyamatawo, ndipo akulamula atumiki ake kuchita chiyani?
Kodi n’chiyani chimene Danieli akupempha chokhudza zakudya ndi zakumwa zake ndi za anzake atatu?
Atadya zomera kwa masiku 10, kodi Danieli ndi anzake atatu aja akuoneka bwanji powayerekezera ndi anyamata ena onse?
Kodi chinachitika n’chiyani kuti Danieli ndi anzake atatu aja akhale m’mphala mwa mfumu, ndipo kodi iwowo akudziŵa zinthu zambiri motani poyerekezera ndi ansembe ndi anzeru?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Danieli 1:1-21.
Kodi pamafunika kuchita khama lotani ngati tikufuna kulimbana ndi ziyeso ndiponso kuthana ndi zofooka? (Dan. 1:8; Gen. 39:7, 10; Agal. 6:9)
Kodi achinyamata masiku ano angakopeke kapena kukakamizidwa motani kuti achite nawo zinthu zimene, kwa ena, zimaoneka zokoma ngati “chakudya cha mfumu”? (Dan. 1:8; Miy. 20:1; 2 Akor. 6:17–7:1)
Kodi nkhani ya m’Baibulo ya anyamata anayi achihebri imatithandiza kuzindikira chiyani chokhudza kuphunzira maphunziro akudziko? (Dan. 1:20; Yes. 54:13; 1 Akor. 3:18-20)
Nkhani 76
Yerusalemu Aonongedwa
Kodi n’chiyani chikuchitikira Yerusalemu ndi Aisrayeli amene awasonyeza m’chithunzichi?
Kodi Ezekieli ndi ndani, ndipo kodi Yehova akumusonyeza zoipa zotani?
Kodi n’chiyani chimene Yehova akulonjeza chifukwa choti Aisrayeli sakum’lemekeza?
Kodi n’chiyani chimene Mfumu Nebukadinezara akuchita Aisrayeli atamupandukira?
N’chifukwa chiyani Yehova akulola kuti Aisrayeli awonongedwe moipa chonchi?
Kodi n’chiyani chikuchititsa kuti dziko la Israyeli likhale lopanda anthu, ndipo linakhala choncho kwa nthaŵi yaitali bwanji?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani 2 Mafumu 25:1-26.
Kodi Zedekiya anali ndani, n’chiyani chinamuchitikira, ndipo kodi zimenezi zinakwaniritsa bwanji ulosi wa m’Baibulo? (2 Maf. 25:5-7; Ezek. 12:13-15)
Kodi Yehova anaona kuti ndani anachititsa kuti Aisrayeli akhale osakhulupirika? (2 Maf. 25:9, 11, 12, 18, 19; 2 Mbiri 36:14, 17)
Ŵerengani Ezekieli 8:1-18.
Kodi Matchalitchi Achikristu atengera bwanji Aisrayeli opanduka amene ankalambira dzuŵa? (Ezek. 8:16; Yes. 5:20, 21; Yoh. 3:19-21; 2 Tim. 4:3)
Nkhani 77
Sakanagwada
Kodi Nebukadinezara, mfumu ya Babulo, wapereka lamulo lotani kwa anthu?
N’chifukwa chiyani anzake atatu a Danieli sakugwadira fano la golidi?
Nebukadinezara atawapatsa Ahebri atatu aja mwayi wina woti agwade, kodi akusonyeza bwanji kuti akudalira Yehova?
Kodi Nebukadinezara akuuza amuna ake kuchita chiyani ndi Sadrake, Mesake, ndi Abedinego?
Kodi Nebukadinezara akuona chiyani atasuzumira m’ng’anjomo?
N’chifukwa chiyani mfumuyo ikulemekeza Mulungu wa Sadrake, Mesake, ndi Abedinego, ndipo kodi anyamata atatuŵa akutipatsa chitsanzo chotani?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Danieli 3:1-30.
Kodi ndi mtima wotani umene anyamata achihebri atatu aja anasonyeza umene atumiki a Mulungu onse ayenera kutsanzira akakumana ndi zinthu zoyesa kukhulupirika kwawo? (Dan. 3:17, 18; Mat. 10:28; Aroma 14:7, 8)
Kodi Yehova Mulungu anaphunzitsa Nebukadinezara phunziro lofunika lotani? (Dan. 3:28, 29; 4:34, 35)
Nkhani 78
Zolembedwa ndi Manja pa Khoma
Kodi chikuchitika n’chiyani pamene mfumu ya ku Babulo yakonza madyerero n’kugwiritsa ntchito zikho ndi mbale zotengedwa m’kachisi wa Yehova ku Yerusalemu?
Kodi Belisazara akuuza anzeru ake chiyani, koma kodi anzeruwo akulephera kuchita chiyani?
Kodi mayi ake a mfumuyo akumuuza kuti achite chiyani?
Malinga ndi zimene Danieli akuuza mfumuyo, n’chifukwa chiyani Mulungu watumiza dzanjalo kudzalemba pa khoma?
Kodi Danieli akufotokoza bwanji tanthauzo la mawu amene ali pakhomawo?
Kodi chikuchitika n’chiyani Danieli akali chilankhulire?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Danieli 5:1-31.
Siyanitsani kuopa Mulungu ndi mantha amene Belisazara anali nawo ataona zolembedwa pakhoma zija. (Dan. 5:6, 7; Sal. 19:9; Aroma 8:35-39)
Kodi Danieli anasonyeza bwanji kulimba mtima kwambiri pamene anali kulankhula ndi Belisazara ndi akulu ake? (Dan. 5:17, 18, 22, 26-28; Mac. 4:29)
Kodi Danieli chaputala 5 chimasonyeza bwanji kuti Yehova ndiye amene ali ndi ulamuliro wachilengedwe chonse? (Dan. 4:17, 25; 5:21)
Nkhani 79
Danieli M’dzenje la Mikango
Kodi Dariyo ndi ndani, ndipo kodi amamuona bwanji Danieli?
Kodi amuna ena ansanje akupangitsa Dariyo kuchita chiyani?
Kodi Danieli akuchita chiyani atamva za lamulo latsopanolo?
N’chifukwa chiyani Dariyo ali wovutika maganizo kwambiri kwakuti sakutha kugona, ndipo akuchita chiyani m’maŵa mwake?
Kodi Danieli akumuyankha bwanji Dariyo?
Kodi n’chiyani chikuchitikira amuna oipa amene anafuna kupha Danieli, ndipo kodi Dariyo akulembera chiyani anthu onse a mu ufumu wake?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Danieli 6:1-28.
Kodi chiwembu chimene anachitira Danieli chikutikumbutsa bwanji za zimene otsutsa ayesera kuchita kuti apondereze ntchito ya Mboni za Yehova masiku athu ano? (Dan. 6:7; Sal. 94:20; Yes. 10:1; Aroma 8:31)
Kodi atumiki a Mulungu angatsanzire bwanji Danieli pankhani yopitiriza kugonjera “maulamuliro a akulu”? (Dan. 6:5, 10; Aroma 13:1; Mac. 5:29)
Kodi tingatsanzire bwanji chitsanzo cha Danieli chotumikira Yehova “kosalekeza”? (Dan. 6:16, 20; Afil. 3:16; Chiv. 7:15)
Nkhani 80
Anthu a Mulungu Atuluka M’Babulo
Monga momwe asonyezera m’chithunzichi, kodi Aisrayeli akuchita chiyani?
Kodi Koresi anakwaniritsa bwanji ulosi wa Yehova umene ananena kudzera mwa Yesaya?
Kodi Koresi akuuza Aisrayeli amene sangathe kubwerera ku Yerusalemu kuti achite chiyani?
Kodi n’chiyani chimene Koresi akupatsa anthuwo kuti atenge popita ku Yerusalemu?
Kodi zikuwatengera Aisrayeliwo nthaŵi yaitali bwanji kuti afike ku Yerusalemu?
Kodi patha zaka zingati kuchokera pamene dzikolo linasiyidwa labwinja kotheratu?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Yesaya 44:28 ndi 45:1-4.
Kodi Yehova anatsimikiza bwanji kuti ulosi wokhudza Koresi udzakwaniritsidwa? (Yes. 55:10, 11; Aroma 4:17)
Kodi ulosi wa Yesaya wokhudza Koresi umasonyeza chiyani za mphamvu ya Yehova Mulungu yotha kuneneratu za m’tsogolo? (Yes. 42:9; 45:21; 46:10, 11; 2 Pet. 1:20)
Ŵerengani Ezara 1:1-11.
Potsatira chitsanzo cha anthu amene sanathe kubwerera ku Yerusalemu, kodi ifeyo masiku ano ‘tingalimbitse’ motani “manja” a anthu amene atha kuyamba utumiki wa nthaŵi zonse? (Ezara 1:4, 6; Aroma 12:13; Akol. 4:12)
Nkhani 81
Kudalira Thandizo la Mulungu
Kodi ndi anthu angati amene akuyenda ulendo wautali wochokera ku Babulo kupita ku Yerusalemu, koma kodi akupeza chiyani pofika?
Kodi n’chiyani chimene Aisrayeli akuyamba kumanga atafika, koma kodi adani awo akuchita chiyani?
Kodi Hagai ndi Zekariya ndi ndani, ndipo kodi akuuza anthuwo chiyani?
N’chifukwa chiyani Tatenayi akutumiza kalata ku Babulo, ndipo kodi akulandira yankho lotani?
Kodi Ezara akuchita chiyani atamva kuti pakufunika kukonza kachisi wa Mulungu?
Kodi Ezara akupempherera chiyani m’chithunzichi, kodi pemphero lake likuyankhidwa motani, ndipo kodi zimenezi zikutiphunzitsa chiyani ifeyo?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Ezara 3:1-13.
Ngati titapezeka kuti tili kudera kumene kulibe mpingo wa anthu a Mulungu, kodi tiyenera kupitiriza kuchita chiyani? (Ezara 3:3, 6; Mac. 17:16, 17; Aheb. 13:15)
Ŵerengani Ezara 4:1-7.
Kodi Zerubabele anasiyira anthu a Yehova chitsanzo chotani chokhudza kupemphera pamodzi ndi anthu a zikhulupiriro zina? (Eks. 34:12; 1 Akor. 15:33; 2 Akor. 6:14-17)
Ŵerengani Ezara 5:1-5, 17 ndi 6:1-22.
N’chifukwa chiyani otsutsa analephera kusiyitsa ntchito yomanga kachisi? (Ezara 5:5; Yes. 54:17)
Kodi zimene anachita amuna aakulu a Ayuda zimalimbikitsa bwanji akulu achikristu kupempha kuti Yehova awatsogolere akamakumana ndi otsutsa? (Ezara 6:14; Sal. 32:8; Aroma 8:31; Yak. 1:5)
Ŵerengani Ezara 8:21-23, 28-36.
Tisanayambe kuchita kanthu kenakake, kodi ndi chitsanzo chiti cha Ezara chimene tingachite bwino kutsatira? (Ezara 8:23; Sal. 127:1; Miy. 10:22; Yak. 4:13-15)
Nkhani 82
Mordekai ndi Estere
Kodi Mordekai ndi Estere ndi ndani?
N’chifukwa chiyani Mfumu Ahaswero akufuna mkazi watsopano, ndipo akusankha ndani?
Kodi Hamani ndi ndani, ndipo n’chiyani chimene chikumukwiyitsa kwambiri?
Kodi kukupangidwa lamulo lotani, ndipo kodi Estere akuchita chiyani atalandira uthenga wochokera kwa Mordekai?
N’chiyani chikuchitikira Hamani, ndipo n’chiyani chikuchitikira Mordekai?
Kodi Aisrayeli akupulumutsidwa bwanji kwa adani awo?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Estere 2:12-18.
Kodi Estere anasonyeza bwanji kufunika kokhala ndi “mzimu wofatsa ndi wachete”? (Estere 2:15; 1 Pet. 3:1-5)
Ŵerengani Estere 4:1-17.
Mofanana ndi mmene Estere anapatsidwira mwayi wochitapo kanthu pothandiza kulambira koona, kodi ifeyo masiku ano timapatsidwa mwayi wotani wosonyeza kudzipereka ndi kukhulupirika kwathu kwa Yehova? (Estere 4:13, 14; Mat. 5:14-16; 24:14)
Ŵerengani Estere 7:1-6.
Kodi anthu a Mulungu ambiri masiku ano alolera motani kuzunzidwa, mofanana ndi mmene anachitira Estere? (Estere 7:4; Mat. 10:16-22; 1 Pet. 2:12)
Nkhani 83
Malinga a Yerusalemu
Kodi Aisrayeli anamva bwanji poona kuti analibe malinga kuzungulira mzinda wawo wa Yerusalemu?
Kodi Nehemiya ndi ndani?
Kodi ntchito ya Nehemiya ndi yotani, ndipo n’chifukwa chiyani ili yofunika?
Kodi ndi nkhani yotani imene ikumvetsa Nehemiya chisoni, ndipo kodi akuchita chiyani?
Kodi Mfumu Aritasasta akukomera mtima Nehemiya motani?
Kodi Nehemiya akulinganiza bwanji ntchito yomanga kuti adani a Aisrayeli asawasiyitse ntchitoyo?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Nehemiya 1:4-6 ndi 2:1-20.
Kodi Nehemiya anapempha bwanji Yehova kuti amutsogolere? (Neh. 2:4, 5; Aroma 12:12; 1 Pet. 4:7)
Ŵerengani Nehemiya 3:3-5.
Kodi akulu ndi atumiki otumikira angaphunzire chiyani pa kusiyana kwa Atekoa ndi “omveka” awo? (Neh. 3:5, 27; 2 Ates. 3:7-10; 1 Pet. 5:5)
Ŵerengani Nehemiya 4:1-23.
Kodi n’chiyani chinalimbikitsa Aisrayeli kupitirizabe kumanga ngakhale kuti anali kutsutsidwa kwambiri? (Neh. 4:6, 8, 9; Sal. 50:15; Yes. 65:13, 14)
Kodi chitsanzo cha Aisrayeli chimatilimbikitsa motani masiku ano?
Ŵerengani Nehemiya 6:15.
Kodi mfundo yakuti malinga a Yerusalemu anamalizidwa m’miyezi iŵiri ikusonyeza chiyani chokhudza mphamvu ya chikhulupiriro? (Sal. 56:3, 4; Mat. 17:20; 19:26)
Nkhani 84
Mngelo Afikira Mariya
Kodi mkazi ali pachithunziyu ndi ndani?
Kodi Gabrieli anauza Mariya chiyani?
Kodi Gabrieli anafotokoza motani kwa Mariya kuti adzakhala ndi mwana ngakhale kuti sanakhale ndi mwamuna?
Kodi n’chiyani chikuchitika pamene Mariya akukazonda mbale wake Elizabeti?
Kodi Yosefe akuganiza chiyani atamva zoti Mariya adzakhala ndi mwana, koma n’chifukwa chiyani akusintha maganizo?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Luka 1:26-56.
Kodi lemba la Luka 1:35 limasonyeza chiyani za kupanda ungwiro kulikonse kochokera kwa Adamu kumene kunali m’chiberekero cha Mariya pamene moyo wa Mwana wa Mulungu unasamutsidwa kuchoka kudziko la zolengedwa zauzimu? (Hag. 2:11-13; Yoh. 6:69; Aheb. 7:26; 10:5)
Kodi Yesu analemekezedwa bwanji asanabadwe? (Luka 1:41-43)
Kodi Mariya anapereka chitsanzo chabwino chotani kwa Akristu amene amakhala ndi mwayi wapadera wa utumiki masiku ano? (Luka 1:38, 46-49; 17:10; Miy. 11:2)
Ŵerengani Mateyu 1:18-25.
Ngakhale kuti Yesu sanapatsidwe dzina lakuti Emanueli, kodi zimene anachita monga munthu zinakwaniritsa motani tanthauzo la dzina limeneli? (Mat. 1:22, 23; Yoh. 14:8-10; Aheb. 1:1-3)
Nkhani 85
Yesu Abadwira M’khola
Kodi khanda lili pachithunzili ndi ndani, ndipo kodi Mariya akuligoneka kuti?
N’chifukwa chiyani Yesu anabadwira m’khola limodzi ndi zifuyo?
M’chithunzichi, kodi amuna amene akuloŵa m’kholawo ndi ndani, ndipo kodi mngelo anawauza chiyani?
N’chifukwa chiyani Yesu ali wapadera kwambiri?
N’chifukwa chiyani Yesu angatchedwe Mwana wa Mulungu?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Luka 2:1-20.
Kodi Kaisara Augusto anachitapo chiyani pa kukwaniritsidwa kwa ulosi wokhudza kubadwa kwa Yesu? (Luka 2:1-4; Mika 5:2)
Kodi munthu angakhale nawo bwanji m’gulu la anthu amene amatchedwa “anthu amene akondwera nawo”? (Luka 2:14; Mat. 16:24; Yoh. 17:3; Mac. 3:19; Aheb. 11:6)
Ngati abusa odzichepetsa a ku Yudeya aja anali ndi chifukwa chosangalalira kubadwa kwa Mpulumutsi, kodi atumiki a Mulungu masiku ano ali ndi chifukwa chachikulu kuposa pamenepa chotani chosangalalira? (Luka 2:10, 11; Aef. 3:8, 9; Chiv. 11:15; 14:6)
Nkhani 86
Amuna Atsogozedwa ndi Nyenyezi
Kodi amuna ali m’chithunziŵa ndi ndani, ndipo n’chifukwa chiyani mmodzi wa iwo akuloza nyenyezi yowala kwambiri?
N’chifukwa chiyani Mfumu Herode akukwiya, ndipo akuchita chiyani?
Kodi nyenyezi yowala ija inawalondolera kuti amunawo, koma n’chifukwa chiyani anabwerera kwawo podzera njira ina?
Kodi Herode akupereka lamulo lotani, ndipo n’chifukwa chiyani akupereka lamulo limeneli?
Kodi Yehova akuuza Yosefe kuchita chiyani?
Kodi ndani anachititsa nyenyezi yatsopanoyo kuwala, ndipo n’chifukwa chiyani anachita zimenezi?
Funso lowonjezera:
Ŵerengani Mateyu 2:1-23.
Kodi Yesu anali ndi zaka zingati pamene okhulupirira nyenyezi anadzamuzonda, ndipo anali kukhala kuti? (Mat. 2:1, 11, 16)
Nkhani 87
Mnyamata Yesu M’kachisi
Kodi Yesu ali ndi zaka zingati pachithunzipa, ndipo ali kuti?
Kodi Yosefe ndi banja lake amachita chiyani chaka chilichonse?
Atayenda tsiku limodzi pa ulendo wobwerera kwawo, n’chifukwa chiyani Yosefe ndi Mariya akubwerera ku Yerusalemu?
Kodi Yosefe ndi Mariya akumupeza kuti Yesu, ndipo n’chifukwa chiyani anthu kumeneko akudabwa?
Kodi Yesu akunena chiyani kwa amayi ake, Mariya?
Kodi tingakhale bwanji ngati Yesu pophunzira za Mulungu?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Luka 2:41-52.
Ngakhale kuti Chilamulo chinanena kuti amuna okha ndi amene sayenera kuphonya madyerero apachaka, kodi Yosefe ndi Mariya anapereka chitsanzo chabwino chotani kwa makolo masiku ano? (Luka 2:41; Deut. 16:16; 31:12; Miy. 22:6)
Kodi Yesu anapereka bwanji chitsanzo chabwino kwa achinyamata masiku ano kuti azimvera makolo awo? (Luka 2:51; Deut. 5:16; Miy. 23:22; Akol. 3:20)
Ŵerengani Mateyu 13:53-56.
Kodi ndi abale a Yesu anayi ati amene atchulidwa m’Baibulo, ndipo kodi aŵiri mwa iwo anadzagwiritsidwa ntchito bwanji mu mpingo wachikristu? (Mat. 13:55; Mac. 12:17; 15:6, 13; 21:18; Agal. 1:19; Yak. 1:1; Yuda 1)
Nkhani 88
Yohane Abatiza Yesu
Kodi amuna aŵiri ali m’chithunziŵa ndi ndani?
Kodi munthu amabatizidwa bwanji?
Kodi Yohane nthaŵi zambiri amabatiza anthu otani?
Kodi Yesu akupempha Yohane kumubatiza pa chifukwa chapadera chotani?
Kodi Mulungu akusonyeza bwanji kuti akukondwera kuti Yesu wabatizidwa?
Kodi n’chiyani chikuchitika Yesu atapita ku malo ayekha kwa masiku 40?
Kodi ena a otsatira, kapena kuti ophunzira a Yesu oyambirira ndi ndani, ndipo kodi chozizwitsa cha Yesu choyamba n’chiyani?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Mateyu 3:13-17.
Kodi Yesu anasiyira ophunzira ake chitsanzo chotani cha mmene ayenera kubatizidwira? (Sal. 40:7, 8; Mat. 28:19, 20; Luka 3:21, 22)
Ŵerengani Mateyu 4:1-11.
Yesu ankagwiritsa ntchito Baibulo mwaluso. Kodi zimenezi zimatilimbikitsa bwanji kuti tiziphunzira Baibulo nthaŵi zonse? (Mat. 4:5-7; 2 Pet. 3:17, 18; 1 Yoh. 4:1)
Ŵerengani Yohane 1:29-51.
Kodi Yohane Mbatizi analozera ophunzira ake kwa ndani, ndipo tingamutsanzire bwanji masiku ano? (Yoh. 1:29, 35, 36; 3:30; Mat. 23:10)
Ŵerengani Yohane 2:1-12.
Kodi chozizwitsa choyamba cha Yesu chinasonyeza bwanji kuti Yehova samana atumiki Ake chinthu chilichonse chabwino? (Yoh. 2:9, 10; Sal. 84:11; Yak. 1:17)
Nkhani 89
Yesu Ayeretsa Kachisi
N’chifukwa chiyani zinyama zikugulitsidwa pakachisi?
Kodi n’chiyani chikukwiyitsa Yesu?
Monga mukuonera pachithunzipa, kodi Yesu akuchita chiyani, ndipo akulamula anthu ogulitsa nkhundawo kuchita chiyani?
Otsatira a Yesu ataona zimene Yesu akuchita, kodi akukumbukira chiyani?
Kodi Yesu akudutsa chigawo chiti paulendo wake wobwerera ku Galileya?
Funso lowonjezera:
Ŵerengani Yohane 2:13-25.
Poona mmene Yesu anakwiyira ndi anthu amene amasinthana ndalama m’kachisi, kodi kuchita zinthu zamalonda m’Nyumba ya Ufumu tiyenera kukuona motani? (Yoh. 2:15, 16; 1 Akor. 10:24, 31-33)
Nkhani 90
Ndi Mkazi pa Chitsime
N’chifukwa chiyani Yesu waima pachitsime m’Samariya, ndipo akunena chiyani kwa mkazi pamenepo?
N’chifukwa chiyani mkaziyo akudabwa, kodi Yesu akumuuza chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani akumuuza zimenezi?
Kodi mkaziyo akuganiza kuti Yesu akunena za madzi otani, koma kodi Yesu akutanthauza madzi otani?
N’chifukwa chiyani mkaziyo akudabwa poona zimene Yesu akudziŵa za iye, ndipo kodi anazidziŵa bwanji?
Kodi tingaphunzire maphunziro otani pa nkhani ya mkazi pachitsime?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Yohane 4:5-43.
Potsatira chitsanzo cha Yesu, kodi anthu a fuko lina kapena opeza mosiyana ndi ife tiyenera kuwaona bwanji? (Yoh. 4:9; 1 Akor. 9:22; 1 Tim. 2:3, 4; Tito 2:11)
Kodi munthu amene wakhala wophunzira wa Yesu amapindula bwanji mwauzimu? (Yoh. 4:14; Yes. 58:11; 2 Akor. 4:16)
Kodi tingasonyeze bwanji kuyamikira ngati mmene anachitira mkazi wachisamariya uja, amene anali wofunitsitsa kuuza ena zimene anaphunzira? (Yoh. 4:7, 28; Mat. 6:33; Luka 10:40-42)
Nkhani 91
Yesu Aphunzitsa pa Phiri
M’chithunzichi, kodi n’kuti kumene Yesu ali pophunzitsa, ndipo amene akhala pafupi kwambiri nayewo ndi ndani?
Kodi mayina a atumwi 12 ndi ndani?
Kodi Ufumu umene Yesu akulalikira n’chiyani?
Kodi Yesu akuphunzitsa anthuwo kupempherera chiyani?
Kodi Yesu akunena kuti anthu ayenera kuchitirana zinthu motani?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Mateyu 5:1-12.
Kodi tingasonyeze kuti tikuzindikira kusoŵa kwathu kwauzimu m’njira zotani? (Mat. 5:3; Aroma 10:13-15; 1 Tim. 4:13, 15, 16)
Ŵerengani Mateyu 5:21-26
Kodi Mateyu 5:23, 24 akugogomezera bwanji kuti ubwenzi wathu ndi abale athu umakhudza ubwenzi wathu ndi Yehova? (Mat. 6:14, 15; Sal. 133:1; Akol. 3:13; 1 Yoh. 4:20)
Ŵerengani Mateyu 6:1-8.
Kodi ndi njira zina ziti zodziona kuti munthuwe ndiwe wolungama zimene Akristu ayenera kupeŵa? (Luka 18:11, 12; 1 Akor. 4:6, 7; 2 Akor. 9:7)
Ŵerengani Mateyu 6:25-34.
Kodi Yesu anaphunzitsa chiyani za kufunika kokhulupirira kuti Yehova adzatipatsa zosoŵeka pamoyo wathu? (Eks. 16:4; Sal. 37:25; Afil. 4:6)
Ŵerengani Mateyu 7:1-11.
Kodi fanizo lomveka bwino kwambiri lopezeka pa Mateyu 7:5 limatiphunzitsa chiyani? (Miy. 26:12; Aroma 2:1; 14:10; Yak. 4:11, 12)
Nkhani 92
Yesu Aukitsa Akufa
Kodi atate wa mtsikana ali pachithunziyu ndi ndani, ndipo n’chifukwa chiyani iye ndi mkazi wake akuda nkhaŵa kwambiri?
Kodi Yairo akuchita chiyani atapeza Yesu?
Kodi n’chiyani chikuchitika pamene Yesu akupita ku nyumba ya Yairo, ndipo kodi Yairo akulandira uthenga wotani ali panjira?
N’chifukwa chiyani anthu amene ali m’nyumba ya Yairo akumuseka Yesu?
Atatenga atumwi atatu ndi atate ndi amayi a buthulo kuloŵa nawo m’chipinda mwa buthulo, kodi Yesu akuchita chiyani?
Kodi ndani winanso amene Yesu wamuukitsa kwa akufa, ndipo kodi zimenezi zikusonyeza chiyani?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Luka 8:40-56.
Kodi Yesu anasonyeza bwanji chifundo ndiponso kum’ganizira mkazi amene anali ndi nthenda yakukha mwazi, ndipo kodi akulu achikristu masiku ano angaphunzirepo chiyani pamenepa? (Luka 8:43, 44, 47, 48; Lev. 15:25-27; Mat. 9:12, 13; Akol. 3:12-14)
Ŵerengani Luka 7:11-17.
Kodi anthu amene wokondedwa wawo anafa angalimbikitsidwe kwambiri bwanji ndi zimene Yesu anachita kwa mkazi wamasiye wa ku Nayini? (Luka 7:13; 2 Akor. 1:3, 4; Aheb. 4:15)
Ŵerengani Yohane 11:17-44.
Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti n’chinthu chachibadwa kulira wokondedwa wathu akamwalira? (Yoh. 11:33-36, 38; 2 Sam. 18:33; 19:1-4)
Nkhani 93
Yesu Adyetsa Khamu
Kodi ndi chinthu choopsa chotani chimene chachitikira Yohane Mbatizi, ndipo kodi zikupangitsa Yesu kumva bwanji?
Kodi Yesu akudyetsa bwanji khamu la anthu limene lamutsatira, ndipo chakudya chimene chatsala n’chochuluka bwanji?
N’chifukwa chiyani ophunzira akuopa usiku, ndipo n’chiyani chikuchitikira Petro?
Kodi Yesu akudyetsa bwanji anthu zikwi zochuluka kachiŵiri?
N’chifukwa chiyani zidzakhala zabwino kwambiri Yesu akamadzalamulira dziko lapansi monga Mfumu ya Mulungu?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Mateyu 14:1-32.
Nkhani imene ili pa Mateyu 14:23-32 ikutiphunzitsa chiyani za khalidwe la Petro?
Kodi Malemba amasonyeza bwanji kuti Petro anakhwima maganizo ndipo anasiya khalidwe lake lochita zinthu asanaganize kaye? (Mat. 14:27-30; Yoh. 18:10; 21:7; Mac. 2:14, 37-40; 1 Pet. 5:6, 10)
Ŵerengani Mateyu 15:29-38.
Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti analemekeza zinthu zochokera kwa Atate ake? (Mat. 15:37; Yoh. 6:12; Akol. 3:15)
Ŵerengani Yohane 6:1-21.
Kodi Akristu masiku ano angatsatire bwanji chitsanzo cha Yesu pankhani zokhudza boma? (Yoh. 6:15; Mat. 22:21; Aroma 12:2; 13:1-4)
Nkhani 94
Akonda Tiana
Kodi atumwi akukanganirana chiyani pobwerera ku ulendo wawo wautali?
N’chifukwa chiyani Yesu akuitana kamnyamata n’kukaimika pakati pa ophunzirawo?
Kodi atumwiwo ayenera kuphunzira kukhala ngati ana m’njira yotani?
Miyezi ingapo izi zitachitika, kodi Yesu akusonyeza bwanji kuti amakonda ana?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Mateyu 18:1-4.
N’chifukwa chiyani Yesu anagwiritsa ntchito mafanizo pophunzitsa? (Mat. 13:34, 36; Marko 4:33, 34)
Ŵerengani Mateyu 19:13-15.
Kodi tiyenera kutsanzira makhalidwe otani a ana aang’ono ngati tikufuna kudzasangalala ndi madalitso a Ufumu? (Sal. 25:9; 138:6; 1 Akor. 14:20)
Ŵerengani Marko 9:33-37.
Kodi Yesu anaphunzitsa ophunzira ake chiyani pa nkhani ya kufuna kukhala ndi maudindo apamwamba? (Marko 9:35; Mat. 20:25, 26; Agal. 6:3; Afil. 2:5-8)
Ŵerengani Marko 10:13-16.
Kodi Yesu anali wosavuta kumufikira motani, ndipo kodi akulu achikristu angaphunzire chiyani ku chitsanzo chake? (Marko 6:30-34; Afil. 2:1-4; 1 Tim. 4:12)
Nkhani 95
Kaphunzitsidwe ka Yesu
Kodi munthu wina akufunsa Yesu funso lotani, ndipo n’chifukwa chiyani akufunsa zimenezi?
Kodi Yesu nthaŵi zina amagwiritsa ntchito chiyani pophunzitsa, ndipo kodi taphunzira kale chiyani za Ayuda ndi Asamariya?
Mu nthano imene Yesu akukamba, kodi n’chiyani chikuchitikira Myuda pamene anali kuyenda mu msewu wopita ku Yeriko?
Kodi chikuchitika n’chiyani pamene wansembe wachiyuda ndi Mlevi akudutsa mumsewuwo?
Pachithunzipa, kodi ndani akuthandiza Myuda amene wavulalayo?
Yesu atatha kukamba nthanoyo, kodi akufunsa funso lotani, ndipo munthuyo akuyankha bwanji?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Luka 10:25-37.
Kodi Yesu anagwiritsa ntchito bwanji mafanizo kuti athetse tsankho limene omvetsera ake anali nalo? (Luka 10:36, 37; 18:9-14; Tito 1:9)
Nkhani 96
Yesu Achiritsa Odwala
Kodi Yesu akuchita chiyani pamene akuyendayenda m’dzikolo?
Patatha zaka zitatu kuchokera pamene anabatizidwa, kodi Yesu akuuza atumwi ake chiyani?
Kodi anthu ali pachithunziŵa ndi ndani, ndipo kodi Yesu anachitira mkaziyo chiyani?
N’chifukwa chiyani yankho limene Yesu akupereka kwa atsogoleri achipembedzo amene akumutsutsa likuwachititsa manyazi?
Yesu ndi atumwi ake ali pafupi ndi Yeriko, kodi Yesu akuchitira chiyani akhungu aŵiri opemphapempha?
N’chifukwa chiyani Yesu amachita zozizwitsa?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Mateyu 15:30, 31.
Kodi ndi mphamvu zodabwitsa zotani za Yehova zimene Yesu anasonyeza, ndipo kodi ziyenera kutichititsa kumva bwanji za zimene Yehova walonjeza m’dziko latsopano? (Sal. 37:29; Yes. 33:24)
Ŵerengani Luka 13:10-17.
Kodi mfundo yakuti Yesu anachita zina mwa zozizwitsa zake zikuluzikulu pa Sabata imasonyeza bwanji mpumulo umene adzabweretsere anthu pa nthaŵi ya Ulamuliro wake wa Zaka 1,000? (Luka 13:10-13; Sal. 46:9; Mat. 12:8; Akol. 2:16, 17; Chiv. 21:1-4)
Ŵerengani Mateyu 20:29-34.
Kodi nkhani imeneyi ikusonyeza bwanji kuti Yesu sanali wotanganidwa kwambiri moti n’kulephera kuthandiza anthu, ndipo tingaphunzirepo chiyani pamenepa? (Deut. 15:7; Yak. 2:15, 16; 1 Yoh. 3:17)
Nkhani 97
Yesu Adza Monga Mfumu
Yesu atafika ku kamudzi kapafupi ndi Yerusalemu, kodi akuuza ophunzira ake kuchita chiyani?
Pachithunzipa, kodi chikuchitika n’chiyani Yesu atayandikira mzinda wa Yerusalemu?
Kodi ana aang’ono akuchita chiyani ataona Yesu akuchiza anthu akhungu ndi opunduka?
Kodi Yesu akuuza ansembe okwiyawo chiyani?
Kodi tingakhale bwanji ngati ana amene akutamanda Yesu?
Kodi ophunzira akufuna kudziŵa chiyani?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Mateyu 21:1-17.
Kodi mmene Yesu analoŵera mu Yerusalemu monga Mfumu zinasiyana bwanji ndi mmene ankachitira olamulira achiroma akagonjetsa ena? (Mat. 21:4, 5; Zek. 9:9; Afil. 2:5-8; Akol. 2:15)
Kodi achinyamata angaphunzire chiyani kwa anyamata achiisrayeli amene ananena mawu a pa Salmo 118 pamene Yesu ankaloŵa m’kachisi? (Mat. 21:9, 15; Sal. 118:25, 26; 2 Tim. 3:15; 2 Pet. 3:18)
Ŵerengani Yohane 12:12-16.
Kodi makhwatha a kanjedza amene anthu omwe ankatamanda Yesu anagwiritsa ntchito amaimira chiyani? (Yoh. 12:13; Afil. 2:10; Chiv. 7:9, 10)
Nkhani 98
Pa Phiri la Azitona
Pachithunzipa, kodi Yesu ndi uti, ndipo ali nayewo ndani?
Kodi ansembe anayesera kumuchita chiyani Yesu m’kachisi, ndipo kodi Yesu ananena chiyani kwa iwo?
Kodi atumwi akumufunsa chiyani Yesu?
N’chifukwa chiyani Yesu akuuza atumwi ake zina mwa zinthu zimene zidzachitike padziko lapansi iye akamadzalamulira monga Mfumu kumwamba?
Kodi Yesu akuti chidzachitike n’chiyani asanathetse kuipa konse padziko lapansi?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Mateyu 23:1-39.
Ngakhale kuti Malemba amasonyeza kuti kugwiritsa ntchito mayina aulemu kungakhale koyenera, kodi mawu a Yesu amene ali pa Mateyu 23:8-11 amasonyeza chiyani ponena za kugwiritsa ntchito mayina okweza anthu ena mu mpingo wachikristu? (Mac. 26:25; Aroma 13:7; 1 Pet. 2:13, 14)
Kodi Afarisi anagwiritsa ntchito chiyani pofuna kulepheretsa anthu kuti asakhale Akristu, ndipo kodi atsogoleri achipembedzo masiku ano agwiritsa ntchito njira zofanana ndi zimenezo motani? (Mat. 23:13; Luka 11:52; Yoh. 9:22; 12:42; 1 Ates. 2:16)
Ŵerengani Mateyu 24:1-14.
Kodi lemba la Mateyu 24:13 likugogomezera motani kufunika kwa kupirira?
Kodi mawu akuti “kuchimaliziro” opezeka pa Mateyu 24:13 amatanthauzanji? (Mat. 16:27; Aroma 14:10-12; 2 Akor. 5:10)
Ŵerengani Marko 13:3-10.
Kodi ndi mawu ati opezeka pa Marko 13:10 amene amasonyeza kufunika kolalikira uthenga wabwino mwachangu, ndipo kodi mawu a Yesu ayenera kutikhudza motani? (Aroma 13:11, 12; 1 Akor. 7:29-31; 2 Tim. 4:2)
Nkhani 99
M’chipinda Chapamwamba
Monga momwe asonyezera pachithunzipa, n’chifukwa chiyani Yesu ndi atumwi ake 12 ali m’chipinda chachikulu chapamwamba?
Kodi mwamuna akuchokayo ndi ndani, ndipo akukachita chiyani?
Kodi Yesu akuyambitsa chakudya chapadera chotani atatha kudya chakudya cha Paskha?
Paskha ankakumbutsa Aisrayeli za chiyani, ndipo chakudya chapadera chimenechi chimakumbutsa otsatira a Yesu za chiyani?
Chakudya Chamadzulo cha Ambuye chitatha, Yesu akuuza otsatira ake chiyani, ndipo iwo akuchita chiyani?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Mateyu 26:14-30.
Kodi lemba la Mateyu 26:15 limasonyeza bwanji kuti zimene Yudasi anachita pomupereka Yesu zinali zochita kukonzekera?
Kodi mwazi wa Yesu wokhetsedwa umagwira ntchito ziŵiri ziti? (Mat. 26:27, 28; Yer. 31:31-33; Aef. 1:7; Aheb. 9:19, 20)
Ŵerengani Luka 22:1-39.
Kodi Satana analoŵa mwa Yudasi m’lingaliro lanji? (Luka 22:3; Yoh. 13:2; Mac. 1:24, 25)
Ŵerengani Yohane 13:1-20.
Malinga ndi zimene nkhani ya pa Yohane 13:2 imanena, kodi tingati Yudasi ndi amene analakwa pochita zimene anachitazo, ndipo kodi atumiki a Mulungu angaphunzirepo phunziro lotani pamenepa? (Gen. 4:7; 2 Akor. 2:11; Agal. 6:1; Yak. 1:13, 14)
Kodi ndi phunziro lamphamvu lotani limene Yesu anaphunzitsa mwa kuchita kanthu kenakake? (Yoh. 13:15; Mat. 23:11; 1 Pet. 2:21)
Ŵerengani Yohane 17:1-26.
Kodi Yesu anapemphera kuti otsatira ake “akhale mmodzi” m’lingaliro lotani? (Yoh. 17:11, 21-23; Aroma 13:8; 14:19; Akol. 3:14)
Nkhani 100
Yesu M’munda
Kodi Yesu ndi ophunzira ake akupita kuti atachoka m’chipinda chapamwamba, ndipo kodi akuwauza kuti achite chiyani?
Kodi Yesu akupeza chiyani atabwerera pamene pali atumwiwo, ndipo zimenezi zikuchitika kangati?
Ndani amene akuloŵa m’mundamo, ndipo Yudasi Isikariote akuchita chiyani, monga momwe asonyezera pachithunzipa?
N’chifukwa chiyani Yudasi akumpsopsona Yesu, ndipo Petro akuchita chiyani?
Kodi Yesu akunena chiyani kwa Petro, koma n’chifukwa chiyani Yesu sakupempha Mulungu kutumiza angelo?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Mateyu 26:36-56.
Kodi njira imene Yesu ankapatsira ophunzira ake malangizo ili chitsanzo chabwino kwambiri bwanji kwa akulu achikristu masiku ano? (Mat. 20:25-28; 26:40, 41; Agal. 5:17; Aef. 4:29, 31, 32)
Kodi Yesu ankaona bwanji kumenya munthu mnzako pogwiritsa ntchito zida zankhondo? (Mat. 26:52; Luka 6:27, 28; Yoh. 18:36)
Ŵerengani Luka 22:39-53.
Pamene mngelo anaonekera kwa Yesu m’munda wa Getsemane kudzamulimbikitsa, kodi zinatanthauza kuti chikhulupiriro cha Yesu chinali kuchepa? Fotokozani. (Luka 22:41-43; Yes. 49:8; Mat. 4:10, 11; Aheb. 5:7)
Ŵerengani Yohane 18:1-12.
Kodi Yesu anateteza motani ophunzira ake kwa anthu omutsutsa, ndipo tingaphunzire chiyani ku chitsanzo chimenechi? (Yoh. 10:11, 12; 18:1, 6-9; Aheb. 13:6; Yak. 2:25)
Nkhani 101
Yesu Akuphedwa
Kodi ndi ndani makamaka amene anachititsa kuti Yesu aphedwe?
Kodi atumwi akuchita chiyani pamene Yesu akutengedwa ndi atsogoleri achipembedzo?
N’chiyani chikuchitika kunyumba ya Kayafa, mkulu wa ansembe?
N’chifukwa chiyani Petro akuchoka n’kukalira?
Kodi akulu ansembe akufuula kuti chiyani Yesu atamubwezera kwa Pilato?
N’chiyani chikuchitikira Yesu Lachisanu masana, ndipo akulonjeza chiyani kwa mpandu amene wakhomeredwa pa mtengo pafupi naye?
Kodi Paradaiso amene Yesu anali kunena adzakhala kuti?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Mateyu 26:57-75.
Kodi anthu a m’bwalo lalikulu la Ayuda anasonyeza bwanji kuti mitima yawo inali yoipa? (Mat. 26:59, 67, 68)
Ŵerengani Mateyu 27:1-50.
N’chifukwa chiyani tinganene kuti chisoni chimene Yudasi anamva sichinali chenicheni? (Mat. 27:3, 4; Marko 3:29; 14:21; 2 Akor. 7:10, 11)
Ŵerengani Luka 22:54-71.
Kodi tingaphunzire chiyani pa kukana Yesu kwa Petro usiku umene Yesu anaperekedwa ndi kumangidwa? (Luka 22:60-62; Mat. 26:31-35; 1 Akor. 10:12)
Ŵerengani Luka 23:1-49.
Kodi Yesu anachita chiyani atamuchitira zinthu zopanda chilungamo, ndipo tingaphunzirepo chiyani pamenepa? (Luka 23:33, 34; Aroma 12:17-19; 1 Pet. 2:23)
Ŵerengani Yohane 18:12-40.
Ngakhale kuti Petro anafooka kwakanthaŵi chifukwa choopa anthu, anasintha n’kukhala mtumwi wochititsa chidwi kwambiri. Kodi mfundo imeneyi ikusonyeza chiyani? (Yoh. 18:25-27; 1 Akor. 4:2; 1 Pet. 3:14, 15; 5:8, 9)
Ŵerengani Yohane 19:1-30.
Kodi Yesu ankaona zinthu zakuthupi moyenera m’njira yotani? (Yoh. 2:1, 2, 9, 10; 19:23, 24; Mat. 6:31, 32; 8:20)
Kodi mawu amene Yesu ananena atatsala pang’ono kufa anasonyeza motani kuti wapambana poikira kumbuyo ulamuliro wa Yehova? (Yoh. 16:33; 19:30; 2 Pet. 3:14; 1 Yoh. 5:4)
Nkhani 102
Yesu Ali Moyo
Kodi mkazi ali m’chithunziyu ndi ndani, amuna aŵiriwo ndi ndani, ndipo ali kuti?
N’chifukwa chiyani Pilato akuuza ansembe kuti atumize asilikali ankhondo kukalondera manda a Yesu?
Kodi mngelo akuchita chiyani mmaŵa kwambiri pa tsiku lachitatu Yesu atafa, koma kodi ansembe akuchita chiyani?
N’chifukwa chiyani akazi ena ali odabwa atapita ku manda a Yesu?
N’chifukwa chiyani Petro ndi Yohane akuthamangira ku manda a Yesu, ndipo akupeza chiyani?
N’chiyani chinachitikira thupi la Yesu, koma kodi akuchita chiyani kuti asonyeze ophunzirawo kuti ali moyo?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Mateyu 27:62-66 ndi 28:1-15.
Panthaŵi ya kuuka kwa Yesu, kodi akulu ansembe, Afarisi, ndi akulu anachimwira motani mzimu woyera? (Mat. 12:24, 31, 32; 28:11-15)
Ŵerengani Luka 24:1-12.
Kodi nkhani ya kuuka kwa Yesu imasonyeza bwanji kuti Yehova amaona akazi monga mboni zodalirika? (Luka 24:4, 9, 10; Mat. 28:1-7)
Ŵerengani Yohane 20:1-12.
Kodi lemba la Yohane 20:8, 9 likutithandiza bwanji kuona kufunika koleza mtima ngati sitikumvetsetsa bwino kukwaniritsidwa kwa ulosi winawake wa m’Baibulo? (Miy. 4:18; Mat. 17:22, 23; Luka 24:5-8; Yoh. 16:12)
Nkhani 103
Akulowa M’chipinda Chotseka
Kodi Mariya akunena chiyani kwa mwamuna amene akuganiza kuti ndi wolima m’munda, koma n’chiyani chikumuchititsa kuzindikira kuti mwamunayo ndi Yesu?
Kodi n’chiyani chikuchitikira ophunzira aŵiri amene akuyenda kupita ku mudzi wa Emau?
Kodi ndi chinthu chodabwitsa chotani chimene chikuchitika ophunzira aŵiri atauza atumwi kuti anaona Yesu?
Kodi Yesu waonekera kangati kwa otsatira ake?
Kodi Tomasi akunena chiyani atamva kuti ophunzirawo aona Ambuye, koma kodi n’chiyani chikuchitika patapita masiku asanu ndi atatu?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Yohane 20:11-29.
Kodi pa Yohane 20:23 Yesu anali kunena kuti anthu ali ndi mphamvu yotha kukhululukira machimo? Fotokozani. (Sal. 49:2, 7; Yes. 55:7; 1 Tim. 2:5, 6; 1 Yoh. 2:1, 2)
Ŵerengani Luka 24:13-43.
Kodi tingakonze bwanji mtima wathu kuti uzichitapo kanthu ukamva choonadi cha m’Baibulo? (Luka 24:32, 33; Ezara 7:10; Mat. 5:3; Mac. 16:14; Aheb. 5:11-14)
Nkhani 104
Yesu Abwerera Kumwamba
Panthaŵi ina, kodi ndi ophunzira angati amene akuona Yesu, ndipo akulankhula nawo za chiyani?
Kodi Ufumu wa Mulungu n’chiyani, ndipo kodi moyo udzakhala wotani Yesu akamadzalamulira monga Mfumu kwa zaka 1,000?
Kodi Yesu wakhala akudzisonyeza kwa ophunzira ake kwa masiku angati, koma tsopano ndi nthaŵi yoti achite chiyani?
Atangotsala pang’ono kuti asiyane ndi ophunzira ake, kodi Yesu akuwauza kuti achite chiyani?
Kodi n’chiyani chikuchitika m’chithunzichi, ndipo kodi n’chiyani chikuphimba Yesu kuti asaoneke?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani 1 Akorinto 15:3-8.
N’chifukwa chiyani mtumwi Paulo anatha kulankhula motsimikiza kwambiri za kuuka kwa Yesu, ndipo Akristu masiku ano angalankhule motsimikiza za chiyani? (1 Akor. 15:4, 7, 8; Yes. 2:2, 3; Mat. 24:14; 2 Tim. 3:1-5)
Ŵerengani Machitidwe 1:1-11.
Kodi ntchito yolalikira inafalikira mpaka kuti, monga momwe zinanenedwera pa Machitidwe 1:8? (Mac. 6:7; 9:31; 11:19-21; Akol. 1:23)
Nkhani 105
Akuyembekezera M’Yerusalemu
Monga momwe chithunzichi chikusonyezera, n’chiyani chikuchitikira otsatira a Yesu amene akhala akuyembekezera m’Yerusalemu?
Kodi alendo amene abwera ku Yerusalemu akuona zodabwitsa zotani?
Kodi Petro akulongosolera anthuwo chiyani?
Kodi anthuwo akumva bwanji atamvetsera Petro, ndipo iye akuwauza kuti achite chiyani?
Kodi ndi anthu angati amene anabatizidwa tsiku limenelo pa Pentekoste wa m’chaka cha 33 Kristu Atabwera?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Machitidwe 2:1-47.
Kodi mawu a Petro opezeka pa Machitidwe 2:23, 36 anasonyeza bwanji kuti mtundu wonse wa Ayuda unali ndi mlandu wakupha Yesu? (1 Ates. 2:14, 15)
Kodi Petro anatipatsa chitsanzo chabwino chotani chokambirana za m’Malemba ndi anthu? (Mac. 2:16, 17, 29, 31, 36, 39; Akol. 4:6)
Kodi Petro anagwiritsa ntchito bwanji “mafungulo a Ufumu wa Kumwamba” oyamba amene Yesu analonjeza kuti adzamupatsa? (Mac. 2:14, 22-24, 37, 38; Mat. 16:19)
Nkhani 106
Amasulidwa M’ndende
Kodi n’chiyani chikuchitikira Petro ndi Yohane masana ena pamene akuloŵa m’kachisi?
Kodi Petro akunena chiyani kwa munthu wopunduka, ndipo Petro akumupatsa chiyani chimene chili chamtengo wapatali kuposa ndalama?
N’chifukwa chiyani atsogoleri a chipembedzo akwiya, ndipo akuchita chiyani kwa Petro ndi Yohane?
Kodi Petro akunena chiyani kwa atsogoleri a chipembedzowo, ndipo atumwiwo akuchenjezedwa chiyani?
N’chifukwa chiyani atsogoleri a chipembedzowo akuchita nsanje, koma n’chiyani chikuchitika atumwiwo ataikidwa m’ndende kachiŵiri?
Kodi atumwiwo akuyankha bwanji atawabweretsa ku holo ya Sanihedirini?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Machitidwe 3:1-10.
Ngakhale kuti masiku ano tilibe mphamvu yochita zozizwitsa, kodi mawu a Petro olembedwa pa Machitidwe 3:6 amatithandiza bwanji kuzindikira kufunika kwa uthenga wa Ufumu? (Yoh. 17:3; 2 Akor. 5:18-20; Afil. 3:8)
Ŵerengani Machitidwe 4:1-31.
Tikakumana ndi otsutsa mu utumiki, kodi tiyenera kutsanzira motani abale athu achikristu a m’zaka 100 zoyambirira? (Mac. 4:29, 31; Aef. 6:18-20; 1 Ates. 2:2)
Ŵerengani Machitidwe 5:17-42.
Kodi anthu ena amene si Mboni, akale komanso amasiku ano, asonyeza bwanji kuti ntchito yathu yolalikira amaimvetsa? (Mac. 5:34-39)
Nkhani 107
Stefano Aponyedwa Miyala
Kodi Stefano ndi ndani, ndipo Mulungu wakhala akumuthandiza kuchita chiyani?
Kodi Stefano akunena chiyani chimene chikukwiyitsa kwambiri atsogoleri a chipembedzo?
Amunawo atamukwakwazira Stefano kunja kwa mzinda, kodi akumuchita chiyani?
Pachithunzipa, kodi mnyamata amene waima pafupi ndi zovalayo ndi ndani?
Asanafe, kodi Stefano akupemphera kuti chiyani kwa Yehova?
Potsanzira Stefano, kodi tiyenera kuchita chiyani munthu wina akatichitira chinthu choipa?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Machitidwe 6:8-15.
Kodi ndi zinthu zachinyengo zotani zimene atsogoleri a chipembedzo ayesera kuchita kuti aletse ntchito yolalikira ya Mboni za Yehova? (Mac. 6:9, 11, 13)
Ŵerengani Machitidwe 7:1-60.
Kodi n’chiyani chinathandiza Stefano kuti akhale wogwira mtima poikira kumbuyo uthenga wabwino pamaso pa Sanihedirini, ndipo tingaphunzire chiyani pa chitsanzo chake? (Mac. 7:51-53; Aroma 15:4; 2 Tim. 3:14-17; 1 Pet. 3:15)
Kodi otsutsa ntchito yathu tiyenera kuwaona motani? (Mac. 7:58-60; Mat. 5:44; Luka 23:33, 34)
Nkhani 108
Pa Njira ya ku Damasiko
Kodi Saulo akuchita chiyani Stefano ataphedwa?
Saulo ali paulendo wopita ku Damasiko, kodi ndi chinthu chozizwitsa chotani chimene chikuchitika?
Kodi Yesu akuuza Saulo kuchita chiyani?
Kodi Yesu akupatsa Hananiya malangizo otani, ndipo kodi chikuchitika n’chiyani kuti Saulo ayambenso kuona?
Kodi Saulo akuyamba kutchedwa dzina loti ndani, ndipo akugwiritsidwa ntchito motani?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Machitidwe 8:1-4.
Kodi chizunzo chachikulu chimene mpingo wachikristu wongoyamba kumene unakumana nacho chinachititsa bwanji kuti chikhulupiriro cha Chikristu chifalikire, ndipo ndi zinthu zotani zofanana ndi zimenezi zimene zachitika masiku athu ano? (Mac. 8:4; Yes. 54:17)
Ŵerengani Machitidwe 9:1-20.
Kodi Yesu ananena kuti anafuna kuti Saulo agwire ntchito zitatu ziti? (Mac. 9:15; 13:5; 26:1; 27:24; Aroma 11:13)
Ŵerengani Machitidwe 22:6-16.
Kodi tingakhale bwanji ngati Hananiya, ndipo kukhala wotero n’kofunika chifukwa chiyani? (Mac. 22:12; 1 Tim. 3:7; 1 Pet. 1:14-16; 2:12)
Ŵerengani Machitidwe 26:8-20.
Kodi kutembenukira ku Chikristu kwa Paulo kumalimbikitsa bwanji anthu amene ali pabanja ndi munthu wosakhulupirira masiku ano? (Mac. 26:11; 1 Tim. 1:14-16; 2 Tim. 4:2; 1 Pet. 3:1-3)
Nkhani 109
Petro Achezera Korneliyo
Kodi munthu wagwadayu m’chithunzichi ndi ndani?
Kodi mngelo akuuza Korneliyo chiyani?
Kodi Mulungu akuchititsa Petro kuona chiyani ali pa tsindwi la nyumba ya Simoni ku Yopa?
N’chifukwa chiyani Petro akuuza Korneliyo kuti asamugwadire ndi kumulambira?
N’chifukwa chiyani ophunzira achiyuda amene ali ndi Petro akudabwa?
Kodi tiyenera kuphunzira phunziro lofunika lotani pa zimene zinachitika Petro atakachezera Korneliyo?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Machitidwe 10:1-48.
Kodi mawu a Petro opezeka pa Machitidwe 10:42 akusonyeza chiyani chokhudza ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu? (Mat. 28:19; Marko 13:10; Mac. 1:8)
Ŵerengani Machitidwe 11:1-18.
Kodi Petro anasonyeza mtima wotani atazindikira cholinga cha Yehova chokhudza anthu Akunja, ndipo tingatsanzire bwanji chitsanzo chake? (Mac. 11:17, 18; 2 Akor. 10:5; Aef. 5:17)
Nkhani 110
Timoteyo—Wothandiza Paulo
Kodi mnyamata ali pachithunziyu ndi ndani, amakhala kuti, ndipo amayi ake ndi agogo ake mayina awo ndi ndani?
Kodi Timoteo akunena chiyani Paulo atamufunsa ngati akufuna kutsagana ndi Sila ndi Paulo pokalalikira kwa anthu akutali?
Kodi n’kuti kumene otsatira a Yesu anayamba kutchedwa kuti Akristu?
Kodi Paulo, Sila, ndi Timoteo akupita ku mizinda ina iti atachoka ku Antiokeya?
Kodi Timoteo akuthandiza bwanji Paulo, ndipo ndi funso lotani limene achinyamata ayenera kudzifunsa masiku ano?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Machitidwe 9:19-30.
Kodi mtumwi Paulo anachita bwanji zinthu mwanzeru atakumana ndi otsutsa uthenga wabwino? (Mac. 9:22-25, 29, 30; Mat. 10:16)
Ŵerengani Machitidwe 11:19-26.
Kodi nkhani yolembedwa pa Machitidwe 11:19-21, 26 imasonyeza bwanji kuti mzimu wa Yehova ukutsogolera ntchito yolalikira?
Ŵerengani Machitidwe 13:13-16, 42-52.
Kodi lemba la Machitidwe 13:51, 52 limasonyeza bwanji kuti ophunzira sanalole otsutsa kuwafooketsa? (Mat. 10:14; Mac. 18:6; 1 Pet. 4:14)
Ŵerengani Machitidwe 14:1-6, 19-28.
Kodi mawu akuti “anaikiza iwo kwa Ambuye” amatithandiza bwanji kuti tisakhale ndi nkhaŵa iliyonse pamene tikuthandiza atsopano? (Mac. 14:21-23; 20:32; Yoh. 6:44)
Ŵerengani Machitidwe 16:1-5.
Kodi kufunitsitsa kwa Timoteo kuti adulidwe kukusonyeza bwanji kufunika kochita “zonse chifukwa cha Uthenga Wabwino”? (Mac. 16:3; 1 Akor. 9:23; 1 Ates. 2:8)
Ŵerengani Machitidwe 18:1-11, 18-22.
Kodi lemba la Machitidwe 18:9, 10 limasonyeza bwanji kuti Yesu akutithandiza potsogolera ntchito yolalikira, ndipo zimenezi zimatilimbikitsa bwanji masiku ano? (Mat. 28:20)
Nkhani 111
Mnyamata Amene Anagona
Pachithunzipa, kodi mnyamata amene wagona pansiyo ndi ndani, ndipo n’chiyani chinamuchitikira?
Kodi Paulo akuchita chiyani ataona kuti mnyamatayo wafa?
Kodi Paulo, Timoteo, ndi anthu amene akuyenda nawo akupita kuti, ndipo n’chiyani chikuchitika ataima ku Mileto?
Kodi mneneri Agabu akuchenjeza Paulo za chiyani, ndipo kodi zinachitika bwanji ndendende monga mmene ananenera mneneriyo?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Machitidwe 20:7-38.
Kodi tingapitirize ‘kukhala opanda kanthu ndi mwazi wa anthu onse’ motani malinga ndi mawu a Paulo olembedwa pa Machitidwe 20:26, 27? (Ezek. 33:8; Mac. 18:6, 7)
N’chifukwa chiyani akulu ayenera ‘kugwira mawu okhulupirika’ pophunzitsa? (Mac. 20:17, 29, 30; Tito 1:7-9; 2 Tim. 1:13)
Ŵerengani Machitidwe 26:24-32.
Kodi Paulo anagwiritsira ntchito bwanji kukhala kwake nzika yachiroma pokwaniritsa ntchito yolalikira imene anapatsidwa ndi Yesu? (Mac. 9:15; 16:37, 38; 25:11, 12; 26:32; Luka 21:12, 13)
Nkhani 112
Chombo Chinasweka pa Chisi
Kodi n’chiyani chikuchitikira bwato limene muli Paulo pamene likudutsa pafupi ndi chisi cha Krete?
Kodi Paulo akuwauza chiyani anthu amene ali m’bwatolo?
Kodi chikuchitika n’chiyani kuti bwatolo lisweke?
Kodi mkulu wa nkhondo woyang’anira akupereka malangizo otani, ndipo ndi anthu angati amene akufika bwino lomwe ku gombe?
Kodi dzina la chisi chimene afikako n’chiyani, ndipo n’chiyani chikuchitikira Paulo patagwa bata?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Machitidwe 27:1-44.
Kodi chikhulupiriro chathu mu nkhani za m’Baibulo chimalimbitsidwa motani tikaŵerenga nkhani ya ulendo wa Paulo wopita ku Roma? (Mac. 27:16-19, 27-32; Luka 1:3; 2 Tim. 3:16, 17)
Ŵerengani Machitidwe 28:1-14.
Anthu osapembedza Mulungu a ku Melita anafunitsitsa kuchitira Paulo ndi anzake amene bwato lawo linasweka zinthu “zokoma zosachitika pena ponsepo.” Choncho, kodi Akristu ayenera kufunitsitsa kusonyeza chiyani ndipo makamaka m’njira yotani? (Mac. 28:1, 2; Aheb. 13:1, 2; 1 Pet. 4:9)
Nkhani 113
Paulo M’Roma
Kodi Paulo akulalikira kwa ndani ali m’kaidi m’Roma?
M’chithunzichi, kodi mlendo ali pa thebuloyo ndi ndani, ndipo akuchitira Paulo chiyani?
Kodi Epafrodito ndi ndani, ndipo akutenga chiyani pobwerera ku Filipi?
N’chifukwa chiyani Paulo akulembera kalata mnzake wa pamtima, Filemoni?
Kodi Paulo atatulutsidwa m’ndende akuchita chiyani, ndipo n’chiyani chikumuchitikira kenako?
Kodi Yehova akugwiritsa ntchito ndani kulemba mabuku omalizira a m’Baibulo, ndipo kodi buku la Chivumbulutso limanena za chiyani?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Machitidwe 28:16-31 ndi Afilipi 1:13.
Kodi Paulo anagwiritsa ntchito nthaŵi yake motani ali m’ndende ku Roma, ndipo kodi chikhulupiriro chake chosasunthika chinakhudza bwanji mpingo wachikristu? (Mac. 28:23, 30; Afil. 1:14)
Ŵerengani Afilipi 2:19-30.
Kodi Paulo ananena mawu otani oyamikira Timoteo ndi Epafrodito, ndipo kodi tingatsatire motani chitsanzo cha Paulo? (Afil. 2:20, 22, 25, 29, 30; 1 Akor. 16:18; 1 Ates. 5:12, 13)
Ŵerengani Filemoni 1-25.
Kodi Paulo analimbikitsa Filemoni kuchita zinthu zoyenera chifukwa cha chiyani, ndipo zimenezi zingathandize akulu masiku ano motani? (Filem. 9; 2 Akor. 8:8; Agal. 5:13)
Kodi mawu a Paulo opezeka pa Filemoni 13, 14 amasonyeza bwanji kuti ankalemekeza chikumbumtima cha ena mu mpingo? (1 Akor. 8:7, 13; 10:31-33)
Ŵerengani 2 Timoteo 4:7-9.
Mofanana ndi mtumwi Paulo, kodi tingakhale bwanji ndi chikhulupiriro kuti Yehova adzatipatsa mphoto ngati tikhala okhulupirika mpaka mapeto? (Mat. 24:13; Aheb. 6:10)
Nkhani 114
Mapeto a Kuipa Konse
N’chifukwa chiyani Baibulo limanena za akavalo ali kumwamba?
Kodi dzina la nkhondo imene Mulungu adzamenye ndi anthu oipa padziko lapansi ndi chiyani, ndipo cholinga cha nkhondo imeneyi n’chiyani?
Kuchokera pachithunzipa, kodi Amene adzatsogolere pomenya nkhondoyo ndi ndani, n’chifukwa chiyani wavala chisoti chachifumu, ndipo kodi lupanga lake likutanthauza chiyani?
Tikakumbukira Nkhani 10, 15, ndi 33, n’chifukwa chiyani sitiyenera kudabwa kuti Mulungu adzawononga anthu oipa?
Kodi Nkhani 36 ndi 76 zikutisonyeza bwanji kuti Mulungu adzawononga anthu oipa ngakhale azinena kuti amalambira iyeyo?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Chivumbulutso 19:11-16.
Kodi Malemba amasonyeza motani moonekeratu kuti Yesu Kristu ndi amene wakwera kavalo woyera? (Chiv. 1:5; 3:14; 19:11; Yes. 11:4)
Kodi mwazi wowazidwa pa chovala chakunja cha Yesu ukutsimikira bwanji kuti Yesu adzapambana mosakayikitsa ndiponso kotheratu? (Chiv. 14:18-20; 19:13)
Kodi ndi ndani mwachionekere amene ali nawo m’gulu lankhondo limene likutsatira Yesu pa kavalo wake woyera? (Chiv. 12:7; 19:14; Mat. 25:31, 32)
Nkhani 115
Paradaiso Watsopano pa Dziko
Kodi Baibulo limasonyeza kuti tidzakhala ndi moyo wotani m’Paradaiso wa padziko lapansi?
Kodi m’Baibulo muli lonjezo lotani kwa anthu amene adzakhale m’Paradaiso?
Kodi ndi liti pamene Yesu adzabweretse kusintha kodabwitsaku?
Yesu ali padziko lapansi, kodi anachita chiyani posonyeza zimene adzachite monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu?
Kodi Yesu ndi ena amene adzalamulire naye kumwamba adzaonetsetsa chiyani akamadzalamulira pa dziko lapansi ali kumwamba?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Chivumbulutso 5:9, 10.
N’chifukwa chiyani tingakhale ndi chikhulupiriro kuti amene adzalamulire dziko lapansi mu Ulamuliro wa Zaka 1,000 adzakhala mafumu ndi ansembe achifundo? (Aef. 4:20-24; 1 Pet. 1:7; 3:8; 5:6-10)
Ŵerengani Chivumbulutso 14:1-3.
Kodi kulembedwa kwa dzina la Atate ndi dzina la Mwanawankhosa pa zipumi za anthu 144,000 kukutanthauza chiyani? (1 Akor. 3:23; 2 Tim. 2:19; Chiv. 3:12)
Nkhani 116
M’mene Tingakhalire Kosatha
Kodi tiyenera kudziŵa chiyani kuti tikhale ndi moyo kosatha?
Kodi tingaphunzire bwanji za Yehova Mulungu ndi Yesu, monga momwe buthuli ndi mabwenzi ake akuchitira pachithunzipa?
Kodi mukuona buku linanso liti pachithunzipa, ndipo n’chifukwa chiyani tiyenera kuliŵerenga nthaŵi zonse?
Kuwonjezera pa kuphunzira za Yehova ndi Yesu, kodi n’chiyaninso chimene tiyenera kuchita kuti tipeze moyo wosatha?
Kodi tikuphunzira chiyani mu Nkhani 69?
Kodi chitsanzo chabwino cha Samueli wachinyamata mu Nkhani 55 chikusonyeza chiyani?
Kodi tingatsatire bwanji chitsanzo cha Yesu Kristu, ndipo ngati titero, tidzatha kuchita chiyani m’tsogolo?
Mafunso owonjezera:
Ŵerengani Yohane 17:3.
Kodi Malemba amasonyeza bwanji kuti kudziŵa za Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu kumatanthauza zambiri osati kungoloweza mfundo chabe? (Mat. 7:21; Yak. 2:18-20; 1 Yoh. 2:17)
Ŵerengani Salmo 145:1-21.
Kodi zifukwa zina n’ziti mwa zifukwa zambiri zimene tili nazo zolemekezera Yehova? (Sal. 145:8-11; Chiv. 4:11)
Kodi Yehova ‘amachitira chokoma onse’ motani, ndipo zimenezi ziyenera kutithandiza bwanji kuyandikirana naye kwambiri? (Sal. 145:9; Mat. 5:43-45)
Ngati timamukondadi Yehova, kodi tidzafuna kuchita chiyani? (Sal. 119:171, 172, 175; 145:11, 12, 21)