Nehemiya
3 Ndiyeno Eliyasibu+ mkulu wa ansembe ndi abale ake, ansembe, anayamba kumanga Geti la Nkhosa+ ndipo analiyeretsa+ nʼkuika zitseko zake. Anayeretsa chigawo chonse mpaka ku Nsanja ya Meya+ nʼkukafika ku Nsanja ya Hananeli.+ 2 Amuna a ku Yeriko+ anamanga kuyambira pamene Eliyasibu ndi abale ake analekezera. Ndipo Zakuri mwana wa Imiri, anapitiriza kuyambira pamene amuna a ku Yeriko analekezera.
3 Ana a Haseneya anamanga Geti la Nsomba.+ Iwo analipangira felemu lamatabwa+ nʼkuika zitseko, anamphatika ndi mipiringidzo. 4 Meremoti+ mwana wa Uliya, mwana wa Hakozi, anakonza mpandawo kuchokera pamene ana a Haseneya analekezera. Mesulamu+ mwana wa Berekiya, mwana wa Mesezabele, anapitiriza kuchokera pamene Meremoti analekezera. Ndipo Zadoki mwana wa Baana, anapitiriza kuchokera pamene Mesulamu analekezera. 5 Atekowa+ anapitiriza kuchokera pamene Zadoki analekezera. Koma anthu otchuka pakati pa Atekowa sanadzichepetse nʼkugwira nawo ntchito ya atsogoleri awo.
6 Yoyada mwana wa Paseya, komanso Mesulamu mwana wa Besodeya, anakonza Geti la Mzinda Wakale.+ Iwo analipangira felemu lamatabwa nʼkuika zitseko, anamphatika* ndi mipiringidzo. 7 Kenako Melatiya wa ku Gibiyoni+ ndi Yadoni wa ku Meronoti anapitiriza kuchokera pamene Yoyada ndi Mesulamu analekezera. Amenewa anali amuna a ku Gibiyoni ndi Mizipa+ amene anali pansi pa ulamuliro wa bwanamkubwa wakutsidya la Mtsinje.*+ 8 Kenako Uziyeli mwana wa Harihaya, mmodzi wa osula golide, anakonza mpandawo kuchokera pamene analekezera. Hananiya mmodzi wa opanga mafuta onunkhira, anapitiriza kuchokera pamene Uziyeli analekezera. Iwo anayala miyala mu Yerusalemu mpaka kukafika ku Khoma Lalikulu.+ 9 Refaya mwana wa Hura, kalonga wa hafu ya chigawo cha Yerusalemu, anapitiriza kuchokera pamene Hananiya analekezera. 10 Yedaya mwana wa Harumafi anakonza mpandawo kutsogolo kwa nyumba yake kuchokera pamene Refaya analekezera. Kenako Hatusi mwana wa Hasabineya anapitiriza kuchokera pamene Yedaya analekezera.
11 Malikiya mwana wa Harimu+ komanso Hasubu mwana wa Pahati-mowabu,+ anakonza gawo lina la mpandawo ndi Nsanja ya Mauvuni.+ 12 Kenako Salumu mwana wa Halohesi, kalonga wa hafu ya chigawo cha Yerusalemu, anapitiriza kukonza mpandawo limodzi ndi ana ake aakazi kuchokera pamene enawo anasiyira.
13 Hanuni ndi anthu a ku Zanowa+ anakonza Geti la Kuchigwa.+ Iwo analikonza nʼkuika zitseko, anamphatika ndi mipiringidzo. Anakonzanso mpandawo mikono 1,000* mpaka kukafika ku Geti la Milu ya Phulusa.+ 14 Malikiya mwana wa Rekabu, kalonga wa chigawo cha Beti-hakeremu,+ anakonza Geti la Milu ya Phulusa. Analikonza nʼkuika zitseko, anamphatika ndi mipiringidzo.
15 Saluni mwana wa Kolihoze, kalonga wa chigawo cha Mizipa,+ anakonza Geti la Kukasupe+ nʼkukhoma denga lake. Anaikanso zitseko, anamphatika ndi mipiringidzo. Anamanganso mpanda wa Dziwe+ la Ngalande kukafika ku Munda wa Mfumu+ ndi ku Masitepe+ ochokera mu Mzinda wa Davide.+
16 Nehemiya mwana wa Azibuki, kalonga wa hafu ya chigawo cha Beti-zuri,+ anapitiriza kuchokera pamene Saluni analekezera. Anakafika patsogolo pa Manda Achifumu a Davide+ mpaka kudziwe+ lochita kukumba komanso ku Nyumba ya Anthu Amphamvu.
17 Alevi, moyangʼaniridwa ndi Rehumu mwana wa Bani, anakonza mpandawo kuchokera pamene Nehemiya analekezera. Hasabiya, kalonga wa hafu ya chigawo cha Keila,+ anakonza mpandawo mʼchigawo chake kuchokera pamene Alevi analekezera. 18 Kuchokera pamenepo, abale awo anakonza mpandawo moyangʼaniridwa ndi Bavai mwana wa Henadadi, kalonga wa hafu ya chigawo cha Keila.
19 Ezeri mwana wa Yesuwa,+ kalonga wa Mizipa, anakonza gawo lina la mpandawo pafupi ndi chitunda chimene anthu ankadutsa popita Kosungira Zida pamene panali khoma lothandizira kuti mpanda usagwe.+
20 Baruki mwana wa Zabai,+ anagwira ntchito mwachangu kwambiri moti anakonza gawo lina la mpandawo, kuchokera pamene panali khoma lothandizira kuti mpanda usagwe kukafika pageti la nyumba ya Eliyasibu+ mkulu wa ansembe.
21 Meremoti+ mwana wa Uliya, mwana wa Hakozi, anakonza gawo lina la mpandawo kuchokera pageti la nyumba ya Eliyasibu mpaka pamene nyumbayo inathera.
22 Ansembe, amuna amʼchigawo cha Yorodano*+ anakonza mpandawo kuchokera pamene Meremoti analekezera. 23 Benjamini ndi Hasubu anakonza mpandawo kutsogolo kwa nyumba yawo kuchokera pamene ansembe analekezera. Azariya mwana wa Maaseya, mwana wa Ananiya, anakonza mpandawo pafupi ndi nyumba yake kuchokera pamene Benjamini ndi Hasubu analekezera. 24 Binui mwana wa Henadadi anakonza gawo lina la mpandawo kuchokera panyumba ya Azariya kukafika pamene panali khoma lothandizira kuti mpanda usagwe+ mpaka pakona ya mpanda wa mzindawo.
25 Palali mwana wa Uzai, anakonza mpandawo kutsogolo kwa khoma lothandizira kuti mpanda usagwe. Anakonzanso nsanja yochokera pa Nyumba ya Mfumu+ imene ili kumtunda mʼBwalo la Alonda.+ Pedaya mwana wa Parosi, anapitiriza kuchokera pamene Palali+ analekezera.
26 Atumiki apakachisi*+ omwe ankakhala ku Ofeli+ anakonza mpandawo mpaka patsogolo pa Geti la Kumadzi,+ kumʼmawa. Iwo anakonzanso nsanja yomwe inatulukira kunja kwa mpanda.
27 Atekowa+ anakonza chigawo chinanso cha mpandawo, kuchokera patsogolo pa nsanja yomwe inatulukira kunja kwa mpanda kukafika kumpanda wa Ofeli.
28 Ansembe anakonza mpandawo kuyambira kumtunda kwa Geti ya Hatchi,+ ndipo aliyense ankakonza patsogolo pa nyumba yake.
29 Zadoki+ mwana wa Imeri anakonza mpandawo kutsogolo kwa nyumba yake.
Semaya mwana wa Sekaniya, woyangʼanira Geti ya Kumʼmawa,+ anapitiriza kuchokera pamene Zadoki analekezera.
30 Hananiya mwana wa Selemiya ndi Hanuni mwana wa 6 wa Zalafi, anakonzanso chigawo china cha mpanda.
Mesulamu+ mwana wa Berekiya, anakonza mpandawo kutsogolo kwa nyumba yake kuchokera pamene Hananiya analekezera.
31 Malikiya amene anali mʼgulu la osula golide, anakonza mpandawo kukafika kunyumba ya atumiki apakachisi*+ ndi amalonda, kutsogolo kwa Geti la Kufufuza mpaka pachipinda chapadenga chapakona.
32 Osula golide ndi amalonda anakonza mpandawo kuyambira pachipinda chapadenga chapakona kukafika pa Geti la Nkhosa.+