2 Mafumu
16 M’chaka cha 17 cha Peka mwana wa Remaliya, Ahazi+ mwana wa Yotamu mfumu ya Yuda anakhala mfumu. 2 Ahazi anali ndi zaka 20 pamene anayamba kulamulira, ndipo analamulira ku Yerusalemu zaka 16. Iye sanachite zoyenera pamaso pa Yehova Mulungu wake monga anachitira Davide kholo lake.+ 3 Anayenda m’njira ya mafumu a ku Isiraeli,+ ndipo ngakhale mwana wake wamwamuna anamuwotcha* pamoto,+ mofanana ndi zonyansa+ za anthu a mitundu ina amene Yehova anawapitikitsa chifukwa cha ana a Isiraeli. 4 Ahazi ankafukiza ndi kupereka nsembe yautsi pamalo okwezeka,+ pamapiri,+ ndi pansi pa mtengo uliwonse waukulu wa masamba obiriwira.+
5 Pa nthawi imeneyo Rezini+ mfumu ya Siriya ndi Peka+ mwana wa Remaliya mfumu ya Isiraeli, anabwera kudzaukira Yerusalemu mwankhondo ndipo anazungulira Ahazi koma sanathe kumenyana naye.+ 6 Pa nthawiyo, Rezini mfumu ya Siriya anabwezeretsa mzinda wa Elati+ ku Edomu. Kenako anachotsa Ayuda mu Elati ndipo Aedomu analowa n’kumakhalamo. Iwo akukhalabe komweko mpaka lero. 7 Chotero Ahazi anatumiza amithenga kwa Tigilati-pilesere+ mfumu ya Asuri ndi uthenga wakuti: “Ndine mtumiki wanu+ ndi mwana wanu. Bwerani mudzandipulumutse+ m’manja mwa mfumu ya Siriya ndi m’manja mwa mfumu ya Isiraeli, amene akundiukira.” 8 Pamenepo Ahazi anatenga siliva ndi golide amene anali panyumba ya Yehova+ ndiponso wochokera pa chuma cha m’nyumba ya mfumu, n’kuzitumiza kwa mfumu ya Asuri ngati chiphuphu.+ 9 Mfumu ya Asuri inamumvera n’kupita ku Damasiko+ ndipo inakalanda mzindawo.+ Anthu a mumzindawo inawatengera ku Kiri,+ ndipo Rezini+ inamupha.
10 Kenako Mfumu Ahazi+ inapita kukakumana ndi Tigilati-pilesere+ mfumu ya Asuri ku Damasiko. Kumeneko inaonako guwa lansembe,+ chotero Mfumu Ahazi inatumizira wansembe Uliya chitsanzo cha kamangidwe ka guwa lansembe lonselo.+ 11 Wansembe Uliya+ anamanga guwa lansembelo.+ Analimanga mogwirizana ndi zonse zimene Mfumu Ahazi inam’tumizira kuchokera ku Damasiko, podikira kuti Mfumu Ahazi ibwereko ku Damasiko. 12 Mfumuyo itabwerako ku Damasiko, inaliona guwa lansembelo, ndipo inayamba kupita kuguwalo+ kukapereka nsembe.+ 13 Paguwa lansembelo, mfumuyo inapitiriza kuwotchapo+ nsembe yopsereza+ ndi nsembe yambewu,+ ndi kuthirapo nsembe yachakumwa+ ndiponso kuwazapo magazi a nsembe zake zachiyanjano. 14 Tsopano guwa lansembe+ lamkuwa limene linali pamaso pa Yehova, Ahazi analichotsa kutsogolo kwa nyumbayo. Analichotsa pakati pa guwa lansembe latsopano ndi nyumba ya Yehova,+ n’kuliika kumpoto kwa guwa lake. 15 Ndiyeno Mfumu Ahazi inalamula wansembe Uliya+ kuti: “Paguwa lansembe lalikululi uziwotchapo nsembe yopsereza yam’mawa,+ nsembe yambewu yamadzulo,+ nsembe yopsereza ya mfumu+ ndi nsembe yake yambewu, nsembe yopsereza ya anthu onse a m’dzikoli ndi nsembe yawo yambewu, ndiponso nsembe zawo zachakumwa. Magazi onse a nsembe yopsereza ndi magazi onse a nsembe zina uziwawaza paguwa langali. Koma guwa lansembe lamkuwalo, ndiona chochita nalo.” 16 Wansembe Uliya+ anachita mogwirizana ndi zonse zimene Mfumu Ahazi inalamula.+
17 Kuwonjezera apo, Mfumu Ahazi inaduladula+ malata a m’mbali+ mwa zotengera zokhala ndi mawilo,+ n’kuchotsa mabeseni+ pamwamba pa zotengerazo. Chosungiramo madzi+ inachichotsa pamwamba pa ng’ombe zamphongo zamkuwa+ n’kuchiika pansi pomanga ndi miyala. 18 Mfumuyo inachotsa chinthu chokhala ndi denga chogwiritsa ntchito pa sabata chimene anachimanga m’nyumba ya Yehova, ndipo inatsekanso khomo lakunja limene mfumu inali kulowera m’nyumbayo. Inachita zimenezi chifukwa choopa mfumu ya Asuri.
19 Nkhani zina zokhudza Ahazi ndi zimene anachita, zinalembedwa m’buku+ la zochitika za m’masiku a mafumu a Yuda. 20 Pomalizira pake, Ahazi anagona pamodzi ndi makolo ake ndipo anaikidwa m’manda mu Mzinda wa Davide+ pamodzi ndi makolo ake. Kenako Hezekiya+ mwana wake anayamba kulamulira m’malo mwake.