Amosi
5 “Tamverani mawu awa amene ndikukuuzani monga nyimbo yoimba polira,+ inu a m’nyumba ya Isiraeli:
2 “Namwali,+ Isiraeli, wagwa m’dziko lake,+
Iye sangathenso kuimirira.+
Aliyense wamuthawa,
Ndipo palibe womudzutsa.+
3 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa wanena kuti, ‘Mzinda umene unali kupita kukamenya nkhondo ndi anthu 1,000 udzatsala ndi anthu 100, ndipo mzinda umene unali kupita kukamenya nkhondo ndi anthu 100 udzatsala ndi anthu 10. Zimenezi ndi zimene zidzachitikira nyumba ya Isiraeli.’+
4 “Yehova wauza anthu a m’nyumba ya Isiraeli kuti, ‘Yesetsani kundiyandikira,+ kuti mupitirize kukhala ndi moyo.+ 5 Musakhale ndi mtima wofuna kupita ku Beteli+ ndipo musabwere ku Giligala.+ Musadutse malire kupita ku Beere-seba+ chifukwa ndithu Giligala adzagwidwa ndi kutengedwa kupita ku ukapolo+ ndipo Beteli adzakhala malo ochitikira zinthu zamatsenga.+ 6 Yesetsani kuyandikira kwa Yehova, inu a m’nyumba ya Yosefe,+ kuti mupitirize kukhala ndi moyo+ ndiponso kuti Mulungu asakuyakireni ngati moto.+ Chitani zimenezi kuti motowo usakunyeketseni chifukwa ku Beteli sikungapezeke munthu wouzimitsa.+ 7 Mukuweruza mopanda chilungamo,+ choncho moyo wakhala wowawa ndi wosautsa kwa anthu, pakuti inuyo mwakana chilungamo.+ 8 Yehova ndilo dzina+ la amene anapanga gulu la nyenyezi la Kima+ ndi gulu la nyenyezi la Kesili,+ amene amachititsa mdima wandiweyani+ kukhala kuwala kwa m’mamawa, amenenso amachititsa masana kukhala mdima ngati wausiku,+ amene amaitana madzi akunyanja kuti awakhuthulire panthaka ya dziko lapansi.+ 9 Iye ndiye amabweretsa chiwonongeko mwamsanga pa munthu wamphamvu ngati kuwala kwa mphezi. Ndiponso amachititsa kuti malo okhala ndi mpanda wolimba kwambiri awonongedwe.
10 “‘Anthuwo amadana ndi munthu wowadzudzula pachipata cha mzinda,+ komanso amanyansidwa ndi munthu wowauza chilungamo.+ 11 Inu mukulamula anthu osauka kuti akulipireni mwa kukupatsani zokolola zawo za m’munda, ndiponso kuti azikhoma msonkho mwa kupereka mbewu za m’munda.+ Choncho chifukwa mwachita zinthu zimenezi, simudzapitiriza kukhala m’nyumba zamiyala yosema zimene mwamanga+ ndipo simudzamwa vinyo wochokera m’minda yanu ya mpesa yosiririkayo.+ 12 Pakuti ndadziwa kuchuluka kwa zochita zanu zondipandukira+ ndiponso kukula kwa machimo anu,+ inu amene mukuchitira nkhanza munthu wolungama,+ amene mukulandira ndalama za chitsekapakamwa+ ndiponso amene mukupondereza anthu osauka+ pachipata cha mzinda.+ 13 Choncho, munthu wozindikira adzakhala chete pa nthawi imeneyo chifukwa chakuti idzakhala nthawi yoopsa.+
14 “‘Yesetsani kuchita zabwino osati zoipa+ kuti mupitirize kukhala ndi moyo+ ndiponso kuti Yehova Mulungu wa makamu akhale ndi inu monga mmene mwanenera.+ 15 Danani ndi choipa ndipo muzikonda chabwino.+ Chitani zinthu zachilungamo pachipata cha mzinda,+ mwina Yehova Mulungu wa makamu adzakomera mtima+ otsala a Yosefe.’+
16 “Choncho Yehova, Mulungu wa makamu, Yehova wanena kuti, ‘Padzamveka kulira m’mabwalo onse a mizinda+ yanu ndipo m’misewu yanu yonse anthu azidzanena kuti: “Aa! Aa!” Pamenepo adzaitana mlimi kuti alire+ ndiponso anthu odziwa kulira maliro kuti alire mokweza.’+ 17 ‘Padzakhala kulira mokweza m’minda yonse ya mpesa+ pakuti ine ndidzadutsa pakati panu,’+ watero Yehova.
18 “‘Tsoka kwa anthu amene akulakalaka tsiku la Yehova!+ Kodi mukuyembekezera chiyani pa tsiku la Yehova anthu inu?+ Limeneli lidzakhala tsiku lamdima osati kuwala,+ 19 monga mmene zingakhalire kuti munthu pothawa mkango akukumana ndi chimbalangondo, ndipo pamene akulowa m’nyumba ndi kugwira khoma njoka ikumuluma.+ 20 Tsiku la Yehova lidzakhala lakuda osati lowala, kudzakhaladi mdima osati kuwala.+ 21 Ine ndimadana ndi zikondwerero zanu ndipo ndikuzikana,+ komanso sindidzasangalala ndi fungo la nsembe zanu zoperekedwa pamisonkhano yanu yapadera.+ 22 Inu mukapereka nsembe zathunthu zopsereza,+ ine sindidzasangalala ndi nsembe zanuzo zoperekedwa ngati mphatso,+ ndipo sindidzayang’ana nsembe zanu zachiyanjano zanyama zonenepa.+ 23 Siyani kuimba nyimbo zanu zaphokoso, ndipo sindikufuna kumva nyimbo zanu zoimbidwa ndi zoimbira za zingwe.+ 24 Chilungamo chiyende ngati madzi+ ndiponso ngati mtsinje wosaphwa nthawi zonse.+ 25 Kodi anthu inu a m’nyumba ya Isiraeli, munandipatsa nsembe zanyama ndi zopereka zina pamene munali m’chipululu muja kwa zaka 40?+ 26 Koma inu mudzanyamula Sakuti+ ndi Kaiwani, mafano amene munadzipangira a mulungu wanu wa nyenyezi.+ 27 Pakuti ndidzakupititsani ku ukapolo, kutali kwambiri ndi ku Damasiko,’+ watero Mulungu wa makamu, amene dzina lake ndi Yehova.”+