Maliko
8 M’masiku amenewo, khamu la anthu linasonkhananso, koma linalibe chakudya. Ndiyeno Yesu anaitana ophunzira ake ndi kuwauza kuti:+ 2 “Khamu la anthuli likundimvetsa chisoni,+ chifukwa anthuwa akhala ndi ine masiku atatu tsopano ndipo alibe chakudya. 3 Koma ndikawauza kuti azipita kwawo ndi njala, alenguka panjira. Ndipo ena a iwo achokera kutali kwambiri.” 4 Pamenepo ophunzira ake anamuyankha kuti: “Munthu angaipeze kuti mitanda ya mkate yokwanira kudyetsa anthu onsewa kutchire ngati kuno?”+ 5 Koma iye anawafunsa kuti: “Muli ndi mitanda ingati ya mkate?” Iwo anayankha kuti: “Tili nayo 7.”+ 6 Ndiyeno anauza anthuwo kuti akhale pansi. Kenako, anatenga mitanda 7 ya mkate ija, ndi kuyamika.+ Atatero anainyemanyema n’kupatsa ophunzira ake kuti agawe, ndipo iwo anagawira khamu la anthulo.+ 7 Ophunzirawo analinso ndi tinsomba towerengeka ndipo atadalitsa tinsombato, anawauza kuti agawirenso anthu tinsombato.+ 8 Chotero anthuwo anadya ndi kukhuta, moti anatolera zotsala zodzaza madengu akuluakulu 7.+ 9 Komatu panali amuna pafupifupi 4,000. Pambuyo pake anawauza kuti azipita.+
10 Nthawi yomweyo iye anakwera ngalawa pamodzi ndi ophunzira ake ndi kufika m’madera a Dalamanuta.+ 11 Kumeneku kunafika Afarisi ndipo anayamba kutsutsana naye. Ankafuna kuti iye awaonetse chizindikiro chochokera kumwamba, pofuna kumuyesa.+ 12 Choncho anadzuma mowawidwa mtima+ ndi kunena kuti: “N’chifukwa chiyani m’badwo umenewu ukufunitsitsa chizindikiro? Ndithu ndikukuuzani, M’badwo umenewu sudzapatsidwa chizindikiro chilichonse.”+ 13 Atatero anawasiya, ndi kukweranso ngalawa kupita kutsidya lina.
14 Komano iwo anaiwala kutenga mikate, chotero analibe chilichonse m’ngalawamo koma mtanda wa mkate umodzi wokha basi.+ 15 Ndipo anayamba kuwachenjeza mwamphamvu kuti: “Khalani maso! Chenjerani ndi chofufumitsa cha Afarisi ndi cha Herode.”+ 16 Choncho ophunzirawo anayamba kukangana pa nkhani yosowa mkate.+ 17 Yesu poona zimenezo, anawafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani mukukangana nkhani yosowa mikate?+ Kodi simukuzindikira ndi kumvetsa tanthauzo lake mpaka pano? Kodi mitima yanu ikadali yosazindikira?+ 18 ‘Ngakhale kuti muli maso, kodi simuona? Ndipo ngakhale kuti muli ndi makutu kodi simumva?’+ Komanso simukukumbukira kodi, 19 kuchuluka kwa madengu a zotsala zimene munatolera, pamene ndinanyemanyema mitanda isanu ya mkate+ koma n’kukwanira amuna 5,000?” Iwo anayankha kuti: “Anali madengu 12.”+ 20 “Pamene ndinanyemanyema mitanda 7 ya mkate koma inakwanira amuna 4,000, kodi munatolera madengu akuluakulu angati a zotsala?” Iwo anamuyankha kuti: “Analipo 7.”+ 21 Pamenepo iye anawafunsa kuti: “Kodi simukumvetsabe tanthauzo lake?”+
22 Tsopano anafika ku Betsaida. Kumeneku anthu anamubweretsera munthu wakhungu. Anthuwo anamuchonderera kuti akhudze+ munthuyo. 23 Iye anagwira dzanja la munthu wakhunguyo, ndi kupita naye kunja kwa mudzi. Kumeneko iye analavulira+ m’maso mwake, ndi kuika manja ake pa munthuyo ndi kumufunsa kuti: “Kodi ukuona chilichonse?” 24 Munthuyo anayang’ana m’mwamba ndi kunena kuti: “Ndikuona anthu, chifukwa ndikuona zinthu zooneka ngati mitengo, koma zikuyendayenda.” 25 Pamenepo anagwiranso m’maso mwa munthuyo. Munthuyo anayamba kuona bwinobwino, chifukwa anam’chiritsa, moti anayamba kuona chilichonse bwinobwino. 26 Kenako anamuuza kuti azipita kwawo, ndi kunena kuti: “Koma usalowe m’mudzimu.”+
27 Tsopano Yesu ndi ophunzira ake anachoka ndi kupita kumidzi ya Kaisareya wa Filipi. Ali m’njira, anayamba kufunsa ophunzira ake, kuti: “Kodi anthu akumanena kuti ine ndine ndani?”+ 28 Iwo anamuyankha kuti: “Akumanena kuti Yohane M’batizi,+ ena akumati Eliya,+ koma ena akumati Mmodzi wa aneneri.”+ 29 Ndiyeno anafunsa ophunzirawo kuti: “Nanga inuyo mumati ndine ndani?” Poyankha, Petulo ananena kuti: “Ndinu Khristu.”+ 30 Pamenepo anawaletsa mwamphamvu kuti asauze aliyense za iye.+ 31 Kenako, anayamba kuwaphunzitsa kuti Mwana wa munthu ayenera kukumana ndi mavuto ambiri. Iye adzakanidwa ndi akulu, ansembe aakulu ndi alembi. Ndiyeno adzaphedwa,+ koma adzauka patapita masiku atatu.+ 32 Ndithudi, iye analankhula mawu amenewa molimba mtima. Koma Petulo anam’tengera pambali ndi kuyamba kum’dzudzula.+ 33 Pamenepo Yesu anatembenuka, ndi kuyang’ana ophunzira ake, kenako anakalipira Petulo kuti: “Pita kumbuyo kwanga Satana, chifukwa zimene umaganiza si maganizo a Mulungu, koma maganizo a anthu.”+
34 Kenako iye anaitana khamu la anthu pamodzi ndi ophunzira ake ndi kuwauza kuti: “Ngati munthu akufuna kunditsatira, adzikane yekha ndi kunyamula mtengo wake wozunzikirapo,* ndi kunditsatira mosalekeza.+ 35 Pakuti aliyense wofuna kupulumutsa moyo wake adzautaya. Koma aliyense wotaya moyo wake chifukwa cha ine ndi uthenga wabwino, adzaupulumutsa.+ 36 Kunena zoona, pali phindu lanji ngati munthu atapeza zinthu zonse za m’dzikoli koma n’kutaya moyo wake?+ 37 N’chiyani kwenikweni chimene munthu angapereke chosinthanitsa ndi moyo wake?+ 38 Pakuti aliyense wochita manyazi ndi ine, komanso ndi mawu anga mu m’badwo wachigololo ndi wochimwa uno, Mwana wa munthu adzachitanso naye manyazi+ akadzafika mu ulemerero wa Atate wake limodzi ndi angelo oyera.”+