Afilipi
3 Pomalizira abale anga, pitirizani kukondwera mwa Ambuye.+ Kukulemberani zinthu zimodzimodzi si vuto kwa ine, koma ndi chitetezo kwa inu.
2 Chenjerani ndi agalu.+ Chenjerani ndi ochita ntchito zovulaza. Chenjerani ndi anthu amene amachita mdulidwe.+ 3 Pakuti ife ndife amdulidwe weniweni,+ amene tikuchita utumiki wopatulika mwa mzimu wa Mulungu.+ Timadzitamandira mwa Khristu Yesu,+ ndipo sitidalira zinthu zimene anthu amaziona kuti ndi zofunika,+ 4 ngakhale kuti ineyo, kuposa wina aliyense, ndili ndi zifukwa zodalira zinthu zimene anthu amaziona kuti ndi zofunika.
Ngati alipo munthu woganiza kuti ali ndi zifukwa zodalira zinthu zimene anthu amaziona kuti ndi zofunika, ine ndiye woposa ameneyo.+ 5 Ineyo ndinadulidwa pa tsiku la 8,+ ndine wa mtundu wa Isiraeli, wa fuko la Benjamini,+ Mheberi wobadwa kwa Aheberi.+ Kunena za chilamulo, ndine Mfarisi.+ 6 Kunena za kudzipereka, ndinali kuzunza mpingo.+ Kunena za chilungamo mwa kutsatira chilamulo, ndinakhaladi wopanda chifukwa chondinenezera. 7 Koma zinthu zimene zinali zaphindu kwa ine, zimenezo ndaziona kukhala zopanda phindu chifukwa cha Khristu.+ 8 Zoonadi, ndimaona zinthu zonse kukhala zosapindulitsa, chifukwa chakuti ndinadziwa Khristu Yesu Ambuye wanga, chimene ndi chinthu chamtengo wapatali kwambiri.+ Chifukwa cha iye, ndimaona zinthu zonse kukhala zosapindulitsa, ndipo ndimaziyesa mulu wa zinyalala,+ kuti ndikhale pa ubwenzi weniweni ndi Khristu. 9 Ndiponso kuti ndikapezeke wogwirizana ndi iye ndikuchita chilungamo. Osati chilungamo changachanga chobwera ndi chilamulo,+ koma chobwera mwa kukhulupirira+ Khristu, chochokera kwa Mulungu pa maziko a chikhulupiriro.+ 10 Ndachita zimenezi kuti ndim’dziwe komanso kuti ndidziwe mphamvu ya kuuka kwake kwa akufa.+ Kutinso ndigawane naye m’masautso+ ake, ndi kulolera kufa imfa monga yake.+ 11 Ndachita izi kuti ndiyesetse ndi kuona ngati n’zotheka kudzauka nawo pa kuuka koyambirira+ kuchokera kwa akufa.
12 Si kuti ndalandira kale mphotoyo, kapena kuti ndakhala kale wangwiro+ ayi. Koma ndikuyesetsabe+ kuti ndione ngati inenso ndingapeze+ chimene chinachititsanso Khristu Yesu kundipeza.+ 13 Abale, ine sindidziyesa ngati ndalandira kale mphotoyo ayi. Koma pali chinthu chimodzi chimene ndikuchita: Ndikuiwala zinthu zakumbuyo+ ndipo ndikuyesetsa kuti ndikapeze zakutsogolo.+ 14 Ndikuyesetsa kuchita zimenezi mpaka nditapeza+ mphoto+ ya chiitano cha Mulungu chopita kumwamba,+ chodzera mwa Khristu Yesu. 15 Choncho, tiyeni tonse amene tili okhwima mwauzimu,+ tikhale ndi maganizo amenewa.+ Ndipo ngati muli ndi maganizo osiyana ndi amenewa m’mbali ina iliyonse, Mulungu adzakuululirani maganizo oyenerawo. 16 Komabe, mulimonse mmene tapitira patsogolo, tiyeni tipitirize kupita patsogolo mwa kuyenda moyenera+ m’njira yomweyo.
17 Mogwirizana, khalani otsanzira+ ine abale, ndipo muzionetsetsa amene akuyenda mogwirizana ndi chitsanzo chimene tinakupatsani.+ 18 Pakuti alipo ambiri amene ndinali kuwatchula kawirikawiri, koma tsopano ndikuwatchula ndi misozi, amene akuyenda monga adani a mtengo wozunzikirapo* wa Khristu.+ 19 Amenewo mapeto awo ndi chiwonongeko,+ ndipo mulungu wawo ndi mimba yawo.+ Ulemerero wawo uli m’zinthu zawo zochititsa manyazi,+ ndipo maganizo awo ali pa zinthu za dziko lapansi.+ 20 Koma ife, ndife nzika+ zakumwamba,+ kumenekonso tikuyembekezera mwachidwi+ mpulumutsi, Ambuye Yesu Khristu.+ 21 Iyeyo adzakonzanso thupi lathu lonyozekali+ kuti lifanane ndi thupi lake laulemerero.+ Adzatero malinga ndi mphamvu+ imene ali nayo, yotha kugonjetsera+ ngakhale zinthu zonse kwa iye mwini.