1 Timoteyo
6 Onse amene ali m’goli laukapolo, aziona kuti ambuye awo ndi oyenera kuwapatsa ulemu wawo wonse,+ kuti dzina la Mulungu ndi chiphunzitsocho asazinenere zoipa.+ 2 Komanso, akapolo amene ambuye awo ndi okhulupirira,+ asamawapeputse+ chifukwa chakuti ndi abale.+ M’malomwake, akhale akapolo odzipereka kwambiri, pakuti amene akupindula ndi utumiki wawo wabwinowo ndi okhulupirira ndiponso okondedwa.
Pitiriza kuwaphunzitsa ndi kuwadandaulira kuti azichita zimenezi.+ 3 Ngati munthu akuphunzitsa chiphunzitso china,+ ndipo sakuvomereza mawu olondola,+ mawu a Ambuye wathu Yesu Khristu, ndiponso sakuvomereza chiphunzitso chogwirizana ndi kudzipereka kwathu kwa Mulungu,+ 4 munthu ameneyo ndi wodzitukumula ndiponso wonyada,+ ndipo samvetsa kanthu kalikonse.+ M’malomwake, amakonda kukangana ndi anthu ndiponso kutsutsana pa mawu.+ Zimenezi zimayambitsa kaduka,+ mikangano, kunenerana mawu achipongwe,+ ndiponso kuganizirana zoipa. 5 Zimayambitsanso mapokoso achiwawa pa zinthu zazing’ono pakati pa anthu opotoka maganizo+ ndi osadziwa choonadi,+ poganiza kuti kukhala wodzipereka kwa Mulungu ndi njira yopezera phindu.+ 6 Ndithudi, kukhala wodzipereka kwa Mulungu+ kumeneko limodzi ndi kukhala wokhutira ndi zimene tili nazo,+ ndi njiradi yopezera phindu lalikulu.+ 7 Pakuti sitinabwere ndi kanthu m’dziko, ndipo sitingatulukemo ndi kanthu.+ 8 Choncho, pokhala ndi chakudya, zovala ndi pogona, tikhale okhutira ndi zinthu zimenezi.+
9 Komabe, anthu ofunitsitsa kulemera, amagwera m’mayesero+ ndi mumsampha. Iwo amakodwa ndi zilakolako zambiri zowapweteketsa ndiponso amachita zinthu mopanda nzeru.+ Zinthu zimenezi zimawawononga ndi kuwabweretsera mavuto.+ 10 Pakuti kukonda+ ndalama ndi muzu+ wa zopweteka za mtundu uliwonse,+ ndipo pokulitsa chikondi chimenechi, ena asocheretsedwa n’kusiya chikhulupiriro ndipo adzibweretsera zopweteka zambiri pathupi lawo.+
11 Koma munthu wa Mulungu iwe, thawa zinthu zimenezi.+ M’malomwake tsatira chilungamo, kudzipereka kwa Mulungu, chikhulupiriro, chikondi, chipiriro, ndi kufatsa.+ 12 Menya nkhondo yabwino yosunga chikhulupiriro.+ Gwira mwamphamvu moyo wosatha. Anakuitanira moyo umenewu ndipo unalengeza momveka bwino+ zinthu zokhudzana ndi moyo umenewu pamaso pa mboni zambiri.
13 Pamaso pa Mulungu, amene amasunga zinthu zonse kuti zikhalebe zamoyo, ndi pamaso pa Khristu Yesu, amene anapereka umboni wabwino kwambiri+ pamaso pa Pontiyo Pilato,+ ndikukulamula+ 14 kuti usunge lamulolo. Ulisunge uli wopanda banga ndi wopanda chifukwa chokunenezera, kufikira kuonekera+ kwa Ambuye wathu Yesu Khristu. 15 Wachimwemwe ndi Wamphamvu yekhayo,+ iye amene ali Mfumu+ ya olamulira monga mafumu ndi Mbuye+ wa olamulira monga ambuye, adzaonekera pa nthawi zake zoikidwiratu.+ 16 Iye yekha ndiye amene ali ndi moyo wosakhoza kufa,+ amene amakhala m’kuwala kosafikirika.+ Palibe munthu ndi mmodzi yemwe amene anamuonapo kapena amene angamuone.+ Iye apatsidwe ulemu+ ndipo mphamvu zake zikhalebe kosatha. Ame.
17 Lamula achuma+ a m’nthawi* ino kuti asakhale odzikweza,+ ndiponso kuti asamadalire chuma chosadalirika,+ koma adalire Mulungu, amene amatipatsa mowolowa manja zinthu zonse kuti tisangalale.+ 18 Uwalamule kuti azichita zabwino,+ akhale olemera pa ntchito zabwino,+ owolowa manja, okonzeka kugawira ena,+ 19 ndiponso asunge+ maziko abwino+ a tsogolo lawo monga chuma, kuti agwire mwamphamvu moyo weniweniwo.+
20 Ndithu Timoteyo, sunga bwino chimene chinaikidwa m’manja mwako.+ Pewa nkhani zopanda pake zimene zimaipitsa zinthu zoyera. Upewenso mitsutso pa zimene ena monama amati ndiye “kudziwa zinthu.”+ 21 Pakuti ena apatuka pa chikhulupiriro chifukwa chodzionetsera kuti ndi odziwa zinthu chonchi.+
Kukoma mtima kwakukulu kukhale nanu.