Chivumbulutso Chimene Yohane Analandira
8 Atamatula+ chidindo cha 7,+ kumwamba sikunamveke phokoso lililonse kwa pafupifupi 30 minitsi. 2 Kenako ndinaona angelo 7+ amene amaimirira pamaso pa Mulungu, ndipo anapatsidwa malipenga 7.
3 Mngelo wina anafika atanyamula chiwiya chofukizira chagolide nʼkuima paguwa lansembe.+ Iye anapatsidwa zofukiza zambiri+ kuti azipereke nsembe limodzi ndi mapemphero a oyera onse paguwa lansembe lagolide,+ limene linali pamaso pa mpando wachifumu. 4 Utsi wa zofukizazo unakwera pamaso pa Mulungu kuchokera mʼdzanja la mngeloyo limodzi ndi mapemphero+ a oyera. 5 Koma nthawi yomweyo, mngeloyo anatenga chiwiya chofukizira chija nʼkudzazitsamo moto umene anapala paguwa lansembe nʼkuuponyera padziko lapansi. Ndiyeno kunagunda mabingu, kunamveka mawu, kunachita mphezi+ komanso chivomerezi. 6 Angelo 7 amene anali ndi malipenga 7 aja, anakonzekera kuliza malipengawo.+
7 Mngelo woyamba analiza lipenga lake. Atatero, panaoneka matalala ndi moto zosakanikirana ndi magazi ndipo zinaponyedwa padziko lapansi.+ Gawo limodzi mwa magawo atatu a dziko lapansi linapsa, gawo limodzi mwa magawo atatu a mitengo linapsa komanso zomera zonse zobiriwira zinapsa.+
8 Mngelo wachiwiri analiza lipenga lake. Ndipo chinachake chokhala ngati phiri lalikulu limene likuyaka moto chinaponyedwa mʼnyanja.+ Zitatero gawo limodzi mwa magawo atatu a nyanja, linasanduka magazi.+ 9 Ndipo gawo limodzi mwa magawo atatu a zamoyo zamʼnyanja zinafa.+ Komanso gawo limodzi mwa magawo atatu a ngalawa, linasweka.
10 Mngelo wachitatu analiza lipenga lake. Ndipo nyenyezi yaikulu imene inkayaka ngati nyale inagwa kuchokera kumwamba. Inagwera pagawo limodzi mwa magawo atatu a mitsinje, ndi pa akasupe a madzi.+ 11 Dzina la nyenyeziyo ndi Chitsamba Chowawa. Choncho gawo limodzi mwa magawo atatu a madzi linakhala lowawa ndipo anthu ambiri anafa ndi madziwo chifukwa anali owawa.+
12 Mngelo wa 4 analiza lipenga lake. Atatero, gawo limodzi mwa magawo atatu a dzuwa linamenyedwa.+ Komanso gawo limodzi mwa magawo atatu a mwezi ndi a nyenyezi linamenyedwa. Zinatero kuti gawo limodzi mwa magawo atatu a zinthu zimenezi lichite mdima,+ komanso kuti gawo limodzi mwa magawo atatu a usana lisalandire kuunika, chimodzimodzinso usiku.
13 Ndiyeno ndinaona chiwombankhanga chikuuluka pafupi mumlengalenga ndipo ndinamva chikulankhula ndi mawu okweza akuti: “Tsoka, tsoka, tsoka+ kwa amene akukhala padziko lapansi, chifukwa cha kulira kwa malipenga otsalawo, amene angelo atatu atsala pangʼono kuwaliza!”+