Levitiko
26 “‘Musadzipangire milungu yopanda pake,+ chifaniziro,+ kapena chipilala chopatulika. Musaike mwala wokhala ndi zithunzi zojambula mochita kugoba+ m’dziko lanu kuti muziugwadira,+ chifukwa ine ndine Yehova Mulungu wanu. 2 Muzisunga masabata anga+ ndi kuopa malo anga opatulika. Ine ndine Yehova.
3 “‘Mukapitiriza kutsatira malangizo anga ndi kusunga malamulo anga,+ 4 ndidzakugwetserani mvula pa nthawi yake.+ Nthaka idzakupatsani chakudya,+ ndipo mitengo ya m’munda idzakupatsani zipatso zake.+ 5 Pamenepo, mudzakhala mukupuntha zimene mwakolola kufikira nyengo yokolola mphesa, ndipo mudzakhala mukukolola mphesa kufikira nyengo yofesa mbewu. Mudzadya mkate wanu ndi kukhuta,+ ndipo mudzakhala otetezeka m’dziko lanu.+ 6 Ndidzakupatsani mtendere m’dzikolo,+ moti mudzagona pansi popanda wokuopsani.+ M’dziko lanu simudzapezeka zilombo zoopsa zakutchire,+ ndipo simudzadutsa lupanga.+ 7 Mudzathamangitsa adani anu+ ndi kuwagonjetsa ndi lupanga. 8 Anthu asanu mwa inu adzathamangitsa adani 100, ndipo anthu 100 adzathamangitsa adani 10,000, moti mudzagonjetsa adani anu ndi lupanga.+
9 “‘Pamenepo ndidzakucheukirani,+ kukuchititsani kubereka ana ambiri ndi kukuchulukitsani.+ Ndipo ndidzasunga pangano langa ndi inu.+ 10 Mudzadya chakudya cha chaka chapita,+ ndipo chimenecho mudzachitulutsa kuti mupeze malo oikapo chatsopano. 11 Ine ndidzaika chihema changa chopatulika pakati panu,+ ndipo sindidzanyansidwa nanu.+ 12 Motero ndidzayendadi pakati panu ndi kukusonyezani kuti ine ndine Mulungu wanu,+ ndipo inu mudzakhala anthu anga.+ 13 Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakutulutsani m’dziko la Iguputo kuti musakhale akapolo a Aiguputo.+ Ndinathyola goli lanu ndi kukuchititsani kuyenda mowongoka.+
14 “‘Koma ngati simudzandimvera kapena kutsatira malamulo onsewa,+ 15 ndipo mukadzakana malangizo anga,+ n’kunyansidwa ndi zigamulo zanga, moti mwakana kutsatira malamulo anga onse, n’kufika pophwanya pangano langa,+ 16 pamenepo ine ndidzakuchitani zotsatirazi: pokulangani ndidzakugwetserani zoopsa za chifuwa chachikulu+ ndi kuphwanya kwa thupi koopsa, kumene kudzachititsa maso anu khungu+ ndi kukufooketsani.+ Simudzapindula ndi mbewu zimene mwafesa, chifukwa adani anu adzadya zokolola zanuzo.+ 17 Ine ndidzakukanani,* ndipo adani anu adzakugonjetsani+ ndi kukuponderezani,+ moti muzidzathawa popanda munthu wokuthamangitsani.+
18 “‘Koma ngati simudzandimverabe pambuyo poona zinthu zimenezi, pamenepo ndidzakulangani mowirikiza ka 7 kuposa poyamba chifukwa cha machimo anu.+ 19 Ndidzathyola kunyada kwanuko, ndi kuchititsa kumwamba kukhala ngati chitsulo+ ndi nthaka yanu ngati mkuwa. 20 Motero mphamvu zanu zidzathera pachabe, chifukwa nthaka yanu siidzakupatsani chakudya,+ ndipo mitengo ya m’munda mwanu siidzakupatsani zipatso zake.+
21 “‘Koma mukapitirizabe kuchita zosemphana ndi zofuna zanga, osafuna kundimvera, pamenepo ndidzakukanthani mowirikiza ka 7 malinga ndi machimo anu.+ 22 Ndidzatumiza zilombo zakutchire pakati panu,+ ndipo zidzakupherani ana anu+ ndi ziweto zanu, ndi kuchepetsa chiwerengero chanu, moti m’misewu yanu mudzakhala mopanda anthu.+
23 “‘Ngati simudzalola kuti ndikukonzeni ndi zinthu zimenezi,+ ndipo mukupitiriza kuyenda motsutsana nane, 24 pamenepo, ineyo ndidzatsutsana nanu,+ ndipo ndidzakukanthani maulendo 7 chifukwa cha machimo anu.+ 25 Ndidzabweretsa lupanga pa inu lobwezera chilango+ chifukwa cha pangano.+ Pamenepo mudzathawira m’mizinda yanu, ndipo ndidzakutumizirani mliri pakati panu+ ndi kukuperekani m’manja mwa mdani.+ 26 Ndikadzathyola ndodo zanu zopachikapo mkate wozungulira woboola pakati,+ akazi 10 adzaphika mkate mu uvuni umodzi, ndipo adzakugawirani mochita kukuyezerani pamuyezo.+ Chotero mudzadya koma simudzakhuta.+
27 “‘Koma ngati simudzandimvera zinthu zimenezi zitakuchitikirani, n’kupitirizabe kuyenda motsutsana nane,+ 28 pamenepo ndidzatsutsana nanu koopsa,+ ndipo ineyo ndidzakukwapulani maulendo 7 chifukwa cha machimo anu.+ 29 Chotero mudzadya ana anu aamuna ndi ana anu aakazi.+ 30 Ndipo ndidzafafaniza malo anu opatulika olambirirako+ ndi kugwetsa maguwa anu ofukizirapo zonunkhira. Ndidzaponya mitembo yanu pamwamba pa mafano anu onyansa* opanda moyowo,+ ndipo mudzakhala onyansa kwa ine.+ 31 Mizinda yanu ndidzaiwononga ndi lupanga+ ndipo malo anu opatulika adzakhala opanda anthu,+ komanso sindidzalandira nsembe zanu zafungo lokhazika mtima pansi.+ 32 Dziko lanu ndidzalisandutsa bwinja,+ ndipo adani anu amene adzakhala m’dzikolo adzaliyang’anitsitsa modabwa.+ 33 Ine ndidzakubalalitsani pakati pa anthu a mitundu ina,+ ndipo ndidzakusololerani lupanga ndi kukupitikitsani.+ Dziko lanu lidzakhala bwinja,+ ndipo mizinda yanu idzawonongedwa ndi kukhala mabwinja.
34 “‘Pa masiku onse amene dzikolo lidzakhala bwinja, lidzabweza masabata ake, inu muli m’dziko la adani anu. Nthawi imeneyo, dziko lidzasunga sabata ndipo lidzabweza masabata ake.+ 35 Masiku onse amene dzikolo lidzakhala bwinja lidzakhala likusunga sabata, chifukwa silinasunge sabata, pakuti inuyo simunasunge masabata anu pamene munali kukhala m’dzikolo.
36 “‘Ndidzaika mantha m’mitima ya otsala pakati panu+ amene ali m’dziko la adani awo, moti adzathawa m’tswatswa wa tsamba louluka, ndipo adzathawa ngati kuti akuthawa lupanga. Pamenepo adzagwa popanda munthu wowathamangitsa.+ 37 Iwo adzagwetsana okhaokha ngati kuti akuthawa lupanga, koma popanda munthu wowathamangitsa. Simudzatha n’komwe kulimbana ndi adani anu.+ 38 Mudzatheratu pakati pa anthu a mitundu ina,+ ndipo dziko la adani anu lidzakumezani. 39 Otsala pakati panu, adzazunzika+ chifukwa cha zolakwa zawo m’mayiko a adani awo. Iwo adzazunzika chifukwa cha zolakwa za makolo awo,+ mmene makolowo anazunzikira. 40 Chotero adzavomereza kuti iwo komanso makolo awo anayenda motsutsana nane,+ anandichimwira+ ndi kundichitira mosakhulupirika. 41 Zimenezi zinachititsa kuti ine nditsutsane nawo+ ndi kuwatengera kudziko la adani awo.+
“‘Izi zinachitika kuti mwina mitima yawo yosadulidwayo+ ingadzichepetse,+ ndi kulipira chifukwa cha zolakwa zawo. 42 Chotero ndidzakumbukira pangano langa limene ndinachita ndi Yakobo.+ Ndidzakumbukiranso pangano langa ndi Isaki+ komanso ndi Abulahamu.+ Ndidzakumbukiranso dzikolo. 43 Pa nthawiyo, adzakhala atasiya dziko lawo, ndipo dzikolo lidzakhala likubweza masabata ake+ pamene lidzakhala bwinja iwowo kulibe. Iwo adzakhala akulipira chifukwa cha zolakwa zawo,+ chifukwa chakuti anakana zigamulo zanga+ ndipo ananyansidwa ndi malamulo anga.+ 44 Koma ngakhale kuti padzachitika zonsezi, pamene iwo akukhala m’dziko la adani awo, sindidzawakana+ kapena kunyansidwa nawo+ moti n’kuwafafaniziratu, kuphwanya pangano langa+ ndi iwo, chifukwa ine ndine Yehova Mulungu wawo. 45 Ndipo ndidzakumbukira m’malo mwawo pangano limene ndinachita ndi makolo awo,+ amene ndinawatulutsa m’dziko la Iguputo, anthu a mitundu ina akuona.+ Ndidzachita zimenezi kuti ndiwasonyeze kuti ndine Mulungu wawo. Ine ndine Yehova.’”
46 Amenewa ndiwo malangizo, zigamulo+ ndi malamulo amene Yehova anaika pakati pa iye ndi ana a Isiraeli m’phiri la Sinai, kudzera mwa Mose.+