Ekisodo
7 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: “Taona, ndakuika kuti ukhale ngati Mulungu* kwa Farao, ndipo Aroni mchimwene wako akhala mneneri wako.+ 2 Iwe uzimuuza zonse zimene ndizikulamula, koma Aroni mchimwene wako ndi amene azikalankhula ndi Farao, ndipo adzaloladi Aisiraeli kuti achoke mʼdziko lake. 3 Koma ine ndidzalola Farao kuti aumitse mtima wake,+ ndipo ndidzachita zizindikiro ndi zodabwitsa zochuluka mʼdziko la Iguputo.+ 4 Komabe Farao sadzakumverani, choncho ndidzaonetsa mphamvu ya dzanja langa pa Iguputo ndi kutulutsa anthu anga Aisiraeli omwe ndi ambiri. Ndidzawatulutsa mʼdziko la Iguputo ndi ziweruzo zamphamvu.+ 5 Pamenepo Aiguputo adzadziwa kuti ine ndine Yehova+ ndikadzatambasula dzanja langa ndi kulanga Iguputo, nʼkutulutsa Aisiraeli mʼdzikolo.” 6 Mose ndi Aroni anachitadi zimene Yehova anawalamula. Anachitadi zomwezo. 7 Pa nthawi imene ankalankhula ndi Farao, Mose anali ndi zaka 80 ndipo Aroni anali ndi zaka 83.+
8 Ndiyeno Yehova anauza Mose ndi Aroni kuti: 9 “Farao akakakuuzani kuti, ‘Chitani chodabwitsa,’ iweyo ukauze Aroni kuti, ‘Tenga ndodo yako nʼkuiponya patsogolo pa Farao.’ Akakachita zimenezo, ikasanduka njoka yaikulu.”+ 10 Choncho Mose ndi Aroni anapita kwa Farao ndipo anachita ndendende mmene Yehova anawalamulira. Aroni anaponya ndodo yake patsogolo pa Farao ndi atumiki ake, ndipo ndodoyo inasanduka njoka yaikulu. 11 Komabe, Farao anaitana amuna anzeru ndi amatsenga ndipo ansembe ochita zamatsenga a ku Iguputo+ nawonso anachita zomwezo mwa matsenga awo.+ 12 Aliyense wa iwo anaponya pansi ndodo yake, ndipo zinasanduka njoka zazikulu. Koma ndodo ya Aroni inameza ndodo zawo. 13 Ngakhale zinali choncho, Farao anaumitsabe mtima wake+ ndipo sanawamvere, mogwirizana ndi zimene Yehova ananena.
14 Kenako Yehova anauza Mose kuti: “Farao waumitsa mtima wake.+ Iye wakana kuti Aisiraeli achoke. 15 Mawa mʼmawa upite kwa Farao. Iye adzakhala akupita kumtsinje. Choncho iweyo udzaime poti udzathe kukumana naye mʼmphepete mwa mtsinje wa Nailo, ndipo udzatenge ndodo imene inasanduka njoka ija.+ 16 Ndiye ukamuuze kuti, ‘Yehova Mulungu wa Aheberi wandituma kwa iwe+ ndi uthenga wakuti: “Lola anthu anga kuchoka kuti akanditumikire mʼchipululu,” koma mpaka pano sukundimvera. 17 Yehova wanena kuti: “Ndimenya madzi amumtsinje wa Nailo ndi ndodo imene ili mʼdzanja langa, ndipo madziwo asanduka magazi. Zikatero udziwa kuti ine ndine Yehova.+ 18 Nsomba zimene zili mumtsinje wa Nailo zifa, ndipo mtsinje wa Nailo ununkha, moti Aiguputo sathanso kumwa madzi ake.”’”
19 Kenako Yehova anauza Mose kuti: “Uza Aroni kuti, ‘Tenga ndodo yako, utambasule dzanja lako nʼkuloza madzi a mu Iguputo.+ Uloze mitsinje yawo, ngalande zawo,* zithaphwi zawo+ ndi malo onse amene amasungira madzi kuti asanduke magazi.’ Choncho madzi amʼdziko lonse la Iguputo, ngakhalenso madzi amʼmitsuko yawo yamtengo ndi yamwala adzakhala magazi.” 20 Nthawi yomweyo Mose ndi Aroni anachita mogwirizana ndi zimene Yehova anawalamula. Aroni anatenga ndodo yake nʼkumenya madzi amumtsinje wa Nailo, Farao ndi atumiki ake akuona ndipo madzi onse amumtsinje wa Nailo anasanduka magazi.+ 21 Zitatero nsomba zamumtsinje wa Nailo zinafa+ ndipo mtsinjewo unayamba kununkha. Aiguputo sanathenso kumwa madzi amumtsinje wa Nailo.+ Mʼdziko lonse la Iguputo munali magazi okhaokha.
22 Koma ansembe ochita zamatsenga a ku Iguputo anachitanso zomwezo mwa matsenga awo,+ moti Farao anapitiriza kuumitsa mtima wake, ndipo sanamvere Mose ndi Aroni, mogwirizana ndi zimene Yehova ananena.+ 23 Kenako Farao anabwerera kunyumba kwake, ndipo sanafune mʼpangʼono pomwe kumvanso za nkhani imeneyi. 24 Choncho Aiguputo onse anayamba kukumba zitsime mʼmphepete mwa mtsinje wa Nailo kuti apeze madzi akumwa, chifukwa sakanatha kumwa madzi a mumtsinje wa Nailo. 25 Ndipo panadutsa masiku 7 kuchokera pamene Yehova anasandutsa madzi amumtsinje wa Nailo kukhala magazi.