Danieli
6 Ndiyeno Dariyo anaona kuti ndi bwino kuti aike masatarapi* 120 oti aziyangʼanira zigawo zonse za ufumu wake.+ 2 Anaikanso nduna zapamwamba zitatu kuti ziziyangʼanira masatarapiwo ndipo Danieli anali mmodzi wa ndunazo.+ Masatarapiwo+ ankayenera kuuza nduna zimenezi chilichonse chimene chikuchitika nʼcholinga chakuti zinthu za mfumu zisawonongeke. 3 Ndiyeno Danieli anaonetsa kuti anali wodziwa kugwira ntchito bwino kuposa nduna zina zapamwamba ndi masatarapi, chifukwa anali ndi luso lodabwitsa+ ndipo mfumu inaganiza zomukweza kuti akhale ndi udindo waukulu mu ufumu wonsewo.
4 Pa nthawiyo, nduna zapamwamba ndi masatarapi aja ankafufuza zifukwa zoti amuimbire mlandu Danieli pa nkhani zokhudza mmene ankayendetsera zinthu mu ufumuwo. Koma iwo sanapeze chifukwa chilichonse chomuimbira mlandu kapena chinthu chilichonse chachinyengo chimene anachita. Zinali choncho chifukwa Danieli anali wokhulupirika ndipo iwo anapeza kuti sankanyalanyaza udindo wake kapena kuchita zachinyengo zilizonse. 5 Choncho amuna amenewa anati: “Danieliyu sitimupezera chifukwa chilichonse. Ngati tikufuna kumupezera chifukwa, chikhale chokhudzana ndi lamulo la Mulungu wake.”+
6 Choncho nduna zapamwamba zimenezi ndi masatarapi aja anapita kwa mfumu ali chigulu ndipo anauza mfumuyo kuti: “Inu Mfumu Dariyo, mukhale ndi moyo mpaka kalekale. 7 Nduna zonse zapamwamba za mu ufumu uno, akuluakulu a boma, masatarapi, alangizi a mfumu ndi abwanamkubwa agwirizana kuti inu mfumu mukhazikitse lamulo loletsa munthu aliyense kupemphera kwa mulungu kapena kwa munthu wina aliyense kwa masiku 30, kupatulapo kwa inu nokha mfumu. Aliyense amene samvera lamulo limeneli aponyedwe mʼdzenje la mikango.+ 8 Ndiyeno inu mfumu khazikitsani lamulo ndipo musaine+ kuti lamulolo lisasinthe, mogwirizana ndi malamulo a Amedi ndi Aperisiya, amene sangasinthidwe.”+
9 Choncho Mfumu Dariyo inasainira lamulo loletsa kupempheralo.
10 Koma Danieli atangodziwa kuti lamulo limeneli lasainidwa, anapita kunyumba kwake. Mawindo a chipinda chake chamʼmwamba anali otsegula ndipo anayangʼana ku Yerusalemu.+ Katatu pa tsiku, iye ankagwada nʼkupemphera kwa Mulungu wake komanso kumutamanda, ngati mmene ankachitira nthawi zonse lamuloli lisanasainidwe. 11 Pa nthawi imeneyo, amuna amenewa analowa mʼnyumbamo ali chigulu ndipo anapeza Danieli akuchonderera ndi kupempha Mulungu wake kuti amukomere mtima.
12 Choncho anapita kwa mfumu kukaikumbutsa za lamulo limene inakhazikitsa lija. Iwo anati: “Kodi inu mfumu, si paja munasainira lamulo lonena kuti kwa masiku 30 munthu aliyense amene angapezeke akupemphera kwa mulungu kapena kwa munthu wina aliyense, kupatulapo kwa inu nokha, aponyedwe mʼdzenje la mikango?” Mfumuyo inayankha kuti: “Nkhani imeneyi ndi yodziwika bwino, mogwirizana ndi malamulo a Amedi ndi Aperisiya, amene sangasinthidwe.”+ 13 Nthawi yomweyo iwo anauza mfumuyo kuti: “Danieli, mmodzi wa anthu amene anatengedwa ukapolo ku Yuda,+ sakukumverani inu mfumu kapena kumvera lamulo limene munasainira koma akumapemphera katatu pa tsiku.”+ 14 Mfumu itangomva zimenezi inakhumudwa kwambiri ndipo inayamba kuganiza zimene ingachite kuti ipulumutse Danieli. Mfumuyo inayesetsa kufunafuna njira yoti imupulumutsire mpaka dzuwa linalowa. 15 Pamapeto pake, amuna amenewa anapita kwa mfumu ali chigulu ndipo anaiuza kuti: “Inu mfumu, mukudziwa kuti malamulo a Amedi ndi Aperisiya amanena kuti lamulo lililonse lokhazikitsidwa ndi mfumu silingasinthidwe.”+
16 Choncho mfumuyo inalamula kuti abweretse Danieli. Atabwera naye anamuponya mʼdzenje la mikango.+ Koma mfumu inauza Danieli kuti: “Mulungu wako amene ukumutumikira mosalekeza akupulumutsa.” 17 Ndiyeno anabweretsa mwala nʼkutseka pakhomo la* dzenjelo. Kenako mfumu inadinda mwalawo ndi mphete yake yodindira ndipo nduna zakenso zinaudinda ndi mphete yawo yodindira, kuti chilichonse chokhudza Danieli chisasinthidwe.
18 Kenako mfumu inapita kunyumba yake yachifumu. Usiku umenewo mfumuyo inasala kudya ndipo inakana zosangalatsa zilizonse* komanso sinathe kugona.* 19 Ndiyeno kutangoyamba kuwala mʼbandakucha, mfumuyo inadzuka ndipo inapita mofulumira kudzenje la mikango lija. 20 Itayandikira dzenjelo, inaitana Danieli ndi mawu achisoni. Mfumuyo inafunsa Danieli kuti: “Danieli mtumiki wa Mulungu wamoyo, kodi Mulungu wako amene umamutumikira mosalekeza wakupulumutsa kwa mikango?” 21 Nthawi yomweyo Danieli anayankha mfumuyo kuti: “Inu mfumu, mukhale ndi moyo mpaka kalekale. 22 Mulungu wanga watumiza mngelo wake kudzatseka pakamwa pa mikango+ moti sinandivulaze,+ chifukwa iye sanandipeze ndi mlandu uliwonse ndipo inunso mfumu sindinakulakwireni chilichonse.”
23 Mfumu inasangalala kwambiri ndipo inalamula kuti Danieli amutulutse mʼdzenjemo. Danieli anatulutsidwadi mʼdzenjemo ndipo sanavulale paliponse chifukwa anakhulupirira Mulungu wake.+
24 Kenako mfumu inalamula kuti abweretse amuna amene ananenera Danieli zoipa aja. Atawabweretsa, anawaponya mʼdzenje la mikango pamodzi ndi ana awo komanso akazi awo. Iwo asanafike nʼkomwe pansi pa dzenjelo, mikango inawakhadzulakhadzula nʼkuphwanya mafupa awo onse.+
25 Ndiyeno Mfumu Dariyo inalemba makalata opita kwa anthu a mitundu yonse ndi anthu olankhula zilankhulo zosiyanasiyana okhala padziko lonse lapansi+ kuti: “Mukhale ndi mtendere wochuluka. 26 Ine ndikulamula kuti mʼzigawo zonse za ufumu wanga, anthu azinjenjemera chifukwa cha mantha pamaso pa Mulungu wa Danieli.+ Chifukwa iye ndi Mulungu wamoyo ndipo adzakhalapo mpaka kalekale. Ufumu wake sudzawonongedwa komanso ulamuliro wake udzakhalapo kwamuyaya.+ 27 Iye amapulumutsa+ ndi kulanditsa anthu ake, ndipo amachita zizindikiro komanso zinthu zodabwitsa kumwamba ndi padziko lapansi,+ moti wapulumutsa Danieli kwa mikango.”
28 Choncho zinthu zinamuyendera bwino Danieli mu ufumu wa Dariyo+ ndiponso mu ufumu wa Koresi wa Chiperisiya.+