Genesis
10 Iyi ndi mbiri ya ana a Nowa, omwe ndi Semu,+ Hamu ndi Yafeti.
Iwowa anabereka ana pambuyo pa Chigumula.+ 2 Ana a Yafeti anali Gomeri,+ Magogi,+ Madai, Yavani, Tubala,+ Meseki+ ndi Tirasi.+
3 Ana a Gomeri anali Asikenazi,+ Rifati ndi Togarima.+
4 Ana a Yavani anali Elisha,+ Tarisi,+ Kitimu+ ndi Dodanimu.
5 Mwa anthu amenewa, munachokera anthu okhala mʼzilumba amene anafalikira mʼzilumbazo malinga ndi zilankhulo zawo, mabanja awo ndi mitundu yawo.
6 Ana a Hamu anali Kusi, Miziraimu,+ Puti+ ndi Kanani.+
7 Ana a Kusi anali Seba,+ Havila, Sabita, Raama+ ndi Sabiteka.
Ana a Raama anali Sheba ndi Dedani.
8 Kusi anabereka Nimurodi, amene anali woyamba kukhala wamphamvu padziko lapansi. 9 Iye anakhala mlenje wamphamvu wotsutsa Yehova. Nʼchifukwa chake pali mawu akuti: “Monga Nimurodi mlenje wamphamvu wotsutsa Yehova.” 10 Ufumu wake unayambira ku* Babele,+ Ereke,+ Akadi mpaka ku Kaline mʼdziko la Sinara.+ 11 Atachoka mʼdzikolo analowera ku Asuri+ ndipo anamangako Nineve,+ Rehoboti-iri, Kala, 12 komanso Resene pakati pa Nineve ndi Kala. Umenewu ndi mzinda waukulu.*
13 Miziraimu anabereka Ludimu,+ Anamimu, Lehabimu, Nafituhimu,+ 14 Patirusimu,+ Kasiluhimu (Afilisiti+ anachokera mwa iyeyu) ndiponso Kafitorimu.+
15 Kanani anabereka Sidoni,+ mwana wake woyamba, kenako anabereka Heti.+ 16 Analinso kholo la Ayebusi,+ Aamori,+ Agirigasi, 17 Ahivi,+ Aariki, Asini, 18 Aarivadi,+ Azemari ndi Ahamati,+ ndipo pambuyo pake, mabanja a Akanani anabalalikana. 19 Choncho malire a dziko la Akanani anachokera ku Sidoni mpaka ku Gerari+ kufupi ndi Gaza,+ nʼkukafika ku Sodomu ndi Gomora+ mpakanso ku Adima ndi Zeboyimu,+ kufupi ndi Lasa. 20 Amenewa ndi omwe anali ana a Hamu malinga ndi mabanja awo ndi zilankhulo zawo, mayiko awo komanso mitundu yawo.
21 Nayenso Semu anabereka ana ndipo anakhala kholo la ana onse a Ebere.+ Semu anali mngʼono wake wa Yafeti, amene anali wamkulu pa onse.* 22 Ana a Semu anali Elamu,+ Ashuri,+ Aripakisadi,+ Ludi ndi Aramu.+
23 Ana a Aramu anali Uzi, Huli, Geteri ndi Masi.
24 Aripakisadi anabereka Shela+ ndipo Shela anabereka Ebere.
25 Ebere anabereka ana awiri. Wina dzina lake anali Pelegi,*+ chifukwa mʼmasiku ake dziko lapansi linagawanika.* Mʼbale wakeyo dzina lake anali Yokitani.+
26 Yokitani anabereka Alamodadi, Selefi, Hazaramaveti, Yera,+ 27 Hadoramu, Uzali, Dikila, 28 Obali, Abimaele, Sheba, 29 Ofiri,+ Havila ndi Yobabi. Onsewa anali ana a Yokitani.
30 Dziko limene ankakhala linayambira ku Mesa mpaka ku Sefara, dera lamapiri la Kumʼmawa.
31 Amenewa ndi ana a Semu malinga ndi mabanja awo ndi zilankhulo zawo komanso malinga ndi mayiko awo ndi mitundu yawo.+
32 Mabanja a ana a Nowa ndi amenewa malinga ndi mibadwo yawo komanso mitundu yawo. Kuchokera mwa anthu amenewa, mitundu inafalikira padziko lapansi pambuyo pa Chigumula.+