Kalata Yopita kwa Aroma
5 Popeza tsopano tikuonedwa kuti ndife olungama chifukwa chokhala ndi chikhulupiriro,+ tingathe kukhala pa mtendere* ndi Mulungu kudzera mwa Ambuye wathu Yesu Khristu.+ 2 Kukhulupirira Yesu kumatithandiza kuti tizitha kufika kwa Mulungu komanso tizisangalala ndi kukoma mtima kwake kwakukulu.+ Ndipo tingathe kusangalala* chifukwa tili ndi chiyembekezo cholandira ulemerero wa Mulungu. 3 Si zokhazo, koma tikhozanso kumasangalala* tikakumana ndi mavuto+ chifukwa tikudziwa kuti mavuto athu amachititsa kuti tipirire.+ 4 Kupirira kumachititsa kuti tikhale ovomerezeka kwa Mulungu+ ndipo kukhala ovomerezeka kwa Mulungu kumachititsa kuti tikhale ndi chiyembekezo.+ 5 Chiyembekezocho sichitikhumudwitsa+ chifukwa Mulungu amasonyeza kuti amatikonda pogwiritsa ntchito mzimu woyera umene amatipatsa.+
6 Pamene tinalibe mtengo wogwira,*+ Khristu anafera anthu osalambira Mulungu pa nthawi imene anakonzeratu. 7 Chifukwa nʼzovuta kuti munthu wina afere munthu wolungama. Koma mwina munthu angalimbe mtima kufera munthu wabwino. 8 Koma Mulungu akutisonyeza chikondi chake, chifukwa pamene tinali ochimwa, Khristu anatifera.+ 9 Ndiponso adzachita zoposa pamenepo potipulumutsa ku mkwiyo wake kudzera mwa Khristu,+ popeza tikuonedwa olungama chifukwa cha magazi a Khristuyo.+ 10 Ngati tinagwirizanitsidwa ndi Mulungu kudzera mu imfa ya Mwana wake+ pa nthawi imene tinali adani, ndiye kuti tidzapulumutsidwa ndithu ndi moyo wake, popeza panopa tagwirizanitsidwa. 11 Ndipo si zokhazo, koma tikusangalalanso chifukwa cha ubwenzi wathu ndi Mulungu kudzera mwa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene tagwirizanitsidwa ndi Mulungu kudzera mwa iye.+
12 Uchimo unalowa mʼdziko kudzera mwa munthu mmodzi ndipo uchimowo unabweretsa imfa.+ Choncho imfayo inafalikira kwa anthu onse chifukwa onse anachimwa . . .+ 13 Chilamulo chisanabwere, uchimo unalipo kale mʼdziko, koma munthu sangapezedwe ndi mlandu woti wachita tchimo ngati palibe lamulo.+ 14 Ngakhale zili choncho, imfa inalamulira ngati mfumu kuyambira nthawi ya Adamu mpaka ya Mose, ngakhalenso kwa anthu amene sanachimwe ngati mmene anachimwira Adamu, yemwe ndi wofanana ndi amene ankabwera.+
15 Koma mmene zilili ndi mphatsoyi, si mmene zinalili ndi uchimowo. Anthu ambiri anafa chifukwa cha uchimo wa munthu mmodzi. Koma kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu ndiponso mphatso yake yaulere imene anaipereka mokoma mtima kudzera mwa munthu mmodzi,+ Yesu Khristu, nʼzapamwamba kwambiri. Pogwiritsa ntchito mphatso imeneyi, Mulungu adzapereka madalitso osaneneka kwa anthu ambiri.+ 16 Pali kusiyananso pakati pa mphatso yaulereyi ndi mmene zinthu zinachitikira kudzera mwa munthu mmodzi amene anachimwa.+ Chiweruzo cha tchimo limodzi lija chinabweretsa uchimo kwa onse,+ koma mphatso imene inaperekedwa chifukwa cha machimo ambiri, inachititsa kuti anthu azionedwa kuti ndi olungama.+ 17 Imfa inalamulira ngati mfumu chifukwa cha uchimo wa munthu mmodziyo.+ Koma anthu amene alandira kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu ndiponso mphatso yake yaulere ya chilungamo,+ adzakhala ndi moyo kuti alamulire ngati mafumu+ kudzera mwa munthu mmodziyu, Yesu Khristu.+
18 Choncho, mmene zinakhalira kuti uchimo umodzi unachititsa kuti anthu osiyanasiyana aweruzidwe kuti ndi ochimwa,+ kuchita chinthu chimodzi cholungama kwachititsanso kuti anthu osiyanasiyana+ aonedwe kuti ndi olungama kuti akhale ndi moyo.+ 19 Popeza kusamvera kwa munthu mmodziyo kunachititsa kuti ambiri akhale ochimwa,+ kumvera kwa munthu mmodziyu kudzachititsanso kuti ambiri akhale olungama.+ 20 Chilamulo chinaperekedwa kuti kuchimwa kwa anthu kuonekere.+ Koma pamene uchimo unaonekera, kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu kunawonjezekanso kwambiri. 21 Chifukwa chiyani? Kuti mmene uchimo unalamulira ngati mfumu pamodzi ndi imfa,+ nakonso kukoma mtima kwakukulu kulamulire ngati mfumu kudzera mʼchilungamo. Ndipo zimenezi zidzachititsa kuti anthu apeze moyo wosatha kudzera mwa Yesu Khristu Ambuye wathu.+