Deuteronomo
5 Ndiyeno Mose anaitana Aisiraeli onse nʼkuwauza kuti: “Inu Aisiraeli, mverani malangizo ndi zigamulo zimene ndikukuuzani lero, ndipo muziphunzire ndi kuzitsatira mosamala. 2 Yehova Mulungu wathu anachita nafe pangano ku Horebe.+ 3 Yehova sanachite pangano limeneli ndi makolo athu, koma ndi ife, tonse amene tili pano lero. 4 Yehova analankhula nanu pamasomʼpamaso mʼphiri, kuchokera mʼmoto.+ 5 Ine ndinaima pakati pa Yehova ndi inu pa nthawi imeneyo,+ kuti ndikuuzeni mawu a Yehova. Inuyo simunakwere mʼphirimo chifukwa munkaopa moto.+ Ndiyeno Mulungu anati:
6 ‘Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakutulutsani mʼdziko la Iguputo, mʼnyumba yaukapolo.+ 7 Musakhale ndi milungu ina iliyonse kupatulapo ine.*+
8 Musadzipangire fano kapena chifaniziro+ cha chinthu chilichonse chakumwamba, kapena chapadziko lapansi, kapenanso chamʼmadzi apadziko lapansi. 9 Musaziweramire kapena kuzitumikira,+ chifukwa ine Yehova Mulungu wanu, ndine Mulungu amene ndimafuna kuti anthu azidzipereka kwa ine ndekha,+ amene ndimalanga ana, zidzukulu ndi ana a zidzukuluzo chifukwa cha zolakwa za abambo a anthu odana ndi ine.+ 10 Koma ndimasonyeza chikondi chokhulupirika* kwa anthu mibadwo masauzande amene amandikonda komanso kusunga malamulo anga.
11 Musagwiritse ntchito dzina la Yehova Mulungu wanu molakwika,+ chifukwa Yehova sadzalekerera aliyense wogwiritsa ntchito dzina lake molakwika osamulanga.+
12 Muzisunga tsiku la Sabata ndipo muziliona kuti ndi lopatulika, mogwirizana ndi zimene Yehova Mulungu wanu anakulamulani.+ 13 Muzigwira ntchito zanu zonse masiku 6,+ 14 koma tsiku la 7 ndi sabata la Yehova Mulungu wanu.+ Musamagwire ntchito iliyonse,+ inuyo kapena mwana wanu wamwamuna, mwana wanu wamkazi, kapolo wanu wamwamuna, kapolo wanu wamkazi, ngʼombe yanu yamphongo, bulu wanu, chiweto chanu chilichonse, kapena mlendo amene akukhala mumzinda wanu,+ kuti nayenso kapolo wanu wamwamuna ndi kapolo wanu wamkazi, azipuma mofanana ndi inu.+ 15 Muzikumbukira kuti munali akapolo mʼdziko la Iguputo ndipo Yehova Mulungu wanu anakutulutsani kumeneko ndi dzanja lamphamvu komanso mkono wotambasula.+ Nʼchifukwa chake Yehova Mulungu wanu anakulamulani kuti muzisunga tsiku la Sabata.
16 Muzilemekeza bambo anu ndi mayi anu+ mogwirizana ndi zimene Yehova Mulungu wanu anakulamulani, kuti mukhale ndi moyo nthawi yaitali komanso kuti zinthu zikuyendereni bwino mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani.+
20 Musapereke umboni wonamizira mnzanu.+
21 Musalakelake mkazi wa mnzanu.+ Musalakelake mwadyera nyumba ya mnzanu, munda wake, kapolo wake wamwamuna, kapolo wake wamkazi, ngʼombe yake yamphongo, bulu wake, kapena chinthu chilichonse cha mnzanu.’+
22 Yehova anapereka malamulo* amenewa ku mpingo wanu wonse, mʼphiri. Analankhula mokweza kuchokera mʼmoto ndi mumtambo wakuda+ ndipo pa malamulowo sanawonjezerepo kalikonse. Kenako anawalemba pamiyala iwiri yosema nʼkundipatsa.+
23 Ndiyeno mutangomva mawu amenewo kuchokera pamalo amdima, phiri likuyaka moto,+ atsogoleri onse a mafuko anu ndi akulu onse anabwera kwa ine. 24 Ndiyeno munati, ‘Yehova Mulungu wathu watisonyeza ulemerero wake ndi ukulu wake, ndipo tamva mawu ake kuchokera mʼmoto.+ Lero taona kuti Mulungu angalankhule ndi munthu, munthuyo nʼkukhalabe ndi moyo.+ 25 Koma ife sitikufuna kufa, chifukwa moto waukuluwu ukhoza kutipsereza. Tikapitiriza kumvetsera mawu a Yehova Mulungu wathu ndithu tifa. 26 Kodi pali munthu aliyense amene anamvapo mawu a Mulungu wamoyo, akulankhula kuchokera mʼmoto ngati mmene ife tachitiramu nʼkukhalabe ndi moyo? 27 Iweyo upite pafupi ukamvetsere zonse zimene Yehova Mulungu wathu akanene. Ndiyeno iweyo udzatiuze zonse zimene Yehova Mulungu wathu wakuuza, ndipo ife tidzamvera nʼkuchita zomwezo.’+
28 Choncho Yehova anamva zonse zimene munandiuza, ndipo Yehova anandiuza kuti, ‘Ndamva mawu amene anthu awa akuuza. Zonse zimene anena ndi zabwino.+ 29 Zikanakhala bwino kwambiri akanakhala ndi mtima wondiopa+ ndi kusunga malamulo anga+ nthawi zonse. Akanachita zimenezi zinthu zikanawayendera bwino, iwowo ndi ana awo mpaka kalekale!+ 30 Pita ukawauze kuti: “Bwererani kumatenti anu.” 31 Koma iwe ukhale pompano, ndipo ndikuuza malamulo onse, malangizo ndi zigamulo zimene ukuyenera kuwaphunzitsa kuti azikazitsatira mʼdziko limene ndikuwapatsa kuti likhale lawo.’ 32 Ndipo anthu inu muonetsetse kuti mukuchita zimene Yehova Mulungu wanu wakulamulani.+ Musatembenukire kudzanja lamanja kapena lamanzere.+ 33 Muziyenda mʼnjira imene Yehova Mulungu wanu wakulamulani,+ kuti mukhale ndi moyo, kuti zinthu zikuyendereni bwino komanso kuti mukhale ndi moyo wautali mʼdziko limene mudzalitenge kuti likhale lanu.”+