Chivumbulutso Chimene Yohane Analandira
19 Zimenezi zitatha, ndinamva mawu kumwamba amene ankamveka ngati mawu ofuula a khamu lalikulu akuti: “Tamandani Ya!*+ Mulungu wathu amapulumutsa anthu ndipo ali ndi mphamvu zazikulu komanso ulemerero, 2 chifukwa ziweruzo zake ndi zoona ndi zolungama.+ Iye waweruza hule lalikulu limene linaipitsa dziko lapansi ndi chiwerewere* chake, ndipo walibwezera chifukwa cha magazi a akapolo ake, amene hulelo linapha.”*+ 3 Nthawi yomweyo, ananenanso kachiwiri kuti: “Tamandani Ya!*+ Utsi umene ukufuka chifukwa cha kuwotchedwa kwake udzafuka mpaka kalekale.”+
4 Ndiye akulu 24+ ndi angelo 4 aja,+ anagwada pansi nʼkuwerama ndipo analambira Mulungu amene wakhala pampando wachifumu, nʼkunena kuti: “Ame! Tamandani Ya!”*+
5 Komanso kumpando wachifumu kunamveka mawu akuti: “Muzitamanda Mulungu wathu, inu nonse akapolo ake,+ amene mumamuopa, olemekezeka ndi onyozeka omwe.”+
6 Kenako ndinamva mawu amene ankamveka ngati mawu a khamu lalikulu, ngati mkokomo wa madzi ambiri komanso ngati mabingu amphamvu. Mawuwo anali akuti: “Tamandani Ya!*+ chifukwa Yehova* Mulungu wathu, Wamphamvuyonse,+ wayamba kulamulira monga mfumu!+ 7 Tiyeni tisangalale ndipo tikhale ndi chimwemwe chodzaza tsaya komanso timupatse ulemerero, chifukwa ukwati wa Mwanawankhosa wafika ndipo mkazi wake wadzikongoletsa. 8 Iye waloledwa kuti avale zovala zapamwamba, zonyezimira ndi zoyera bwino, chifukwa zovala zapamwambazo zikuimira ntchito zolungama za oyera.”+
9 Mngeloyo anandiuza kuti, “Lemba kuti: Osangalala ndi amene aitanidwa kuchakudya chamadzulo cha phwando la ukwati wa Mwanawankhosa.”+ Anandiuzanso kuti: “Amenewa ndi mawu oona a Mulungu.” 10 Zitatero ndinagwada pansi nʼkuwerama patsogolo pa mapazi ake kuti ndimulambire. Koma iye anandiuza kuti: “Samala! Usachite zimenezo!+ Inetu ndangokhala kapolo mnzako ndi wa abale ako amene ali ndi ntchito yochitira umboni za Yesu.+ Lambira Mulungu,+ chifukwa cholinga cha maulosi ndi kuchitira umboni zokhudza Yesu.”+
11 Ndinaona kumwamba kutatseguka, kenako ndinaona hatchi yoyera.+ Amene anakwera pahatchiyo dzina lake linali lakuti Wokhulupirika+ ndi Woona.+ Iye amaweruza molungama ndipo akumenya nkhondo mwachilungamo.+ 12 Maso ake anali ngati lawi la moto+ ndipo pamutu pake panali zisoti zachifumu zambiri. Iye analembedwa dzina limene palibe wina aliyense amene akulidziwa koma iye yekha. 13 Iye anavala malaya akunja amene anadonthera* magazi, ndipo amadziwika ndi dzina lakuti Mawu+ a Mulungu. 14 Komanso magulu ankhondo akumwamba ankamutsatira atakwera mahatchi oyera, atavala zovala zapamwamba, zoyera bwino, za mbee! 15 Mʼkamwa mwake munkatuluka lupanga lalitali+ lakuthwa, loti aphere mitundu ya anthu ndipo adzawakusa ndi ndodo yachitsulo.+ Komanso iye ankapondaponda muchopondera mphesa cha mkwiyo waukulu wa Mulungu Wamphamvuyonse.+ 16 Pamalaya ake akunja komanso pantchafu yake, panalembedwa dzina lakuti, Mfumu ya mafumu ndi Mbuye wa ambuye.+
17 Ndinaonanso mngelo ataimirira padzuwa. Iye anafuula ndi mawu okweza kwa mbalame zonse zouluka chapafupi mumlengalenga kuti: “Bwerani kuno, dzasonkhaneni kuphwando lalikulu la Mulungu la chakudya chamadzulo,+ 18 kuti mudzadye minofu ya mafumu, ya akuluakulu a asilikali, ya amuna amphamvu,+ ya mahatchi ndi ya amene akwera pamahatchiwo,+ minofu ya onse, ya mfulu ndi ya akapolo, ya olemekezeka ndi ya onyozeka.”
19 Ndiyeno ndinaona chilombo, mafumu a dziko lapansi ndi asilikali awo atasonkhana pamodzi kuti amenyane ndi amene anakwera pahatchi uja ndi gulu lake lankhondo.+ 20 Koma chilombocho chinagwidwa limodzi ndi mneneri wabodza+ uja, amene anachita zizindikiro pamaso pa chilombocho. Zizindikiro zimenezi anasocheretsa nazo amene analandira chizindikiro cha chilombo+ komanso amene ankalambira chifaniziro chake.+ Onse awiri adakali amoyo, anaponyedwa mʼnyanja ya moto yoyaka ndi sulufule.+ 21 Koma ena onse anaphedwa ndi lupanga lalitali limene linkatuluka mʼkamwa mwa amene anakwera pahatchi+ uja. Ndipo mbalame zonse zinakhuta minofu yawo.+