Yesaya
9 Komabe mdima wake sudzakhala ngati wa pa nthawi imene dzikolo linali m’masautso, ngati kale pamene anthu ankanyoza dziko la Zebuloni ndi dziko la Nafitali.+ Koma patsogolo pake anthu analilemekeza dzikolo,+ dera limene kuli njira ya m’mphepete mwa nyanja, m’chigawo cha Yorodano, ku Galileya kumene kunali kukhala anthu a mitundu ina.+ 2 Anthu amene anali kuyenda mu mdima, aona kuwala kwakukulu.+ Anthu amene anali kukhala m’dziko la mdima wandiweyani,+ kuwala kwawawalira.+ 3 Mwachulukitsa mtundu,+ mwaupangitsa kusangalala kwambiri.+ Iwo asangalala pamaso panu ngati mmene amasangalalira pa nthawi yokolola,+ ngati anthu amene amasangalala akamagawana katundu amene alanda.+
4 Pakuti goli la katundu wawo,+ ndodo yomwe inali pamapewa awo, ndiponso ndodo ya amene anali kuwakusira ku ntchito,+ mwazithyolathyola ngati pa tsiku limene Amidiyani anagonjetsedwa.+ 5 Nsapato iliyonse ya munthu woyenda mwamgugu+ ndi chovala choviikidwa m’magazi, zakhala zoyenera kutenthedwa pamoto ngati nkhuni.+ 6 Pakuti kwa ife kwabadwa mwana.+ Ife tapatsidwa mwana wamwamuna,+ ndipo paphewa pake padzakhala ulamuliro.+ Iye adzapatsidwa dzina lakuti Mlangizi Wodabwitsa,+ Mulungu Wamphamvu,+ Atate Wosatha,+ Kalonga Wamtendere.+ 7 Ulamuliro wake wangati wa kalonga udzafika kutali+ ndipo mtendere sudzatha+ pampando wachifumu wa Davide+ ndiponso mu ufumu wake, kuti iye achititse ufumuwo kukhazikika+ ndi kukhala wolimba pogwiritsa ntchito chilungamo,+ ndiponso pogwiritsa ntchito mtima wowongoka,+ kuyambira panopa mpaka kalekale.* Yehova wa makamu adzachita zimenezi modzipereka kwambiri.+
8 Yehova anatumiza mawu otsutsana ndi Yakobo, ndipo mawuwo anafikira Isiraeli.+ 9 Mawu onsewa anthu adzawadziwa.+ Efuraimu ndi anthu okhala ku Samariya,+ adzawadziwa mawuwo chifukwa cha kudzikweza kwawo ndiponso chifukwa cha mwano wa mumtima mwawo. Pakuti iwo anena kuti:+ 10 “Nyumba za njerwa n’zimene zagwazi, koma ife timanga zina za miyala yosema.+ Mitengo ya mkuyu ndi imene yathyoledwayi, koma m’malo mwake ife tipezerapo mitengo ya mkungudza.”+ 11 Yehova adzakweza adani a Rezini pamwamba kwambiri kuti alimbane naye, ndipo adzalimbikitsa adani a Isiraeli.+ 12 Siriya adzachokera kum’mawa+ ndipo Afilisiti adzachokera kumadzulo.+ Iwo adzadya Isiraeli ndi pakamwa potsegula.+ Chifukwa cha zonsezi, mkwiyo wake sunabwerere, ndipo dzanja lake lidakali lotambasula.+
13 Anthuwo sanabwerere kwa amene akuwamenya+ ndipo sanafunefune Yehova wa makamu,+ 14 chotero Yehova adzadula mutu+ ndi mchira+ wa Isiraeli. Adzadulanso mphukira ndi udzu* tsiku limodzi.+ 15 Munthu wokalamba ndi wolemekezeka kwambiri ndiye mutu,+ ndipo mneneri wopereka malangizo abodza ndiye mchira.+ 16 Amene akutsogolera anthuwa ndiwo amene akuwasocheretsa,+ ndipo amene akutsogoleredwawo ndiwo amene akusokonezedwa.+ 17 N’chifukwa chake Yehova sadzasangalalira ngakhale anyamata awo,+ ndipo sadzamvera chisoni ana awo amasiye* ndi akazi awo amasiye, pakuti onsewo ndi opanduka+ ndi ochita zoipa ndipo pakamwa paliponse pakulankhula zopanda nzeru. Chifukwa cha zonsezi, mkwiyo wake sunabwerere, ndipo dzanja lake lidakali lotambasula.+
18 Pakuti kuipa kwayaka ngati moto,+ ndipo kudzanyeketsa zitsamba zaminga ndi udzu.+ Kuipako kudzayaka m’zitsamba zowirira za m’nkhalango,+ ndipo utsi wa mitengoyo udzakwera m’mwamba kuti tolo!+ 19 Chifukwa cha mkwiyo wa Yehova wa makamu, dzikolo layaka moto ndipo anthu adzakhala ngati chakudya cha motowo.+ Palibe amene adzamvere chisoni aliyense, ngakhale m’bale wake.+ 20 Munthu adzacheka kumbali yake yakumanja, koma adzakhala ndi njala. Adzadya kumanzere kwake, koma sadzakhuta.+ Aliyense adzadya mnofu wa dzanja lake.+ 21 Manase adzadya Efuraimu ndipo Efuraimu adzadya Manase. Awiriwa adzaukira Yuda pamodzi.+ Chifukwa cha zonsezi, mkwiyo wake sunabwerere, ndipo dzanja lake lidakali lotambasula.+