Aroma
12 Chotero ndikukudandaulirani mwa chifundo chachikulu cha Mulungu abale, kuti mupereke matupi anu+ ngati nsembe+ yamoyo,+ yoyera+ ndi yovomerezeka kwa Mulungu,+ ndiyo utumiki wopatulika+ mwa kugwiritsa ntchito luntha la kuganiza.+ 2 Musamatengere+ nzeru za nthawi* ino, koma sandulikani mwa kusintha maganizo anu,+ kuti muzindikire+ chimene chili chifuniro+ cha Mulungu, chabwino, chovomerezeka ndi changwiro.
3 Pakuti mwa kukoma mtima kwakukulu kumene ndinapatsidwa, ndikuuza aliyense wa inu kumeneko kuti musamadziganizire kuposa mmene muyenera kudziganizira.+ Koma aliyense aziganiza m’njira yakuti akhale munthu woganiza bwino,+ malinga ndi chikhulupiriro+ chimene Mulungu wamupatsa.+ 4 Pakuti monga tilili ndi ziwalo zambiri+ m’thupi limodzi, koma ziwalozo sizigwira ntchito yofanana, 5 momwemonso ifeyo, ngakhale kuti ndife ambiri, tili thupi limodzi+ mwa Khristu, ndipo aliyense payekha ndi chiwalo cha mnzake.+ 6 Chotero, popeza kuti tili ndi mphatso zosiyanasiyana+ mogwirizana ndi kukoma mtima kwakukulu+ kumene tinapatsidwa, kaya tili ndi mphatso ya ulosi, tiyeni tilosere malinga ndi chikhulupiriro chimene tapatsidwa. 7 Ngati tili ndi mphatso ya utumiki, tiyeni tichitebe utumikiwo.+ Amene akuphunzitsa,+ aziphunzitsa ndithu.+ 8 Wochenjeza, aike mtima wake pa kuchenjeza.+ Wogawa, agawe mowolowa manja.+ Wotsogolera,+ atsogolere mwakhama. Ndipo wosonyeza chifundo,+ achite zimenezo mokondwa.
9 Chikondi+ chanu chisakhale cha chiphamaso.+ Nyansidwani ndi choipa,+ gwiritsitsani chabwino.+ 10 Pokonda abale,+ khalani ndi chikondi chenicheni pakati panu. Posonyezana ulemu,+ khalani patsogolo. 11 Musakhale aulesi pa ntchito yanu.+ Yakani ndi mzimu.+ Tumikirani Yehova monga akapolo.+ 12 Kondwerani ndi chiyembekezocho.+ Pirirani chisautso.+ Limbikirani kupemphera.+ 13 Gawanani ndi oyera malinga ndi zosowa zawo.+ Khalani ochereza.+ 14 Pitirizani kudalitsa anthu amene amakuzunzani.+ Muzidalitsa,+ osatemberera ayi.+ 15 Sangalalani ndi anthu amene akusangalala.+ Lirani ndi anthu amene akulira. 16 Muziona ena mmene inuyo mumadzionera.+ Musamaganize modzikweza,+ koma khalani ndi mtima wodzichepetsa.+ Musadziyese anzeru.+
17 Musabwezere choipa pa choipa.+ Chitani zimene anthu onse amaziona kuti ndi zabwino. 18 Ngati ndi kotheka, khalani mwamtendere+ ndi anthu onse, monga mmene mungathere. 19 Okondedwa, musabwezere choipa,+ koma siyirani malo mkwiyo wa Mulungu.+ Pakuti Malemba amati: “Kubwezera ndi kwanga, ndidzawabwezera ndine, watero Yehova.”+ 20 Koma “ngati mdani wako ali ndi njala, um’patse chakudya. Ngati ali ndi ludzu, um’patse chakumwa.+ Pakuti mwa kutero udzamuunjikira makala a moto pamutu pake.”+ 21 Musalole kuti choipa chikugonjetseni, koma pitirizani kugonjetsa choipa mwa kuchita chabwino.+