Deuteronomo
4 “Tsopano inu Aisiraeli, mverani malangizo ndi zigamulo zimene ndikukuphunzitsani kuti muzitsatira. Mukatero mudzakhala ndi moyo+ nʼkukalowa mʼdziko limene Yehova Mulungu wa makolo anu akukupatsani kuti mukalitenge nʼkukhala lanu. 2 Musawonjezerepo kalikonse pa mawu amene ndikukulamulani, ndipo musachotsepo kalikonse pa mawu amenewa,+ kuti muzisunga malamulo a Yehova Mulungu wanu amene ndikukupatsani.
3 Inu munaona ndi maso anu zimene Yehova anachita pa nkhani ya Baala wa ku Peori. Yehova Mulungu wanu anawononga pakati panu munthu aliyense amene anatsatira Baala wa ku Peori.+ 4 Koma nonsenu amene mwagwiritsitsa Yehova Mulungu wanu muli ndi moyo lero. 5 Taonani, ndakuuzani malangizo ndi zigamulo,+ mogwirizana ndi zimene Yehova Mulungu wanga wandilamula, kuti muzikatsatira zimenezo mʼdziko limene mukupita kukalitenga kuti likhale lanu. 6 Muzitsatira malangizo ndi zigamulo zimenezi mosamala kwambiri,+ chifukwa mukachita zimenezi mudzasonyeza kuti ndinu anzeru+ komanso ozindikira+ pamaso pa anthu a mitundu ina amene adzamva za malangizo onsewa ndipo adzanena kuti, ‘Mtundu waukulu umenewu ndi wa anthu anzerudi komanso ozindikira.’+ 7 Pajatu Yehova Mulungu wathu amayankha mapemphero athu nthawi zonse. Kodi pali mtundu winanso wamphamvu umene milungu yake ili nawo pafupi chonchi?+ 8 Ndipo ndi mtundu winanso uti wamphamvu umene uli ndi malangizo komanso zigamulo zolungama zofanana ndi Chilamulo chonsechi chimene ndikukupatsani lero?+
9 Koma samalani ndipo mukhale tcheru* kuti musaiwale zinthu zimene maso anu anaona, komanso kuti zinthu zimenezo zisachoke mumtima mwanu masiku onse a moyo wanu. Ana anu ndi zidzukulu zanu muziwauzanso zinthu zimenezo.+ 10 Pa tsiku limene munaima pamaso pa Yehova Mulungu wanu ku Horebe, Yehova anandiuza kuti, ‘Sonkhanitsa anthu kwa ine kuti amve mawu anga,+ nʼcholinga choti aphunzire kundiopa+ masiku onse amene iwo adzakhale ndi moyo padzikoli komanso kuti aphunzitse ana awo.’+
11 Choncho anthu inu munayandikira nʼkuimirira mʼmunsi mwa phiri. Phirilo linkayaka moto umene unkafika kumwamba,* ndipo kunali mdima ndi mtambo wakuda.+ 12 Ndiyeno Yehova anayamba kukulankhulani kuchokera mʼmoto.+ Inu munamva mawu koma simunaone kalikonse.+ Munangomva mawu okha basi.+ 13 Iye anakuuzani pangano lake,+ kapena kuti Malamulo Khumi,*+ amene anakulamulani kuti muziwatsatira. Kenako analemba Malamulowo pamiyala iwiri yosema.+ 14 Pa nthawi imeneyo Yehova anandilamula kuti ndikuphunzitseni malangizo ndi zigamulo, zimene mukuyenera kukazitsatira mukakalowa mʼdziko limene mukukalitenga kuti likhale lanu.
15 Mukhale tcheru,* chifukwa pa tsiku limene Yehova analankhula nanu kuchokera pakati pa moto ku Horebe, simunaone kalikonse mʼmotowo. 16 Choncho musamale kuti musachite zinthu mosakhulupirika popanga chifaniziro chilichonse chosema, chifaniziro cha chinthu chilichonse chachimuna kapena chachikazi,+ 17 chifaniziro cha nyama iliyonse yapadziko lapansi kapena chifaniziro cha mbalame iliyonse youluka mumlengalenga,+ 18 chifaniziro cha chinthu chilichonse chimene chimakwawa panthaka kapena chifaniziro cha nsomba iliyonse yamʼmadzi apansi pa dziko.+ 19 Mukakweza maso anu kuthambo nʼkuona dzuwa, mwezi ndi nyenyezi, gulu lonse la zinthu zakuthambo, musakopeke nazo nʼkuyamba kuzigwadira komanso kuzitumikira.+ Yehova Mulungu wanu wazipereka kwa anthu onse okhala pansi pa thambo lonse. 20 Musachite zimenezo chifukwa Yehova ndi amene anakutengani nʼkukutulutsani mungʼanjo yosungunulira zitsulo, anakutulutsani mu Iguputo, kuti mukhale anthu ake,*+ monga mmene mulili lero.
21 Yehova anandikwiyira chifukwa cha inu,+ ndipo analumbira kuti sadzandilola kuti ndiwoloke Yorodano kapena kupita mʼdziko labwino limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani kuti likhale cholowa chanu.+ 22 Ineyo ndifera mʼdziko lino. Sindiwoloka Yorodano,+ koma inu muwoloka nʼkukatenga dziko labwinoli. 23 Samalani kuti musaiwale pangano la Yehova Mulungu wanu limene anachita ndi inu+ ndipo musapange chifaniziro chosema, chifaniziro cha chinthu chilichonse chimene Yehova Mulungu wanu anakuletsani.+ 24 Chifukwa Yehova Mulungu wanu ndi moto wowononga,+ iye ndi Mulungu amene amafuna kuti anthu azidzipereka kwa iye yekha basi.+
25 Mukakakhala ndi ana komanso zidzukulu ndipo mukakakhala nthawi yaitali mʼdzikomo, nʼkuchita zinthu zokuwonongetsani popanga chifaniziro chosema+ cha chinthu chilichonse, nʼkuchita choipa pamaso pa Yehova Mulungu wanu, moti nʼkumukhumudwitsa,+ 26 ndikutenga kumwamba ndi dziko lapansi lero monga mboni zokutsutsani, kuti mudzafa mwamsanga mʼdziko limene mukupita kukalitenga mutawoloka Yorodano. Simudzakhala mʼdzikomo kwa nthawi yaitali chifukwa mudzawonongedwa ndithu.+ 27 Yehova adzakubalalitsani pakati pa anthu a mitundu ina,+ ndipo anthu ochepa okha pakati panu ndi amene adzapulumuke+ mʼmayiko a mitundu imene Yehova adzakuthamangitsireni. 28 Kumeneko mudzatumikira milungu yamtengo ndi mwala, yopangidwa ndi manja a anthu,+ milungu imene singaone, kumva, kudya kapena kununkhiza.
29 Mukadzafufuza Yehova Mulungu wanu muli kumeneko, mukadzamufunafuna ndi mtima wanu wonse komanso moyo wanu wonse, mudzamupezadi.+ 30 Pamapeto pake, zinthu zonsezi zikadzakuchitikirani nʼkukhala pamavuto aakulu, mudzabwerera kwa Yehova Mulungu wanu ndipo mudzamvera mawu ake.+ 31 Pajatu Yehova Mulungu wanu ndi Mulungu wachifundo.+ Sadzakusiyani kapena kukuwonongani kapenanso kuiwala pangano limene analumbira kwa makolo anu.+
32 Tafunsani tsopano, za masiku akale inu musanakhalepo, kuchokera pa tsiku limene Mulungu analenga munthu padziko lapansi. Mufufuze kuchokera kumalekezero a thambo kukafika kumalekezero ena a thambo. Kodi zinthu zazikulu ngati zimenezi zinayamba zachitikapo, kapena kodi pali amene anamvapo zinthu ngati zimenezi?+ 33 Kodi pali anthu enanso amene anamvapo mawu a Mulungu akumveka kuchokera pamoto ngati mmene inuyo munawamvera nʼkukhalabe ndi moyo?+ 34 Kapena kodi Mulungu anayamba wapitapo kukatenga mtundu wa anthu kuti ukhale wake kuchokera pakati pa mtundu wina pogwiritsa ntchito ziweruzo,* zizindikiro, zodabwitsa,+ nkhondo,+ dzanja lamphamvu,+ mkono wotambasula komanso zinthu zoopsa+ zofanana ndi zimene Yehova Mulungu wanu anakuchitirani ku Iguputo inu mukuona? 35 Inuyo mwasonyezedwa zinthu zimenezi kuti mudziwe kuti Yehova ndi Mulungu woona.+ Palibenso Mulungu wina kupatulapo iyeyo.+ 36 Anakuchititsani kuti mumve mawu ake kuchokera kumwamba nʼcholinga chakuti akulangizeni kuti muzimumvera. Padziko lapansi pano, iye anakuchititsani kuti muone moto waukulu, ndipo munamva mawu ake kuchokera pamotowo.+
37 Chifukwa choti ankakonda makolo anu ndipo anasankha mbadwa* zawo zobwera pambuyo pawo,+ anakutulutsani ku Iguputo ndi mphamvu zake zazikulu ndipo ankakuyangʼanirani. 38 Anachotsa pamaso panu mitundu yaikulu ndi yamphamvu kuposa inu, kuti akulowetseni mʼdziko lawo nʼkukupatsani kuti likhale cholowa chanu ngati mmene zilili lero.+ 39 Choncho mudziwe lero, ndipo muzikumbukira mumtima mwanu kuti Yehova ndi Mulungu woona, kumwamba ndiponso padziko lapansi.+ Palibenso wina.+ 40 Muzisunga malangizo ndi malamulo ake amene ndikukulamulani lero kuti zikuyendereni bwino, inuyo ndi ana anu obwera pambuyo panu, kuti mukhale kwa nthawi yaitali mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani.”+
41 Pa nthawi imeneyo, Mose anapatula mizinda itatu mbali yakumʼmawa kwa Yorodano.+ 42 Ngati munthu wapha mnzake mwangozi ndipo sanayambe wadanapo naye,+ munthu ameneyu azithawira ku umodzi mwa mizinda imeneyi kuti akhale ndi moyo.+ 43 Mizinda yake ndi Bezeri,+ mʼchipululu chimene chili mʼdera lokwererapo, woti anthu a fuko la Rubeni azithawirako. Mzinda wa Ramoti+ ku Giliyadi, woti anthu a fuko la Gadi azithawirako ndi mzinda wa Golani+ ku Basana, woti anthu a fuko la Manase+ azithawirako.
44 Tsopano Chilamulo+ chimene Mose anaika pamaso pa Aisiraeli ndi ichi. 45 Chilamulocho ndi zikumbutso, malangizo ndi zigamulo zimene Mose anapatsa Aisiraeli atatuluka mu Iguputo.+ 46 Anawapatsa zimenezi ali pafupi ndi Yorodano, mʼchigwa, moyangʼanizana ndi Beti-peori.+ Dera limeneli ndi dziko la Mfumu Sihoni ya Aamori, imene inkakhala ku Hesiboni+ ndipo Mose ndi Aisiraeli anaigonjetsa atatuluka mu Iguputo.+ 47 Iwo anamulanda dziko lakelo komanso dziko la Ogi+ mfumu ya Basana. Amenewa ndi mafumu awiri a Aamori amene anali kuchigawo chakumʼmawa kwa Yorodano. 48 Dera limeneli linayambira ku Aroweli+ mʼmphepete mwa chigwa cha Arinoni* mpaka kuphiri la Sione, limene ndi phiri la Herimoni,+ 49 ndiponso dera lonse la Araba mʼchigawo chakumʼmawa kwa Yorodano, mpaka ku Nyanja ya Araba,* mʼmunsi mwa zitunda za Pisiga.+