Kalata Yopita kwa Aroma
1 Ine Paulo kapolo wa Khristu Yesu, ndinaitanidwa kuti ndikhale mtumwi ndiponso ndinasankhidwa kuti ndilalikire uthenga wabwino wa Mulungu.+ 2 Iye analonjeza uthenga umenewu kalekale kudzera mwa aneneri ake mʼMalemba oyera. 3 Uthengawo umanena za Mwana wake, amene ndi mbadwa* ya Davide,+ 4 ndipo Mulungu anaukitsa Mwana+ wakeyu pogwiritsa ntchito mphamvu ya mzimu wake woyera. Ameneyu ndi Yesu Khristu Ambuye wathu. 5 Kudzera mwa iyeyu, Mulungu anatisonyeza kukoma mtima kwakukulu ndipo ndinasankhidwa kukhala mtumwi+ kuti ndikathandize anthu a mitundu yonse kuti asonyeze chikhulupiriro, akhale omvera+ ndiponso kuti alemekeze dzina lake. 6 Pakati pa anthu a mitundu imeneyo palinso inuyo amene munaitanidwa kuti mukhale otsatira a Yesu Khristu. 7 Kalatayi ndalembera inu nonse okhala ku Roma amene mumakondedwa ndi Mulungu komanso munaitanidwa kuti mukhale oyera:
Mukhale ndi kukoma mtima kwakukulu ndiponso mtendere wochokera kwa Mulungu Atate wathu ndi Ambuye wathu Yesu Khristu.
8 Choyamba, ndikuthokoza Mulungu wanga kudzera mwa Yesu Khristu chifukwa cha nonsenu, chifukwa anthu padziko lonse akunena za chikhulupiriro chanu. 9 Nthawi zonse ndikamapemphera ndimakutchulani mʼmapemphero anga ndipo Mulungu, amene ndikumuchitira utumiki wopatulika ndi mtima wanga wonse polalikira uthenga wabwino wonena za Mwana wake, akundichitira umboni.+ 10 Ndimamupempha kuti ngati nʼkotheka komanso ngati nʼzimene akufuna, ulendo uno wokha ndibwere kwanuko. 11 Chifukwa ndikulakalaka nditakuonani kuti ndikupatseni mphatso inayake yauzimu kuti mukhale olimba, 12 kapena kuti ndidzalimbikitsidwe ndi chikhulupiriro chanu, nanunso mudzalimbikitsidwe+ ndi chikhulupiriro changa.
13 Koma abale ndikufuna mudziwe kuti kwa nthawi yaitali ndakhala ndikufuna kubwera kwanuko, koma zakhala zikulephereka. Ndikufuna ndidzaone zotsatira zabwino za ntchito yathu yolalikira ngati mmene zilili pakati pa anthu a mitundu ina yonse. 14 Ineyo ndili ndi ngongole kwa Agiriki ndi kwa anthu amene si Agiriki komanso kwa anthu anzeru ndi kwa anthu opusa. 15 Choncho ndikufunitsitsa kudzalalikira uthenga wabwino kwa inunso kumeneko ku Roma.+ 16 Ine sindichita manyazi ndi uthenga wabwino.+ Kunena zoona, uthengawo ndi njira yamphamvu imene Mulungu akuigwiritsa ntchito pofuna kupulumutsa aliyense amene ali ndi chikhulupiriro,+ choyamba Ayuda+ kenako Agiriki.+ 17 Mu uthenga wabwinowu, Mulungu amaulula chilungamo chake kwa anthu amene ali ndi chikhulupiriro.+ Zikatero, chikhulupiriro cha anthuwo chimalimba mogwirizana ndi zimene Malemba amanena kuti: “Koma wolungama adzakhala ndi moyo chifukwa cha chikhulupiriro chake.”+
18 Kuchokera kumwamba, Mulungu akusonyeza mkwiyo wake+ kwa anthu onse osaopa Mulungu ndi ochita zoipa amene akuchititsa kuti choonadi chisadziwike.+ 19 Zili choncho chifukwa Mulungu wawapatsa umboni wokwanira wowathandiza kuti amudziwe.+ 20 Kuchokera pamene dziko linalengedwa, makhalidwe a Mulungu osaoneka ndi maso akuonekera bwino. Makhalidwe a Mulungu amenewa,+ ngakhalenso mphamvu zake zosatha+ ndiponso Umulungu wake,+ zikuonekera mʼzinthu zimene anapanga moti anthuwo alibenso chifukwa chomveka chosakhulupirira kuti kuli Mulungu. 21 Ngakhale kuti ankadziwa Mulungu, iwo sanamulemekeze monga Mulungu komanso sanamuthokoze. Mʼmalomwake anayamba kuganiza zinthu zopanda nzeru ndipo mitima yawo yopusayo inachita mdima.+ 22 Ngakhale amanena kuti ndi anzeru, iwo ndi opusa. 23 Mʼmalo molemekeza Mulungu yemwe sangafe, iwo amalemekeza zifaniziro za anthu omwe amafa komanso zifaniziro za mbalame, nyama za miyendo 4 ndiponso nyama zokwawa.+
24 Choncho mogwirizana ndi zilakolako zamʼmitima mwawo, Mulungu anawasiya kuti achite zonyansa, kuti achite zochititsa manyazi ndi matupi awo. 25 Choonadi chonena za Mulungu anachisinthanitsa ndi bodza ndipo amalambira ndiponso kutumikira chilengedwe mʼmalo mwa Mlengi amene ayenera kutamandidwa mpaka kalekale. Ame. 26 Ndiye chifukwa chake Mulungu anawasiya kuti atsatire zilakolako zosalamulirika za kugonana,+ popeza akazi pakati pawo anasiya njira yachibadwa ya matupi awo nʼkumachita zosemphana ndi chibadwa.+ 27 Amunanso chimodzimodzi. Iwo anasiya njira yachibadwa yofuna akazi nʼkumatenthetsana okhaokha mwachiwawa ndi chilakolako choipa, amuna okhaokha+ kuchitirana zonyansa nʼkulandiriratu mphoto yoyenerera kulakwa kwawo.+
28 Popeza sankaona kuti nʼzofunika kudziwa Mulungu molondola, iye anawasiya kuti apitirize kuganiza zoipa nʼkumachita zinthu zosayenera.+ 29 Ndipo ankachita zosalungama za mtundu ulionse,+ kuipa konse, dyera*+ ndiponso zinthu zonse zoipa. Mtima wawo unadzaza ndi kaduka,+ kupha anthu,+ ndewu, chinyengo+ ndi njiru.+ Ankakondanso miseche 30 ndiponso kujeda anzawo.+ Ankadana ndi Mulungu, anali achipongwe, odzikuza, odzitama, achiwembu, osamvera makolo,+ 31 osazindikira,+ osasunga mapangano, opanda chikondi chachibadwa ndiponso opanda chifundo. 32 Ngakhale kuti anthuwa amalidziwa bwino lamulo lolungama la Mulungu, lakuti amene amachita zinthu zimenezi ndi oyenera imfa,+ amapitiriza kuzichita. Kuwonjezera pamenepo, amagwirizananso ndi anthu amene amachita zimenezi.