Chivumbulutso Chimene Yohane Analandira
3 “Kwa mngelo wa mpingo wa ku Sade lemba kuti: Izi ndi zimene akunena iye amene ali ndi mizimu 7 ya Mulungu+ ndi nyenyezi 7:+ ‘Ndikudziwa ntchito zako, anthu amaona ngati uli ndi moyo, koma kwenikweni ndiwe wakufa.+ 2 Khala maso,+ ndipo limbikitsa otsala amene atsala pangʼono kufa, chifukwa ndapeza kuti ntchito zako sizinachitidwe mokwanira pamaso pa Mulungu wanga. 3 Choncho, pitiriza kukumbukira zimene unalandira ndi zimene unamva. Pitiriza kuzitsatira ndipo ulape.+ Ndithudi, ukapanda kudzuka, ndidzabwera ngati wakuba+ ndipo sudzadziwa ngakhale pangʼono ola limene ndidzafike kwa iwe.+
4 Ngakhale zili choncho, uli ndi anthu angapo* mu Sade amene sanadetse zovala zawo+ ndipo adzayenda ndi ine atavala zovala zoyera,+ chifukwa ndi oyenerera. 5 Choncho amene wapambana pankhondo+ adzavekedwa zovala zoyera+ ndipo sindidzafufuta dzina lake mʼbuku la moyo.+ Koma ndidzavomereza dzina lake pamaso pa Atate wanga ndi pamaso pa angelo ake.+ 6 Amene ali ndi makutu amve zimene mzimu ukunena ku mipingo.’
7 Kwa mngelo wa mpingo wa ku Filadefiya lemba kuti: Izi ndi zimene akunena woyerayo,+ amene ndi woona,+ yemwe ali ndi kiyi wa Davide.+ Iye amene amati akatsegula palibe amene angatseke, ndipo akatseka palibe amene angatsegule. 8 ‘Ndikudziwa ntchito zako. Taona! Ndatsegula khomo pamaso pako+ limene wina sangalitseke. Ndikudziwa kuti uli ndi mphamvu zochepa ndiponso kuti unasunga mawu anga. Ndikudziwanso kuti wakhala wokhulupirika ku dzina langa. 9 Taona! Anthu ochokera mʼsunagoge wa Satana, amene amanama kuti ndi Ayuda pamene si Ayuda,+ ndidzawachititsa kuti abwere kudzagwada nʼkuwerama pamapazi ako. Ndipo ndidzawachititsa kuti adziwe kuti ndimakukonda. 10 Chifukwa chakuti unasunga mawu onena za kupirira kwanga,*+ inenso ndidzakuteteza pa ola la kuyesedwa+ limene likubwera padziko lonse lapansi kumene kuli anthu. Ndidzakuteteza pa ola limene likubwera kudzayesa anthu amene akukhala padziko lapansi. 11 Ndikubwera mofulumira.+ Pitiriza kugwira mwamphamvu chimene uli nacho, kuti wina asakulande mphoto* yako.+
12 Amene wapambana pankhondo, ndidzamuika kuti akhale mzati mʼkachisi wa Mulungu wanga ndipo sadzachokamonso. Ndidzalemba pachipumi pake dzina la Mulungu wanga+ ndiponso dzina la mzinda wa Mulungu wanga, womwe ndi Yerusalemu Watsopano,+ amene akutsika kuchokera kumwamba kwa Mulungu wanga. Ndidzamulembanso dzina langa latsopano.+ 13 Amene ali ndi makutu amve zimene mzimu ukunena ku mipingo.’
14 Kwa mngelo wa mpingo wa ku Laodikaya,+ lemba kuti: Izi ndi zimene Ame+ akunena, yemwe ndi mboni+ yokhulupirika komanso yoona,+ woyamba wa chilengedwe cha Mulungu.+ 15 ‘Ndikudziwa ntchito zako, kuti si iwe wozizira kapena wotentha. Ndikanakonda ukanakhala wozizira kapena wotentha. 16 Koma chifukwa choti ndiwe wofunda, osati wotentha+ kapena wozizira,+ ndikulavula mʼkamwa mwanga. 17 Iwe ukunena kuti: “Ndine wolemera,+ ndapeza chuma chambiri ndipo sindikusowa kanthu,” koma sukudziwa kuti ndiwe wovutika, womvetsa chisoni, wosauka, wakhungu ndiponso wamaliseche. 18 Choncho ndikukulangiza kuti ugule kwa ine golide woyengedwa ndi moto, kuti ukhale wolemera. Ugulenso zovala zoyera kuti uvale, nʼcholinga choti maliseche ako asaonekere nʼkuchita manyazi.+ Ndiponso ugule mankhwala opaka mʼmaso ako+ kuti uone.+
19 Onse amene ndimawakonda, ndimawadzudzula komanso kuwalanga.+ Choncho khala wodzipereka ndipo ulape.+ 20 Taona! Ndaima pakhomo ndipo ndikugogoda. Wina akamva mawu anga nʼkutsegula chitseko, ndidzalowa mʼnyumba mwake ndipo iye ndi ine tidzadyera limodzi chakudya chamadzulo. 21 Amene wapambana pankhondo+ ndidzamulola kuti akhale ndi ine pampando wanga wachifumu,+ ngati mmene ine ndinakhalira+ ndi Atate wanga pampando wawo wachifumu nditapambana pankhondo. 22 Amene ali ndi makutu amve zimene mzimu ukunena ku mipingo.’”