Kalata yachiwiri yopita kwa Timoteyo
1 Ine Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu mwakufuna kwa Mulungu, mogwirizana ndi lonjezo la moyo umene tingapeze chifukwa chokhala otsatira a Khristu Yesu,+ 2 ndikulembera iwe Timoteyo mwana wanga wokondedwa:+
Kukoma mtima kwakukulu, chifundo ndi mtendere zochokera kwa Atate wathu Mulungu, ndi kwa Khristu Yesu Ambuye wathu, zikhale nawe.
3 Ndikuthokoza Mulungu amene ndikumuchitira utumiki wopatulika ngati mmene makolo anga akale anachitira. Ndikuuchita ndi chikumbumtima choyera ndipo sindiiwala kukutchula mʼmapemphero anga opembedzera, usana ndi usiku. 4 Ndikakumbukira misozi yako ndimalakalaka kukuona kuti ndidzasangalale kwambiri. 5 Chifukwa ndikukumbukira chikhulupiriro chako chopanda chinyengo,+ chimene anayamba kukhala nacho ndi agogo ako aakazi a Loisi komanso amayi ako a Yunike, ndipo ndikukhulupirira kuti iwenso uli nacho.
6 Chifukwa cha zimenezi, ndikukukumbutsa kuti mphatso ya Mulungu imene uli nayo, yomwe unailandira pamene ndinaika manja pa iwe,+ uikolezere ngati moto. 7 Chifukwatu Mulungu sanatipatse mzimu wamantha,+ koma wamphamvu,+ wachikondi ndi woti tiziganiza bwino. 8 Choncho usachite manyazi ndi ntchito yolalikira za Ambuye wathu,+ kapena kuchita manyazi ndi ineyo amene ndine mkaidi chifukwa cha iye. Koma khala wokonzeka kuvutika+ chifukwa cha uthenga wabwino ndipo uzidalira mphamvu ya Mulungu.+ 9 Iye anatipulumutsa ndiponso anatiitana kuti tikhale oyera,+ osati chifukwa cha ntchito zathu, koma chifukwa cha cholinga chake ndi kukoma mtima kwake kwakukulu.+ Mulungu anatisonyeza kukoma mtimaku kalekale chifukwa cha Khristu Yesu. 10 Koma tsopano izi zatsimikizirika chifukwa cha kuonekera kwa Mpulumutsi wathu Khristu Yesu,+ amene wathetsa mphamvu za imfa.+ Komanso pogwiritsa ntchito uthenga wabwino,+ watidziwitsa mmene tingapezere moyo+ wosawonongeka.+ 11 Ndipo ndinasankhidwa kuti ndikhale mlaliki, mtumwi ndi mphunzitsi+ wa uthenga wabwinowu.
12 Nʼchifukwa chake ndikuvutika chonchi,+ koma sindikuchita manyazi.+ Ndikudziwa amene ndikumukhulupirira, ndipo sindikukayikira kuti adzateteza zonse zimene ndamupatsa mpaka tsiku lachiweruzo.+ 13 Gwiritsitsabe chitsanzo cha mawu olondola+ amene unawamva kwa ine pamene ukusonyeza chikhulupiriro ndi chikondi zomwe timakhala nazo chifukwa chogwirizana ndi Khristu Yesu. 14 Usunge chuma chapadera chimene unapatsidwachi. Uchisunge mothandizidwa ndi mzimu woyera umene tili nawo.+
15 Iwe ukudziwa kuti anthu onse mʼchigawo cha Asia+ andisiya. Ena mwa anthuwa ndi Fugelo ndi Heremogene. 16 Ambuye achitire chifundo banja la Onesiforo,+ chifukwa ankabwera kawirikawiri kudzandilimbikitsa, ndipo sanachite manyazi ndi maunyolo anga. 17 Moti pamene anali ku Roma, anandifunafuna mwakhama mpaka anandipeza. 18 Ambuye Yehova* adzamuchitire chifundo pa tsiku lachiweruzo. Iwe ukudziwa bwino za utumiki wonse umene anachita ku Efeso.