Miyambo
5 Mwana wanga, tchera makutu ako ku mawu anga anzeru.
Mvetsera mosamala zimene ndikukuphunzitsa zokhudza kukhala wozindikira,+
2 Kuti uteteze luso lako loganiza bwino,
Ndiponso kuti milomo yako iteteze kudziwa zinthu.+
3 Chifukwa milomo ya mkazi wamakhalidwe oipa* imakha uchi ngati chisa cha njuchi,+
Ndipo mʼkamwa mwake ndi mosalala kuposa mafuta.+
4 Koma pamapeto pake amawawa kwambiri ngati chitsamba chowawa.+
Ndipo amakhala wakuthwa ngati lupanga lakuthwa konsekonse.+
5 Mapazi ake amatsikira ku imfa.
Miyendo yake imalowera ku Manda.*
6 Iye saganizira zimene zingamuthandize kukapeza moyo.
Amangoyendayenda, osadziwa kumene akulowera.
8 Ukhale kutali kwambiri ndi iye.
Usayandikire pakhomo la nyumba yake,+
9 Kuti usapereke ulemu wako kwa anthu ena+
Komanso kuti usakumane ndi mavuto mʼzaka zotsala za moyo wako.*+
10 Ndiponso kuti alendo asakuwonongere zinthu zako,*+
Komanso kuti zinthu zimene unazipeza movutikira zisapite kunyumba ya mlendo.
11 Ukapanda kumvera, udzabuula kumapeto kwa moyo wako,
Mphamvu zako zikadzatha komanso ukadzawonda kwambiri.+
Ndipo mtima wanga sunkamvera, ena akandidzudzula.
13 Sindinamvere mawu a alangizi anga,
Kapena kutchera khutu kwa aphunzitsi anga.
18 Kasupe wako akhale wodalitsidwa,*
Ndipo uzisangalala ndi mkazi amene unamukwatira udakali wachinyamata.+
19 Iye akhale ngati mbawala yaikazi yachikondi komanso ngati kamwana ka mbuzi zamʼmapiri kokongola.+
Mabere ake azikukhutiritsa* nthawi zonse.
Chikondi chake chizikusangalatsa kwambiri nthawi zonse.+
20 Ndiye mwana wanga, kodi pali chifukwa chilichonse choti uzisangalalira ndi mkazi wamakhalidwe oipa,*
Kapena choti uzikumbatirira chifuwa cha mkazi wachiwerewere?*+
21 Chifukwa maso a Yehova amaona chilichonse chimene munthu akuchita,
Ndipo iye amafufuza njira zake zonse.+
23 Iye adzafa chifukwa chosamvera malangizo,
Ndipo adzasochera chifukwa cha kuchuluka kwa uchitsiru wake.