Kalata Yoyamba ya Petulo
5 Choncho, ine monga mkulu mnzanu, amene ndinaona mmene Khristu anavutikira komanso ndikuyembekezera kudzalandira nawo ulemerero umene udzaonekere,+ ndikupempha akulu amene ali pakati panu kuti: 2 Wetani gulu la nkhosa za Mulungu+ zomwe zili mʼmanja mwanu. Monga oyangʼanira, muzigwira ntchito yanu, osati mokakamizika koma mofunitsitsa monga atumiki a Mulungu.+ Muziigwira ndi mtima wonse, osati chifukwa chofuna kupindulapo kenakake.+ 3 Musamachite zinthu ngati mafumu pakati pa anthu a Mulungu,*+ koma muzipereka chitsanzo chabwino kwa gulu la nkhosa.+ 4 Ndipo mʼbusa wamkulu+ akadzaonekera, mudzalandira mphoto* yosawonongeka yomwe ndi yaulemerero.+
5 Chimodzimodzinso inu achinyamata, muzigonjera amuna achikulire.*+ Komanso nonsenu muzichitirana zinthu modzichepetsa* chifukwa Mulungu sasangalala ndi anthu odzikuza. Koma anthu odzichepetsa amawasonyeza kukoma mtima kwake kwakukulu.+
6 Choncho dzichepetseni pamaso pa Mulungu wathu wamphamvu* kuti adzakukwezeni nthawi yake ikadzakwana.+ 7 Muzichita zimenezi pamene mukumutulira nkhawa zanu zonse,+ chifukwa amakufunirani zabwino.+ 8 Khalanibe oganiza bwino ndipo khalani tcheru+ chifukwa mdani wanu Mdyerekezi akuyendayenda ngati mkango wobangula, kuti ameze winawake.*+ 9 Choncho mukhale ndi chikhulupiriro cholimba ndipo mulimbane naye,+ podziwa kuti abale anu padziko lonse akukumananso ndi mavuto ngati omwewo.+ 10 Mukavutika kwa nthawi yochepa, Mulungu yemwe amasonyeza kukoma mtima konse kwakukulu, amenenso anakuitanani kuti mukhale ogwirizana ndi Khristu komanso kuti mulandire ulemerero wosatha,+ adzamalizitsa kukuphunzitsani. Iye adzakupatsani mphamvu,+ adzakuthandizani kuti mukhalebe okhulupirika+ komanso adzakulimbitsani. 11 Mphamvu ndi zake mpaka muyaya. Ame.
12 Ndakulemberani kalata yachiduleyi kudzera mwa Silivano,*+ mʼbale amene ndikumuona kuti ndi wokhulupirika. Ndakulemberani zimenezi kuti ndikulimbikitseni ndi kukutsimikizirani kuti kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu nʼkumeneku, ndipo mukugwire mwamphamvu. 13 Mayi* amene ali ku Babulo, yemwe Mulungu anamusankha mwapadera ngati inuyo, komanso mwana wanga Maliko,+ akupereka moni. 14 Patsanani moni mwachikondi.*
Nonse amene muli ogwirizana ndi Khristu, mukhale ndi mtendere.