Machitidwe a Atumwi
4 Pamene Petulo ndi Yohane ankalankhula ndi anthuwo, ansembe, woyangʼanira kachisi ndiponso Asaduki+ anafika. 2 Iwo anakwiya chifukwa atumwiwo ankaphunzitsa anthu ndiponso kulalikira mosapita mʼmbali zoti Yesu anaukitsidwa.+ 3 Choncho anawagwira nʼkuwatsekera mʼndende+ mpaka tsiku lotsatira, chifukwa kunali kutada kale. 4 Koma anthu ambiri amene anamvetsera mawu awo anakhulupirira, ndipo chiwerengero cha amuna chinakwana pafupifupi 5,000.+
5 Tsiku lotsatira, olamulira ndi akulu ndiponso alembi anasonkhana ku Yerusalemu. 6 Panalinso Anasi+ wansembe wamkulu, Kayafa,+ Yohane, Alekizanda ndiponso anthu onse omwe anali achibale a wansembe wamkuluyo. 7 Ndiyeno anaimika Petulo ndi Yohane pakati pawo nʼkuyamba kuwafunsa kuti: “Kodi mphamvu zochitira zimenezi mwazitenga kuti, kapena mwachita izi mʼdzina la ndani?” 8 Petulo, atadzazidwa ndi mzimu woyera,+ anawayankha kuti:
“Inu olamulira ndiponso akulu, 9 ngati lero tikufunsidwa pa zinthu zabwino zimene tachitira munthu wolumalayu+ ndipo mukufuna kudziwa kuti wamuchiritsa ndi ndani, 10 dziwani nonsenu ndi Aisiraeli onse, kuti mʼdzina la Yesu Khristu wa ku Nazareti uja,+ amene inu munamuphera pamtengo,+ koma amene Mulungu anamuukitsa,+ kudzera mwa iyeyo munthuyu waima patsogolo panu ali bwinobwino. 11 Yesu ameneyu ndi ‘mwala umene inu omanga nyumba munauona ngati wopanda pake, umene tsopano wakhala mwala wofunika kwambiri wapakona.’+ 12 Ndiponso palibe munthu aliyense amene angatipulumutse, chifukwa palibe dzina lina+ padziko lapansi limene laperekedwa kwa anthu, lomwe lingatipulumutse.”+
13 Ataona kuti Petulo ndi Yohane akulankhula molimba mtima komanso atakumbukira kuti anali osaphunzira* ndiponso anthu wamba,+ anadabwa kwambiri. Ndipo anazindikira kuti ankayenda ndi Yesu.+ 14 Ndiyeno popeza munthu wochiritsidwa uja anali ataimanso pomwepo,+ iwo anasowa chonena.+ 15 Choncho anawalamula kuti atuluke muholo ya Khoti Lalikulu la Ayuda,* ndipo anayamba kukambirana 16 kuti: “Titani nawo anthu amenewa?+ Chifukwa kunena zoona, iwo achita chizindikiro chachikulu moti anthu onse a ku Yerusalemu aona.+ Ndipo ife sitingatsutse zimenezi. 17 Choncho kuti nkhaniyi isapitirire kufalikira kwa anthu ena, tiyeni tiwaopseze nʼkuwauza kuti asalankhulenso mʼdzina limeneli kwa munthu wina aliyense.”+
18 Atatero anawaitana nʼkuwalamula kuti asalankhulenso kapena kuphunzitsa mʼdzina la Yesu. 19 Koma Petulo ndi Yohane anawayankha kuti: “Weruzani nokha, ngati nʼzoyenera pamaso pa Mulungu kumvera inu mʼmalo momvera Mulunguyo. 20 Koma ife sitingasiye kulankhula za zinthu zimene tinaziona ndi kuzimva.”+ 21 Choncho atawaopsezanso, anawamasula, popeza sanapeze chifukwa chilichonse chowapatsira chilango. Komanso ankaopa anthu,+ poti onse ankatamanda Mulungu chifukwa cha zimene zinachitikazo. 22 Chifukwatu munthu amene anachiritsidwa modabwitsayu anali wazaka zoposa 40.
23 Atawamasula anapita kwa okhulupirira anzawo, ndipo anawafotokozera zonse zimene ansembe aakulu ndi akulu anawauza. 24 Atamva zimenezi, onse pamodzi anafuula kwa Mulungu kuti:
“Ambuye Wamkulu Koposa, inu ndi amene munapanga kumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zimene zimakhala mmenemo.+ 25 Pogwiritsa ntchito mzimu woyera, inu munanena kudzera pakamwa pa kholo lathu Davide+ mtumiki wanu kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani anthu a mitundu ina akuchita chipolowe ndiponso nʼchifukwa chiyani mitundu ya anthu ikuganizira* zinthu zopanda pake? 26 Mafumu a dziko lapansi anaima pamalo awo, ndipo olamulira anasonkhana mogwirizana kuti alimbane ndi Yehova* komanso wodzozedwa* wake.’+ 27 Zimenezi zinachitikadi pamene Herode, Pontiyo Pilato,+ anthu a mitundu ina komanso anthu a mu Isiraeli, anasonkhana mumzindawu nʼkuukira Yesu, mtumiki wanu woyera, amene inu munamudzoza.+ 28 Anasonkhana kuti achite zimene munaneneratu. Zimenezi zinachitika chifukwa inu muli ndi mphamvu komanso chifukwa zinali zogwirizana ndi chifuniro chanu.+ 29 Koma tsopano Yehova,* imvani mmene akutiopsezera ndipo tithandizeni ife akapolo anu kuti tipitirize kulankhula mawu anu molimba mtima. 30 Pitirizani kuchiritsa anthu ndi dzanja lanu komanso kuthandiza kuti zodabwitsa zipitirize kuchitika+ mʼdzina la Yesu, mtumiki wanu woyera.”+
31 Atamaliza kupemphera mochonderera, malo amene anasonkhanawo anagwedezeka. Kenako onse anadzazidwa ndi mzimu woyera+ ndipo anayamba kulankhula mawu a Mulungu molimba mtima.+
32 Komanso, onse amene anakhulupirira anali ndi maganizo ofanana.* Panalibe aliyense amene ankanena kuti zinthu zimene anali nazo zinali zayekha. Zonse zimene anali nazo zinali za onse.+ 33 Komanso, atumwiwo anapitiriza kuchitira umboni mwamphamvu kwambiri za kuuka kwa Ambuye Yesu.+ Ndipo Mulungu ankawasonyeza onsewo kukoma mtima kwakukulu. 34 Ndipotu panalibe aliyense amene ankasowa kanthu.+ Onse amene anali ndi minda kapena nyumba, ankagulitsa nʼkubweretsa ndalamazo. 35 Ndipo ankazipereka kwa atumwi.+ Ndiyeno ndalamazo ankazigawa kwa aliyense mogwirizana ndi zimene ankafunikira.+ 36 Choncho Yosefe, amene atumwiwo anamupatsa dzina lakuti Baranaba,+ kutanthauza “Mwana Wotonthoza,” amenenso anali Mlevi wobadwira ku Kupuro, 37 anali ndi munda. Iye anagulitsa mundawo nʼkubweretsa ndalamazo kudzazipereka kwa atumwi.+