2 Akorinto
3 Kodi tikuyambanso kudzichitira umboni tokha?+ Kapena kodi n’kofunika kuti ifenso, mofanana ndi anthu ena, tikhale ndi makalata+ otichitira umboni kwa inu kapena ochokera kwa inu? 2 Inuyo ndiye kalata yathu,+ yolembedwa pamitima yathu, yodziwika ndiponso yowerengedwa ndi anthu onse.+ 3 Pakuti zikuonekeratu kuti ndinu kalata yochokera kwa Khristu yolembedwa ndi ifeyo kudzera mu utumiki wathu.+ Kalatayo siyolembedwa ndi inki koma ndi mzimu+ wa Mulungu wamoyo. Siyolembedwa pazolembapo zamiyala,+ koma zamnofu, pamitima.+
4 Tsopano kudzera mwa Khristu, tikhoza kunena zimenezi molimba mtima+ pamaso pa Mulungu. 5 Sitinganene kuti ndife oyenera kugwira ntchito imeneyi chifukwa cha mphamvu zathu,+ koma ndife oyenera kugwira ntchito imeneyi chifukwa cha Mulungu,+ 6 ndipo chifukwa cha iyeyo ndife oyenera kukhala atumiki a pangano latsopano,+ ndipo ndife ogwirizana osati kudzera m’malamulo olembedwa,+ koma mu mzimu.+ Pakuti malamulo olembedwa amaweruza munthu+ kuti afe, koma mzimu umapatsa munthu moyo.+
7 Ndiponso malamulo amene amapereka imfa,+ amenenso analembedwa pamiyala,+ anabwera ndi ulemerero waukulu kwambiri+ moti ana a Isiraeli sanathe kuyang’anitsitsa nkhope ya Mose chifukwa inali kuwala ndi ulemerero,+ ulemerero umene unatha patapita nthawi. 8 Chotero, kodi mzimu+ sukuyenera kuperekedwa ndi ulemerero waukulu koposa pamenepa?+ 9 Pakuti ngati malamulo oweruza anthu kuti alangidwe+ anaperekedwa ndi ulemerero,+ chilungamo chikuyenera kuperekedwa+ ndi ulemerero waukulu kuposa pamenepa.+ 10 Nawonso malamulo olembedwa amene anapatsidwa ulemerero poyamba achotsedwa ulemererowo,+ chifukwa ulemerero umene wabwera pambuyo pawo ndi wokulirapo.+ 11 Pakuti ngati malamulo olembedwa, amene anatha patapita nthawi, anaperekedwa ndi ulemerero,+ ndiye kuti okhalapo nthawi zonse adzakhala ndi ulemerero woposa pamenepo.+
12 Chotero popeza tili ndi chiyembekezo chimenechi,+ tikulankhula momasuka kwambiri, 13 osati ngati Mose amene anaphimba nkhope yake ndi nsalu,+ kuti ana a Isiraeli asaone kutha+ kwa ulemerero wosakhalitsawo. 14 Ndipo maganizo awo anachita khungu.+ Pakuti mpaka lero, nsaluyo imakhalabe yophimba powerenga pangano lakale,+ chifukwa imachotsedwa kudzera mwa Khristu basi.+ 15 Moti mpaka lero, pamene zolemba za Mose zikuwerengedwa,+ mitima yawo imakhalabe yophimba.+ 16 Koma munthu akatembenukira kwa Yehova, chophimbacho chimachotsedwa.+ 17 Tsopano Yehova ndiye Mzimu,+ ndipo pamene pali mzimu+ wa Yehova,+ pali ufulu.+ 18 Tonsefe+ tili ndi nkhope zosaphimba ndipo tili ngati magalasi oonera amene amaonetsa ulemerero wa Yehova.+ Pamene tikuonetsa ulemerero umenewu, timasintha+ n’kukhala ngati chifaniziro chake+ ndipo timaonetsa ulemerero wowonjezerekawonjezereka+ mofanana ndendende ndi mmene Yehova, amene ndi Mzimu, watisinthira.+