Kalata Yachiwiri Yopita kwa Akorinto
6 Pamene tikugwira naye ntchito limodzi,+ tikukulimbikitsani kuti musalandire kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu nʼkuphonya cholinga cha kukoma mtimako.+ 2 Chifukwa iye anati: “Pa nthawi yovomerezedwa ndinakumvera, ndipo pa tsiku lachipulumutso ndinakuthandiza.”+ Ndithudi, inoyo ndi nthawi yeniyeni yovomerezedwa. Lero ndi tsiku lachipulumutso.
3 Sitikuchita chilichonse chokhumudwitsa, kuti anthu asapezere chifukwa utumiki wathu.+ 4 Koma tikusonyeza mʼnjira iliyonse kuti ndife atumiki a Mulungu.+ Tikuchita zimenezi popirira zinthu zambiri, pokumana ndi mavuto, pokhala opanda zinthu zofunika, pokumana ndi zinthu zovuta,+ 5 pomenyedwa, kuikidwa mʼndende,+ zipolowe, pogwira ntchito mwakhama, kusagona tulo ndiponso kukhala osadya.+ 6 Tikusonyezanso zimenezi pokhala oyera, odziwa zinthu, oleza mtima,+ okoma mtima,+ potsogoleredwa ndi mzimu woyera, posonyeza chikondi chopanda chinyengo,+ 7 polankhula zoona ndiponso pokhala ndi mphamvu ya Mulungu.+ Komanso tikuchita zimenezi ponyamula zida za chilungamo+ kudzanja lamanja* ndi lamanzere,* 8 popatsidwa ulemerero ndi kunyozedwa ndiponso poneneredwa zoipa ndi zabwino. Tikuonedwa ngati achinyengo koma ndife oona mtima, 9 ngati osadziwika koma ndife odziwika bwino, ngati oti tikufa* koma tikukhalabe ndi moyo,+ ngati olangidwa koma osaperekedwa kuti tikaphedwe,+ 10 ngati achisoni koma osangalala nthawi zonse, ngati osauka koma olemeretsa anthu ambiri komanso ngati opanda chilichonse koma okhala ndi zinthu zonse.+
11 Takhala tikulankhula nanu inu Akorinto, ife tatsegula kwambiri* mtima wathu. 12 Ife sitikuumira pa nkhani yokusonyezani chikondi,+ koma inuyo ndi amene mukutikonda moumira. 13 Choncho ndikulankhula nanu ngati ana anga, inunso muzichita zomwezo, tsegulani kwambiri* mitima yanu.+
14 Musamangidwe mʼgoli ndi osakhulupirira, chifukwa ndinu osiyana.+ Pali mgwirizano wotani pakati pa chilungamo ndi kusamvera malamulo?+ Kapena pali kugwirizana kotani pakati pa kuwala ndi mdima?+ 15 Ndiponso pali mgwirizano wotani pakati pa Khristu ndi Beliyali?*+ Nanga munthu wokhulupirira* ndi wosakhulupirira angafanane pa zinthu ziti?+ 16 Ndipo pali kugwirizana kotani pakati pa kachisi wa Mulungu ndi mafano?+ Chifukwa ifeyo ndife kachisi wa Mulungu wamoyo,+ ngati mmene Mulungu ananenera kuti: “Ndidzakhala pakati pawo+ ndiponso ndidzayenda pakati pawo. Ndidzakhala Mulungu wawo ndipo iwo adzakhala anthu anga.”+ 17 “‘Choncho chokani pakati pawo ndipo musiyane nawo,’ watero Yehova.* ‘Musakhudze chinthu chodetsedwa,’”+ “‘ndipo ndidzakulandirani.’”+ 18 “‘Ndidzakhala bambo anu+ ndipo inu mudzakhala ana anga aamuna ndi aakazi,’+ watero Yehova* Wamphamvuyonse.”