Kalata Yoyamba Yopita kwa Akorinto
9 Kodi ndilibe ufulu wochita zimene ndikufuna? Kodi si ine mtumwi? Kodi sindinaone Yesu Ambuye wathu?+ Kodi inu si ntchito yanga mwa Ambuye? 2 Ngati si ine mtumwi kwa ena, mosakayikira ndine mtumwi kwa inu, chifukwa ndinu chidindo chotsimikizira kuti ndine mtumwi mwa Ambuye.
3 Yankho langa kwa amene amandikayikira ndi ili: 4 Kodi tilibe ufulu wa kudya ndiponso kumwa? 5 Kodi tilibe ufulu woyenda limodzi ndi akazi athu okhulupirira+ ngati mmene amachitira atumwi ena onse, abale awo a Ambuye+ komanso Kefa?*+ 6 Kapena kodi ine ndekha ndi Baranaba+ ndi amene tilibe ufulu wosiya kugwira ntchito kuti tizipeza zofunika pa moyo? 7 Kodi alipo msilikali amene amatumikira, koma nʼkumadzilipira yekha? Ndani amalima munda wa mpesa koma osadya zipatso zake?+ Kapena ndani amaweta ziweto koma osamwa mkaka wake?
8 Kodi zimene ndikulankhulazi ndi maganizo a anthu basi? Kodi Chilamulo sichinenanso zomwezi? 9 Chilamulo cha Mose chimati: “Usamange ngʼombe pakamwa pamene ikupuntha mbewu.”+ Kodi Mulungu amangodera nkhawa ngʼombe zokha? 10 Kapena kodi ananena mawu amenewa poganizira ifeyo? Mawu amenewa anawalembadi poganizira ifeyo, chifukwa wolima ndiponso wopuntha mbewu ayenera kugwira ntchito ndi chiyembekezo choti alandira kenakake.
11 Ngati tinakupatsani zinthu zauzimu,* kodi nʼkulakwa kulandira* zinthu zofunika pa moyo kuchokera kwa inu?+ 12 Ngati anthu ena amayembekezera kuti muwachitire zimenezi, ndiye kuli bwanji ifeyo? Komatu ife sitinagwiritse ntchito ufulu umenewo.+ Koma timapirira zinthu zonse kuti tisalepheretse ena kumva uthenga wabwino wonena za Khristu.+ 13 Kodi simukudziwa kuti anthu amene amagwira ntchito zopatulika amadya zamʼkachisi, ndipo amene amatumikira kuguwa lansembe nthawi zonse amalandira zina mwa zinthu zoperekedwa paguwa lansembelo?+ 14 Komanso Ambuye analamula kuti anthu amene amalalikira uthenga wabwino azipeza zofunika pa moyo kudzera mu uthenga wabwino.+
15 Koma sindinagwiritsepo ntchito ufulu umenewu.+ Ndiponso sikuti ndalemba zimenezi kuti ndiyambe kugwiritsa ntchito ufuluwu, chifukwa zingakhale bwino kuti ineyo ndife, kusiyana nʼkuti . . . palibe munthu amene angandilande zifukwa zomwe ndikudzitamira!+ 16 Ngati ndikulalikira uthenga wabwino, chimenecho si chifukwa chodzitamira, chifukwa ndinalamulidwa kuchita zimenezi. Tsoka kwa ine ngati sindilalikira uthenga wabwino.+ 17 Ndikamachita zimenezi mwa kufuna kwanga, ndidzalandira mphoto. Koma ngakhale nditachita mokakamizika, ndinebe woyangʼanira mogwirizana ndi udindo umene ndinapatsidwa.+ 18 Ndiye kodi mphoto yanga nʼchiyani? Ndi yakuti ndikamalalikira uthenga wabwino ndiziulalikira kwaulere, kuti ndisagwiritse ntchito molakwa ufulu wanga pa zinthu zokhudza uthenga wabwino.
19 Ngakhale kuti ndili ndi ufulu, ndadzichititsa kukhala kapolo wa anthu onse, kuti ndithandize anthu ambiri. 20 Kwa Ayuda ndinakhala ngati Myuda, kuti ndithandize Ayuda.+ Kwa anthu otsatira Chilamulo ndinakhala ngati wotsatira Chilamulo kuti ndithandize anthu otsatira chilamulo, ngakhale kuti sinditsatira Chilamulo.+ 21 Kwa anthu amene sayendera Chilamulo ndinakhala ngati wosayendera Chilamulo, kuti ndithandize anthu osayendera Chilamulo. Ndinachita zimenezi ngakhale kuti ndimatsatira malamulo a Mulungu komanso lamulo la Khristu.+ 22 Kwa ofooka ndinakhala wofooka, kuti ndithandize ofooka.+ Ndakhala zinthu zonse kwa anthu osiyanasiyana, kuti ndiyesetse mmene ndingathere kupulumutsa ena. 23 Ndimachita zinthu zonse chifukwa cha uthenga wabwino, kuti ndilalikire uthengawu kwa anthu ena.+
24 Kodi simukudziwa kuti ochita mpikisano wothamanga amathamanga onse, koma amene amakalandira mphoto ndi mmodzi yekha? Muzithamanga mʼnjira yoti mukalandire mphotoyo.+ 25 Munthu aliyense wochita nawo mpikisano amakhala wodziletsa pa zinthu zonse. Anthu amachita zimenezo kuti akalandire nkhata yakumutu imene imawonongeka,+ koma ife, kuti tikapeze nkhata yakumutu yomwe singawonongeke.+ 26 Choncho sikuti ndikungothamanga osadziwa kumene ndikupita.+ Mmene ndikuponyera zibakera zanga, sikuti ndikungomenya mphepo ayi. 27 Koma ndikumenya* thupi langa+ nʼkulichititsa kukhala ngati kapolo, kuti pambuyo poti ndalalikira kwa ena, ineyo ndisakhale wosayenera mʼnjira inayake.