2 Mafumu
17 Mʼchaka cha 12 cha Ahazi mfumu ya Yuda, Hoshiya+ mwana wa Ela anakhala mfumu ya Isiraeli ku Samariya ndipo analamulira zaka 9. 2 Hoshiya anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova, koma osati ngati mmene anachitira mafumu a Isiraeli amene analamulira iye asanayambe kulamulira. 3 Salimanesere mfumu ya Asuri anabwera kudzamenyana naye+ ndipo Hoshiya anakhala mtumiki wake nʼkuyamba kupereka msonkho kwa iye.+ 4 Koma mfumu ya Asuri inamva kuti Hoshiya akuikonzera chiwembu, chifukwa anatumiza anthu kwa So mfumu ya Iguputo+ ndiponso sanapereke msonkho kwa mfumu ya Asuri ngati mmene ankachitira zaka zamʼmbuyo. Choncho mfumu ya Asuri inamʼmanga nʼkumutsekera mʼndende.
5 Mfumu ya Asuri inabwera kudzaukira dziko lonselo ndipo inazungulira mzinda wa Samariya kwa zaka zitatu. 6 Mʼchaka cha 9 cha Hoshiya, mfumu ya Asuri inalanda Samariya+ nʼkutenga Aisiraeli kupita nawo ku Asuri.+ Mfumuyo inakaika Aisiraeliwo ku Hala ndi ku Habori pafupi ndi mtsinje wa Gozani+ ndiponso mʼmizinda ya Amedi.+
7 Zimenezi zinachitika chifukwa chakuti Aisiraeli anachimwira Yehova Mulungu wawo, yemwe anawatulutsa mʼdziko la Iguputo nʼkuwachotsa mʼmanja mwa Farao mfumu ya Iguputo+ ndipo anayamba kulambira* milungu ina.+ 8 Iwo ankatsatira miyambo ya mitundu imene Yehova anaithamangitsa pamaso pa Aisiraeli ndiponso ankatsatira miyambo imene mafumu a Isiraeli anayambitsa.
9 Aisiraeli ankachita zinthu zosayenera kwa Yehova Mulungu wawo. Anapitiriza kumanga malo okwezeka mʼmizinda yawo yonse,+ kuyambira kunsanja ya alonda mpaka kumzinda wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri.* 10 Iwo anapitiriza kuika zipilala zopatulika ndi mizati yopatulika*+ paphiri lililonse lalitali ndi pansi pa mtengo uliwonse waukulu wa masamba obiriwira.+ 11 Iwo anapitiriza kupereka nsembe zautsi pamalo okwezeka onse ngati mmene inkachitira mitundu imene Yehova anaithamangitsa mʼdzikolo chifukwa cha Aisiraeliwo.+ Iwo anapitiriza kuchita zinthu zoipa zokwiyitsa Yehova.
12 Anapitiriza kulambira mafano onyansa*+ omwe Yehova anawauza kuti: “Musachite zimenezi.”+ 13 Yehova ankachenjeza Aisiraeli ndi Ayuda kudzera mwa aneneri ake onse ndiponso amasomphenya onse+ kuti: “Siyani njira zanu zoipa+ ndipo muzisunga malamulo anga, mogwirizana ndi malamulo onse amene ndinalamula makolo anu ndiponso amene ndinakutumizirani kudzera mwa atumiki anga, aneneri.” 14 Koma iwo sanamvere ndipo anali ankhutukumve* ngati makolo awo amene sanasonyeze chikhulupiriro mwa Yehova Mulungu wawo.+ 15 Iwo anapitiriza kukana malamulo ndi pangano+ limene iye anachita ndi makolo awo, ndiponso zikumbutso zimene iye anawapatsa powachenjeza.+ Mʼmalomwake ankatsatira mafano opanda pake+ ndipo nawonso anakhala opanda pake.+ Ankatengera mitundu yowazungulira imene Yehova anawalamula kuti asamaitsanzire.+
16 Anasiya malamulo onse a Yehova Mulungu wawo nʼkupanga zifaniziro ziwiri zachitsulo za ana a ngʼombe+ komanso mzati wopatulika.*+ Anayamba kugwadira gulu lonse la zinthu zakuthambo+ ndiponso kulambira Baala.+ 17 Komanso iwo ankawotcha* pamoto ana awo aamuna ndi aakazi,+ kulosera+ ndiponso kuwombeza. Anatsimikiza mtima kuchita zoipa pamaso pa Yehova nʼcholinga chomukwiyitsa.
18 Choncho Yehova anawakwiyira kwambiri Aisiraeli moti anawachotsa pamaso pake.+ Sanasiye aliyense kupatulapo fuko la Yuda lokha.
19 Komabe Ayuda nawonso sanatsatire malamulo a Yehova Mulungu wawo.+ Iwonso ankatsatira miyambo imene Aisiraeli ankatsatira.+ 20 Yehova anakana anthu onse omwe anali mbadwa za Isiraeli ndipo anawachititsa manyazi nʼkuwapereka mʼmanja mwa anthu omwe anawalanda katundu, mpaka iye anawachotsa pamaso pake. 21 Anangʼamba Isiraeli kumusiyanitsa ndi nyumba ya Davide ndipo iwo anaveka ufumu Yerobowamu mwana wa Nebati.+ Yerobowamuyo anasocheretsa Aisiraeli kuti asiye kutsatira Yehova nʼkuwachititsa tchimo lalikulu. 22 Aisiraeli anapitiriza kuyenda mʼmachimo onse amene Yerobowamu anachita.+ Sanawasiye 23 mpaka Yehova anachotsa Aisiraeli pamaso pake ngati mmene ananenera kudzera mwa atumiki ake onse, aneneri.+ Choncho Aisiraeli anatengedwa mʼdziko lawo nʼkupita nawo ku Asuri+ ndipo ali komweko mpaka lero.
24 Kenako mfumu ya Asuri inatenga anthu kuchokera ku Babulo, ku Kuta, ku Ava, ku Hamati ndi ku Sefaravaimu+ nʼkuwaika mʼmizinda ya ku Samariya mʼmalo mwa Aisiraeli. Anthuwo anatenga Samariya nʼkumakhala mʼmizinda yake. 25 Atayamba kukhala kumeneko, sankaopa* Yehova. Choncho Yehova anawatumizira mikango+ ndipo inapha ena mwa anthuwo. 26 Mfumu ya Asuri inauzidwa kuti: “Mitundu imene munaichotsa kwawo nʼkukaiika mʼmizinda ya ku Samariya sikudziwa chipembedzo* cha Mulungu wa kumeneko. Choncho iye wakhala akuwatumizira mikango imene ikuwapha chifukwa palibe amene akudziwa chipembedzo cha Mulungu wa kumeneko.”
27 Zitatero, mfumu ya Asuri inalamula kuti: “Mutumize mmodzi mwa ansembe amene munawagwira kuti abwerere azikakhala kumeneko ndipo akaphunzitse anthuwo chipembedzo cha Mulungu wa mʼderalo.” 28 Choncho mmodzi mwa ansembe amene anatengedwa kuchokera ku Samariya, anabwerera nʼkumakakhala ku Beteli.+ Iye ankawaphunzitsa kuopa* Yehova.+
29 Komabe mtundu uliwonse unapanga mulungu wake nʼkukamuika* mʼkachisi pamalo okwezeka amene Asamariya anamanga. Mtundu uliwonse unachita zimenezi mʼmizinda imene unkakhala. 30 Anthu a ku Babulo anapanga Sukoti-benoti, a ku Kuta anapanga Nerigali ndipo a ku Hamati+ anapanga Asima. 31 Aava anapanga Nibazi ndi Tarataka, pamene Asefaravaimu ankawotcha ana awo aamuna pamoto powapereka nsembe kwa Adarameleki ndi Anameleki, milungu ya Sefaravaimu.+ 32 Ngakhale kuti anthuwo ankaopa Yehova, anasankha anthu wamba kuti akhale ansembe amʼmalo okwezeka, kuti aziwatumikira mu akachisi pamalo okwezeka.+ 33 Choncho ankaopa Yehova koma ankalambira milungu yawo, mogwirizana ndi chipembedzo cha mitundu imene anawatengako.+
34 Mpaka lero akutsatirabe zipembedzo zawo zakale. Palibe amene akulambira* Yehova ndipo palibe amene akutsatira malamulo ake, ziweruzo zake ndiponso Chilamulo chimene Yehova anapatsa ana a Yakobo yemwe Mulungu anamusintha dzina nʼkukhala Isiraeli.+ 35 Pamene Yehova anachita nawo pangano,+ anawalamula kuti: “Musamaope milungu ina. Musamaigwadire, kapena kuitumikira kapena kupereka nsembe kwa milunguyo.+ 36 Koma Yehova amene anakutulutsani mʼdziko la Iguputo ndi mphamvu zazikulu ndiponso mkono wamphamvu,*+ ndi amene muyenera kumuopa,+ kumugwadira komanso kupereka nsembe kwa iye. 37 Nthawi zonse muzitsatira mosamala malamulo, ziweruzo ndiponso Chilamulo chimene anakulemberani+ ndipo musamaope milungu ina. 38 Musaiwale pangano limene ndinachita nanu+ ndipo musamaope milungu ina. 39 Koma muziopa Yehova Mulungu wanu, chifukwa iye ndi amene adzakupulumutseni kwa adani anu onse.”
40 Koma iwo sanamvere ndipo ankatsatira chipembedzo chawo chakale.+ 41 Mitundu imeneyi inkaopa Yehova,+ koma inkatumikiranso zifaniziro zawo zogoba. Mpaka lero, ana awo ndi zidzukulu zawo akuchitabe zimene makolo awo ankachita.