Kalata Yoyamba Yopita kwa Akorinto
11 Muzitsanzira ine, ngati mmene inenso ndimatsanzirira Khristu.+
2 Ndikukuyamikirani chifukwa mukundikumbukira pa zinthu zonse ndipo mukusunga miyambo ngati mmene ndinaiperekera kwa inu. 3 Koma ndikufuna mudziwe kuti mutu wa mwamuna aliyense ndi Khristu.+ Mutu wa mkazi ndi mwamuna+ ndipo mutu wa Khristu ndi Mulungu.+ 4 Mwamuna aliyense amene amapemphera kapena kunenera atavala chinachake kumutu akuchititsa manyazi mutu wake. 5 Koma mkazi amene amapemphera kapena kunenera+ osavala kanthu kumutu amachititsa manyazi mutu wake, popeza nʼchimodzimodzi ndi kumeta mpala. 6 Chifukwa ngati mkazi savala kanthu kumutu ayenera kumeta mpala. Koma poti kumeta kwambiri tsitsi kapena kumeta mpala nʼkochititsa manyazi kwa mkazi, azivala chakumutu.
7 Mwamuna sayenera kuvala chophimba kumutu, popeza iye ndi chifaniziro ndi ulemerero wa Mulungu,+ koma mkazi ndi ulemerero wa mwamuna. 8 Chifukwa mwamuna sanachokere kwa mkazi, koma mkazi anachokera kwa mwamuna.+ 9 Ndiponso mwamuna sanalengedwere mkazi, koma mkazi analengedwera mwamuna.+ 10 Pa chifukwa chimenechi komanso chifukwa cha angelo,+ mkazi ayenera kuvala chinachake kumutu posonyeza kuti ali pansi pa ulamuliro.
11 Ndiponso pakati pa anthu otsatira Ambuye, mkazi amadalira mwamuna ndipo mwamuna amadalira mkazi. 12 Chifukwa mmene zilili kuti mkazi anachokera kwa mwamuna,+ mwamunanso amabadwa kuchokera kwa mkazi. Koma zinthu zonse zimachokera kwa Mulungu.+ 13 Weruzani nokha: Kodi nʼzoyenera kuti mkazi azipemphera kwa Mulungu osavala chophimba kumutu? 14 Kodi chikhalidwe sichikuphunzitsani kuti ngati mwamuna ali ndi tsitsi lalitali, zimakhala zochititsa manyazi? 15 Koma ngati mkazi ali ndi tsitsi lalitali umakhala ulemerero kwa iye. Zili choncho chifukwa anapatsidwa tsitsi lakelo mʼmalo mwa chovala kumutu. 16 Komabe, ngati alipo wina amene akutsutsa zimenezi pofuna chikhalidwe china, ifeyo komanso mipingo ya Mulungu, tilibe chikhalidwe chinacho.
17 Koma pamene ndikupereka malangizo amenewa, sikuti ndikukuyamikirani, chifukwa zimene zimachitika mukasonkhana si zabwino, koma zoipa. 18 Choyamba, ndamva kuti mukasonkhana mumpingo, pakumakhala kugawanika, ndipo kumbali ina ndikuona kuti ndi zoona. 19 Payeneradi kukhala magulu ampatuko pakati panu,+ kuti anthu ovomerezeka kwa Mulungu adziwike.
20 Mukasonkhana kuti mudye Chakudya Chamadzulo cha Ambuye+ simukuchita zinthu mʼnjira yoyenera. 21 Chifukwa nthawi yakudya ikamafika, aliyense amakhala atadyeratu chakudya chake, choncho wina amakhala ndi njala pomwe wina amakhala ataledzera. 22 Kodi mulibe nyumba kumene mungadyereko ndi kumwerako? Kapena kodi mukunyoza mpingo wa Mulungu nʼkumachititsa manyazi anthu amene alibe chilichonse? Kodi ndinene chiyani kwa inu? Ndikuyamikireni? Pa izi zokha ndiye sindingakuyamikireni.
23 Zimene ndinamva kwa Ambuye nʼzimene inenso ndinakuphunzitsani, kuti Ambuye Yesu, usiku+ umene anaperekedwa anatenga mkate, 24 ndipo atayamika anaugawagawa* nʼkunena kuti: “Mkate uwu ukuimira thupi langa+ limene likuperekedwa chifukwa cha inu. Muzichita zimenezi pondikumbukira.”+ 25 Anachitanso chimodzimodzi ndi kapu+ atadya chakudya chamadzulo, ndipo anati: “Kapu iyi ikuimira pangano latsopano+ limene linakhazikitsidwa pogwiritsa ntchito magazi anga.+ Muzichita zimenezi mukamamwa zamʼkapu imeneyi pondikumbukira.”+ 26 Chifukwa nthawi iliyonse imene mukudya mkate umenewu ndi kumwa zamʼkapu imeneyi, mumakhala kuti mukulengeza imfa ya Ambuye, mpaka iye adzabwere.
27 Choncho aliyense wakudya mkatewu kapena kumwa za mʼkapu ya Ambuye mosayenera, adzakhala ndi mlandu wokhudza thupi ndi magazi a Ambuye. 28 Munthu azidzifufuza kaye+ ngati ali woyenera kudya mkatewu ndi kumwa zamʼkapuyi. 29 Chifukwa ngati munthu akudya ndi kumwa asakuzindikira kuti zikuimira thupilo, akudzibweretsera chilango. 30 Nʼchifukwa chake ambiri a inu ndi ofooka komanso odwala ndipo angapo afa.*+ 31 Koma ngati tingazindikire mmene tilili, sitingaweruzidwe. 32 Komabe tikaweruzidwa, ndiye kuti Yehova* watiphunzitsa+ kuti tisalandire chilango limodzi ndi dziko.+ 33 Choncho abale anga, mukasonkhana kuti mudye Chakudya Chamadzulo cha Ambuye, muzidikirana. 34 Ngati wina ali ndi njala, adye kunyumba, kuti mukasonkhana musaweruzidwe.+ Koma nkhani zimene zatsala ndidzaziona ndikabwera.