Kalata yachiwiri yopita kwa Timoteyo
3 Koma dziwa kuti masiku otsiriza+ adzakhala nthawi yapadera komanso yovuta. 2 Anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, odzitama, odzikweza, onyoza, osamvera makolo, osayamika, osakhulupirika, 3 osakonda achibale awo, osafuna kugwirizana ndi ena, onenera ena zoipa, osadziletsa, oopsa, osakonda zabwino, 4 ochitira anzawo zoipa, osamva za ena, odzitukumula chifukwa cha kunyada, okonda zosangalatsa mʼmalo mokonda Mulungu, 5 ndiponso ooneka ngati odzipereka kwa Mulungu koma amakana kuti mphamvu ya kudziperekako iwasinthe.+ Anthu amenewa uziwapewa. 6 Ena mwa anthuwa amalowerera mozemba mʼmabanja nʼkumachititsa amayi ena kuti akhale akapolo awo. Amayiwa amakhala ofooka chifukwa cha machimo awo ndiponso otengeka ndi zilakolako zosiyanasiyana. 7 Nthawi zonse amaphunzira, koma satha kudziwa choonadi molondola.
8 Mofanana ndi Yane ndi Yambure, amene anatsutsa Mose, anthu amenewanso akupitiriza kutsutsa choonadi. Iwo ali ndi maganizo opotoka kwambiri, ndipo sakuyenerera chikhulupirirochi. 9 Koma sangapite patali, chifukwa kupusa kwawo kuonekera bwino kwa anthu onse, ngati mmene zinakhalira ndi anthu awiri aja.+ 10 Koma iwe wayesetsa kutsatira zimene ndimaphunzitsa, moyo wanga,+ cholinga changa, chikhulupiriro changa, kuleza mtima kwanga, chikondi changa ndi kupirira kwanga. 11 Ukudziwanso mmene ndinazunzikira komanso masautso amene ndinakumana nawo ku Antiokeya,+ ku Ikoniyo+ ndi ku Lusitara.+ Komabe ndinapirira ndipo Ambuye anandipulumutsa ku zonsezi.+ 12 Pajatu onse ofuna kukhala ndi moyo wodzipereka kwa Mulungu mogwirizana ndi Khristu Yesu, nawonso adzazunzidwa.+ 13 Koma anthu oipa ndi achinyengo adzaipiraipirabe. Iwo azidzasocheretsa ena ndiponso azidzasocheretsedwa.+
14 Koma iwe, pitiriza kutsatira zimene unaphunzira ndi zimene unakhulupirira pambuyo pokhutira nazo,+ chifukwa ukudziwa amene anakuphunzitsa. 15 Kuyambira pamene unali wakhanda,+ wadziwa malemba oyera+ amene angakupatse nzeru zokuthandiza kuti udzapulumuke chifukwa chokhulupirira Khristu Yesu.+ 16 Malemba onse anauziridwa ndi Mulungu,+ ndipo ndi othandiza pophunzitsa,+ kudzudzula, kukonza zinthu ndi kulangiza mwachilungamo,+ 17 kuti munthu wa Mulungu akhale woyenerera kwambiri ndi wokonzeka mokwanira kugwira ntchito iliyonse yabwino.