Wolembedwa ndi Mateyu
8 Atatsika mʼphirimo, chigulu cha anthu chinamutsatira. 2 Kenako panafika munthu wakhate. Munthuyo anamugwadira nʼkunena kuti: “Ambuye, ndikudziwa kuti ngati mukufuna, mukhoza kundiyeretsa.”+ 3 Choncho Yesu anatambasula dzanja lake nʼkumukhudza ndipo ananena kuti: “Inde ndikufuna. Khala woyera.”+ Nthawi yomweyo khate lakelo linatha.+ 4 Ndiyeno Yesu anamuuza kuti: “Samala, usauze aliyense zimenezi,+ koma upite ukadzionetse kwa wansembe+ ndipo ukapereke mphatso imene Mose analamula,+ kuti ikhale umboni kwa iwo.”
5 Atalowa mumzinda wa Kaperenao, mtsogoleri wa asilikali anabwera kwa iye nʼkumupempha+ 6 kuti: “Ambuye, wantchito wanga wafa ziwalo moti ali chigonere mʼnyumba ndipo akuvutika koopsa.” 7 Iye anamuuza kuti: “Ndikafika kumeneko ndikamuchiritsa.” 8 Mtsogoleri wa asilikali uja anayankha kuti: “Ambuye, sindine munthu woyenera kuti inu mukalowe mʼnyumba mwanga, koma mungonena mawu okha ndipo wantchito wangayo achira. 9 Chifukwa inenso ndili ndi akuluakulu ondiyangʼanira komanso ndili ndi asilikali amene ndimawayangʼanira. Ndikauza mmodzi kuti, ‘Pita!’ amapita, wina ndikamuuza kuti, ‘Bwera!’ amabwera. Kapolo wanga ndikamuuza kuti, ‘Chita ichi!’ amachita.” 10 Yesu atamva zimenezo, anadabwa ndipo anauza amene ankamutsatira aja kuti: “Kunena zoona, mu Isiraeli sindinapezemo aliyense wachikhulupiriro chachikulu ngati chimenechi.+ 11 Koma ndikukuuzani kuti ambiri ochokera kumʼmawa ndi kumadzulo adzabwera nʼkukhala patebulo limodzi ndi Abulahamu, Isaki ndi Yakobo mu Ufumu wakumwamba,+ 12 pamene ana a Ufumuwo adzaponyedwa kunja kumdima. Kumeneko adzalira ndi kukukuta mano.”+ 13 Kenako Yesu anauza mtsogoleri wa asilikaliyo kuti: “Pita. Chifukwa chakuti wasonyeza chikhulupiriro, zimene wapemphazo zichitike.”+ Mu ola lomwelo wantchito uja anachira.+
14 Tsopano Yesu, atalowa mʼnyumba mwa Petulo, anaona apongozi aakazi a Petulo+ ali chigonere, akudwala malungo.*+ 15 Choncho anagwira dzanja la mayiwo+ ndipo malungowo anatheratu, moti anadzuka nʼkuyamba kumutumikira. 16 Koma chakumadzulo, anthu anamubweretsera anthu ambiri ogwidwa ndi ziwanda. Iye anatulutsa mizimu imeneyo ndi mawu okha ndipo anachiritsa anthu onse amene ankadwala. 17 Anachita zimenezi kuti zimene Mulungu ananena kudzera mwa mneneri Yesaya zikwaniritsidwe. Iye ananena kuti: “Iye anatenga matenda athu nʼkunyamula zowawa zathu.”+
18 Yesu ataona kuti gulu la anthu lamuzungulira, analamula kuti achoke nʼkupita kutsidya lina.+ 19 Ndiyeno kunabwera mlembi nʼkumuuza kuti: “Mphunzitsi, ndikutsatirani kulikonse kumene mungapite.”+ 20 Koma Yesu anamuuza kuti: “Nkhandwe zili ndi mapanga ndipo mbalame zamumlengalenga zili ndi zisa, koma Mwana wa munthu alibiretu poti nʼkutsamiritsa mutu wake.”+ 21 Kenako mmodzi mwa ophunzira ake anamuuza kuti: “Ambuye, ndiloleni ndiyambe ndapita kukaika maliro a bambo anga.”+ 22 Koma Yesu anamuyankha kuti: “Iwe upitirizebe kunditsatira, ndipo asiye akufa aike akufa awo.”+
23 Ndiyeno atakwera mʼngalawa, ophunzira ake anamʼtsatira.+ 24 Kenako panyanjapo panabuka mphepo yamphamvu moti mafunde ankalowetsa madzi mʼngalawamo, koma iye anali mʼtulo.+ 25 Ndipo iwo anapita kukamudzutsa kuti: “Ambuye, tipulumutseni tikufa!” 26 Koma iye anawafunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani mukuchita mantha chonchi, anthu achikhulupiriro chochepa inu?”+ Kenako anadzuka nʼkudzudzula mphepo ndi nyanjayo, ndipo panachita bata lalikulu.+ 27 Choncho amunawo anadabwa nʼkunena kuti: “Kodi munthu ameneyu ndi wotani? Ngakhale mphepo ndi nyanja zikumumvera.”
28 Atafika kutsidya linalo, mʼdera la Agadara, anakumana ndi amuna awiri ogwidwa ndi ziwanda akuchokera mʼmanda.*+ Amunawa anali ochititsa mantha kwambiri moti panalibe aliyense amene ankalimba mtima kudutsa msewu umenewo. 29 Nthawi yomweyo iwo anafuula kuti: “Kodi mukufuna chiyani kwa ife, Mwana wa Mulungu?+ Kodi mwabwera kudzatipatsa chilango+ nthawi yoikidwiratu isanakwane?”+ 30 Koma pamtunda wautali ndithu kuchokera pamenepo, panali nkhumba zambiri zimene zinkadya.+ 31 Choncho ziwandazo zinayamba kumʼchonderera kuti: “Ngati mukufuna kutitulutsa, mutitumize munkhumbazo.”+ 32 Iye anaziuza kuti: “Pitani!” Choncho zinatuluka nʼkukalowa munkhumba zija. Nthawi yomweyo nkhumba zonsezo zinathamangira kuphedi nʼkulumphira mʼnyanja, ndipo zinafera mʼmadzimo. 33 Koma abusa a ziwetozo anathawa ndipo atalowa mumzinda anafotokoza zonse, kuphatikizapo zimene zinachitikira amuna ogwidwa ndi ziwanda aja. 34 Zitatero, anthu onse mumzindawo anapita kukakumana ndi Yesu. Atamuona, anamʼpempha kuti achoke mʼdera lawolo.+