Wolembedwa ndi Luka
9 Kenako Yesu anasonkhanitsa atumwi 12 aja nʼkuwapatsa mphamvu ndi ulamuliro pa ziwanda zonse+ komanso kuti azitha kuchiritsa matenda.+ 2 Ndiyeno anawatumiza kuti azikalalikira za Ufumu wa Mulungu ndiponso kuchiritsa anthu. 3 Iye anawauza kuti: “Musatenge kanthu pa ulendowu, kaya ndodo, thumba la chakudya, mkate, ndalama kapena malaya awiri.*+ 4 Mukafika panyumba iliyonse, muzikhala mʼnyumbayo mpaka nthawi yochoka kumeneko itakwana.+ 5 Kulikonse kumene munthu sakakulandirani, mukamatuluka mumzinda umenewo muzisansa fumbi kumapazi anu kuti ukhale umboni wowatsutsa.”+ 6 Pamenepo ananyamuka nʼkulowa mʼderalo mudzi ndi mudzi nʼkumalengeza uthenga wabwino komanso kuchiritsa anthu kwina kulikonse.+
7 Tsopano Herode,* wolamulira chigawo,* anamva zonse zimene zinkachitika. Iye anathedwa nzeru chifukwa ena ankanena kuti Yohane waukitsidwa.+ 8 Koma ena ankanena kuti Eliya waonekera. Enanso ankanena kuti mmodzi wa aneneri akale wauka.+ 9 Ndiyeno Herode anati: “Yohane ndinamudula mutu.+ Nanga amene akuchita zomwe ndikumvazi ndi ndani?” Choncho ankafunitsitsa atamuona.+
10 Atumwi aja atabwerako anafotokozera Yesu zimene anachita.+ Atatero anawatenga nʼkupita nawo kwaokha mumzinda wotchedwa Betsaida.+ 11 Koma gulu la anthu linadziwa zimenezi moti linamutsatira. Yesu anawalandira bwino nʼkuyamba kuwauza za Ufumu wa Mulungu, ndipo anachiritsa amene ankafunika kuchiritsidwa.+ 12 Komano nthawi inali chakumadzulo. Choncho atumwi 12 aja anabwera kwa iye nʼkunena kuti: “Kuno nʼkopanda anthu ndipo nthawi yatha, auzeni anthuwa kuti anyamuke, apite mʼmidzi ndi mʼmadera ozungulira kuti akapeze malo ogona komanso chakudya choti adye.”+ 13 Koma iye anawayankha kuti: “Inuyo muwapatse chakudya.”+ Iwo anati: “Tilibe chilichonse kupatulapo mitanda ya mkate isanu ndi nsomba ziwiri zokha basi. Kapenatu tipite kukagula chakudya chokwanira anthu onsewa.” 14 Panali amuna pafupifupi 5,000 ndipo Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Uzani anthuwa kuti akhale mʼmagulu a anthu 50.” 15 Ophunzirawo anachitadi zimenezo, moti anthu onsewo anakhala pansi. 16 Kenako anatenga mitanda ya mkate 5 ndi nsomba ziwiri zija nʼkuyangʼana kumwamba ndipo anadalitsa chakudyacho. Atatero ananyemanyema mitanda ya mkateyo nʼkuipereka kwa ophunzira ake kuti aipereke kwa anthuwo. 17 Choncho onse anadya nʼkukhuta, ndipo anatolera zotsala zodzaza madengu 12.+
18 Kenako akupemphera payekha, ophunzira ake anafika kwa iye. Ndiyeno iye anawafunsa kuti: “Kodi anthu akumanena kuti ine ndine ndani?”+ 19 Iwo anamuyankha kuti: “Akumanena kuti Yohane Mʼbatizi, ena akumati Eliya, koma ena akumanena kuti mmodzi wa aneneri akale.”+ 20 Pamenepo anawafunsa kuti: “Nanga inuyo mumati ndine ndani?” Petulo anayankha kuti: “Ndinu Khristu wa Mulungu.”+ 21 Ndiyeno anawalangiza mwamphamvu kuti asauze aliyense zimenezo.+ 22 Kenako anati: “Mwana wa munthu akuyenera kukumana ndi mavuto ambiri ndiponso kukanidwa ndi akulu, ansembe aakulu ndi alembi. Ndipo adzaphedwa+ nʼkuukitsidwa patapita masiku atatu.”+
23 Kenako anauza onse kuti: “Ngati munthu akufuna kunditsatira, adzikane yekha+ ndipo anyamule mtengo wake wozunzikirapo* nʼkupitiriza kunditsatira tsiku ndi tsiku.+ 24 Chifukwa aliyense amene akufuna kupulumutsa moyo wake adzautaya, koma aliyense amene wataya moyo wake chifukwa cha ine adzaupeza.+ 25 Kodi munthu angapindule chiyani ngati atapeza zinthu zonse zamʼdzikoli koma nʼkutaya moyo wake kapena kudzivulaza?+ 26 Chifukwa aliyense wochita manyazi ndi ine komanso mawu anga, Mwana wa munthu adzachita nayenso manyazi akadzabwera mu ulemerero wake, wa Atate wake ndi wa angelo oyera.+ 27 Koma ndithu ndikukuuzani, pali ena mwa amene aimirira pano amene sadzalawa imfa mʼpangʼono pomwe mpaka choyamba ataona Ufumu wa Mulungu.”+
28 Patapita masiku pafupifupi 8 atanena mawu amenewa, iye anatenga Petulo, Yohane ndi Yakobo nʼkukwera nawo phiri kukapemphera.+ 29 Pamene ankapemphera, maonekedwe a nkhope yake anasintha ndipo chovala chake chinaoneka choyera kwambiri ndi chonyezimira. 30 Ndiyeno panaoneka anthu awiri akukambirana naye. Anthu amenewa anali Mose ndi Eliya. 31 Iwo anaonekera ndi ulemerero ndipo anayamba kukambirana za mmene Yesu adzachokere mʼdzikoli, ku Yerusalemu.+ 32 Apa nʼkuti Petulo ndi ena amene anali naye atatheratu ndi tulo. Koma tulo titawathera, anaona ulemerero wake+ ndiponso amuna awiri ataima naye. 33 Ndiyeno pamene amunawa ankasiyana naye, Petulo anauza Yesu kuti: “Mlangizi, zingakhale bwino ife titamakhala pano. Choncho timange matenti atatu pano, imodzi yanu, imodzi ya Mose ndi ina ya Eliya.” Koma iye sankazindikira zimene ankanena. 34 Pamene ankanena zimenezi, kunachita mtambo ndipo unayamba kuwaphimba. Mtambowo utawaphimba, anachita mantha. 35 Ndiyeno panamveka mawu+ kuchokera mumtambomo akuti: “Uyu ndi Mwana wanga, amene ndinamusankha.+ Muzimumvera.”+ 36 Pamene mawuwo ankamveka, anaona kuti Yesu ali yekha. Koma iwo anakhala chete ndipo sanauze aliyense mʼmasiku amenewo chilichonse pa zimene anaonazo.+
37 Tsiku lotsatira, atatsika mʼphirimo, chigulu cha anthu chinamuchingamira.+ 38 Munthu wina amene anali mʼgululo anafuula kuti: “Mphunzitsi, ndikukupemphani kuti mukaone mwana wanga wamwamuna, chifukwa ndi mmodzi yekhayo.+ 39 Mzimu umamugwira, ndipo mwadzidzidzi amafuula, kenako umamuchititsa kuti aphuphe kwinaku akuchita thovu. Mzimu umenewu umamuvulaza kwambiri ndipo zimavuta kuti umusiye. 40 Ndinapempha ophunzira anu kuti autulutse koma alephera.” 41 Yesu anayankha kuti: “Inu mʼbadwo wopanda chikhulupiriro ndi wopotoka maganizo,+ kodi ndikhala nanube mpaka liti? Ndipitirize kukupirirani mpaka liti? Bwera naye kuno mwana wakoyo.”+ 42 Koma ngakhale pamene ankamupititsa kwa iye, chiwandacho chinamugwetsa pansi nʼkumuchititsa kuti aphuphe mwamphamvu. Yesu anakalipira mzimu wonyansawo nʼkuchiritsa mnyamatayo ndipo anamupereka kwa bambo ake. 43 Anthu onse anadabwa ndi mphamvu zodabwitsa za Mulungu.
Anthuwo adakali odabwa ndi zonse zimene iye ankachita, Yesu anauza ophunzira ake kuti: 44 “Mvetserani mosamala ndipo muzikumbukira mawu awa, chifukwa Mwana wa munthu adzaperekedwa mʼmanja mwa anthu.”+ 45 Koma ophunzirawo sanamvetse zimene anawauzazo. Tanthauzo lake linali lobisika kwa iwo kuti asazindikire ndipo ankaopa kumufunsa za mawu amenewa.
46 Kenako iwo anayamba kukangana zokhudza amene anali wamkulu pakati pawo.+ 47 Yesu atazindikira zimene ankaganiza mumtima mwawo, anatenga mwana wamngʼono nʼkumuimika pambali pake. 48 Ndiyeno anawauza kuti: “Aliyense amene walandira mwana wamngʼono ngati uyu mʼdzina langa walandiranso ine. Ndipo aliyense amene walandira ine walandiranso amene anandituma.+ Chifukwa aliyense amene amachita zinthu ngati mwana wamngʼono pakati panu ndi amene ali wamkulu.”+
49 Kenako Yohane ananena kuti: “Mlangizi, ife tinaona munthu wina akutulutsa ziwanda mʼdzina lanu ndiye tinamuletsa, chifukwa sakuyenda ndi ife.”+ 50 Koma Yesu anamuuza kuti: “Musamuletse chifukwa amene sakutsutsana nanu, ali kumbali yanu.”
51 Pamene masiku oti atengedwe kupita kumwamba ankayandikira,*+ anatsimikiza mtima kupita ku Yerusalemu. 52 Choncho anatuma anthu kuti atsogole. Anthuwo anakalowa mʼmudzi wa Asamariya kuti akakonzekere kufika kwake. 53 Koma anthu amʼmudziwo sanamulandire bwino+ chifukwa anatsimikiza mumtima mwake kuti apite ku Yerusalemu. 54 Ophunzira ake, Yakobo ndi Yohane+ ataona zimenezi, ananena kuti: “Ambuye, kodi mukufuna tiwaitanire moto kuchokera kumwamba kuti uwanyeketse?”+ 55 Koma iye anatembenuka nʼkuwadzudzula. 56 Choncho Yesu ndi ophunzira ake anapita kumudzi wina.
57 Ndiyeno ali pa ulendowo, winawake anauza Yesu kuti: “Ndikutsatirani kulikonse kumene mungapite.” 58 Koma Yesu anamuuza kuti: “Nkhandwe zili ndi mapanga ndipo mbalame zamumlengalenga zili ndi zisa, koma Mwana wa munthu alibiretu poti nʼkutsamiritsa mutu wake.”+ 59 Kenako anauza munthu wina kuti: “Ukhale wotsatira wanga.” Koma munthuyo anati: “Ambuye, ndiloleni ndiyambe ndapita kukaika maliro a bambo anga.”+ 60 Yesu anamuuza kuti: “Asiye akufa+ aike akufa awo, koma iwe pita ukalengeze zokhudza Ufumu wa Mulungu kulikonse.”+ 61 Winanso ananena kuti: “Ine ndikutsatirani Ambuye, koma mundilole ndiyambe ndakatsanzika amʼbanja langa.” 62 Yesu anamuuza kuti: “Aliyense wogwira pulawo nʼkumayangʼana zinthu zakumbuyo+ sakuyenera Ufumu wa Mulungu.”+