2 Mafumu
18 Mʼchaka chachitatu cha Hoshiya+ mwana wa Ela mfumu ya Isiraeli, Hezekiya+ mwana wa Ahazi,+ mfumu ya Yuda anakhala mfumu. 2 Hezekiya anakhala mfumu ali ndi zaka 25 ndipo analamulira ku Yerusalemu zaka 29. Mayi ake dzina lawo linali Abi* mwana wa Zekariya.+ 3 Iye ankachita zoyenera pamaso pa Yehova,+ ngati mmene anachitira Davide kholo lake.+ 4 Hezekiya ndi amene anachotsa malo okwezeka,+ kugwetsa zipilala zopatulika ndiponso kudula mzati wopatulika.*+ Komanso iye anaphwanyaphwanya njoka yakopa* imene Mose anapanga,+ chifukwa pa nthawiyi Aisiraeli ankafukiza nsembe yautsi kwa njokayo ndipo inkatchedwa fano la njoka yakopa.* 5 Iye ankadalira Yehova+ Mulungu wa Isiraeli. Pa mafumu onse a Yuda amene anakhalapo iye asanakhale mfumu, ngakhalenso amene anakhalapo iye atafa, palibe amene anafanana naye. 6 Hezekiya sanamusiye Yehova+ ndipo anapitiriza kumutsatira. Sanasiye kusunga malamulo amene Yehova analamula Mose. 7 Yehova anali naye ndipo kulikonse kumene ankapita ankachita zinthu mwanzeru. Anagalukira mfumu ya Asuri ndipo ankakana kuitumikira.+ 8 Iye anagonjetsanso Afilisiti+ mpaka ku Gaza ndi madera ake, kuyambira kunsanja ya alonda mpaka kumzinda wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri.*
9 Mʼchaka cha 4 cha Mfumu Hezekiya, chomwenso chinali chaka cha 7 cha Hoshiya+ mwana wa Ela mfumu ya Isiraeli, Salimanesere mfumu ya Asuri anapita kukaukira Samariya ndipo anazungulira mzindawo.+ 10 Asuriwo analanda mzindawo+ patatha zaka zitatu. Anaulanda mʼchaka cha 6 cha Hezekiya, chomwe chinali chaka cha 9 cha Hoshiya mfumu ya Isiraeli. Choncho Samariya analandidwa. 11 Kenako mfumu ya Asuri inatenga Aisiraeli nʼkupita nawo ku Asuri.+ Mfumuyo inakaika Aisiraeliwo ku Hala ndi ku Habori pafupi ndi mtsinje wa Gozani ndiponso mʼmizinda ya Amedi.+ 12 Zimenezi zinachitika chifukwa chakuti Aisiraeliwo sanamvere mawu a Yehova Mulungu wawo, koma anaphwanya pangano lake ndi zonse zimene Mose mtumiki wa Yehova anawalamula.+ Iwo sanamvere kapena kutsatira zimenezi.
13 Mʼchaka cha 14 cha Mfumu Hezekiya, Senakeribu mfumu ya Asuri+ anabwera kudzaukira mizinda yonse ya Yuda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri ndipo analanda mizindayo.+ 14 Choncho Hezekiya mfumu ya Yuda anatumiza uthenga kwa mfumu ya Asuri ku Lakisi, wakuti: “Wolakwa ndine. Siyani kundiukira. Ndikupatsani chilichonse chimene mungandilamule.” Zitatero mfumu ya Asuri inalamula Hezekiya mfumu ya Yuda kuti apereke matalente* 300 a siliva ndi matalente 30 a golide. 15 Choncho Hezekiya anapereka siliva yense amene anali panyumba ya Yehova ndiponso amene anali mosungira chuma cha mʼnyumba ya mfumu.+ 16 Pa nthawi imeneyi Hezekiya mfumu ya Yuda anachotsa zitseko za kachisi+ wa Yehova ndi mafelemu ake, zimene iye anazikuta ndi golide,+ nʼkupereka golideyo kwa mfumu ya Asuri.
17 Kenako mfumu ya Asuri inatuma Tatani,* Rabisarisi* ndi Rabisake* kwa Mfumu Hezekiya ku Yerusalemu.+ Inawatumiza kuchokera ku Lakisi+ ndi gulu lalikulu la asilikali. Iwo anakaima pafupi ndi ngalande yochokera kudziwe lakumtunda, pamsewu waukulu wopita kumalo a wochapa zovala.+ 18 Atayamba kuitana mfumu, kunapita Eliyakimu+ mwana wa Hilikiya amene ankayangʼanira banja lachifumu, Sebina+ mlembi komanso Yowa mwana wa Asafu wolemba zochitika kukakumana nawo.
19 Choncho Rabisake anawauza kuti: “Mukauze Hezekiya kuti, ‘Mfumu yaikulu, mfumu ya Asuri yanena kuti: “Kodi ukudalira chiyani?+ 20 Iwe wanena kuti, ‘Ndili ndi mphamvu komanso njira yabwino yomenyera nkhondoʼ koma mawu amenewa ndi osathandiza. Kodi ukudalira ndani pondigalukira ineyo?+ 21 Ukudalira thandizo la Iguputo,+ bango lophwanyika loti munthu ataligwira kuti alitsamire, lingamucheke mʼmanja. Ndi mmene zilili ndi Farao mfumu ya Iguputo kwa onse omudalira. 22 Ngati mungandiuze kuti, ‘Tikudalira Yehova Mulungu wathu,’+ kodi iyeyo si amene Hezekiya wamuchotsera malo ake okwezeka ndi maguwa ake ansembe+ nʼkuuza Yuda ndi Yerusalemu kuti, ‘Muzigwada patsogolo pa guwa lansembe la ku Yerusalemuliʼ?”’+ 23 Ndiye ubetcherane ndi mbuye wanga mfumu ya Asuri ndipo ine ndikupatsa mahatchi 2,000 kuti tione ngati iweyo ungathe kupeza okwerapo.+ 24 Kodi ungathe bwanji kuthamangitsa bwanamkubwa mmodzi, yemwe ndi mtumiki wotsika kwambiri wa mbuye wanga, pamene iweyo ukuchita kudalira Iguputo kuti akupatse magaleta ndi okwera pamahatchi? 25 Kodi ukuganiza kuti ndabwera kudzawononga malowa popanda chilolezo cha Yehova? Yehova weniweniyo wandiuza kuti, ‘Pita ukamenyane ndi dzikolo ndipo ukaliwononge.’”
26 Atamva zimenezi, Eliyakimu mwana wa Hilikiya, Sebina+ ndi Yowa anauza Rabisake+ kuti: “Chonde lankhulani ndi ife atumiki anu mʼchilankhulo cha Chiaramu*+ chifukwa timachimva. Musalankhule nafe mʼchilankhulo cha Ayuda, kuti anthu amene ali pamakomawa asamve.”+ 27 Koma Rabisake anawayankha kuti: “Kodi mbuye wanga wandituma kuti uthengawu ndidzauze mbuye wanu ndi inuyo basi? Kodi sananditumenso kwa amuna amene akhala pamakomawo, amene adzadye chimbudzi chawo ndi kumwa mkodzo wawo limodzi ndi inuyo?”
28 Kenako Rabisake anaimirira nʼkulankhula mokweza mʼchilankhulo cha Ayuda kuti: “Imvani mawu a mfumu yaikulu, mfumu ya Asuri.+ 29 Mfumuyo yanena kuti, ‘Musalole kuti Hezekiya akupusitseni, chifukwa sangathe kukupulumutsani mʼmanja mwanga.+ 30 Musalole kuti Hezekiya akuchititseni kudalira Yehova, pokuuzani kuti: “Ndithu Yehova atipulumutsa ndipo mzindawu superekedwa mʼmanja mwa mfumu ya Asuri.”+ 31 Musamvere Hezekiya chifukwa mfumu ya Asuri yanena kuti: “Tiyeni tigwirizane zamtendere ndipo ingonenani kuti mwagonja. Mukatero, aliyense azidya zochokera mumtengo wake wa mpesa ndi mumtengo wake wa mkuyu komanso azimwa madzi apachitsime chake, 32 mpaka ine nditabwera kudzakutengani nʼkupita nanu kudziko lofanana ndi lanulo,+ dziko la mbewu ndi la vinyo watsopano, dziko la mkate ndi minda ya mpesa, dziko la mitengo ya maolivi ndiponso la uchi. Mukatero mudzakhalabe ndi moyo. Musamumvere Hezekiya chifukwa akukunamizani pokuuzani kuti, ‘Yehova atipulumutsa.’ 33 Kodi pali mulungu aliyense amene wakwanitsa kupulumutsa anthu ake mʼmanja mwa mfumu ya Asuri? 34 Kodi milungu ya Hamati+ ndi Aripadi ili kuti? Nanga milungu ya Sefaravaimu,+ Hena ndi Iva ili kuti? Kodi yapulumutsa Samariya mʼmanja mwanga?+ 35 Ndi mulungu uti pa milungu yonse ya mayiko, amene wapulumutsa dziko lake mʼmanja mwanga, kuti Yehova athe kupulumutsa Yerusalemu mʼmanja mwanga?”’”+
36 Koma anthuwo anangokhala chete osamuyankha chilichonse, chifukwa mfumu inawalamula kuti: “Musakamuyankhe.”+ 37 Koma Eliyakimu mwana wa Hilikiya amene ankayangʼanira banja lachifumu, Sebina mlembi ndi Yowa mwana wa Asafu wolemba zochitika, anapita kwa Hezekiya atangʼamba zovala zawo ndipo anamuuza zomwe Rabisake ananena.