Salimo
Yamikani Yehova chifukwa iye ndi wabwino.+
Chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.+
2 Ndi ndani amene anganene za ntchito zonse zazikulu za Yehova,
Kapena kulengeza zochita zake zonse zotamandika?+
3 Osangalala ndi anthu amene amachita zinthu mwachilungamo,
Amene amachita zinthu zolungama nthawi zonse.+
4 Ndikumbukireni inu Yehova, pamene mukusonyeza anthu anu kukoma mtima.+
Ndisamalireni ndi kundipulumutsa,
5 Kuti ndisangalale ndi ubwino umene mumasonyeza osankhidwa anu,+
Kuti ndikondwere limodzi ndi mtundu wanu,
Ndiponso kuti ndikutamandeni monyadira pamodzi ndi cholowa chanu.
7 Makolo athu ku Iguputo, sanayamikire* ntchito zanu zodabwitsa.
Sanakumbukire chikondi chanu chokhulupirika chomwe ndi chochuluka,
Koma anapanduka panyanja, pafupi ndi Nyanja Yofiira.+
9 Iye analamula* ndipo Nyanja Yofiira inauma.
Anatsogolera anthu ake kudutsa pakati pa madzi akuya ngati akudutsa mʼchipululu.+
10 Anawapulumutsa mʼmanja mwa anthu amene ankadana nawo+
Ndipo anawawombola mʼmanja mwa mdani.+
15 Mulungu anawapatsa zimene anapempha,
Koma anawagwetsera matenda amene anawachititsa kuti awonde kwambiri.+
17 Kenako dziko lapansi linatseguka ndipo linameza Datani,
Nʼkukwirira anthu onse amene anali kumbali ya Abiramu.+
19 Iwo anapanga mwana wa ngʼombe ku Horebe,
Ndipo anagwadira fano lachitsulo.*+
20 Anasinthanitsa ulemerero wanga
Ndi chifaniziro cha ngʼombe yamphongo yodya udzu.+
21 Iwo anaiwala Mulungu,+ Mpulumutsi wawo,
Amene anachita zinthu zazikulu ku Iguputo,+
22 Amene anachita zodabwitsa mʼdziko la Hamu,+
Amene anachita zochititsa mantha pa Nyanja Yofiira.+
23 Iye anangotsala pangʼono kulamula kuti awonongedwe,
Koma Mose wosankhidwa wake, anamuchonderera*
Kuti asawagwetsere mkwiyo wake wowononga.+
26 Choncho Mulungu anawalumbirira atakweza dzanja lake,
Kuti adzachititsa kuti afere mʼchipululu.+
27 Adzachititsa kuti mbadwa zawo ziphedwe ndi anthu a mitundu ina,
Ndiponso kuwamwaza mʼmayiko osiyanasiyana.+
32 Iwo anamukwiyitsanso pa madzi a ku Meriba,*
Moti Mose sizinamuyendere bwino chifukwa cha anthu amenewa.+
38 Ankakhetsa magazi a anthu osalakwa,+
Magazi a ana awo aamuna komanso a ana awo aakazi,
Amene anawapereka nsembe kwa mafano a ku Kanani.+
Ndipo dzikolo linaipa ndi magazi amene iwo anakhetsa.
39 Iwo anakhala odetsedwa chifukwa cha ntchito zawo.
Anachita uhule ndi milungu ina chifukwa cha zochita zawo.+
40 Choncho mkwiyo wa Yehova unayakira anthu ake,
Ndipo iye anayamba kunyansidwa ndi cholowa chake.
41 Mobwerezabwereza ankawapereka mʼmanja mwa anthu a mitundu ina,+
Kuti anthu amene ankadana nawo aziwalamulira.+
42 Adani awo ankawapondereza,
Ndipo anali pansi pa ulamuliro wawo.
43 Nthawi zambiri ankawapulumutsa,+
Koma iwo ankamupandukira komanso sankamvera,+
Ndipo ankawonongedwa chifukwa cha zolakwa zawo.+
45 Pofuna kuwathandiza iye ankakumbukira pangano lake,
Ndipo ankawamvera chisoni* chifukwa cha chikondi chake chokhulupirika chomwe ndi chachikulu.*+
47 Tipulumutseni inu Yehova Mulungu wathu,+
Ndi kutisonkhanitsa pamodzi kuchokera mʼmitundu ina,+
Kuti titamande dzina lanu loyera,
Komanso kuti tikutamandeni mosangalala.+
Ndipo anthu onse anene kuti, “Ame!”
Tamandani Ya,*