Danieli
2 M’chaka chachiwiri cha ufumu wa Nebukadinezara, Nebukadinezarayo analota maloto.+ Malotowo anamuvutitsa maganizo+ ndipo tulo tinamuthera. 2 Pamenepo mfumuyo inalamula kuti aitane ansembe onse ochita zamatsenga,+ anthu olankhula ndi mizimu, Akasidi* ndi anthu ena ochita zamatsenga kuti adzauze mfumu maloto akewo.+ Anthu amenewa anafika ndi kuima pamaso pa mfumu. 3 Ndiyeno mfumuyo inawauza kuti: “Pali zimene ndalota, ndipo ndikuvutika maganizo kwambiri kuti ndidziwe malotowo.” 4 Pamenepo Akasidi anayankha mfumu m’chinenero cha Chiaramu+ kuti: “Inu mfumu mukhale ndi moyo mpaka kalekale.*+ Tiuzeni ife atumiki anu zimene mwalota ndipo tikumasulirani malotowo.”+
5 Mfumuyo inayankha Akasidiwo kuti: “Ine ndikulamula kuti: Amuna inu mukapanda kundiuza malotowo ndi kuwamasulira, mudzadulidwa nthulinthuli+ ndipo nyumba zanu zidzasanduka zimbudzi za anthu onse.+ 6 Koma mukandiuza malotowo ndi kuwamasulira, ine ndikupatsani mphatso, mphoto ndi ulemerero wochuluka.+ Choncho ndiuzeni malotowo ndipo muwamasulire.”
7 Pamenepo iwo anayankhanso kachiwiri kuti: “Inu mfumu, tiuzeni ife atumiki anu zimene mwalota ndipo ife tikumasulirani malotowo.”
8 Ndiyeno mfumuyo inanena kuti: “Ine ndikudziwa kuti amuna inu mukuzengereza dala chifukwa mwadziwa kuti ine ndalamula zimenezi. 9 Pakuti mukapanda kundiuza malotowo, chilango chija+ sichidzakuphonyani. Koma mwagwirizana kuti mundiuze mawu abodza+ kufikira zinthu zitasintha. Choncho ndiuzeni zimene ndalota. Mukatero, ndidziwa kuti mungathe kumasulira malotowo.”
10 Akasidiwo anayankha mfumuyo kuti: “Palibe munthu padziko lapansi amene angathe kuuza inu mfumu zimene mukufuna, pakuti palibe mfumu yaikulu kapena bwanamkubwa amene anauzapo wansembe wochita zamatsenga kapena munthu wolankhula ndi mizimu kapena Mkasidi kuti achite zimenezi. 11 Zimene inu mfumu mukufuna kuti tichite ndi zovuta, ndipo palibe munthu amene angakuuzeni maloto anu, kupatulapo milungu.+ Komano milunguyo siikhalanso pakati pa anthu.”+
12 Mfumu itamva zimenezi inapsa mtima ndipo inakwiya kwambiri,+ moti inanena kuti amuna onse anzeru a m’Babulo ayenera kuphedwa.+ 13 Lamulo limenelo linaperekedwa, ndipo amuna anzeru anatsala pang’ono kuphedwa, moti anthu anayamba kufunafuna Danieli ndi anzake kuti awaphe.
14 Pa nthawi imeneyo Danieli analankhula mwanzeru ndi mozindikira+ kwa Arioki mkulu wa asilikali olondera mfumu, amene anali atanyamuka kale kuti akaphe amuna anzeru a m’Babulo. 15 Iye anafunsa Arioki mkulu wa asilikali olondera mfumu uja kuti: “Chavuta n’chiyani kuti mfumu ipereke lamulo lokhwima chonchi?” Pamenepo, Arioki anafotokoza nkhani yonse ija kwa Danieli.+ 16 Chotero Danieli anapita kwa mfumu kukapempha kuti imupatse nthawi kuti adzamasulire maloto ake.+
17 Kenako Danieli anabwerera kunyumba kwake ndipo anauza anzake aja, Hananiya, Misayeli ndi Azariya za nkhani imeneyi. 18 Anawauza zimenezi ndi cholinga choti iwo apemphe Mulungu wakumwamba+ kuti awachitire chifundo+ ndi kuwaululira chinsinsi chimenechi,+ kuti Danieli, anzakewo ndi amuna anzeru ena onse a m’Babulo asaphedwe.+
19 Ndiyeno usiku, chinsinsicho chinaululidwa kwa Danieli m’masomphenya.+ Pamenepo Danieli anatamanda+ Mulungu wakumwamba. 20 Iye anati: “Dzina la Mulungu likhale lotamandika+ kuyambira kalekale mpaka kalekale, pakuti nzeru ndi mphamvu ndi zake.+ 21 Iye amasintha nthawi ndi nyengo,+ amachotsa mafumu ndi kuika mafumu,+ amapereka nzeru kwa anthu anzeru ndiponso amachititsa kuti anthu ozindikira adziwe zinthu.+ 22 Amaulula zinthu zozama ndi zinthu zobisika+ ndipo amadziwa zimene zili mu mdima.+ Komanso wazunguliridwa ndi kuwala.+ 23 Ndikukutamandani ndi kukuyamikani,+ inu Mulungu wa makolo anga, chifukwa mwandipatsa nzeru+ ndi mphamvu. Tsopano mwandiuza zimene tinakupemphani, pakuti mwatidziwitsa zimene mfumu inali kufuna.”+
24 Zitatero, Danieli anapita kwa Arioki,+ amene mfumu inali itamutuma kuti akaphe amuna anzeru a m’Babulo.+ Anapita kwa iye n’kumuuza kuti: “Musaphe mwamuna aliyense wanzeru m’Babulo. Ndipititseni kwa mfumu,+ kuti ndikamasulire maloto ake.”
25 Mofulumira, Arioki anapititsa Danieli kwa mfumu ndi kuiuza kuti: “Ndapeza mwamuna wamphamvu pakati pa anthu amene anatengedwa ukapolo+ ku Yuda yemwe angamasulire maloto anu mfumu.” 26 Mfumuyo inafunsa Danieli, amene anali kutchedwa kuti Belitesazara,+ kuti: “Kodi ungathe kundiuza maloto amene ndinalota ndi kuwamasulira?”+ 27 Danieli anayankha mfumuyo kuti: “Chinsinsi chimene inu mfumu mukufuna kudziwa, amuna anzeru, anthu olankhula ndi mizimu, ansembe ochita zamatsenga ndi anthu okhulupirira nyenyezi, alephera kukuuzani.+ 28 Koma kuli Mulungu kumwamba amene ndi Woulula zinsinsi,+ ndipo wakudziwitsani, inu Mfumu Nebukadinezara, zimene zidzachitike m’masiku otsiriza.+ Maloto anu ndi masomphenya amene munaona muli pabedi lanu ndi awa:
29 “Inu mfumu, mutagona pabedi lanu,+ munayamba kuganiza za zimene zidzachitike m’tsogolo, ndipo Mulungu amene ndi Woulula zinsinsi wakudziwitsani zimene zidzachitike.+ 30 Sikuti chinsinsi chimenechi chaululidwa kwa ine chifukwa chakuti ndine wanzeru kuposa munthu wina aliyense ayi,+ koma chaululidwa ndi cholinga chakuti ndikumasulireni malotowo mfumu, ndiponso kuti mudziwe maganizo a mumtima mwanu.+
31 “Inuyo mfumu munaona chifaniziro chinachake chachikulu kwambiri. Chifaniziro chimenechi chinali chitaima patsogolo panu ndipo maonekedwe ake anali ochititsa mantha. Chinali chachikulu ndiponso chowala modabwitsa. 32 Mutu wa chifaniziro chimenechi unali wopangidwa ndi golide wabwino,+ chifuwa chake ndi manja ake zinali zasiliva,+ mimba yake ndi ntchafu zake zinali zamkuwa,+ 33 miyendo yake inali yachitsulo,+ ndipo mapazi ake anali achitsulo chosakanizika ndi dongo.+ 34 Munapitiriza kuchiyang’ana kufikira mwala unadulidwa kuphiri koma osati ndi manja a munthu.+ Mwalawo unamenya chifanizirocho kumapazi ake achitsulo chosakanizika ndi dongo ndipo unawapera.+ 35 Pamenepo chitsulo, dongo, mkuwa, siliva ndi golide, zonsezi zinaphwanyikaphwanyika ndipo zinakhala ngati mankhusu* apamalo opunthirapo mbewu+ m’chilimwe. Mphepo inaziuluza moti sizinaonekenso.+ Koma mwala umene unamenya chifanizirocho unakhala phiri lalikulu ndipo linadzaza dziko lonse lapansi.+
36 “Maloto anu ndi amenewa ndipo kumasulira kwake tikuuzani mfumu.+ 37 Inuyo mfumu, mfumu ya mafumu, inu amene Mulungu wakumwamba wakupatsani ufumu,+ mphamvu, ndi ulemerero, 38 inuyo amene Mulungu wakupatsani+ nyama zakutchire ndi mbalame zam’mlengalenga kulikonse kumene kuli anthu, amene Mulungu wakuikani kukhala wolamulira zonsezo, inuyo ndiye mutu wagolide.+
39 “Pambuyo panu padzabwera ufumu wina+ wotsikirapo kwa inu.+ Kenako padzabweranso ufumu wina wachitatu, wamkuwa, umene udzalamulira dziko lonse lapansi.+
40 “Ufumu wachinayi+ udzakhala wolimba ngati chitsulo.+ Popeza kuti chitsulo chimaphwanya ndi kupera china chilichonse, ufumuwo udzaphwanya ndi kuswa maufumu ena onsewa mofanana ndi chitsulo chimene chimaswa zinthu.+
41 “Popeza munaona kuti mapazi ndi zala zakumiyendo zinali zadongo la woumba mbiya losakanizika ndi chitsulo,+ ufumuwo udzakhala wogawanika,+ koma udzakhala wolimba pa zinthu zina ngati chitsulo. Zimenezi zili choncho chifukwa munaona kuti chitsulocho chinali chosakanizika ndi dongo lonyowa.+ 42 Popeza zala zakumiyendo zinali zachitsulo chosakanizika ndi dongo, pa zinthu zina ufumuwo udzakhala wolimba koma pa zinthu zina udzakhala wosalimba. 43 Popeza munaona chitsulo chosakanizika ndi dongo lonyowa, mbali zake zina zidzasakanizika ndi ana a anthu koma sadzagwirizana monga mmene zilili zosatheka kuti chitsulo chisakanizike bwinobwino ndi dongo.
44 “M’masiku a mafumu amenewo,+ Mulungu wakumwamba+ adzakhazikitsa ufumu+ umene sudzawonongedwa ku nthawi zonse.+ Ufumuwo sudzaperekedwa kwa mtundu wina uliwonse wa anthu,+ koma udzaphwanya ndi kuthetsa maufumu ena onsewo,+ ndipo udzakhalapo mpaka kalekale.+ 45 Zidzakhala choncho chifukwa munaona kuti mwala unadulidwa kuphiri koma osati ndi manja a munthu,+ ndipo unaphwanya chitsulo, mkuwa, dongo, siliva ndi golide.+ Inu mfumu, Mulungu Wamkulu+ wakudziwitsani zimene zidzachitike m’tsogolo.+ Maloto amenewa ndi odalirika ndipo kumasulira kwake ndi kokhulupirika.”+
46 Pamenepo Mfumu Nebukadinezara anagwada ndi kuwerama mpaka nkhope yake pansi, ndipo anapereka ulemu kwa Danieli. Iye analamulanso kuti Danieli apatsidwe mphatso ndipo amufukizire zofukiza zonunkhira.+ 47 Mfumuyo inauza Danieli kuti: “Ndithudi Mulungu wa anthu inu ndi Mulungu wa milungu yonse,+ Ambuye wa mafumu onse+ ndiponso Woulula zinsinsi, chifukwa iwe wakwanitsa kuulula chinsinsi chimenechi.”+ 48 Pa chifukwa chimenechi, mfumu inamukweza pa udindo Danieli+ ndipo inamupatsa mphatso zambiri. Inamuikanso kukhala wolamulira chigawo chonse cha Babulo+ ndiponso wamkulu wa akuluakulu a boma* oyang’anira amuna onse anzeru a m’Babulo. 49 Ndipo Danieli anapempha mfumu kuti iike Sadirake, Mesake ndi Abedinego+ kuti akhale oyang’anira chigawo cha Babulo, ndipo mfumuyo inawaikadi. Koma Danieli anali kutumikira m’nyumba ya mfumu.+