Aheberi
10 Popeza Chilamulo ndicho mthunzi chabe+ wa zinthu zabwino zimene zikubwera osati zinthu zenizenizo, ndiye kuti anthu wamba sangachititse anthu amene amalambira Mulungu kukhala angwiro. Iwo sangathe kuchita zimenezi mwa nsembe zimodzimodzizo zimene amapereka mosalekeza chaka ndi chaka.+ 2 Zikanakhala choncho, kodi nsembezo sakanasiya kuzipereka? Akanasiya chifukwa chakuti anthu ochita utumiki wopatulika, amene akanayeretsedwa kwathunthu kamodzi n’kamodziwo, sakanakhalanso ndi chikumbumtima chakuti ndi ochimwa.+ 3 Koma mosiyana ndi zimenezo, chaka ndi chaka nsembe zimenezi zimawakumbutsa za machimo awo.+ 4 Pakuti n’kosatheka kuti magazi a ng’ombe zamphongo ndi mbuzi achotseretu machimo.+
5 Chotero pobwera m’dziko iye anati: “‘Nsembe ndiponso zopereka simunazifune,+ koma munandikonzera thupi.+ 6 Nsembe zopsereza zathunthu ndi nsembe zamachimo simunazivomereze.’+ 7 Ndiyeno ndinati, ‘Taonani! Ine ndabwera (mumpukutu munalembedwa za ine)+ kudzachita chifuniro chanu, inu Mulungu wanga.’”+ 8 Choyamba atanena kuti: “Nsembe, zopereka, nsembe zopsereza zathunthu, ndi nsembe zamachimo simunazifune kapena kuzivomereza,”+ nsembe zimene zimaperekedwa malinga ndi Chilamulo,+ 9 ananenanso kuti: “Taonani! Ine ndabwera kudzachita chifuniro chanu.”+ Akuchotsa dongosolo loyambalo kuti akhazikitse lachiwiri.+ 10 Mwa “chifuniro”+ chimenecho, tayeretsedwa+ kudzera m’thupi la Yesu Khristu loperekedwa nsembe+ kamodzi+ kokha.
11 Komanso, wansembe aliyense amaima pamalo ake+ kuti achite ntchito yotumikira ena ndi kupereka nsembe zimodzimodzizo mobwerezabwereza,+ popeza zimenezi sizingachotseretu machimo.+ 12 Koma munthu ameneyu anapereka nsembe imodzi yamachimo kwamuyaya,+ ndipo anakhala pansi kudzanja lamanja la Mulungu.+ 13 Kuyambira pamenepo, akuyembekezera kufikira pamene adani ake adzaikidwe monga chopondapo mapazi ake.+ 14 Iye akuchititsa anthu amene akuyeretsedwa kukhala angwiro kwamuyaya,+ kudzera mu nsembe imodzi yokha basi.+ 15 Komanso, mzimu woyera+ nawonso ukuchitira umboni kwa ife, chifukwa utanena kuti: 16 “‘Pangano limene ndidzapanga nawo pambuyo pa pangano loyamba lija ndi ili: Ndidzaika malamulo anga m’mitima yawo ndi kuwalemba m’maganizo mwawo,’ watero Yehova,”+ 17 pambuyo pake ukunenanso kuti: “Ndipo sindidzakumbukiranso machimo awo komanso zochita zawo zosonyeza kusamvera malamulo.”+ 18 Tsopano, pamene zimenezi zakhululukidwa,+ nsembe yamachimo si yofunikanso.+
19 Chotero abale, ndife olimba mtima chifukwa tikugwiritsa ntchito njira yolowera+ m’malo oyera+ kudzera m’magazi a Yesu. 20 Iye ndi amene anatikhazikitsira njira imeneyi monga njira yatsopano ndi yamoyo, yodutsa nsalu yotchinga,+ imene ndi thupi lake.+ 21 Popeza ndife olimba mtima chotero, komanso popeza kuti tili ndi wansembe wamkulu kwambiri woyang’anira nyumba ya Mulungu,+ 22 tiyeni timufikire Mulungu ndi mitima yoona. Tichite zimenezi tilibe chikayikiro chilichonse komanso tili ndi chikhulupiriro, pakuti mitima yathu yayeretsedwa* kuti isakhalenso ndi chikumbumtima choipa,+ ndipo matupi athu asambitsidwa m’madzi oyera.+ 23 Tiyeni tipitirize kulengeza poyera chiyembekezo+ chathu ndipo tisagwedezeke,+ pakuti amene anapereka lonjezo lija ndi wokhulupirika.+ 24 Ndipo tiyeni tiganizirane kuti tilimbikitsane+ pa chikondi ndi ntchito zabwino.+ 25 Tisaleke kusonkhana pamodzi,+ monga mmene ena achizolowezi chosafika pamisonkhano akuchitira. Koma tiyeni tilimbikitsane,+ ndipo tiwonjezere kuchita zimenezi, makamaka pamene mukuona kuti tsikulo likuyandikira.+
26 Pakuti ngati tikuchita machimo mwadala+ pambuyo podziwa choonadi molondola,+ palibe nsembe ina yotsala imene ingaperekedwe chifukwa cha machimo athuwo.+ 27 Koma pali chiyembekezo china choopsa cha chiweruzo,+ ndiponso pali nsanje yoyaka moto imene idzawononge otsutsawo.+ 28 Munthu aliyense amene wanyalanyaza chilamulo cha Mose amafa popanda kumuchitira chifundo, ngati anthu awiri kapena atatu apereka umboni.+ 29 Ndiye kuli bwanji munthu amene wapondaponda+ Mwana wa Mulungu, amene akuona magazi+ a pangano amene anayeretsedwa nawo ngati chinthu wamba, amenenso wanyoza mzimu+ wa Mulungu, yemwe amasonyeza kukoma mtima kwakukulu? Munthu ameneyu akuyenera kulandira chilango chachikulu kwambiri.+ 30 Pakuti timamudziwa amene anati: “Kubwezera ndi kwanga, ndidzabwezera ndine.”+ Ndiponso: “Yehova adzaweruza anthu ake.”+ 31 Kulandira chilango chochokera kwa Mulungu wamoyo n’chinthu choopsa.+
32 Komabe, pitirizani kukumbukira masiku akale. Mutalandira kuwala kochokera kwa Mulungu m’masiku amenewo,+ munapirira mayesero aakulu ndi masautso.+ 33 Nthawi zina munali kupirira potonzedwa ndi posautsidwa poyera ngati chionetsero m’bwalo la masewera.+ Ndipo nthawi zina munali kupirira pamene munamva zowawa limodzi ndi ena amene anali kukumana ndi zimenezo.+ 34 Pakuti munasonyeza chifundo kwa amene anali m’ndende, ndipo munalola mokondwa kuti katundu wanu alandidwe,+ podziwa kuti inuyo muli ndi chuma chabwino kuposa pamenepo ndiponso chokhalitsa.+
35 Chotero, musataye ufulu wanu wa kulankhula,+ umene udzabweretse mphoto yaikulu kwambiri.+ 36 Pakuti mukufunika kupirira,+ kuti mutachita chifuniro cha Mulungu,+ mudzalandire zimene Mulungu walonjeza.+ 37 Pakuti “kwatsala kanthawi kochepa kwambiri,”+ ndipo “amene akubwerayo afika ndithu, sachedwa ayi.”+ 38 “Koma wolungama wanga adzakhala ndi moyo mwa chikhulupiriro chake,”+ ndipo “ngati wabwerera m’mbuyo, ine sindikondwera naye.”+ 39 Tsopano, ife si mtundu wa anthu obwerera m’mbuyo kupita kuchiwonongeko,+ koma mtundu wa anthu okhala ndi chikhulupiriro chosunga moyo.+