Aheberi
11 Chikhulupiriro+ ndicho chiyembekezo chotsimikizika cha zinthu zoyembekezeredwa,+ umboni wooneka wa zinthu zenizeni, ngakhale kuti n’zosaoneka.+ 2 Pakuti mwa chikhulupiriro, anthu a nthawi zakale anali ndi umboni wakuti Mulungu akukondwera nawo.+
3 Mwa chikhulupiriro, timazindikira kuti mwa mawu a Mulungu, nthawi* zosiyanasiyana+ anaziika m’malo mwake,+ moti zimene zikuoneka zatuluka m’zinthu zosaoneka.+
4 Mwa chikhulupiriro, Abele anapereka kwa Mulungu nsembe yamtengo wapatali kuposa ya Kaini.+ Ndipo mwa chikhulupirirocho, anachitiridwa umboni kuti anali wolungama, pakuti Mulungu anachitira umboni+ kuti walandira mphatso zakezo. Komanso mwa chikhulupiriro chimenecho, ngakhale kuti anafa, iye akulankhulabe.+
5 Mwa chikhulupiriro, Inoki+ anasamutsidwa kuti asafe mozunzika, moti sanapezeke kwina kulikonse chifukwa Mulungu anamusamutsa.+ Pakuti asanasamutsidwe, Mulungu anamuchitira umboni kuti akukondwera naye.+ 6 Ndiponso, popanda chikhulupiriro+ n’zosatheka kukondweretsa Mulungu.+ Pakuti aliyense wofika kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti iye alikodi,+ ndi kuti amapereka mphoto+ kwa anthu omufunafuna ndi mtima wonse.+
7 Mwa chikhulupiriro, Nowa+ atachenjezedwa ndi Mulungu za zinthu zimene zinali zisanaoneke,+ anasonyeza kuopa Mulungu ndipo anamanga chingalawa+ kuti banja lake lipulumukiremo. Mwa chikhulupiriro chimenecho, anatsutsa dziko,+ ndipo anakhala wolandira cholowa cha chilungamo,+ chimene chimabwera ndi chikhulupiriro.
8 Mwa chikhulupiriro, Abulahamu+ ataitanidwa, anamvera ndi kupita kumalo amene anali kuyembekezera kuwalandira monga cholowa. Iye anapitadi, ngakhale sanadziwe kumene anali kupita.+ 9 Mwa chikhulupiriro, anakhala monga mlendo m’dziko la lonjezo ngati kuti akukhala m’dziko lachilendo.+ Ndipo anali kukhala m’mahema+ pamodzi ndi Isaki+ ndi Yakobo,+ anzake olandira nawo limodzi lonjezolo.+ 10 Pakuti anali kuyembekezera mzinda+ wokhala ndi maziko enieni, mzinda umene Mulungu ndiye anaumanga ndi kuupanga.+
11 Mwa chikhulupiriro, Sara+ nayenso analandira mphamvu yokhala ndi pakati* ngakhale kuti anali atapitirira zaka zobereka,+ chifukwa anaona kuti wolonjezayo ndi wokhulupirika.+ 12 Choteronso, kuchokera mwa mwamuna mmodzi,+ amene anali ngati wakufa,+ kunabadwa ana ochuluka ngati nyenyezi zakumwamba komanso osawerengeka ngati mchenga wa m’mbali mwa nyanja.+
13 Onsewa anafa ali ndi chikhulupiriro,+ ngakhale kuti sanaone kukwaniritsidwa kwa malonjezowo.+ Koma anawaona ali patali+ ndi kuwalandira, ndipo analengeza poyera kuti iwo anali alendo ndi osakhalitsa m’dzikolo.+ 14 Pakuti onena zinthu zimenezi amapereka umboni wakuti akufunafuna mwakhama malo awoawo.+ 15 Koma akanakhala kuti anali kumangokumbukira malo amene anachokera,+ mpata wobwerera akanakhala nawo.+ 16 Koma tsopano akufunitsitsa malo abwino koposa, amene ndi malo akumwamba.+ Pa chifukwa chimenechi, Mulungu sachita nawo manyazi kuti azimuitana monga Mulungu wawo,+ pakuti iye wawakonzera mzinda.+
17 Mwa chikhulupiriro, pamene Abulahamu anayesedwa,+ zinali ngati wapereka kale Isaki nsembe. Choncho munthu ameneyu, amene analandira malonjezo mokondwera, anali wokonzeka kupereka nsembe mwana wake wobadwa yekha.+ 18 Anali wokonzeka kuchita zimenezo ngakhale kuti anali atauzidwa kuti: “Amene adzatchedwa ‘mbewu yako’ adzachokera mwa Isaki.”+ 19 Koma anadziwa kuti Mulungu ali ndi mphamvu zomuukitsa kwa akufa.+ Ndipo iye anamulandiradi kuchokera kwa akufa m’njira ya fanizo.+
20 Mwa chikhulupiriro, Isaki nayenso anadalitsa Yakobo+ ndi Esau,+ pa nkhani yokhudza zinthu zimene zinali kubwera.
21 Mwa chikhulupiriro, Yakobo ali pafupi kufa,+ anadalitsa ana aamuna a Yosefe mmodzimmodzi,+ ndipo analambira Mulungu atatsamira pamutu wa ndodo yake.+
22 Mwa chikhulupiriro, Yosefe atayandikira mapeto a moyo wake, anatchula za kusamuka+ kwa ana a Isiraeli, ndipo anapereka lamulo lokhudza mafupa ake.+
23 Mwa chikhulupiriro, Mose atabadwa, makolo ake anamubisa kwa miyezi itatu,+ chifukwa anaona kuti mwanayo anali wokongola.+ Iwo sanaope lamulo+ la mfumu. 24 Mwa chikhulupiriro, Mose atakula+ anakana kutchedwa mwana wa mwana wamkazi wa Farao,+ 25 ndipo anasankha kuzunzidwa pamodzi ndi anthu a Mulungu, m’malo mochita zinthu zosangalatsa koma zosakhalitsa zauchimo. 26 Iye anachita zimenezi chifukwa anaona kutonzedwa kwake monga Wodzozedwa* kukhala chuma chochuluka+ kuposa chuma cha Iguputo, pakuti anayang’anitsitsa pamphoto imene adzalandire.+ 27 Mwa chikhulupiriro anachoka mu Iguputo,+ koma osati chifukwa choopa mfumu ayi,+ pakuti anapitiriza kupirira moleza mtima ngati kuti akuona Wosaonekayo.+ 28 Mwa chikhulupiriro, iye anachita pasika+ ndiponso anawaza magazi pamafelemu a pakhomo,+ kuti wowonongayo asakhudze ana awo oyamba kubadwa.+
29 Mwa chikhulupiriro, anthu a Mulunguwo anawoloka Nyanja Yofiira ngati kuti akudutsa pamtunda pouma,+ koma Aiguputo atalimba mtima ndi kulowa panyanjapo, nyanjayo inawamiza.+
30 Mwa chikhulupiriro, makoma a Yeriko anagwa, atawazungulira masiku 7.+ 31 Mwa chikhulupiriro, Rahabi+ hule lija, sanawonongedwe limodzi ndi anthu amene anachita zinthu mosamvera, chifukwa iye analandira azondi mwamtendere.+
32 Nanga ndinenenso chiyani pamenepa? Nthawi indichepera kuti ndipitirize kufotokoza za Gidiyoni,+ Baraki,+ Samisoni,+ Yefita,+ Davide,+ komanso Samueli+ ndi aneneri enanso.+ 33 Mwa chikhulupiriro, anthu amenewa anagonjetsa maufumu pa nkhondo,+ anachita chilungamo,+ analandira malonjezo+ ndiponso anatseka mikango pakamwa.+ 34 Anagonjetsa mphamvu ya moto,+ anathawa lupanga,+ anali ofooka koma anapatsidwa mphamvu,+ analimba mtima pa nkhondo,+ ndiponso anagonjetsa magulu ankhondo a mayiko ena.+ 35 Akazi analandira akufa awo amene anauka kwa akufa.+ Koma anthu ena anazunzidwa chifukwa sanalole kusiya chikhulupiriro chawo kuti amasulidwe. Iwo anachita zimenezi kuti adzauke kwa akufa, komwe ndi kuuka kwabwino kwambiri. 36 Ena analandira mayesero awo mwa kutonzedwa ndi kukwapulidwa, komanso kuposa pamenepo, mwa maunyolo+ ndi ndende.+ 37 Anaponyedwa miyala,+ anayesedwa,+ anachekedwa pakati ndi macheka, anaphedwa+ mwankhanza ndi lupanga, anayendayenda atavala zikopa za nkhosa+ ndi zikopa za mbuzi pamene anali osowa,+ pamene anali m’masautso+ komanso pamene anali kuzunzidwa.+ 38 Iwo anali abwino kwambiri, osayenera kukhala m’dziko lotereli. Anayenda uku ndi uku m’zipululu, m’mapiri, m’mapanga,+ ndi m’maenje a dziko lapansi.
39 Komabe onsewa, ngakhale kuti anachitiridwa umboni chifukwa cha chikhulupiriro chawo, sanaone kukwaniritsidwa kwa lonjezolo.+ 40 Zinatero chifukwa chakuti Mulungu anaoneratu chinthu chabwino kwambiri+ choti atipatse,+ kuti iwo+ asakhale angwiro+ popanda ife.+