Kalata Yopita kwa Aheberi
10 Popeza Chilamulo chimangochitira chithunzi+ zinthu zabwino zimene zikubwera+ ndipo si zinthu zenizenizo, sichingachititse* amene amalambira Mulungu kukhala angwiro pogwiritsa ntchito nsembe zimene amapereka mosalekeza chaka chilichonse.+ 2 Zikanakhala choncho, kodi nsembezo sakanasiya kuzipereka? Akanasiya chifukwa zikanakhala kuti anthu ochita utumiki wopatulikawo ayeretsedwa, sakanakhalanso ndi chikumbumtima chakuti ndi ochimwa. 3 Koma mosiyana ndi zimenezo, chaka chilichonse nsembe zimenezi zimawakumbutsa za machimo awo.+ 4 Chifukwa nʼzosatheka kuti magazi a ngʼombe zamphongo ndi mbuzi achotseretu machimo.
5 Choncho atabwera padzikoli iye anati: “‘Nsembe zanyama komanso nsembe zina simunazifune, koma munandikonzera thupi. 6 Nsembe zopsereza zathunthu ndi nsembe zamachimo simunazivomereze.’+ 7 Ndiyeno ine ndinati, ‘Taonani! Ine ndabwera (mumpukutu munalembedwa za ine) kudzachita chifuniro chanu, inu Mulungu wanga.’”+ 8 Atanena kuti: “Nsembe zanyama, nsembe zopsereza zathunthu, nsembe zamachimo ndiponso nsembe zina simunazifune kapena kuzivomereza,” zomwe ndi nsembe zoperekedwa mogwirizana ndi Chilamulo. 9 Ananenanso kuti: “Taonani! Ine ndabwera kudzachita chifuniro chanu.”+ Akuchotsa dongosolo loyambalo kuti akhazikitse lachiwiri. 10 Tayeretsedwa ndi “chifuniro” chimenecho,+ kudzera mʼthupi la Yesu Khristu limene analipereka nsembe kamodzi kokha.+
11 Komanso, wansembe aliyense amaima pamalo ake kuti achite utumiki wopatulika+ ndiponso kuti apereke nsembe zimodzimodzizo mobwerezabwereza,+ zimene sizingachotseretu machimo.+ 12 Koma munthu ameneyu anapereka nsembe imodzi yamachimo yothandiza mpaka kalekale, ndipo anakhala kudzanja lamanja la Mulungu.+ 13 Kuyambira nthawi imeneyo, akudikira mpaka pamene adani ake adzaikidwe kuti akhale chopondapo mapazi ake.+ 14 Kudzera mu nsembe imodzi yokha, iye akuchititsa anthu amene akuyeretsedwa kukhala angwiro+ mpaka kalekale. 15 Nawonso mzimu woyera ukuchitira umboni kwa ife, chifukwa unanena kuti: 16 “‘Pangano limene ndidzapangane nawo pambuyo pa masiku amenewo ndi ili: Ndidzaika malamulo anga mʼmitima yawo ndipo ndidzawalemba mʼmaganizo awo,’+ akutero Yehova.”* 17 Kenako unanenanso kuti: “Ndipo sindidzakumbukiranso machimo awo komanso zochita zawo zosonyeza kusamvera malamulo.”+ 18 Ndiyeno zimenezi zikakhululukidwa, nsembe yamachimo sikhalanso yofunika.
19 Choncho abale, timalimba mtima kulowa mʼmalo oyera+ chifukwa cha magazi a Yesu. 20 Iye ndi amene anatitsegulira njira imeneyi yomwe ndi yatsopano komanso yamoyo ndipo imadutsa katani yotchingira,+ imene ndi thupi lake. 21 Popeza tili ndi wansembe wamkulu kwambiri woyangʼanira nyumba ya Mulungu,+ 22 tiyeni tifike kwa Mulungu ndi mtima wonse komanso tili ndi chikhulupiriro chonse, chifukwa mitima yathu yayeretsedwa* kuti tisakhalenso ndi chikumbumtima choipa,+ ndipo matupi athu asambitsidwa mʼmadzi oyera.+ 23 Tiyeni tipitirize kulengeza poyera chiyembekezo chathu ndipo tisagwedezeke,+ chifukwa amene watilonjeza ndi wokhulupirika. 24 Ndipo tiyeni tiganizirane* kuti tilimbikitsane pa nkhani yosonyezana chikondi ndiponso kuchita zabwino.+ 25 Tisasiye kusonkhana pamodzi,+ ngati mmene ena achizolowezi chosafika pamisonkhano akuchitira. Koma tiyeni tilimbikitsane+ ndipo tizichita zimenezi kwambiri, makamaka panopa pamene mukuona kuti tsikulo likuyandikira.+
26 Ngati tikuchita machimo mwadala pambuyo podziwa choonadi molondola,+ palibenso nsembe ina imene ingaperekedwe chifukwa cha machimo athuwo.+ 27 Koma pali chiyembekezo china choopsa cha chiweruzo, ndiponso mkwiyo woyaka moto umene udzawononge otsutsawo.+ 28 Munthu aliyense amene wanyalanyaza Chilamulo cha Mose amafa popanda kumuchitira chifundo, ngati anthu awiri kapena atatu apereka umboni.+ 29 Ndiye kuli bwanji munthu amene wapondaponda Mwana wa Mulungu, amene akuona magazi a pangano amene anayeretsedwa nawo ngati chinthu wamba,+ amenenso wanyoza mzimu umene Mulungu amasonyezera kukoma mtima kwakukulu?+ Munthu ameneyu akuyenera kulandira chilango chachikulu kwambiri. 30 Popeza tikumudziwa amene anati: “Kubwezera ndi kwanga, ndidzabwezera ndine.” Amenenso anati: “Yehova* adzaweruza anthu ake.”+ 31 Kupatsidwa chilango ndi Mulungu wamoyo nʼkoopsa.
32 Komabe, pitirizani kukumbukira masiku akale. Paja mutalandira kuwala kochokera kwa Mulungu,+ munakumana ndi mavuto aakulu. 33 Nthawi zina munkanyozedwa ndiponso kuzunzidwa pagulu* ndipo nthawi zina munkathandiza anthu ena amene ankakumana ndi mavuto ngati amenewa. 34 Munkachitira chifundo anthu amene anali mʼndende, ndipo munkasangalalabe ngakhale katundu wanu akulandidwa,+ podziwa kuti muli ndi chuma chabwino kwambiri ndiponso chokhalitsa.+
35 Choncho, musasiye kukhala olimba mtima* chifukwa mudzalandira mphoto yaikulu kwambiri.+ 36 Mukufunika kukhala opirira+ komanso kuchita chifuniro cha Mulungu kuti mudzalandire zimene Mulunguyo walonjeza. 37 “Kwatsala kanthawi kochepa”+ ndipo “amene akubwerayo afika ndithu, sachedwa.”+ 38 “Koma wolungama wanga adzakhala ndi moyo chifukwa cha chikhulupiriro chake,”+ ndipo “ngati angabwerere mʼmbuyo, ine sindikondwera naye.”+ 39 Ife sitili mʼgulu la anthu obwerera mʼmbuyo kupita kuchiwonongeko,+ koma ndife anthu okhala ndi chikhulupiriro chomwe chingatithandize kudzapeza moyo.